Mawu a Mulungu Azikuthandizani Ndipo Muzithandiza Nawo Ena
“Ndaona kuti malamulo anu onse okhudza chilichonse ndi olungama.”—SAL. 119:128.
1. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira kwambiri Mawu a Mulungu?
AKULU akamakambirana ndi munthu amene akufuna kukhala wofalitsa wosabatizidwa, amafuna kuona ngati zonena za munthuyo zikusonyeza kuti amakhulupiriradi kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu. * Munthu amene akufuna kukhala wofalitsa komanso atumiki onse a Mulungu ayenera kukhulupirira zimenezi. N’chifukwa chiyani tikutero? Ngati timakhulupirira Mawu a Mulungu ndiponso kuwagwiritsa ntchito bwino mu utumiki, tidzathandiza ena kudziwa Yehova ndiponso kupulumuka.
2. N’chifukwa chiyani tiyenera ‘kupitiriza kutsatira zimene tinaphunzira’?
2 Mtumwi Paulo anasonyeza kuti Mawu a Mulungu ndi ofunika kwambiri. Iye analembera Timoteyo kuti: “Pitiriza kutsatira zimene unaphunzira ndi zimene unakhulupirira pambuyo pokhutira nazo.” Paulo ankanena za mfundo za choonadi zimene zinachititsa Timoteyo kukhulupirira uthenga wabwino. Mfundozi n’zofunikanso masiku ano kuti tikhale ndi chikhulupiriro ndipo zimatipatsa ‘nzeru zotithandiza kuti tidzapulumuke.’ (2 Tim. 3:14, 15) Nthawi zambiri timagwiritsa ntchito mawu a Paulo a m’vesi lotsatira posonyeza anthu kuti Baibulo linauziridwa ndi Mulungu. Koma kodi ifeyo tingaphunzirenso chiyani pa mawu omwe ali pa vesi limeneli? (Werengani 2 Timoteyo 3:16.) Tiyeni tikambirane vesili mwatsatanetsatane. Tikatero, tizikhulupirira kwambiri kuti zinthu zonse zimene Yehova amaphunzitsa ndi zolondola.—Sal. 119:128.
“NDI OPINDULITSA PA KUPHUNZITSA”
3-5. (a) Kodi anthu anatani atamva nkhani ya Petulo pa Pentekosite ndipo n’chifukwa chiyani anatero? (b) N’chifukwa chiyani anthu ambiri ku Tesalonika anakhala okhulupirira? (c) Kodi masiku ano, anthu amachita chidwi ndi chiyani tikamalalikira?
3 Yesu anauza Aisiraeli kuti: “Ndikukutumizirani aneneri, anthu anzeru ndi aphunzitsi.” (Mat. 23:34) Apa Yesu ankanena za ophunzira ake amene iye anawaphunzitsa kugwiritsa ntchito Malemba mu utumiki. Mmodzi mwa “aphunzitsi” amenewa anali mtumwi Petulo. Pa Pentekosite mu 33 C.E., iye anakambira nkhani khamu lalikulu limene linasonkhana ku Yerusalemu ndipo anagwira mawu mbali zambiri zochokera m’Malemba Achiheberi. Anthu ambiri atamva Petulo akufotokoza Malemba, “anavutika kwambiri mumtima.” Iwo analapa machimo awo n’kupempha Mulungu kuti awakhululukire. Pa tsikulo, anthu pafupifupi 3,000 anakhala Akhristu.—Mac. 2:37-41.
4 Mphunzitsi wina anali mtumwi Paulo. Iye analalikira m’madera ena akutali ndi Yerusalemu. Mwachitsanzo, iye analalikira kwa Ayuda amene ankalambira musunagoge wa mumzinda wa Tesalonika ku Makedoniya. Kwa masiku atatu a Sabata, Paulo “anakambirana nawo mfundo za m’Malemba. Iye anali kufotokoza ndi kusonyeza umboni wolembedwa powatsimikizira kuti kunali koyenera kuti Khristu avutike ndi kuuka kwa akufa.” Zotsatira zake n’zakuti ena mwa Ayudawo limodzi ndi “khamu lalikulu la Agiriki” anakhala okhulupirira.—Mac. 17:1-4.
