Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzisankha Zinthu Mwanzeru Kuti Musataye Madalitso Anu

Muzisankha Zinthu Mwanzeru Kuti Musataye Madalitso Anu

“Nyansidwani ndi choipa, gwiritsitsani chabwino.”—AROMA 12:9.

1, 2. (a) Kodi zinakhala bwanji kuti musankhe kutumikira Mulungu? (b) Kodi tikambirana mafunso ati okhudza madalitso athu?

AMBIRIFE tinasankha mwanzeru kuti tizitumikira Yehova Mulungu ndiponso kutsatira chitsanzo cha Yesu Khristu mosamala kwambiri. (Mat. 16:24; 1 Pet. 2:21) Timaona kuti kudzipereka kwathu kwa Mulungu ndi nkhani yaikulu. Tinasankha zimenezi chifukwa chophunzira Mawu a Mulungu mozama osati chifukwa chongodziwa zinthu zochepa zokhudza malemba ena. Izi zachititsa kuti tidziwe zinthu zambiri zotithandiza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Zinthu zake ndi zokhudza madalitso amene Yehova amapereka kwa anthu amene ‘amaphunzira za iye ndiponso za Yesu Khristu, amene anamutuma.’—Yoh. 17:3; Aroma 12:2.

2 Kuti tipitirize kukhala Akhristu oona, tiyenera kusankha zinthu zimene zimasangalatsa Atate wathu wakumwamba. Choncho nkhaniyi iyankha mafunso ofunika awa: Kodi tili ndi madalitso ati? Kodi tiyenera kuwaona bwanji? Kodi tingatani kuti tisataye madalitsowo? Nanga n’chiyani chingatithandize kusankha zinthu mwanzeru?

KODI TILI NDI MADALITSO ATI?

3. (a) Kodi odzozedwa akuyembekezera chiyani? (b) Nanga a “nkhosa zina” akuyembekezera zotani?

3 Pali Akhristu ochepa amene akuyembekezera kulandira “cholowa chosawonongeka, chosadetsedwa ndiponso chosasuluka.” (1 Pet. 1:3, 4) Iwo akuyembekezera mwayi waukulu kwambiri wokalamulira limodzi ndi Khristu kumwamba. Kuti apeze madalitso amenewa, amafunika “kubadwanso.” (Yoh. 3:1-3) Palinso anthu mamiliyoni, amene ndi “nkhosa zina” za Yesu, omwe amathandiza odzozedwa pa ntchito yolalikira uthenga wa Ufumu wa Mulungu. (Yoh. 10:16) Nanga iwo akuyembekezera  zotani? Iwo adzalandira madalitso amene Adamu ndi Hava anataya chifukwa chochimwa. Adzalandira moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi ndipo sipadzakhalanso kuvutika, imfa ndiponso kulira. (Chiv. 21:1-4) N’chifukwa chake Yesu analonjeza munthu wochimwa amene anapachikidwa naye limodzi uja kuti: “Ndithu ndikukuuza lero, Iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso.”—Luka 23:43.

4. Kodi panopa talandira kale madalitso ati?

4 Pali madalitso ena amene talandira kale panopa. Popeza timakhulupirira “dipo lolipiridwa ndi Khristu Yesu,” timakhala ndi mtendere wa mumtima komanso ubwenzi wabwino ndi Mulungu. (Aroma 3:23-25) Panopa timadziwa bwino malonjezo amtengo wapatali amene ali m’Mawu a Mulungu. Timasangalalanso kwambiri chifukwa chakuti tili m’gulu lapadziko lonse la abale ndi alongo achikondi. Kungokhala wa Mboni za Yehova ndi mwayinso wamtengo wapatali. Kodi sitiyenera kuyamikira madalitso onsewa?

5. Kodi Satana wakhala akuyesetsa kuchita chiyani? Nanga tingatani kuti tisasunthike polimbana naye?

5 Koma tiyenera kusamala kuti Satana asatitayitse madalitso athu. Kuyambira kale, Satana wakhala akuyesetsa kuchititsa anthu a Mulungu kusankha zinthu zimene zingawatayitse madalitso awo. (Num. 25:1-3, 9) Panopa Satana watsala ndi kanthawi kochepa choncho akuchita chilichonse chimene angathe kuti atisocheretse. (Werengani Chivumbulutso 12:12, 17.) Kuti ‘tisasunthike polimbana ndi zochita zachinyengo za Mdyerekezi,’ tiyenera kupitiriza kuyamikira kwambiri madalitso athu. (Aef. 6:11) Kodi pa nkhani imeneyi, tingaphunzire chiyani pa zimene Esau anachita? Tiyeni tione.

MUSAKHALE NGATI ESAU

6, 7. Kodi Esau anali ndani ndipo anali ndi mwayi uti?

