Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndinu “Odzipereka pa Ntchito Zabwino”?

Kodi Ndinu “Odzipereka pa Ntchito Zabwino”?

“Khristu Yesu . . . anadzipereka m’malo mwa ife kuti . . . atiyeretse, kuti tikhale anthu akeake, odzipereka pa ntchito zabwino.”—TITO 2:13, 14.

1, 2. Kodi Mboni za Yehova zili ndi mwayi waukulu uti? Kodi mumaona bwanji mwayi umenewu?

ANTHU ambiri amanyadira akapatsidwa mphoto chifukwa chochita zinthu zinazake zabwino. Mwachitsanzo, ena alandirapo maulemu chifukwa chogwira ntchito modzipereka kwambiri kuti akhazikitse mtendere pakati pa anthu. Ngati anthuwo amalemekezedwa pa zifukwa zimenezo, kuli bwanji ifeyo? Pajatu Mulungu watipatsa mwayi waukulu wokhala akazembe kapena nthumwi zake kuti tithandize anthu kugwirizananso ndi Mlengi wawo.

2 Mulungu ndi Khristu atilamula kuti tichonderere anthu kuti ‘agwirizanenso ndi Mulungu.’ (2 Akor. 5:20) Yehova akutigwiritsa ntchito kuti athandize anthu kukhala pa ubwenzi wabwino ndi iye. Panopa, anthu mamiliyoni ambiri m’mayiko oposa 235 athandizidwa kale ndipo akuyembekeza kudzalandira moyo wosatha. (Tito 2:11) Timagwira ntchito modzipereka kwambiri poitana ‘aliyense amene akufuna, kuti amwe madzi a moyo kwaulere.’ (Chiv. 22:17) Timaona kuti ntchito imeneyi ndi yamtengo wapatali kwambiri ndipo timaigwira mwakhama. Chifukwa cha zimenezi, tingati ndife “odzipereka pa ntchito zabwino.” (Tito 2:14) M’nkhaniyi, tiona kuti kudzipereka kwathu pa ntchito zabwino kumathandiza kuti anthu ayambe kuphunzira za Yehova. Imodzi mwa ntchito zabwino zimene timagwira modzipereka ndi yolalikira.

TSANZIRANI YEHOVA NDI YESU PA NKHANI YA KUDZIPEREKA

3. Kodi mawu a pa Yesaya 9:7 amasonyeza chiyani?

3 Lemba la Yesaya 9:7 limafotokoza mmene Yehova adzachitire zinthu zabwino mu ulamuliro wa Mwana wake. Limati: “Yehova wa makamu adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.” Mawu amenewa amasonyeza kuti Yehova amafunitsitsa kupulumutsa anthu. Popeza kuti Yehova amachita zinthu modzipereka, ifenso timalimbikitsidwa kugwira ntchito imene watipatsa modzipereka. Timatsanzira Yehova tikamathandiza anthu mofunitsitsa  kuti aphunzire za iye. Popeza ndife antchito anzake a Mulungu, kodi timafunitsitsa kugwira ntchito yolalikira mwakhama kwambiri?—1 Akor. 3:9.

4. Kodi Yesu anatipatsa chitsanzo chotani pa nkhani yodzipereka mu utumiki?

4 Nayenso Yesu ndi wodzipereka potumikira Mulungu. Iye anapereka chitsanzo pa nkhani yolalikira mwakhama. Ngakhale kuti ankatsutsidwa kwambiri, anapitiriza kudzipereka pa ntchito yolalikira mpaka pamene anafa mozunzika. (Yoh. 18:36, 37) Khama lake lofuna kuthandiza anthu kuti adziwe Yehova linkawonjezeka kwambiri pamene imfa yake inkayandikira.

