Muzilemekeza Dzina Lalikulu la Yehova
“Ndidzalemekeza dzina lanu mpaka kalekale.”—SAL. 86:12.
1, 2. Mosiyana ndi matchalitchi amene amati ndi achikhristu, kodi Mboni za Yehova zimaona bwanji dzina la Mulungu?
MATCHALITCHI amene amati ndi achikhristu safuna kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu. Mwachitsanzo, mawu oyamba mu Baibulo lina lachingelezi amafotokoza kuti: “Kugwiritsa ntchito dzina lenileni la Mulungu woona yekha . . . n’kosayenera pa chikhulupiriro cha Akhristu.”—Revised Standard Version.
2 Koma mosiyana ndi zimenezi, Mboni za Yehova zimanyadira kutchulidwa ndi dzina la Mulungu komanso zimalilemekeza. (Werengani Salimo 86:12; Yesaya 43:10.) Komanso timaona kuti ndi mwayi waukulu kudziwa tanthauzo la dzinali ndiponso nkhani yokhudza kuyeretsedwa kwake komwe kumakhudza chilengedwe chonse. (Mat. 6:9) Mwayi umenewu sitiyenera kuuona mopepuka. Tiyeni tikambirane mafunso ofunika atatu okhudza nkhaniyi. Kodi kudziwa dzina la Mulungu kumatanthauza chiyani? Kodi Yehova amachita bwanji zinthu mogwirizana ndi dzina lake lalikulu zimene zathandiza kuti lilemekezeke? Ndipo kodi tingayende bwanji m’dzina la Yehova?
KODI KUDZIWA DZINA LA MULUNGU KUMATANTHAUZA CHIYANI?
3. Kodi kudziwa dzina la Mulungu kumatanthauza chiyani?
3 Kudziwa dzina la Mulungu sikumangotanthauza kudziwa kuti dzina lake ndi “Yehova.” Kumatanthauza kudziwa mbiri yake, makhalidwe ake ndiponso cholinga chake. Kumaphatikizaponso kudziwa zimene wachita zomwe zinalembedwa m’Baibulo monga zokhudza mmene amachitira zinthu ndi atumiki ake. Yehova amatithandiza kumudziwa pang’onopang’ono akamakwaniritsa cholinga chake. (Miy. 4:18) Iye anauza anthu oyambirira dzina lake moti Hava anatchula dzinali atabereka Kaini. (Gen. 4:1) Anthu akale okhulupirika monga Nowa, Abulahamu, Isaki ndi Yakobo ankadziwa dzina la Mulungu. Komanso anthuwa ankamvetsa kwambiri tanthauzo la dzinali akamaona mmene Yehova ankawadalitsira, kuwasamalira komanso kuwaululira mbali zosiyanasiyana za cholinga chake. Mose anapatsidwa mwayi wodziwa dzina la Mulungu mwapadera.
4. N’chifukwa chiyani Mose anafunsa Mulungu zokhudza dzina lake? Nanga n’chifukwa chiyani nkhawa ya Mose inali yomveka?
4 Werengani Ekisodo 3:10-15. Mose ali ndi zaka 80, Mulungu anamupatsa ntchito yovuta kwambiri. Anamulamula kuti: “Ukatulutse anthu anga ana a Isiraeli ku Iguputo.” Mose anayankha mwaulemu pomufunsa Yehova funso lochititsa chidwi losonyeza kuti ankafuna kudziwa dzina la Mulunguyo. Koma popeza pa nthawiyi n’kuti dzina la Mulungu likudziwika kale, n’chifukwa chiyani Mose anafunsa funso limeneli? Iye ankafuna kudziwa zambiri zokhudza Mulungu yemwe ndi mwini wake wa dzinali. Mose ankadziwa kuti zimenezi zikathandiza Aisiraeli kukhulupirira kuti Mulunguyo awapulumutsadi. Nkhawa imene Mose anali nayo inali yoyenera chifukwa Aisiraeli anali atakhala akapolo kwa zaka zambiri. Mwina iwo sakanakhulupirira kuti Mulungu wamakolo awo angawapulumutsedi. Komanso Aisiraeli ena anali atayamba kulambira milungu ya Aiguputo.—Ezek. 20:7, 8.
