Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Anthu Osakhalitsa M’dzikoli” Ndi Ogwirizana Polambira Mulungu

“Anthu Osakhalitsa M’dzikoli” Ndi Ogwirizana Polambira Mulungu

“Anthu ochokera kwina adzakhala olima minda yanu ndi osamalira minda yanu ya mpesa. Inuyo mudzatchedwa ansembe a Yehova.”—YES. 61:5, 6.

1. Kodi anthu ena amaona bwanji alendo? Koma n’chifukwa chiyani zimenezi si zabwino?

MONGA tinaonera m’nkhani yapita ija, anthu ena amanyoza ndiponso kudana ndi anthu ochokera kwina. Koma n’chipongwe kuganiza kuti anthu ochokera kudziko lina ndi otsika poyerekezera ndi anthu a m’dziko lathu. Komanso kuganiza choncho kumasonyeza kuti ndife operewera nzeru. Buku lina lofotokoza za mitundu ya anthu limanena kuti: “Baibulo limanena zoona kuti anthu a mitundu yonse ndi apachibale.” Ngakhale anthu apachibale atakhala osiyana kwambiri, amakhalabe pachibale basi.

2, 3. Kodi Yehova amaona bwanji alendo?

2 Kulikonse kumene tingakhale kumapezeka alendo. Ndi mmenenso zinalili ndi Aisiraeli akale. Yehova anachita nawo pangano la Chilamulo choncho anali pa ubwenzi wapadera ndi iye. Koma ankauzidwa kuti azilemekeza ndiponso kukomera mtima anthu a mitundu ina. Chimenechitu ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa ife. Akhristu oona sayenera kukhala okondera kapena atsankho. N’chifukwa chiyani tikutero? Mtumwi Petulo ananena kuti: “Ndazindikira ndithu kuti Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”—Mac. 10:34, 35.

3 Alendo amene ankakhala pakati pa Aisiraeli ankapindula. Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova amakonda alendo ndipo n’zimene mtumwi Paulo ananena pa nthawi inayake. Iye analemba kuti: “Kodi iye ndi Mulungu wa Ayuda okha? Kodi salinso Mulungu wa anthu a mitundu ina? Inde, iye alinso Mulungu wa anthu a mitundu ina.”—Aroma 3:29; Yow. 2:32.

4. N’chifukwa chiyani tinganene kuti mu “Isiraeli wa Mulungu” mulibe mlendo?

4 Mulungu atachita pangano latsopano ndi Akhristu odzozedwa, mtundu wa Aisiraeli sunakhalenso naye pa ubwenzi wapadera. M’malomwake, Akhristu odzozedwawa anakhala “Isiraeli wa Mulungu.” (Agal. 6:16) Paulo ananena kuti mu mtundu umenewu simudzakhala “Mgiriki kapena Myuda, kudulidwa kapena kusadulidwa, mlendo, Msukuti, kapolo, kapena mfulu, koma Khristu ndiye zinthu zonse ndipo ali mwa onse.” (Akol. 3:11) Choncho tinganene kuti palibe amene angatchedwe mlendo mu mpingo wachikhristu.

5, 6. (a) N’chifukwa chiyani anthu ena akhoza kudabwa akawerenga Yesaya 61:5, 6? (b) Kodi “ansembe a Yehova” ndiponso “anthu ochokera kwina” otchulidwa ndi Yesaya ndi ndani? (c) Kodi magulu awiriwa amagwira limodzi ntchito iti?

5 Koma ena angadabwe ndi ulosi wa pa Yesaya chaputala 61 umene umakwaniritsidwa mu mpingo wachikhristu. Pa vesi 6, timawerenga za anthu odzatumikira monga “ansembe a Yehova.” Koma vesi 5 limanena za “anthu ochokera kwina,” kapena kuti alendo, amene azidzagwira ntchito mogwirizana ndi “ansembe.” Ndiyeno kodi mawu amenewa akutanthauza chiyani?