5. Kodi Yesu anachita chiyani mogwirizana ndi fanizo la mtengo wa mkuyu?

5 Mwachitsanzo, chakumapeto kwa 32 C.E., Yesu anapereka fanizo la munthu amene anali ndi mtengo wa mkuyu m’munda mwake. Mtengowu unakhala wosabala zipatso kwa zaka zitatu. Wosamalira munda atauzidwa kuti audule, anapempha kuti athire kaye manyowa. (Werengani Luka 13:6-9.) Pa nthawiyo, ophunzira ochepa okha ndi amene anali ngati zipatso za ntchito yolalikira ya Yesu. Iye anali ngati wosamalira mundawo ndipo analalikira mwakhama kwambiri ku Yudeya ndi ku Pereya pa miyezi 6 imene inatsala asanaphedwe. Ndipo kutatsala masiku ochepa kuti aphedwe, Yesu analirira anthu a mtundu wake amene “anamva ndi makutu awo koma osalabadira.”—Mat. 13:15; Luka 19:41.

6. N’chifukwa chiyani tiyenera kulalikira mwakhama kwambiri kuposa kale?

6 Popeza kuti tili m’masiku otsiriza enieni, ifenso tiyenera kulalikira mwakhama kwambiri kuposa kale. (Werengani Danieli 2:41-45.) Ndi mwayi waukulu kwambiri kukhala Mboni za Yehova. Ndife tokha m’dzikoli amene timauza anthu mmene mavuto athu adzathere. Munthu wina wolemba nkhani m’nyuzipepala anafotokoza za funso lovuta limene anthu sangapeze yankho lake. Funso lake ndi lakuti, “N’chifukwa chiyani anthu abwino amakumananso ndi mavuto?” Ndi udindo wathu komanso mwayi waukulu kuuza anthu mayankho ochokera m’Baibulo a mafunso ngati amenewa. Pali zifukwa zambiri zotilimbikitsa ‘kuyaka ndi mzimu’ pogwira ntchito imene Mulungu watipatsa. (Aroma 12:11) Yehova amatidalitsa tikamalalikira modzipereka ndipo tidzatha kuthandiza anthu kuti ayambe kudziwa komanso kukonda Yehova.

YEHOVA AMALEMEKEZEKA TIKAKHALA NDI MTIMA WODZIPEREKA

7, 8. Kodi anthu amene ali ndi mtima wodzipereka amalemekeza bwanji Yehova?

7 Mofanana ndi mtumwi Paulo, timadzipereka kwambiri pochita utumiki wathu moti nthawi zina ‘sitigona tulo’ kapena ‘kudya.’ (2 Akor. 6:5) Pali apainiya ambiri amene amaika utumiki wawo patsogolo uku akugwira ntchito zina kuti azipeza kangachepe. Palinso amishonale amene amadzipereka “ngati nsembe yachakumwa” pofuna kuthandiza anthu m’mayiko ena. (Afil. 2:17) Ndiye palinso akulu amene amagwira ntchito mwakhama moti nthawi zina sadya kapena kugona chifukwa chosamalira nkhosa za Yehova. Mu mpingo mulinso achikulire ndi anthu odwala amene amayesetsa kwambiri kupezeka pa misonkhano ndiponso kulowa mu utumiki. Timayamikira ndi mtima wonse atumiki a Mulungu onsewa. Zimene amachitazi zimathandiza kuti anthu aziyamikira utumiki wathu.

8 Munthu wina analemba kalata n’kuitumiza ku nyuzipepala ina ya ku United Kingdom. M’kalatayo ananena kuti: “Anthu akusiya kukhulupirira zipembedzo . . . Kodi atsogoleri a zipembedzowa kwenikweni amagwira ntchito yotani? Iwo sayenda n’kumafufuza anthu ngati mmene Khristu ankachitira . . . A Mboni za Yehova okha ndi amene amakonda anthu. Iwo amayenda n’kumalalikira mfundo zoona  za m’Baibulo.” Masiku ano, anthu amangochita zofuna zawo. Choncho tikamakhala ndi mtima wodzipereka timalemekeza kwambiri Yehova.—Aroma 12:1

Mukalowa mu utumiki, mumachitira umboni wamphamvu ngakhale kwa anthu amene akungokuonani

9. N’chiyani chingatilimbikitse kukhalabe odzipereka pa ntchito zabwino?

9 Kodi tingatani ngati tikuona kuti khama lathu mu utumiki layamba kuchepa? Tingachite bwino kuganizira chifukwa chake Yehova watiuza kuti tizigwira nawo ntchito yolalikira. (Werengani Aroma 10:13-15.) Kuti anthu adzapulumuke, ayenera kukhulupirira Mulungu ndiponso kuitana pa dzina lake. Koma anthuwa sangachite zimenezi ngati sitiwalalikira. Kuzindikira zimenezi kungatilimbikitse kukhalabe odzipereka pa ntchito zabwino ndiponso kuchita khama polengeza uthenga wabwino wa Ufumu.