6 Pafupifupi zaka 4,000 zapitazo, Isaki ndi Rabeka anabereka mapasa. Mayina a anawa anali Esau ndi Yakobo ndipo anali osiyana makhalidwe komanso zochita. “Esau anakhala munthu wodziwa kusaka, munthu wokonda kuyenda m’tchire. Koma Yakobo anali kukhala nthawi yambiri m’mahema. Iye anali munthu wosalakwa.” (Gen. 25:27) Katswiri wina womasulira Baibulo ananena kuti mawu achiheberi amene anamasuliridwa kuti “wosalakwa” amatanthauza “wokhulupirika kapena wosachimwa.”

7 Pamene Esau ndi Yakobo anali ndi zaka 15, Abulahamu yemwe anali agogo awo anamwalira. Koma zimene Yehova analonjeza Abulahamuyo sizinathere pomwepo. Pa nthawi ina, Yehova anauzanso Isaki lonjezolo ndipo ananena kuti mitundu yonse ya padziko lapansi idzapeza madalitso kudzera mwa mbewu ya Abulahamu. (Werengani Genesis 26:3-5.) Lonjezoli linasonyeza kuti Mesiya, yemwe ndi “mbewu” yokhulupirika imene inatchulidwa pa Genesis 3:15, adzabadwa m’banja la Abulahamu. Popeza kuti Esau anali woyamba kubadwa, iye anali woyenera kulandira madalitso a lonjezo limeneli. Apatu iye anali ndi mwayi waukulu kwambiri. Koma kodi Esau anayamikira mwayiwu?

Pewani chilichonse chimene chingakutayitseni madalitso anu

8, 9. (a) Kodi Esau anasankha kuchita chiyani ndi madalitso ake? (b) Patapita zaka, kodi Esau anazindikira chiyani ndipo anachita chiyani?

8 Tsiku lina Esau atafika kuchokera kutchire, anapeza Yakobo “akuphika mphodza.” Ndiyeno Esau anati: “Chonde, fulumira ndipatseko chakudya chofiiracho pang’ono, icho chofiiracho! Ndatopatu ine!” Poyankha, Yakobo anauza Esau kuti: “Choyamba, undigulitse ukulu wako monga woyamba kubadwa.” Kodi Esau anasankha kuchita chiyani? Mukhoza kudabwa mutamva yankho lake. Iye anati: “Ndiye ukuluwo uli ndi phindu lanji kwa ine?” Esau anasankha kusinthanitsa ukulu wake ndi mbale imodzi ya mphodza basi. Kuti Yakobo atenge ukuluwo m’njira yovomerezeka,  anati: “Choyamba lumbira kwa ine!” Ndiyeno Esau anapereka ukuluwo nthawi yomweyo. Zitatero, “Yakobo anapatsa Esau mkate ndi mphodza, ndipo iye anadya n’kumwa. Kenako, ananyamuka n’kumapita. Umu ndi mmene Esau ananyozera ukulu wake.”—Gen. 25:29-34.

9 Patapita zaka zambiri, Isaki anaona kuti watsala pang’ono kumwalira. Ndiyeno Rabeka anakonza zoti Yakobo alandiredi madalitso amene Esau anataya. Esau anazindikira mochedwa kuti sanasankhe mwanzeru. Iye anachonderera Isaki kuti: “Bambo ndidalitseni, ndidalitseni inenso chonde! . . . Kodi bambo, zoona palibiretu dalitso lililonse limene mwandisungirako?” Isaki atanena kuti sangasinthe madalitso amene wapereka kwa Yakobo, Esau “analira mofuula kwambiri, misozi ili mbwembwembwe.”—Gen. 27:30-38.

10. Kodi Yehova ankaona bwanji Esau ndi Yakobo ndipo n’chifukwa chiyani?

10 Malinga ndi zimene Malemba amanena, kodi Esau anali munthu wotani? Iye anasonyeza kuti zimene ankalakalaka zinali zofunika kwambiri kuposa madalitso amene akanalandira m’tsogolo. Esau sankaona kuti ukulu wake ndi wofunika kwambiri komanso zikuoneka kuti sankakonda kwenikweni Mulungu. Sanaganizirenso mmene zochita zake zingakhudzire ana ake. Koma Yakobo ankaona kuti madalitso ochokera kwa Mulungu ndi ofunika kwambiri. Mwachitsanzo, iye anatsatira malangizo a makolo ake posankha mkazi. (Gen. 27:46–28:3) Kuti achite zimenezi, analeza mtima ndiponso kupirira mavuto ena. Koma kenako anadzakhala kholo la Mesiya. Kodi Yehova ankaona bwanji Esau ndi Yakobo? Kudzera mwa mneneri Malaki, Yehova anati: ‘Ndinakonda Yakobo koma Esau ndinadana naye.’—Mal. 1:2, 3.