6 “Ansembe a Yehova” akuimira Akhristu odzozedwa amene ali m’gulu la “kuuka koyamba.” Iwo adzatumikira monga “ansembe a Mulungu ndi a Khristu, ndipo adzalamulira monga mafumu limodzi naye zaka 1,000.” (Chiv. 20:6) Koma palinso Akhristu ena okhulupirika ambirimbiri amene akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi. Iwo amagwirizana ndiponso kugwira ntchito limodzi ndi odzozedwawa. Koma popeza sali mu “Isiraeli wa Mulungu” tinganene kuti iwo ndi anthu ochokera kwina kapena kuti alendo. Iwo amasangalala kutumikira limodzi ndi “ansembe a Yehova” ndipo amagwira ntchito monga “olima minda” ndi ‘osamalira minda ya mpesa.’ Amathandiza odzozedwa kupereka ulemerero kwa Mulungu pogwira ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa. Odzozedwa limodzi ndi “nkhosa zina” amaphunzitsa anthu choonadi komanso kuwathandiza mwachikondi kuti azitsatira zimene akuwaphunzitsazo.—Yoh. 10:16.

NDIFE “OSAKHALITSA M’DZIKOLI” NGATI ABRAHAMU

7. Kodi Akhristu masiku ano amafanana bwanji ndi Abulahamu komanso anthu ena okhulupirika akale?

7 Monga taonera m’nkhani yapita ija, Akhristu oona ali ngati alendo, kapena kuti anthu osakhalitsa m’dziko la Satana loipali. Iwo amafanana ndi anthu okhulupirika akale monga Abulahamu. Ponena za anthuwo, Baibulo limati: “Iwo anali alendo ndi osakhalitsa m’dzikolo.” (Aheb. 11:13) Kaya chiyembekezo chathu ndi chotani, tili ndi mwayi wokhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ngati mmene zinalili ndi Abulahamu. Yakobo anati: “‘Abulahamu anakhulupirira mwa Yehova, ndipo anaonedwa ngati wolungama,’ choncho anatchedwa ‘bwenzi la Yehova.’”—Yak. 2:23.

8. Kodi Yehova analonjeza chiyani Abulahamu? Nanga Abulahamu ankaona bwanji lonjezolo?

8 Mulungu analonjeza kuti kudzera mwa Abulahamu ndi ana ake, mitundu yonse ya anthu idzadalitsidwa, osati mtundu umodzi wokha. (Werengani Genesis 22:15-18.) Ngakhale kuti zimene Mulungu analonjezazo zidzakwaniritsidwa m’tsogolo, Abulahamu ankazikhulupirira ndi mtima wonse. Nthawi yambiri ya moyo wake, Abulahamu ankangokhalira kusamuka. Koma nthawi yonseyo, sanasiye kukhala bwenzi la Yehova.

9, 10. (a) Kodi tingatsanzire Abulahamu m’njira ziti? (b) Kodi tingagwire nawo ntchito iti?

9 Ngakhale kuti sankadziwa nthawi imene lonjezolo lidzakwaniritsidwe, Abulahamu ankakondabe Yehova ndipo ankadzipereka kwa iye. Iye sanaiwale kuti ndi wosakhalitsa m’dzikoli ndipo sanaganize zomanga maziko pamalo enaake. (Aheb. 11:14, 15) Tingachite bwino kwambiri kutsanzira Abulahamu ndipo tizikhala moyo wosalira zambiri. Tizipewa kufunafuna chuma, kutchuka kapena ntchito yapamwamba. Si nzeru kufunafuna moyo umene timaona ngati ndi wabwino m’dziko limene latsala pang’ono kuthali. Kutaya nthawi ndi zinthu zosakhalitsa n’kosathandiza. Mofanana ndi Abulahamu, tikuyembekezera zinthu zabwino kwambiri. Tiyenera kukhala oleza mtima n’kumadikira nthawi imene zinthu zimene talonjezedwa zidzachitike.—Werengani Aroma 8:25.

10 Yehova akuitanabe anthu a mitundu yonse kuti adalitsidwe kudzera mu mbewu ya Abulahamu. “Ansembe a Yehova,” omwe ndi odzozedwa, komanso nkhosa zina, zomwe ndi “anthu ochokera kwina,” akugwira nawo ntchito yoitana anthu padziko lonse m’zinenero zoposa 600.

