Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Tisanaphunzire choonadi, tinkafunitsitsa mwana. Choncho ine ndi mkazi wanga tinatsatira njira yochotsa mazira m’mimba mwa mkazi n’kukawaphatikiza ndi umuna. Koma sitinagwiritse ntchito mazira onse amene anali atayamba kukula ndipo otsalawo anasungidwa kuchipatala. Kodi ayenera kupitiriza kuwasunga kapena akhoza kuwataya?

Kusankha zochita pa nkhani ngati imeneyi n’kovuta kwambiri. Banja lililonse lomwe lachita zimenezi lili ndi udindo wosankha zochita zomwe zingalemekeze Yehova. Koma kudziwa bwino za njira yotengera pathupi imeneyi kungathandize banja kuti lisankhe mwanzeru.

Mu 1978, mayi wina wa ku England anabereka mwana m’njira imeneyi. Iye anali woyamba kuchita zimenezi. Mayiyu ankalephera kutenga mimba chifukwa tinjira topita kuchiberekero chake tinatsekeka. Choncho umuna unkalephera kukumana ndi mazira kuti iye akhale ndi mimba. Akuchipatala anachotsa m’mimba mwake dzira lokhwima n’kuliika m’mbale yagalasi kuti aliphatikize ndi umuna wa mwamuna wake. Analola kuti dziralo liyambe kukula kaye ndipo kenako anakaliika m’chiberekero cha mayiyo kuti lipitirize kukula. Nthawi itakwana, anabereka mwana wamkazi.

Mayiko ena akhoza kutsatira njirayi mosiyanasiyana koma mayiko ambiri amachita zotsatirazi: Choyamba, kwa milungu ingapo achipatala amapatsa mkazi mankhwala amphamvu othandiza kuti thupi lake lipange mazira ambiri. Kenako amauza mwamuna kuti apereke umuna wake. Akatero, amaphatikiza umunawo ndi mazira amene anachotsa m’mimba mwa mkaziyo. Pakapita tsiku limodzi kapena masiku angapo, amasankha mosamala kwambiri mazira amene ayamba kukula omwenso akuoneka kuti angapitirize kukula bwinobwino m’mimba. Pa tsiku lachitatu, amatenga mazira awiri kapena atatu amene akuoneka kuti akapitiriza kukula bwino n’kuwaika m’mimba mwa mkaziyo. Dzira limodzi kapena angapo akayamba kukula m’chiberekero, mkaziyu amakhala ndi mimba ndipo pakapita nthawi, amadzabereka. Anthu amalipira ndalama zambiri kuti atenge pathupi m’njira imeneyi.

Nanga bwanji za mazira omwe anatsala aja, ngakhale amene ankaoneka kuti si abwino kwenikweni koma anali atayamba kukula? Akangowasiya, mazirawo akhoza kufa. Koma amawaika m’firiji kuti asafe. Kodi amawasunga chifukwa chiyani? Mazira oyamba aja akakanika kukula, amatenga enawo n’kukawaikanso m’mimba mwa mkazi. Koma amachita zimenezi pa mtengo wotsikirapo. Mofanana ndi banja limene talitchula kumayambiriro kwa nkhani ino, anthu ambiri amavutika kusankha zimene ayenera kuchita ndi mazira amene akusungidwawo. Mwina sangafunenso ana ena. N’kutheka kuti anthuwo akalamba kapena alibe ndalama zochitiranso zimenezi. Mwinanso akuopa kuti mkaziyo angadzabereke ana angapo. * N’kuthekanso kuti mwamuna kapena mkazi m’banjalo wamwalira kapena wina, ngakhale onse awiri, anapeza mabanja ena. N’zoona kuti pali zambiri zoganizira pa nkhaniyi choncho mabanja ena amapitiriza kulipira ndalama kwa zaka zambiri kuti apitirize kuwasungira mazirawo.

Mu 2008, katswiri wina woona za mmene ana amakulira m’chiberekero anafotokoza m’nyuzipepala ina kuti anthu ambiri, amene atsatira njira yotengera pathupi imeneyi yochotsa mazira m’mimba mwa mayi n’kuwaphatikiza ndi umuna, amavutika kwambiri posankha zimene adzachite ndi mazira otsala. Nkhaniyi inati: “M’dzikoli [United States] mazira 400,000 akusungidwa m’mafiriji kuzipatala ndipo chiwerengerochi chikuwonjezeka tsiku lililonse . . . Mazirawo akhoza kugwiritsidwabe ntchito patapita zaka 10 kapena zoposerapo ngati akusungidwa bwinobwino. Koma si mazira onse amene amapitiriza kukula akawachotsa m’firiji.” (The New York Times) Chiganizo chimene tadetsa mawu akechi n’chofunika kuchiganizira. N’chifukwa chiyani tikutero?