5. Kodi Yehova anafotokoza zotani zokhudza dzina lake poyankha Mose?
5 Kodi Yehova anamuyankha kuti chiyani Mose? Iye anati: “Ana a Isiraeli ukawauze kuti, ‘NDIDZAKHALA AMENE NDIDZAFUNE KUKHALA ndiye wandituma kwa inu.’” * Kenako anauza Mose kuti akauze Aisiraeli kuti: “Yehova Mulungu wa makolo anu, . . . wandituma kwa inu.” Mulungu ananena kuti adzakhala aliyense amene angafune, kapena kuti adzachita chilichonse chimene chingafunike, kuti akwaniritse cholinga chake ndipo nthawi zonse azichita zomwe wanena. N’chifukwa chake mu vesi 15 Yehova ananena kuti: “Limeneli ndilo dzina langa mpaka kalekale, ndipo ndicho chondikumbukirira ku mibadwomibadwo.” Mawu amenewa ayenera kuti analimbitsa kwambiri chikhulupiriro cha Mose.
YEHOVA ANACHITA ZINTHU MOGWIRIZANA NDI DZINA LAKE
6, 7. Kodi Yehova anachita zinthu ziti zogwirizana ndi tanthauzo la dzina lake?
6 Pasanapite nthawi kuchokera pamene Yehova anatuma Mose kukatulutsa Aisiraeli, iye anachita zinthu mogwirizana ndi dzina lake mwa ‘kukhala’ Mpulumutsi wa Aisiraeli. Iye anagwetsera Aiguputo miliri yokwana 10 komanso anasonyeza kuti milungu yawo, kuphatikizapo Farao, inali yopanda mphamvu. (Eks. 12:12) Kenako Yehova anachititsa kuti Aisiraeli adutse pa Nyanja Yofiira koma Farao ndi ankhondo ake anafera m’nyanjayo. (Sal. 136:13-15) ‘M’chipululu chachikulu ndi chochititsa mantha’ Yehova anateteza moyo wa anthu ake, omwe analipo mwina oposa 2 kapena 3 miliyoni, powapatsa chakudya ndi madzi. Yehova anachititsanso kuti zovala ndi nsapato za Aisiraeli zisathe. (Deut. 1:19; 29:5) Choncho tingathe kuona kuti palibe chimene chingamulepheretse Yehova kuchita zinthu mogwirizana ndi dzina lake. Kenako Yehova anauza Yesaya kuti: “Ine ndine Yehova. Popanda ine palibenso mpulumutsi wina.”—Yes. 43:11.
7 Nayenso Yoswa, amene analowa m’malo mwa Mose, anaona zinthu zodabwitsa zimene Yehova anachita ku Iguputo ndiponso m’chipululu. Choncho chakumapeto kwa moyo wake, iye anauza Aisiraeli anzake motsimikiza kuti: “Inu mukudziwa bwino ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kuti pamawu onse abwino amene Yehova Mulungu wanu ananena kwa inu, palibe ngakhale amodzi omwe sanakwaniritsidwe. Onse akwaniritsidwa kwa inu. Palibe ngakhale mawu amodzi omwe sanakwaniritsidwe.” (Yos. 23:14) Yehova anakwaniritsadi mawu akuti ‘adzakhala amene adzafune kukhala.’
8. Kodi Yehova wachita zinthu ziti masiku ano zogwirizana ndi tanthauzo la dzina lake?
8 Masiku anonso Yehova ‘amakhala amene akufuna kukhala.’ Kudzera mwa Mwana wake, iye analosera kuti m’masiku otsiriza uthenga wa Ufumu udzalalikidwa “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Mat. 24:14) Mulungu Wamphamvuyonse yekha ndi amene angalosere zimenezi, kuonetsetsa kuti zachitika komanso kugwiritsa ntchito anthu “osaphunzira ndiponso anthu wamba” kugwira ntchito imeneyi. (Mac. 4:13) Chotero tikamagwira ntchito yolalikira, timakhala tikuthandizira kukwaniritsa ulosi wa m’Baibulo. Timakhalanso tikulemekeza Atate wathu komanso kusonyeza kuti timanenadi zoona tikamapemphera kuti: “Dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.”—Mat. 6:9, 10.
