Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwawerenga mosamala magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:

Kodi tingapewe bwanji kusalankhula bwino?

Choyamba tiyenera kufufuza mtima wathu. M’malo mokayikira m’bale wathu, ndi bwino kudzifufuza mosamala kuti tidziwe zimene zikutipangitsa kumukayikira. Tiyenera kudzifunsa kuti, Kodi ndikumukayikira chifukwa chakuti ndikufuna kuti nditchuke ineyo? Komanso kukayikira ena kumangochititsa zinthu kuipiraipira.​—8/15, tsamba 21.

Kodi Chilamulo chinasonyeza bwanji mmene Mulungu amaonera akazi?

Akazi achiisiraeli anali ndi ufulu wambiri ndiponso mwayi wamaphunziro. Iwo ankalemekezedwa, kupatsidwa ulemu komanso kutetezedwa.​—9/1, tsamba 5-7.

Pamene tsiku la Yehova likuyandikira, kodi tikuyembekezera zochitika ziti?

Anthu adzanena za “bata ndi mtendere.” Mayiko adzaukira ndiponso kuwononga Babulo Wamkulu. Anthu a Mulungu adzaukiridwa. Padzachitika nkhondo ya Aramagedo ndipo kenako Satana ndi ziwanda zake adzaponyedwa kuphompho.​—9/15, tsamba 4.

Kodi kusadziwa nthawi imene mapeto adzafika n’kwabwino pa zifukwa ziti?

Kusadziwa tsiku ndiponso ola la mapeto kumatithandiza kusonyeza zimene zili mumtima mwathu. Kumatipatsa mwayi wokondweretsa mtima wa Mulungu. Kumatilimbikitsa kukhala ndi moyo wosalira zambiri ndiponso kumatithandiza kudalira kwambiri Mulungu ndi Mawu ake. Komanso timatha kuphunzira pa mavuto amene tikukumana nawo ndipo chikhulupiriro chathu chimalimba.​—9/15, tsamba 24-25.

Kodi lemba la Genesis 3:19, tingaligwiritse ntchito bwanji pokambirana ndi munthu amene amakhulupirira kuti Mulungu amalanga anthu kumoto?

Vesili limanena kuti Adamu akadzafa adzabwerera kufumbi osati adzapita kukalangidwa kumoto.​—10/1, tsamba 13.

Kodi “nyenyezi 7” zomwe zili m’dzanja lamanja la Yesu, zotchulidwa pa Chivumbulutso 1:16, 20, zimaimira ndani?

Zimaimira oyang’anira odzozedwa m’mipingo. Koma zingaimirenso oyang’anira onse m’mipingo.​—10/15, tsamba 14.

Kodi banja lingachite bwanji ngati lili ndi ngongole?

Okwatiranawo ayenera kukambirana momasuka komanso mwamtendere za ngongoleyo. Angachite bwino kuonanso mmene bajeti yawo ilili panopa. Zingakhalenso bwino kuona ngati pali njira zina zimene angapezere ndalama kapena kuchepetsa ndalama zimene amaononga. Ayenera kukambirana mmene angabwezere ngongoleyo. Nthawi zina zingakhalenso bwino kukambirana ndi okongozawo kuti agwirizane njira zina zimene angabwezere ngongoleyo. Komabe ndi bwino kumaona ndalama moyenera ndi kuzigwiritsa ntchito bwino. (1 Tim. 6:8)​—11/1, tsamba 19-21.

Kodi Yesu anasonyeza bwanji kudzichepetsa malinga ndi zimene zili pa Yesaya 50:4, 5?

Mavesiwo amafotokoza za munthu ‘wopatsidwa lilime la anthu ophunzitsidwa bwino’ kuti ‘sanatembenukire kwina.’ Yesu anali wodzichepetsa ndipo ankamvetsera mwatcheru zimene Atate ake ankamuphunzitsa. Iye anali wofunitsitsa kuphunzitsidwa ndi Yehova ndipo ankaona bwinobwino mmene Mulungu ankadzichepetsera pochitira chifundo anthu ochimwa.​—11/15, tsamba 11.

Kodi sitampu ya chikumbutso imene boma la Estonia linatulutsa, inasonyeza bwanji kuti Mboni za Yehova zinali zokhulupirika?

Mu 2007, boma la Estonia linatulutsa sitampu yokumbukira anthu amene anazunzidwa ndi ulamuliro wankhanza wa Stalin m’dzikolo. Sitampuyi inali ndi nambala ya 382 yoimira nambala ya Mboni za Yehova ndiponso ana awo amene anatengedwa kupita ku ndende za ku Russia mu 1951.​—12/1, tsamba 27-28.