Mabanja achikhristu amene atsatira njira yotengera pathupi imeneyi angachite bwino kuganizira nkhani ina imene ingawathandize kusankha zochita. Angaganizire nkhani ya zimene Mkhristu angachite ngati wachibale wake wadwala mwakayakaya matenda oti sangachirenso. Mwina wodwalayo akungokhala pamakina enaake, monga othandizira munthu kupuma. Akhristu oona amalemekeza kwambiri moyo ndipo amafunitsitsa kulandira chithandizo akadwala. Zimenezi zimagwirizana ndi malangizo a pa Ekisodo 20:13 ndi Salimo 36:9. Galamukani! ya Chingelezi ya May 8, 1974 inati: “Akhristu amalemekeza maganizo a Mulungu oona kuti moyo ndi wopatulika. Choncho Mkhristu amene akufuna kumvera mfundo za m’Baibulo sangalole kumalizitsa moyo wa munthu amene akudwala kwambiri chifukwa chomumvera chisoni. Sangatero chifukwa chofuna kutsatira malamulo a boma ndiponso chifukwa cha chikumbumtima chake.” Koma nthawi zina munthu wodwala amakhala moyo chifukwa chongothandizidwa ndi makina moti akachotsedwa pamakinawo munthuyo amafa. Zikatero, achibale a wodwalayo amakhala ndi udindo wosankha kuti munthuyo apitirize kukhala pamakinawo kapena ayi.

N’zoona kuti izi ndi zosiyana ndi banja limene latsatira njira yotengera pathupi imene tikufotokozayi ndipo akuchipatala akuwasungira mazira otsala. Mwina banjali lingasankhe kuti mazirawo achotsedwe m’firiji. Koma akachotsedwa, akhoza kufa. Choncho banjalo liyenera kusankha ngati lingalole zimenezi kapena ayi.—Agal. 6:7.

Popeza mabanja amatsatira njira imeneyi chifukwa chofuna kuti akhale ndi mwana, mwina banja lina lingasankhe kuti mazirawo asungidwebe m’firiji n’cholinga choti lidzawagwiritsenso ntchito m’tsogolo. Koma banja lina lingasankhe kuti mazirawo achotsedwe popeza zili ngati akungosungidwa m’makina. Pa nkhani imeneyi, Akhristu amakhala ndi udindo wotsatira chikumbumtima chawo chophunzitsidwa Baibulo kuti asankhe zimene zingalemekeze Mulungu. Iwo ayenera kusankha zimene sizingavutitse chikumbumtima chawo kapena cha anthu ena.—1 Tim. 1:19.

Akhristu amakhala ndi udindo wotsatira chikumbumtima chawo chophunzitsidwa Baibulo kuti asankhe zimene zingalemekeze Mulungu

Katswiri wina woona za kubereka ananena kuti mabanja ambiri “amada nkhawa ndiponso kuvutika kusankha zochita pa nkhani ya mazira otsala amene akusungidwa.” Iye ananenanso kuti: “Zikuoneka kuti mabanja ambiri amaona kuti palibe njira yabwino imene angasankhe.”

Akhristu oona ayenera kuganizira bwinobwino mbali zonsezi asanasankhe kutsatira njira imeneyi. Baibulo limatilangiza kuti: “Munthu wanzeru aona zoipa, nabisala, koma anthu opusa apitira, nabvutika pomwepo.”—Miy. 22:3, Malembo Oyera.

Pali mwamuna ndi mkazi amene akukhalira limodzi ndipo akuphunzira Baibulo. Iwo akufuna kubatizidwa koma sangakwatirane mwalamulo chifukwa mwamunayo akukhala m’dzikolo popanda chilolezo. Bomalo sililola kuti munthu amene akukhala m’dzikolo popanda chilolezo akwatire. Kodi anthuwa angasaine Chikalata Cholumbira Kukhulupirika mu Ukwati kuti abatizidwe?

Kuchita zimenezi kungaoneke ngati n’kothandiza koma si njira ya m’Malemba yothetsera vuto lawolo. Tikutero chifukwa chakuti vuto lawo silikugwirizana ndi cholinga cha Chikalata Cholumbira Kukhulupirika mu Ukwati. Kuti timvetse zimenezi, tiyeni tione kaye cholinga cha chikalatacho, mmene chiyenera kugwirira ntchito ndiponso mayiko amene angachigwiritse ntchito.

Chikalatachi chimasainidwa ndi mwamuna ndi mkazi amene akukhalira limodzi koma sangakwatirane mwalamulo pa zifukwa zimene tifotokoze m’munsimu. Iwo amasaina pa maso pa mboni. M’chikalata chimenechi, amalonjeza kuti adzakhala okhulupirika mu ukwati ndiponso kuti adzakwatirana mwalamulo zikadzatheka. Iwo akasaina, amalonjeza pa maso pa Mulungu ndi anthu kuti adzakhala okhulupirika mu ukwati. Choncho mpingo umawaona ngati anthu okwatirana movomerezedwa ndi boma.