5 Masiku anonso, anthu ambiri amachita chidwi ndi mmene atumiki a Yehova amagwiritsira ntchito Baibulo. Munthu wina ku Switzerland atamva mlongo akuwerenga Baibulo, anamufunsa kuti: “Kodi ndinu a chipembedzo chiti?” Mlongoyo anayankha kuti: “Ine ndi mnzangayu ndife Mboni za Yehova.” Kenako munthuyo anati: “Komadi. Palibenso anthu a chipembedzo china amene angabwere pano n’kumawerenga Baibulo.”
6, 7. (a) Kodi anthu amene amakamba nkhani mu mpingo angatani kuti azigwiritsa ntchito bwino Baibulo? (b) Kodi kugwiritsa ntchito bwino Malemba pophunzira ndi anthu n’kofunika bwanji?
6 Koma kodi tingatani kuti tizigwiritsa ntchito bwino Mawu a Mulungu tikamaphunzitsa? Ngati mumapatsidwa nkhani zokamba mu mpingo, musamangotchula mawu a m’Baibulo kapena kungowawerenga papepala kapena pazipangizo zina. Koma muzitsegula Baibulo lenilenilo n’kumawerenga ndipo muzilimbikitsa anthu kutsegulanso Mabaibulo awo. Muzifotokozanso Malemba m’njira imene ingathandize omvera kulimbitsa ubwenzi wawo ndi Yehova. M’malo mofotokoza mafanizo ovuta kapena zochitika zina zongofuna kuseketsa anthu, muzigwiritsa ntchito nthawi imeneyo pofotokoza Mawu a Mulungu.
7 Kodi tiyenera kukumbukira chiyani tikamaphunzitsa anthu Baibulo? Tikamaphunzira nawo mabuku athu n’kupeza malemba, tisamangowadutsa. Tizilimbikitsa wophunzirayo kuwerenga malemba ndiponso kumuthandiza kumvetsa tanthauzo lake. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Sikuti tizingolankhula tokha pofotokoza Malemba. Ndi bwino kufunsa wophunzirayo kuti anene maganizo ake pa lembalo. M’malo momuuza zoyenera kukhulupirira kapena njira yabwino yochitira zinthu, tizimufunsa mafunso abwino amene angamuthandize kumvetsa zimene Baibulo limaphunzitsa. *
“NDI OPINDULITSA PA . . . KUDZUDZULA”
8. Kodi Paulo anali pa nkhondo yolimbana ndi chiyani?
8 Nthawi zambiri timaganiza kuti akulu okha ndi amene ali ndi udindo ‘wodzudzula’ anthu. N’zoona kuti akulu ali ndi udindo ‘wodzudzula anthu amene ali ndi chizolowezi chochita tchimo.’ (1 Tim. 5:20; Tito 1:13) Komatu anthufe timafunikanso kudzidzudzula tokha. Paulo anali Mkhristu wabwino amene analinso ndi chikumbumtima choyera. (2 Tim. 1:3) Koma iye analemba kuti: “Ndimaona chilamulo china m’ziwalo zanga chikumenyana ndi chilamulo cha m’maganizo mwanga n’kundipanga kukhala kapolo wa chilamulo cha uchimo.” Tikawerenga nkhani yonse pamene pakupezeka mawu amenewa, titha kuona kuti Paulo anali pa nkhondo yaikulu yolimbana ndi zofooka zake.—Werengani Aroma 7:21-25.
9, 10. (a) Kodi mwina Paulo ankalimbana ndi chiyani? (b) Kodi Paulo ankamenya bwanji nkhondo yake?