MUZIKONDA ANTHU A MAYIKO ENA

11. Kodi pemphero la Solomo linasonyeza kuti anthu a mitundu ina ali ndi mwayi wotani?

11 Popereka kachisi kwa Yehova mu 1026 B.C.E., Solomo anapereka pemphero losonyeza kuti anthu a mitundu yonse ndi olandiridwa kudzatamanda nawo Yehova. Zimenezi n’zogwirizana ndi zimene Yehova analonjeza Abulahamu. M’pempherolo, Solomo anati: “Komanso mlendo amene sali mmodzi wa anthu anu Aisiraeli, amene wabwera kuchokera kudziko lakutali chifukwa cha dzina lanu (popeza adzamva za dzina lanu lalikulu, za dzanja lanu lamphamvu ndi mkono wanu wotambasuka), ndipo wabwera n’kupemphera atayang’ana nyumba ino, inuyo mumve muli kumwamba, malo anu okhala okhazikika, ndipo muchite mogwirizana ndi zonse zimene mlendoyo wakupemphani. Mutero n’cholinga choti anthu a mitundu yonse ya padziko lapansi adziwe dzina lanu, kuti akuopeni mofanana ndi mmene anthu anu Aisiraeli amachitira.”—1 Maf. 8:41-43.

12. N’chifukwa chiyani Mboni za Yehova zimakhala ngati alendo?

12 Munthu akapita kudera lina kapena kudziko lina, amakakhala mlendo. Mboni za Yehova zili ngati alendo. Iwo amakhala m’mayiko osiyanasiyana koma ali ku mbali ya Ufumu wa Mulungu wolamulidwa ndi Yesu Khristu. N’chifukwa chake salowerera ndale ngakhale kuti anthu ena sasangalala ndi zimenezi.

13. (a) Kodi tingatani kuti tisamaone ena ngati alendo? (b) Kodi poyambirira, Yehova ankafuna kuti anthu ena azikhala alendo? Fotokozani.

13 Nthawi zambiri alendo amadziwika chifukwa cha chilankhulo, chikhalidwe, maonekedwe kapena kavalidwe kawo. Koma sasiyana ndi anthu a m’mayiko enawo pa zinthu zina zofunika kwambiri. Choncho, munthu amatchedwa mlendo chifukwa chakuti amangosiyana ndi ena m’njira zina. Ngati titasiya kuganizira zinthu zimenezi, mwina sitingamuonenso ngati mlendo. Padziko lonse pakanakhala boma limodzi, palibe amene akanakhala mlendo m’dzikoli. Poyambirira, Yehova ankafuna kuti anthu onse azikhala ngati banja limodzi lolamulidwa ndi iyeyo. Kodi zoterezi zingachitike m’dzikoli panopa?

14, 15. Kodi gulu la Mboni za Yehova limaona bwanji anthu?

14 M’dzikoli anthu ambiri ndi odzikonda ndipo amaganiza kuti dziko lawo ndi labwino kwambiri kuposa mayiko ena. N’zoona kuti kusiya tsankho n’kovuta. Koma zimakhala zosangalatsa kuona anthu amene amakonda anthu a mitundu yonse. Munthu wina amene anayambitsa tchanelo cha TV chotchedwa CNN, dzina lake Ted Turner, anagwira ntchito limodzi ndi anthu aluso ochokera m’mayiko osiyanasiyana. Iye anati: “Ndinapindula kwambiri kugwira ntchito ndi anthu amenewa. Ndinasiya kuona anthu ochokera m’mayiko ena ngati ‘alendo.’ Ndinkangowaona ngati nzika zinzanga za padziko lapansi. Ndinakhazikitsa lamulo loti tisamatchule munthu aliyense kuti ‘mlendo’ pa tchanelo chathu kapena m’maofesi athu.”