KHALIDWE LATHU LABWINO NDI LOFUNIKA

Anthu amaona mukamagwira ntchito mwakhama ndiponso moona mtima

10. N’chifukwa chiyani tinganene kuti khalidwe lathu labwino ndi lofunika?

10 Ngakhale kuti tiyenera kuchita khama mu utumiki, zimenezi pazokha sizingathandize anthu kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Tiyeneranso kukhala ndi khalidwe labwino. Paulo anasonyeza kufunika kwa khalidwe labwino pamene analemba kuti: “Sitikuchita chilichonse chokhumudwitsa, kuti utumiki wathu usapezedwe chifukwa.” (2 Akor. 6:3) Kalankhulidwe kathu ndiponso khalidwe lathu labwino zimathandiza kuti anthu azimvetsera uthenga wathu ndiponso ayambe kulambira Yehova. (Tito 2:10) Nthawi zambiri timamva za anthu amene anayamba kuphunzira choonadi chifukwa choona khalidwe labwino la Akhristu.

11. N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira mozama za khalidwe lathu?

11 N’zoona kuti khalidwe lathu labwino lingathandize anthu. Koma ngati silili bwino likhoza kulepheretsa anthu kuphunzira za Yehova. Kaya tili kuntchito, kunyumba kapena kusukulu, tiyenera kuyesetsa kukhala ndi khalidwe labwino kuti anthu asapeze chifukwa  chonenezera ifeyo kapena utumiki wathu. Tizikumbukiranso kuti tikamachita machimo mwadala, zotsatira zake zidzakhala zoopsa. (Aheb. 10:26, 27) Mfundo imeneyi iyenera kutilimbikitsa kuganizira mozama zimene timachita ndiponso mmene ena amationera. Pamene makhalidwe a m’dzikoli akulowa pansi, anthu amitima yabwino amatha kuona bwinobwino “kusiyana . . . pakati pa munthu amene akutumikira Mulungu ndi amene sanatumikirepo Mulungu.” (Mal. 3:18) Choncho khalidwe lathu labwino ndi lofunika kwambiri chifukwa limathandiza kuti anthu ayambe kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu.

12-14. Kodi kupirira kwathu kumathandiza bwanji anthu ena? Perekani chitsanzo.

12 Paulo analembera Akhristu a ku Korinto kuti iye anakumana ndi masautso, zovuta, kumenyedwa ndiponso kutsekeredwa m’ndende. (Werengani 2 Akorinto 6:4, 5.) Tikamapirira mavuto, anthu amene akuona akhoza kuyamba kuphunzira za Yehova. Mwachitsanzo, zaka zapitazo anthu ena a ku Angola ankafuna kupha a Mboni za Yehova onse a kumeneko. A Mboni awiri ndiponso anthu ena 30 omwe anali pa misonkhano anagwidwa. Kenako anthu a m’deralo anasonkhana kuti aonerere pamene anthu osalakwawa ankamenyedwa koopsa mpaka kutuluka magazi. Ngakhale akazi ndi ana anamenyedwanso. Anachita zimenezi pofuna kuopseza anthu kuti asamamvetsere a Mboni za Yehova akamalalikira. Koma pambuyo pa zimenezi, anthu ambiri a m’deralo anapempha a Mboni kuti aziphunzira nawo Baibulo. Ndiyeno Yehova anadalitsa kwambiri ntchito yolalikira ndipo anthu ambiri anakhala a Mboni.

13 Chitsanzo chimenechi chikusonyeza kuti anthu ena amathandizidwa kwambiri tikamatsatira mfundo za m’Baibulo mokhulupirika. Anthu ambiri ayenera kuti anayamba kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu chifukwa choona kulimba mtima kwa Petulo ndi atumwi ena. (Mac. 5:17-29) Masiku anonso, anzathu akusukulu, akuntchito kapena achibale athu akhoza kumvetsera uthenga wabwino akaona kuti tikumvera Mulungu molimba mtima.