Kodi Chikalata Cholumbira Kukhulupirika mu Ukwati chimagwiritsidwa ntchito pa chifukwa chiti ndiponso liti? Yehova ndi amene anayambitsa ukwati ndipo amauona kuti ndi wamtengo wapatali kwambiri. Mwana wake ananena kuti: “Chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.” (Mat. 19:5, 6; Gen. 2:22-24) Iye ananenanso kuti: “Aliyense wosiya mkazi wake n’kukwatira wina wachita chigololo, kupatulapo ngati wamusiya chifukwa cha dama.” (Mat. 19:9) Choncho “dama,” kapena kuti chiwerewere, ndi chifukwa chokhacho cha m’Malemba chothetsera ukwati. Mwachitsanzo, ngati mwamuna wachita chigololo, mkazi wake angasankhe kuthetsa ukwati kapena ayi. Ngati wathetsa ndiye kuti ali ndi ufulu wokwatiwanso.

Koma m’mayiko ena, chipembedzo chimene chimaonedwa kukhala chachikulu sichigwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. M’malomwake, chimakaniza kuthetsa ukwati. Choncho m’mayiko amene chipembedzochi ndi champhamvu kwambiri malamulo a mayikowo amaletsa munthu kuthetsa banja ngakhale pa chifukwa chimene Yesu anatchula. M’mbuyomu, zoterezi zinkachitikachitika. M’mayiko ena, boma limalola anthu kuthetsa banja koma zimatenga nthawi yaitali ndipo zimakhala zovuta kwambiri. Zikhoza kutenga zaka zambiri kuti zitheke. Zimakhala ngati chipembedzo kapena boma ‘likuletsa’ zimene Mulungu amavomereza.—Mac. 11:17.

Mwachitsanzo, mwina anthuwo amakhala m’dziko limene limaletsa kuthetsa banja kapena zimakhala zovuta kwambiri kuthetsa kapenanso zimatenga zaka zambiri kuti zitheke. Ngati anthuwo achita zonse zimene angathe kuti athetse banja lakalelo ndipo ali omasuka pa maso pa Mulungu kuti akhoza kukwatiranso, angasaine Chikalata Cholumbira Kukhulupirika mu Ukwati. Limeneli ndi dongosolo lachikondi limene gulu la Yehova limalola m’mayiko ngati amenewa. Koma dongosololi siligwira ntchito m’mayiko ambiri omwe amaloleza kuthetsa ukwati. Siligwiranso ntchito ngakhale m’mayiko amene kuthetsa ukwati kumakhala kodulirapo kapena kovutirapo.

Anthu ena amene amakhala kumene boma sililetsa kuthetsa banja amapempha kuti asaine Chikalata Cholumbira Kukhulupirika mu Ukwati chifukwa chongofuna kuti asamavutike ndi mavuto othetsa banja. Koma iwo samvetsa bwino cholinga cha chikalatachi.

Tsopano tibwerere ku funso lathu lija lokhudza mwamuna ndi mkazi amene akukhalira limodzi koma akufuna kukwatirana mwalamulo. Malinga ndi Baibulo, aliyense ndi womasuka kukwatira chifukwa onse awiri sali pabanja. Sikuti ali ndi vuto lakuti wina akufunikira kuthetsa banja lake lakale ndipo akuletsedwa kuchita zimenezi ndi malamulo a dziko. Choncho iwo sangagwiritse ntchito Chikalata Cholumbira Kukhulupirika mu Ukwati. M’malomwake, vuto lawo n’lakuti mwamunayo akukhala m’dzikolo popanda chilolezo. Pa chifukwa chimenechi, boma silingalole kuti akwatirane. (M’mayiko ambiri, boma limalola anthu kukwatirana ngakhale kuti mwamuna kapena mkazi, kapenanso onse awiri, akukhala m’dzikolo popanda chilolezo.) Ndiyeno kodi anthuwa angachite chiyani? Mwina akhoza kupita kudziko lina kumene angaloledwe kukwatirana mwalamulo. Kapena ngati n’zotheka, akhoza kukwatirana m’dziko lomwelo ngati mwamunayo angachite zofunika kuti akhale ndi chilolezo chokhala m’dzikolo.

Chotero n’zotheka kuti anthuwa achite zogwirizana ndi malamulo a Mulungu komanso a Kaisara. (Maliko 12:17; Aroma 13:1) Iwo akachita zimenezi, m’pamene akhoza kubatizidwa.—Aheb. 13:4.

^ ndime 6 Nanga bwanji ngati kamwanako m’mimba mwa mayiyo kakuoneka kuti sikadzabadwa kabwinobwino, kapenanso ngati zikuoneka kuti adzabereka ana angapo? Zikatero, ena amasankha kuchotsa mimbayo. Amayi amene amatsatira njira yochotsa mazira m’mimba n’kukawaphatikiza ndi umuna, nthawi zambiri amabereka ana awiri, atatu kapena kuposerapo. Zimenezi zimabweretsa mavuto monga kubereka ana masiku asanakwane ndiponso kutaya magazi ambiri pobereka. Chotero mayi amene akuoneka kuti adzabereka ana ambiri amamulimbikitsa kuti asankhe ana oti abereke ndipo enawo awaphe. Kuchita zimenezi n’kuchotsa mimba kwadala ndipo n’chimodzimodzi ndi kupha munthu.—Eks. 21:22, 23; Sal. 139:16.