15 Padziko lonse, gulu la Mboni za Yehova lokha ndi limene limaona anthu mmene Yehova amawaonera. Chifukwa chophunzira kuona anthu m’njira imeneyi, iwo sasankha anthu a m’mayiko ena. Iwo sakayikira kapena kudana ndi anthu a mitundu ina. M’malomwake, amasangalala kukhala ndi anthu amene akusiyana nawo maonekedwe komanso maluso. Kodi inuyo mumamva bwanji mukaganizira zimene zimachitika m’gulu la Mboni za Yehova komanso mmene zakuthandizirani kugwirizana ndi anthu ena?

DZIKO LOPANDA ALENDO

16, 17. Kodi mudzamva bwanji malemba a Chivumbulutso 16:16 ndi Danieli 2:44 akadzakwaniritsidwa?

16 Posachedwapa, Yesu Khristu adzamenya nkhondo ndi mitundu yonse yodana ndi ulamuliro wa Mulungu. Nkhondo imeneyi ‘m’Chiheberi imatchedwa Haramagedo.’ (Chiv. 16:14, 16; 19:11-16) Zaka zoposa 2,500 zapitazo, mneneri Danieli anauziridwa kulemba zimene zidzachitikire maboma a anthu amene amatsutsana ndi cholinga cha Mulungu. Iye analemba kuti: “M’masiku a mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse. Ufumuwo sudzaperekedwa kwa mtundu wina uliwonse wa anthu, koma udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo, ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.”—Dan. 2:44.

17 Kodi inu mudzamva bwanji zimenezi zikadzachitika? Malire a mayiko, amene amachititsa kuti tikayenda tizikhala alendo, sadzakhalaponso. N’zoona kuti anthu azidzasiyanabe, koma zimenezi zidzangosonyeza kuti Mulungu analenga zinthu zosiyanasiyana m’njira yosangalatsa. Chiyembekezo chosangalatsa chimenechi chiyenera kutilimbikitsa kutamanda ndiponso kulemekeza kwambiri Mlengi wathu, Yehova Mulungu.

Kodi mukuyembekeza nthawi imene sipadzakhalanso malire a mayiko ndipo aliyense sadzakhala mlendo?

18. N’chiyani chikusonyeza kuti Mboni za Yehova siziganizira za kusiyana mitundu ndi mayiko?

18 Kodi kuganizira kuti zimenezi zidzachitika, n’kukhulupirira za m’maluwa? Ayi ndithu. Zimenezi si nkhambakamwa koma zidzachitikadi. Ngakhale masiku ano, Mboni za Yehova siziganizira kwenikweni za kusiyana mitundu kapena mayiko. Mwachitsanzo, posachedwapa nthambi zina zing’onozing’ono anaziphatikiza pofuna kuchepetsa ntchito yoyang’anira. Zimenezi zathandizanso kuti ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu izigwirika mosavuta. (Mat. 24:14) Pochita zimenezi, sanaganizire malire a mayiko kusiyapo ngati panali malamulo ena a m’mayikowo. Umenewu ndi umboni winanso wosonyeza kuti Yesu Khristu, yemwe ndi wolamulira woikidwa ndi Yehova, akufufuta malire oikidwa ndi anthu. Posachedwapa, iye ‘adzapambana pa nkhondo’ yake.—Chiv. 6:2.

19. Kodi anthu a Yehova akwanitsa kuchita chiyani chifukwa chophunzira choonadi?

19 Mboni za Yehova zimachokera m’mayiko osiyanasiyana ndipo zimalankhula zilankhulo zosiyanasiyana. Koma iwo amayesetsa kuti azilankhula chilankhulo choyera cha choonadi ndipo zimenezi zimawagwirizanitsa mwamphamvu kwambiri. (Werengani Zefaniya 3:9.) Iwo ali ngati banja limodzi lokhala m’dzikoli koma sali mbali ya dziko. Zimenezi zangokhala chiyambi chabe, koma m’dziko latsopano simudzakhala mlendo ngakhale mmodzi. Pa nthawiyo, aliyense adzavomerezadi mfundo ya m’buku limene talitchula kumayambiriro kwa nkhani ino. Paja limati: “Baibulo limanena zoona kuti anthu a mitundu yonse ndi apachibale.”