9 Kodi zofooka zimene Paulo ankalimbana nazo zinali ziti? Ngakhale kuti sanatchule mwachindunji, pa nthawi ina analembera Timoteyo kuti iye asanakhale Mkhristu anali “wachipongwe.” (1 Tim. 1:13) Paulo ankazunza kwambiri Akhristu. Pofotokoza mmene ankaonera Akhristu, iye anati: “Ndinali nditakwiya nawo kwambiri.” (Mac. 26:11) Paulo anaphunzira kuugwira mtima koma ayenera kuti nthawi zina ankavutika kuti asakhale ndi maganizo oipa kapena kulankhula mawu achipongwe. (Mac. 15:36-39) N’chiyani chinamuthandiza kuti apambane pa nkhondoyi?
10 M’kalata yake yopita kwa Akhristu a ku Korinto, Paulo anafotokoza njira imene anatsatira podzidzudzula. (Werengani 1 Akorinto 9:26, 27.) Ankaponya bwino nkhonya zake kuti amenye makhalidwe oipa amene anali nawo chifukwa chopanda ungwiro. Ayenera kuti ankafufuza malangizo a m’Malemba, kuchonderera Yehova kuti amuthandize kuwatsatira komanso kuchita zonse zimene akanatha kuti asinthe. * Popeza ifenso tili pa nkhondo ngati yomweyi, tingachite bwino kutsanzira Paulo.
11. Kodi tingapitirize bwanji “kudziyesa” kuti tidziwe ngati tikuyendadi m’njira ya choonadi?
11 Tisayerekeze ngakhale pang’ono kuganiza kuti tikhoza kusiya kumenya nkhondo yathuyi. M’malomwake, tipitirize “kudziyesa” kuti tione ngati tikuyendadi m’njira ya choonadi. (2 Akor. 13:5) Tikamawerenga malemba monga Akolose 3:5-10, tizidzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndikuyesetsa kuchititsa ziwalo zanga kukhala zakufa? Nanga makhalidwe anga sakulowa pansi? Ngati ndikufufuza zinthu pa Intaneti, kodi ndimatseka mwamsanga mawebusaiti oipa amene abwera mwangozi kapena ndimafufuza mwadala mawebusaiti oterowo?’ Kutsatira malangizo a m’Mawu a Mulungu pa nkhani ngati zimenezi kungatithandize kuti “tikhalebe maso ndipo tikhalebe oganiza bwino.”—1 Ates. 5:6-8.
“NDI OPINDULITSA PA . . . KUWONGOLA ZINTHU”
12, 13. (a) Kodi cholinga chathu chiyenera kukhala chiyani ‘tikamawongola zinthu’? Nanga tingatsanzire bwanji Yesu pa nkhaniyi? (b) Kodi ndi mawu ati amene tiyenera kupeweratu ‘tikamawongola zinthu’?
12 Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “kuwongola zinthu” amatanthauza “kukonza zinthu kapena kuzibwezeretsa pamalo abwino.” Nthawi zina, timafunika kuwongola zinthu ngati anthu ena sanamvetse bwino zimene tanena kapena kuchita. Mwachitsanzo, atsogoleri achipembedzo achiyuda anadandaula kuti Yesu ankakomera mtima “okhometsa misonkho ndi anthu ochimwa.” Poyankha, Yesu anawauza kuti: “Anthu abwinobwino safuna dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna. Choncho pitani mukaphunzire tanthauzo la mawu akuti, ‘Ndikufuna chifundo, osati nsembe.’” (Mat. 9:11-13) Iye ankafotokozera anthu onse Mawu a Mulungu moleza mtima komanso mokoma mtima. Izi zinathandiza anthu odzichepetsa kudziwa kuti Yehova ndi “Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi choonadi.” (Eks. 34:6) Popeza Mwana wa Mulungu anayesetsa “kuwongola zinthu,” anthu ambiri anayamba kukhulupirira uthenga wabwino.