DZINA LAKE NDI LALIKULU
9, 10. Kodi tikuphunzira chiyani za Yehova tikaona mmene ankachitira zinthu ndi Aisiraeli?
9 Aisiraeli atangochoka ku Iguputo, Yehova anachitanso zinthu zina zogwirizana ndi dzina lake. Kudzera m’pangano la Chilamulo, iye anakhala ‘mwamuna wawo’ ndipo ankawasamalira mofunitsitsa ngati mmene mwamuna wachikondi amasamalirira mkazi wake. (Yer. 3:14) Choncho Aisiraeli anakhala mkazi wake wophiphiritsa komanso anthu a dzina lake. (Yes. 54:5, 6) Iwo akamamumvera komanso kutsatira malamulo ake, iye ankakhala ngati “mwamuna” wawo wabwino kwambiri. Ankawadalitsa, kuwasunga komanso kuwapatsa mtendere. (Num. 6:22-27) Zimenezi zinkathandiza kuti dzina lalikulu la Mulungu lilemekezedwe pakati pa anthu a mitundu ina. (Werengani Deuteronomo 4:5-8; Salimo 86:7-10.) Pa nthawi ya Aisiraeli, anthu ambiri a mitundu ina anayamba kulambira Yehova. Tingati iwo ananena zofanana ndi zimene Rute anauza Naomi kuti: “Anthu a mtundu wanu adzakhala anthu a mtundu wanga, ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga.”—Rute 1:16.
10 Pa zaka pafupifupi 1,500 zimene Yehova ankachita zinthu ndi Aisiraeli, iye anasonyeza kuti ali ndi makhalidwe abwino osiyanasiyana. Ngakhale kuti anthuwa ankamupandukira mobwerezabwereza, Yehova anakhala “Mulungu wachifundo” ndi “wosakwiya msanga.” Iye anasonyeza kuti ndi Mulungu woleza mtima kwambiri. (Eks. 34:5-7) Komabe kuleza mtima kwa Yehova kunali ndi malire ndipo kunatha pamene Ayuda anakana ndi kupha Mwana wake. (Mat. 23:37, 38) Choncho mtundu wa Aisiraeli unasiya kukhala anthu odziwika ndi dzina la Mulungu. Kwa Yehova, iwo anali ngati mtengo wakufa. (Luka 23:31) Kodi Aisiraeli opandukawa anayamba kuliona bwanji dzina la Mulungu?
11. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti dzina la Mulungu lisamamvekenso pakati pa Ayuda?
11 Patapita nthawi, Ayuda anayamba kuona dzina la Mulungu molakwa. Anayamba kuliona kuti ndi loyera kwambiri moti sankafunika kumalitchula n’komwe. (Eks. 20:7) Izi zinachititsa kuti pang’ono ndi pang’ono dzinali lisamamvekenso pakati pa Ayuda. Zimenezi ziyenera kuti zinakhumudwitsa kwambiri Yehova chifukwa zinasonyeza kuti Ayudawo sankalemekeza dzina lake. (Sal. 78:40, 41) Komabe Mulungu, “amene dzina lake ndi Nsanje,” sakanalola kuti anthu amene anamukana komanso amene iyeyo anawakana apitirize kudziwika ndi dzina lake. (Eks. 34:14) Mfundo imeneyi iyenera kutithandiza kuona kufunika kolemekeza dzina la Mlengi wathu.
