Kale Lathu
Sewero la Chilengedwe Linali la pa Nthawi Yake
ANTHU ambiri amene anaonera “Sewero la Chilengedwe” ankaona kuti linali losaiwalika. Seweroli linatuluka kutangotsala pang’ono kuti Hitler ayambe kuzunza anthu ku Ulaya ndipo linathandiza kuti Yehova alemekezeke. Koma kodi “Sewero la Chilengedwe” linali chiyani?
Mu 1914, seweroli linatulutsidwa kulikulu la Mboni za Yehova ku Brooklyn, New York ku United States. Sewero limeneli linali la maola 8 ndipo linali lazithunzi komanso mawu. Padziko lonse lapansi, anthu ambiri analionera. Mu 1914 momwemo, anatulutsanso sewero lomweli koma analifupikitsa ndipo linali la mutu wakuti “Eureka Drama.” Koma pofika cha m’ma 1920 seweroli silinkaonekanso bwino chifukwa zithunzi, mafilimu komanso zinthu zina zinali zitawonongeka. Komabe panali anthu ambiri amene ankafunitsitsa kulionera. Mwachitsanzo, anthu a mumzinda wa Ludwigsburg ku Germany anafunsa kuti: “Kodi tidzaoneranso liti Sewero la Chilengedwe lija?” Kodi pamenepa abalewo akanatani?
Kuti athe kupitirizabe kuonetsa seweroli, mu 1920 abale oimira nthambi mumzinda wa Magdeburg ku Germany anagula mafilimu kuchokera ku kampani inayake ya mumzinda wa Paris ku France komanso zithunzi kuchokera mumzinda wa Leipzig ndi Dresden. Zinthu zimenezi anaziphatikiza ndi zithunzi za mu sewero lija zomwe zinali zisanawonongeke.
M’bale Erich Frost, yemwe anali katswiri woimba, anaimba nyimbo zoti zizimveka mu seweroli. Mawu ofotokozera amene anali m’seweroli anawatenga m’buku lachingelezi lakuti Creation (Chilengedwe). N’chifukwa chake seweroli linayamba kutchedwa Sewero la Chilengedwe chifukwa poyamba linkatchedwa Sewero la Pakanema.
Sewero latsopanoli linkatenganso maola 8. Anthu ankaonera madzulo pang’onopang’ono kwa masiku angapo mpaka kulimaliza. Linkafotokoza mogwira mtima za masiku amene Mulungu analenga zinthu. Linkafotokozanso mbiri ya m’Baibulo komanso mbiri yakale ndipo linkasonyeza kuti zipembedzo zalephera kuthandiza anthu. Seweroli linaonetsedwa ku Austria, Germany, Luxemburg, Switzerland ndiponso madera a anthu olankhula Chijeremani.
M’bale Frost anati: “Poonetsa seweroli ndinkauza anzanga, makamaka amene ndinkaimba nawo, kuti pa nthawi yopuma azipereka mabuku athu kwa anthu. Zimenezi zinathandiza kuti tigawire mabuku ambiri kuposa amene tinkagawira kunyumba ndi nyumba.” M’bale Johannes Rauthe ndi amene ankayang’anira ntchito yoonetsa seweroli ku Poland ndi ku Czech Republic. Iye ananena kuti anthu ambiri ankapereka maadiresi awo n’cholinga choti tidzapitenso kukawalalikira. Izi zinathandiza kuti tikhale ndi maulendo obwereza.
Pofika m’ma 1930, nthawi zonse seweroli likamaonetsedwa pankakhala anthu ambiri ndipo aliyense ankangokamba za Mboni za Yehova. Pofika mu 1933 anthu pafupifupi 1 miliyoni anali ataonera seweroli lomwe linakonzedwa ndi nthambi ya ku Germany. M’bale Käthe Krauss ananena kuti: “Kuti tikaonere seweroli, tinkafunika kuyenda makilomita 10 kupita kokha. Misewu yake inkadutsa m’tchire, m’mapiri ndiponso m’zigwa.” M’bale wina, dzina lake Else Billharz, ananena kuti: “Sewero la Chilengedwe linandithandiza kuti ndiyambe kukonda choonadi.”
M’bale Alfred Almendinger anafotokoza kuti mayi ake ataonera seweroli, “anasangalala kwambiri ndipo anagula Baibulo n’kufufuza mawu akuti ‘puligatoliyo.’” Ataona kuti mawuwa sapezeka m’Baibulo anasiya kupita kutchalitchi kwawo ndipo kenako anabatizidwa. M’bale Frost ananena kuti: “Sewero la Chilengedwe linathandiza anthu ambiri kukhala Mboni.”—3 Yoh. 1-3.
Pamene kuonetsa seweroli kunkafika pachimake ulamuliro wa Nazi unayamba kufalikira ku Europe. Koma mu 1933 boma la Germany linaletsa ntchito ya Mboni za Yehova. Kuyambira chaka chimenechi mpaka kumapeto kwa nkhondo yachiwiri yapadziko lonse mu 1945, Mboni za Yehova ku Ulaya zinazunzidwa koopsa. M’bale Frost anakhala m’ndende zaka 8. Koma kenako anatuluka ndipo anayamba kutumikira ku Beteli mumzinda wa Wiesbaden ku Germany. Sewero la Chilengedwe linafika pa nthawi yake chifukwa linathandiza Akhristu kukhala olimba mtima. Izi zinawathandiza kukonzekera mayesero amene anakumana nawo pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse.—Kuchokera ku Germany.