11. (a) Kodi Akhristufe tingaphunzire chiyani pa nkhani ya Esau? (b) N’chifukwa chiyani Paulo anayerekezera zimene Esau anachita ndi dama?

11 Kodi Akhristu a masiku ano angaphunzire chiyani pa nkhani ya Esau? Mtumwi Paulo anachenjeza Akhristu anzake kuti aonetsetse kuti “pasakhale wadama kapena aliyense wosayamikira zinthu zopatulika, ngati Esau, amene anapereka udindo wake monga woyamba kubadwa pousinthanitsa ndi chakudya chodya kamodzi kokha.” (Aheb. 12:16) Akhristu masiku anonso ayenera kumvera chenjezo limeneli. Tisasiye kuyamikira zinthu zopatulika. Tikatero, sitidzalola kuti zilakolako zathu zitilepheretse kulandira madalitso ochokera kwa Mulungu. N’chifukwa chiyani Paulo anayerekezera zimene Esau anachita ndi dama? Anatero chifukwa chakuti Esau anali ndi mtima woona kuti zilakolako zake ndi zofunika kwambiri. Munthu akakhala ndi mtima umenewu, akhoza kutaya zinthu zopatulika pongofuna kusangalala ndi zinthu ngati dama.

 KONZEKERETSANI MTIMA WANU PANOPA

12. (a) Kodi Satana amatiyesa bwanji? (b) Perekani zitsanzo za m’Baibulo zimene zingatithandize posankha zochita.

12 Atumiki a Yehovafe timayesetsa kupewa zinthu zimene zingatigwetsere mumsampha wochita chiwerewere. Timapempheranso kuti Yehova Mulungu atithandize kuti tisagonje tikamayesedwa. (Mat. 6:13) Koma nthawi zonse Satana amayesetsa kuti atilepheretse kukhala okhulupirika kwa Mulungu m’dziko loipali. (Aef. 6:12) Iye ndi mulungu wa dzikoli ndipo amadziwa kutchera misampha imene ikhoza kuchititsa anthu opanda ungwirofe kuti titsatire zilakolako zathu. (1 Akor. 10:8, 13) Tiyerekeze kuti pa nthawi ina mpata wapezeka woti mukhoza kuchita zinthu zolakwika zimene mwakhala mukulakalaka. Kodi mungatani? Kodi mungasankhe kuchita zimene Esau anachita n’kumanena kuti: ‘Chonde, fulumira ndipatseko’? Kapena kodi mungathawe mayeserowo ngati mmene Yosefe anachitira atayesedwa ndi mkazi wa Potifara?—Werengani Genesis 39:10-12.

13. (a) Kodi Akhristu ambiri masiku ano atsatira bwanji chitsanzo cha Yosefe? Nanga ena atsatira bwanji Esau? (b) Kodi tifunika kuchita chiyani kuti nafenso tisakhale ngati Esau?

13 Abale ndi alongo athu ambiri anakumanapo ndi mayesero ndipo anayenera kusankha kuti achite zinthu ngati Esau kapena Yosefe. Ambiri anasankha bwino ndipo anakondweretsa mtima wa Yehova. (Miy. 27:11) Koma pali Akhristu ena amene tingawayerekezere ndi Esau chifukwa anachita zinthu zimene zingawatayitse madalitso awo. Ndipotu anthu ambiri amene amadzudzulidwa kapena kuchotsedwa mu mpingo chaka chilichonse amakhala oti anachita chiwerewere. Choncho tifunika kukonzekeretsa mitima yathu panopa, tisanakumane ndi mayesero. (Sal. 78:8) Pali zinthu ziwiri zimene zingatithandize kuti tisagonje poyesedwa komanso kuti tizisankha zinthu mwanzeru.

GANIZIRANI ZOTSATIRA ZAKE NDIPONSO KONZEKERANI

Tikamafunafuna nzeru yochokera kwa Yehova, timakonzekera kuti tisagonje pa mayesero