ANTHU ATSOPANO ODZIWIKA NDI DZINA LA MULUNGU
12. Kodi ndani amene anakhala anthu odziwika ndi dzina la Mulungu?
12 Kudzera mwa Yeremiya, Yehova ananena cholinga chake chofuna kukhazikitsa “pangano latsopano” ndi mtundu wa Isiraeli wauzimu. Yeremiya analosera kuti, ‘kuyambira wamng’ono mpaka wamkulu adzadziwa Yehova.’ (Yer. 31:31, 33, 34) Ulosi umenewu unayamba kukwaniritsidwa pa Pentekosite wa mu 33 C.E. pamene Mulungu anakhazikitsa pangano latsopano. Mtundu watsopano, kapena kuti “Isiraeli wa Mulungu,” umene umaphatikizapo Ayuda ndi anthu a mitundu ina, unakhala “anthu odziwika ndi dzina” la Mulungu. Malinga ndi zimene Yehova ananena, iwo anali ‘anthu otchedwa ndi dzina lake.’—Agal. 6:16; werengani Machitidwe 15:14-17; Mat. 21:43.
13. (a) Kodi Akhristu oyambirira ankagwiritsa ntchito dzina Mulungu? Fotokozani. (b) Kodi mumamva bwanji mukamagwiritsa ntchito dzina la Mulungu mu utumiki?
13 Akhristu oyambirira, omwe anali m’gulu la Isiraeli wauzimu, ankagwiritsa ntchito dzina la Mulungu. Mwachitsanzo, iwo ankachita zimenezi pogwira mawu a m’Malemba Achiheberi. * Choncho pa Pentekosite wa mu 33 C.E., pamene mtumwi Petulo ankalankhula kwa Ayuda komanso anthu amene analowa Chiyuda omwe anachokera m’madera osiyanasiyana, anatchula dzina la Mulungu kangapo konse. (Mac. 2:14, 20, 21, 25, 34) Popeza Akhristu oyambirira ankalemekeza Yehova, iye anadalitsa khama lawo pa ntchito yolalikira. Masiku anonso, Yehova amadalitsa utumiki wathu tikamauza anthu dzina lake komanso kuwaonetsa dzinali m’Mabaibulo awo. Tikamachita zimenezi timathandiza anthuwa kudziwa Mulungu woona. Umenewutu ndi mwayi waukulu kwambiri kwa iwowo komanso ifeyo. Zimenezi zikhoza kukhala chiyambi choti akhale pa ubwenzi ndi Yehova ndipo ubwenzi umenewu ukhoza kukula ndiponso kukhalapo mpaka kalekale.
14, 15. Ngakhale kuti anthu ampatuko anayesetsa kuthetsa dzina la Mulungu, kodi Yehova anachita chiyani?
14 Anthu ampatuko anayamba kuwononga mpingo wachikhristu makamaka atumwi onse atamwalira. (2 Ates. 2:3-7) Aphunzitsi onyenga anatengera khalidwe la Ayuda losagwiritsa ntchito dzina la Mulungu. Koma kodi Yehova akanalola kuti dzina lake litheretu? Ayi. Ngakhale kuti katchulidwe kenikeni ka dzinali sikadziwika bwinobwino, dzinali lilipobe mpaka pano. Kwa zaka zambirimbiri, dzinali lakhala likupezeka m’Mabaibulo osiyanasiyana komanso m’mabuku a akatswiri a maphunziro a Baibulo. Mwachitsanzo, mu 1757 Charles Peters analemba kuti dzina lakuti “Yehova,” mosiyana ndi mayina ake onse audindo, “limafotokoza bwino mmene Mulungu alili.” Mu 1797, Hopton Haynes analemba buku lonena za kulambira Mulungu. M’chaputala 7 cha bukuli, iye anayamba ndi mawu akuti: “YEHOVA ndi dzina lenileni la MULUNGU amene Ayuda ankamulambira. Iye ndi Mulungu amenenso Yesu komanso atumwi ankalambira.” Henry Grew (anakhalako kuyambira mu 1781 mpaka mu 1862) ankagwiritsanso ntchito dzina la Mulungu ndipo anazindikira kuti dzinali lanyozedwa ndipo liyenera kuyeretsedwa. Nayenso George Storrs (anakhalako kuyambira mu 1796 mpaka mu 1879), yemwe anali mnzake wa Charles T. Russell, ankatchula dzina la Mulungu mofanana ndi mmene Russell ankachitira.
