NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) April 2013

Magaziniyi ikufotokoza njira yothandiza kwambiri pophunzira Baibulo komanso ikusonyeza zimene tingachite kuti nzeru zochokera kwa Mulungu zizititsogolera pa utumiki wathu komanso pa moyo wathu.

Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Mexico

Werengani kuti mumve kuti ndi achinyamata angati amene apirira mavuto osiyanasiyana ndi cholinga choti awonjezere zimene amachita mu utumiki.

Zimene Mungachite Kuti Muzipindula Powerenga Baibulo

Tingapindule ndi Baibulo ngati timaliphunizira komanso kutsatira zimene limanena. Werengani kuti mudziwe zimene mungachite kuti muzipindula mukamawerenga Baibulo.

Mawu a Mulungu Azikuthandizani Ndipo Muzithandiza Nawo Ena

Kodi mumaona kuti Baibulo ndi lamtengo wapatali? Kuwerenga mosamala lemba la 2 Timoteyo 3:16 kungakuthandize kwambiri kuti muziyamikira kwambiri mphatso yochokera kwa Yehova imeneyi.

MBIRI YA MOYO WANGA

Tachita Utumiki wa Nthawi Zonse kwa Zaka 50 Kumpoto Kwenikweni

Werengani nkhani ya Aili ndi Annikki Mattila, omwe anaona ubwino wodalira Yehova pomwe ankatumikira ngati apainiya apadera ku kumpoto kwa dziko la Finland.

“Muzitsimikizira Kuti Zinthu Zofunika Kwambiri Ndi Ziti”

Tili ndi mwayi kukhala m’gulu la Mulungu la padziko lonse. Kodi tizitani pothandizira ntchito imene gululi likugwira masiku ano?

”Musatope Kuchita Zabwino”

Kodi chingatithandize n’chiyani kuti tiziyendera limodzi ndi gulu la Yehova komanso kuti tikhalebe achangu potumikira Mulungu?

Kodi Mukudziwa?

Yesu analosera kuti kachisi wa Yehova adzawonongedweratu. Kodi m’zinda wa Yerusalemu unamangidwanso pambuyo pa 70 C.E.?