14. Kodi tiyenera kuganizira mafunso ati kuti ‘tizinyansidwa ndi choipa n’kugwiritsitsa chabwino’?

14 Chinthu choyamba chimene tiyenera kuchita ndi kuganizira zotsatira za tchimo limene tingachite. Ngati timakonda kwambiri Yehova amene watipatsa madalitso, tidzayamikiranso kwambiri madalitsowo. Anthufe sitifuna kukhumudwitsa munthu amene timamukonda koma timayesetsa kuti timusangalatse. Choncho tisanachite zinthu zoipa zimene timalakalaka, tiyenera kuganizira mmene zochita zathuzo zingatikhudzire ifeyo komanso anzathu. Tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi zochita zanga zikhudza bwanji ubwenzi wanga ndi Yehova? Nanga zikhudza bwanji banja langa? Nanga bwanji abale ndi alongo anga mu mpingo? Kodi ndikhoza kukhumudwitsa ena?’ (Afil. 1:10) Tingadzifunsenso kuti: ‘Kodi ndingachite bwino kusankha kungosangalala pa nthawi yochepa koma n’kudzapeza mavuto ambirimbiri? Kodi ndikufuna kukhala ngati Esau yemwe analira momvetsa chisoni atazindikira kuti sanasankhe bwino?’ (Aheb. 12:17) Kuganizira mafunso ngati amenewa kungatithandize kuti ‘tizinyansidwa ndi choipa, n’kugwiritsitsa chabwino.’ (Aroma 12:9) Kukonda Yehova n’kumene kungatithandize kwambiri kuti tisataye madalitso athu.—Sal. 73:28.

15. Kodi tingakonzekere bwanji kuti tisagonje pa mayesero?

15 Chinthu chachiwiri chimene chingatithandize ndi kukonzekera kuti tisagonje pa mayesero. Yehova watipatsa zinthu zambiri zotithandiza kuteteza ubwenzi wathu ndi iye m’dziko loipali. Watipatsa zinthu monga Baibulo, misonkhano, utumiki ndiponso pemphero. (1 Akor. 15:58) Nthawi iliyonse  imene timapemphera kwa Yehova kuchokera mumtima kapena kulalikira ndi mtima wonse, timakonzekera kuti tisagonje pa mayesero. (Werengani 1 Timoteyo 6:12, 19.) Chomwe tiyenera kudziwa n’chakuti ngati tikufuna kuti tisagonje pa mayesero, tiyenera kuchita khama kwambiri. (Agal. 6:7) Chaputala chachiwiri cha buku la Miyambo chikusonyeza bwino zimenezi.

PITIRIZANI KUFUNAFUNA NZERU

16, 17. N’chiyani chingatithandize kusankha zinthu mwanzeru?

16 Chaputala chachiwiri cha buku la Miyambo chimatilimbikitsa kufunafuna nzeru ndi luso loganiza bwino. Munthu akapeza zinthu zimenezi, amatha kusiyanitsa pakati pa zabwino ndi zoipa. M’malo mongochita zimene zimamusangalatsa, iye amatha kudziletsa. Koma kuti tipeze nzeru ndi luso loganiza bwino, tiyenera kuchita khama kwambiri. Pofotokoza mfundo imeneyi, Baibulo limati: “Mwana wanga, ukamvera mawu anga ndi kusunga malamulo anga ngati chuma chamtengo wapatali, ukamvetsera nzeru ndi khutu lako, ukaika mtima wako pa kuzindikira, komanso ukaitana kumvetsa zinthu ndi kufuulira kuzindikira, ukamazifunafuna ngati siliva, ndi kuzifufuza ngati chuma chobisika, udzamvetsa tanthauzo la kuopa Yehova ndipo udzamudziwadi Mulungu. Pakuti Yehova amapereka nzeru. Kudziwa zinthu ndi kuzindikira kumatuluka m’kamwa mwake.”—Miy. 2:1-6.

17 Apa n’zoonekeratu kuti tiyenera kuchita zinthu zimene zalembedwa m’mavesi amenewa kuti tizitha kusankha zochita mwanzeru. Tikhoza kukhala olimba tikamayesedwa ngati tilola mawu a Yehova kutisintha, ngati timapemphera kwa Mulungu nthawi zonse kuti azititsogolera ndiponso ngati timapitiriza kufunafuna nzeru yochokera kwa Mulungu monga mmene anthu amachitira akamafufuza chuma chobisika.

18. Kodi inuyo simudzasiya kuchita chiyani ndipo chifukwa chiyani?

18 Tikamachita khama kwambiri, Yehova amatithandiza kupeza nzeru, kudziwa zinthu, kumvetsa zinthuzo ndiponso kukhala ozindikira. Tikamayesetsa kufufuza zinthu zimenezi m’pamene timalimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Ndiyeno ubwenzi umenewu ndi umene umatiteteza tikamayesedwa. Tikakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ndiponso tikamamuopa, timayesetsa kupewa zoipa. (Sal. 25:14; Yak. 4:8) Tiyeni tizinyadira kwambiri ubwenzi wathu ndi Yehova komanso kugwiritsa ntchito nzeru imene amatipatsa. Tikatero, tidzatha kusankha zinthu zimene zimakondweretsa mtima wake ndiponso kupewa zinthu zimene zingatitayitse madalitso athu.