13 Pothandiza anthu ena, tiyenera kutengera chitsanzo cha Yesu. Malangizo a pa 2 Timoteyo 3:16 sakutanthauza kuti tizilankhula mwaukali kwa anthu ena pofuna kuti tiwongole zinthu. Baibulo silitilimbikitsa kulankhula anthu ena mosawaganizira. Mawu oterowo amakhala “olasa ngati lupanga.” (Miy. 12:18) M’malo mothandiza munthu, mawuwo angamupweteke kwambiri.
14-16. (a) Kodi akulu angawongole bwanji zinthu pothandiza anthu kuthetsa mavuto awo? (b) Kodi “kuwongola zinthu” pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu n’kofunika bwanji polera ana?
14 Ndiyeno kodi tingatani kuti ‘tiwongole zinthu’ moleza mtima komanso mokoma mtima? Tiyerekeze kuti banja lina lapempha mkulu kuti alithandize kuthetsa mavuto awo a m’banja. Kodi mkuluyo ayenera kuchita chiyani? Iye sayenera kuikira kumbuyo munthu wina koma kukambirana ndi onse awiri mfundo za m’Baibulo. Mwina angagwiritse ntchito malangizo a m’mutu 3 wa buku lakuti, Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. Pokambirana nawo mfundozi, mwamuna ndi mkazi akhoza kuzindikira okha zimene ayenera kusintha kuti athetse vutolo. Pakapita nthawi, mwina mkuluyo angawafunse ngati zinthu zayamba kuyenda bwino kapena ngati pakufunika thandizo lina.
15 Kodi makolo angathandize bwanji ana awo “kuwongola zinthu”? Tiyerekeze kuti muli ndi mwana wamkazi ndipo mukufuna kumuthandiza kuti asamacheze ndi munthu wolakwika. Choyamba, muyenera kudziwa bwino mnzakeyo. Ndiyeno ngati mwaona kuti pali vuto, mungakambirane naye. Mungagwiritse ntchito mfundo ngati za m’buku lakuti, Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri. Mungapezenso nthawi ina yocheza naye ndiponso kuchita naye zinthu zina. Muziona mmene amachitira zinthu akakhala mu utumiki komanso pa nthawi imene mukuchita zosangalatsa. Mukakhala oleza mtima komanso okoma mtima, mwana wanuyo angaone kuti mumamukonda ndiponso mumamufunira zabwino. Izi zidzathandiza kuti azitsatira malangizo anu n’kumapewa mavuto pa moyo wake.
16 Tingachite chimodzimodzinso pothandiza anthu amene akuda nkhawa chifukwa chakuti akudwala, ntchito yawathera kapena sakumvetsa mfundo zina za m’Malemba. Zinthu zimatiyendera bwino kwambiri ngati tikugwiritsa ntchito Baibulo ‘powongola zinthu.’
“NDI OPINDULITSA PA . . . KULANGIZA M’CHILUNGAMO”
17. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira tikapatsidwa malangizo?
17 Baibulo limati: “Palibe chilango chimene chimamveka chosangalatsa pa nthawi yomwe ukuchilandira, koma chimakhala chowawa. Komabe pambuyo pake, kwa anthu amene aphunzirapo kanthu pa chilangocho, chimabala chipatso chamtendere, chomwe ndi chilungamo.” (Aheb. 12:11) Akhristu achikulire ambiri amavomereza kuti malangizo amene makolo awo ankawapatsa anawathandiza kwambiri. Kulandira malangizo amene Yehova amapereka kudzera mwa akulu, kungatithandizenso kuyendabe panjira ya ku moyo.—Miy. 4:13.
18, 19. (a) Kodi malangizo a pa Miyambo 18:13 ndi ofunika bwanji ‘polangiza munthu m’chilungamo’? (b) Kodi chingachitike n’chiyani ngati akulu akhala ofatsa komanso achikondi pothandiza munthu wochimwa?