15 Chaka cha 1931 chinali chapadera kwambiri chifukwa ndi chimene Ophunzira Baibulo anavomera kudziwika ndi dzina la m’Malemba lakuti Mboni za Yehova. (Yes. 43:10-12) Pamenepa iwo analengeza padziko lonse kuti amanyadira kukhala atumiki a Mulungu woona yekha, “anthu odziwika ndi dzina lake,” ndiponso kulilemekeza. (Mac. 15:14) Zimenezi zimatikumbutsa mawu a Yehova amene amapezeka pa Malaki 1:11 akuti: “Kuchokera kotulukira dzuwa kukafika kumene limalowera, dzina langa lidzakwezeka pakati pa anthu a mitundu ina.”
YENDANI M’DZINA LA YEHOVA
16. N’chifukwa chiyani tiyenera kuona kuti kuyenda m’dzina la Yehova ndi mwayi waukulu?
16 Mneneri Mika analemba kuti: “Mtundu uliwonse wa anthu udzayenda m’dzina la mulungu wake. Koma ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu mpaka kalekale, inde mpaka muyaya.” (Mika 4:5) Ophunzira Baibulo atayamba kudziwika ndi dzina la Mulungu, anaona kuti ndi mwayi wapadera komanso kuti ndi umboni woti Mulungu akusangalala nawo. (Werengani Malaki 3:16-18.) Nanga bwanji inuyo? Kodi mukuyesetsa ‘kuyenda m’dzina la Yehova’? Kodi mumadziwa zimene kuyenda m’dzina la Yehova kumatanthauza?
17. Kodi kuyenda m’dzina Mulungu kumafuna chiyani?
17 Kuti tiyende m’dzina la Mulungu, tiyenera kuchita zinthu zitatu zotsatirazi: Choyamba, tiyenera kulengeza dzinali kwa anthu ena chifukwa tikudziwa kuti “amene adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.” (Aroma 10:13) Chachiwiri, tiyenera kusonyeza makhalidwe a Yehova, makamaka chikondi. Chachitatu, timayenda m’dzina la Mulungu tikamatsatira mfundo zake zolungama n’cholinga choti tisanyozetse dzina loyera la Atate wathu. (1 Yoh. 4:8; 5:3) Kodi inuyo ndinu wofunitsitsa ‘kuyenda m’dzina la Yehova Mulungu wanu mpaka kalekale’?
18. N’chifukwa chiyani tinganene kuti anthu onse amene amalemekeza dzina la Yehova ali ndi chiyembekezo chabwino?
18 Posachedwapa, anthu onse amene amanyoza Yehova adzadziwa kuti iye ndiye woyenera kulemekezedwa. (Ezek. 38:23) Anthu amenewa akuphatikizapo onse amene ali ngati Farao yemwe ananena kuti: “Yehova ndani kuti ndimvere mawu ake?” Koma pasanapite nthawi, anamudziwa. (Eks. 5:1, 2; 9:16; 12:29) Koma ife tinasankha kudziwa Yehova. Timasangalala kudziwika ndi dzina lake komanso kukhala anthu ake omvera. Choncho timayembekezera mwachidwi kukwaniritsidwa kwa lonjezo lopezeka pa Salimo 9:10 lakuti: “Anthu odziwa dzina lanu adzakukhulupirirani, pakuti simudzasiya ndithu anthu okufunafunani, inu Yehova.”
^ ndime 5 Dzina la Mulungu ndi lochokera ku verebu lachiheberi limene limatanthauza “kukhala.” Choncho dzina lakuti Yehova limatanthauza kuti “Iye Amachititsa Kukhala.”—Gen. 2:4, (Onani Zakumapeto 1 ndime 1 m’Baibulo la Dziko Latsopano.)
^ ndime 13 Baibulo lachiheberi limene Akhristu oyambirira ankagwiritsa ntchito linali ndi dzina la Mulungu. Pali umboni wosonyeza kuti dzinali linkapezekanso m’Mabaibulo omasuliridwa m’Chigiriki.