18 Kupereka malangizo othandiza si kophweka. Yehova amalimbikitsa Akhristu kulangiza ena “m’chilungamo.” (2 Tim. 3:16) Choncho tikafuna kulangiza anthu, tiyenera kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo. Mfundo ina yofunika kuitsatira ili pa Miyambo 18:13. Lembali limati: “Munthu aliyense woyankhira nkhani asanaimvetsetse n’ngopusa, ndipo amachita manyazi.” Choncho akulu akamva kuti munthu wina wachita tchimo lalikulu, ayenera kufufuza mosamala nkhaniyo kuti aidziwe bwino. (Deut. 13:14) Akatero m’pamene angakwanitse kumulangiza “m’chilungamo.”
19 Mawu a Mulungu amalimbikitsanso akulu kulangiza anthu “mofatsa.” (Werengani 2 Timoteyo 2:24-26.) N’zoona kuti tchimo la munthu linganyozetse dzina la Yehova komanso kupweteka anthu osalakwa. Koma ngati mkulu atakwiya pa nthawi imene akukambirana ndi wochimwayo ndiye kuti sangamuthandize. Choncho mkulu ayenera kutsanzira “kukoma mtima kwa Mulungu” kuti athandize munthuyo kulapa.—Aroma 2:4.
20. Kodi makolo ayenera kutsatira mfundo ziti akamalangiza ana awo?
20 Makolo ayenera kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo polera ana “m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4) Mwachitsanzo, si bwino kuti bambo azifulumira kupereka chilango kwa mwana akangomva wina akunena kuti mwanayo walakwitsa zinazake. Aliyense m’banja lachikhristu sayenera kukwiya kwambiri mpaka kufika pochita nkhanza. Anthu amene apatsidwa udindo wolangiza ana ayenera kutsanzira Yehova yemwe ndi “wachikondi chachikulu ndi wachifundo.”—Yak. 5:11.
BAIBULO NDI MPHATSO YAMTENGO WAPATALI IMENE YEHOVA WATIPATSA
21, 22. Kodi ndi mawu ati mu Salimo 119:97-104 amene akufotokoza bwino mmene inuyo mumaonera Mawu a Yehova?
21 Mtumiki wina wa Mulungu anafotokoza chifukwa chake ankakonda chilamulo cha Yehova. (Werengani Salimo 119:97-104.) Kuphunzira chilamulo cha Yehova kunamuthandiza kukhala wanzeru komanso wozindikira. Kutsatira malangizo a m’Baibulo kunamuthandiza kupewa njira zachinyengo ndiponso mavuto amene anthu ena amakumana nawo. Iye ankasangalala kwambiri kuphunzira Malemba ndipo akawatsatira zinthu zinkamuyendera bwino. Choncho anatsimikiza mumtima mwake kutsatira malangizo a Mulungu nthawi zonse.
22 Kodi inuyo mumaona kuti “Malemba onse” ndi amtengo wapatali? Mukamaphunzira Malemba, mumakhulupirira kwambiri kuti Mulungu adzakwaniritsa cholinga chake. Malangizo a m’Baibulo akhoza kukuthandizani kupewa machimo ndiponso imfa. Mukamafotokoza bwino Malemba, mudzathandiza anthu ena kuti ayambe kuyenda panjira ya ku moyo ndiponso asapatuke panjirayo. Tiyeni tonse tizigwiritsa ntchito kwambiri Baibulo pamene tikutumikira Yehova Mulungu wathu, yemwe ndi wachikondi ndiponso wanzeru zopanda malire.
^ ndime 1 Onani buku lakuti Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova, tsamba 79.
^ ndime 7 Pophunzitsa anthu, Yesu ankakonda kuwafunsa kuti: “Mukuganiza bwanji?” Akatero, ankayembekezera yankho.—Mat. 18:12; 21:28; 22:42.
^ ndime 10 Makalata a Paulo ali ndi malangizo othandiza kwambiri polimbana ndi kupanda ungwiro. (Aroma 6:12; Agal. 5:16-18) Iyenso ayenera kuti ankatsatira malangizo amene ankapereka kwa anthu ena.—Aroma 2:21.