14 Nthawi iliyonse, pamakhala abale ena amene akuzunzidwa. Mwachitsanzo, ku Armenia kuli abale pafupifupi 40 amene ali kundende chifukwa chosalowerera ndale. Zikuonekanso kuti abale ena ambiri akhoza kumangidwa m’miyezi ikubwerayi. Ku Eritrea, atumiki a Yehova 55 ali kundende ndipo ena ndi a zaka zoposa 60. Ku South Korea, a Mboni pafupifupi 700 amangidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Ndipo izi zakhala zikuchitika kumeneko kwa zaka 60. Abale athu amene akuzunzidwa m’mayiko osiyanasiyana akukhalabe okhulupirika. Tiyeni tizipemphera kuti zimenezi zithandize kuti Mulungu alemekezeke ndiponso kuti anthu ofuna chilungamo ayambe kumulambira.—Sal. 76:8-10.

15. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti anthu angayambe kuphunzira Baibulo akaona kuti ndife oona mtima.

15 Anthu amathanso kuyamba kuphunzira Baibulo chifukwa choona kuti ndife oona mtima. (Werengani 2 Akorinto 6:4, 7.) Mwachitsanzo, mlongo wina ali m’basi ankafuna kugula tikiti pamakina ogulitsira matikiti. Koma mayi wina anamuuza kuti asagule tikitiyo chifukwa kaulendoko ndi kakafupi. Ndiyeno mlongoyu anafotokoza kuti ayenera kulipira ngakhale kaulendo katakhala kakang’ono. Mayiyo atatsika, dalaivala anafunsa mlongoyu kuti: “Kodi anti ndinu a Mboni?” Mlongoyu anayankha kuti: “Ee ndine wa Mboni. Kodi mwafunsiranji?” Iye anayankha kuti: “Ndinamva zimene mumakambirana ndi anzanu aja zokhudza kulipira tikiti. Ndikudziwa kuti a Mboni za Yehova ali m’gulu la anthu ochepa amene amachita zimenezi komanso nthawi zonse amakhala oona mtima.” Patapita miyezi yochepa, mlongoyu ali ku msonkhano, munthu wina anabwera n’kumufunsa kuti: “Kodi mukundikumbukira? Ndine dalaivala wa basi amene  ndinakufunsani za tikiti zija. Nditaona zimene munachita, ndinaganiza zoyamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova.” Nthawi zambiri anthu amafuna kuphunzira nafe Baibulo chifukwa choona kuti ndife oona mtima.

KHALIDWE LANU LIZILEMEKEZA MULUNGU NTHAWI ZONSE

16. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi makhalidwe monga kuleza mtima, chikondi ndi kukoma mtima? Perekani chitsanzo cha zimene atsogoleri a zipembedzo zonyenga amachita.

16 Timafunikanso kukhala ndi makhalidwe monga kuleza mtima, chikondi ndiponso kukoma mtima. Anthu akaona kuti tili ndi makhalidwe amenewa angafune kuphunzira za Yehova, zolinga zake ndiponso anthu ake. Khalidwe la Akhristu oona limasiyana kwambiri ndi la anthu amene amangodzionetsera pa maso chabe kuti ndi opembedza. Atsogoleri a zipembedzo ena alemera kwambiri chifukwa chodyera masuku pamutu nkhosa zawo. Iwo amagula nyumba ndi magalimoto odula pogwiritsa ntchito ndalama zimene anthu awo amapereka. Wina mpaka anafika pogulira galu wake kanyumba kokhala ndi makina oziziritsa mpweya. Anthu ambiri amene amati ndi otsatira a Khristu safuna n’komwe ‘kupatsa kwaulere.’ (Mat. 10:8) Mofanana ndi ansembe achinyengo mu Isiraeli, iwo “amaphunzitsa kuti apeze malipiro” ndipo zinthu zambiri zimene amaphunzitsa sizichokera m’Malemba. (Mika 3:11) Khalidwe lotereli silingathandize aliyense kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu.

17, 18. (a) Kodi timalemekeza bwanji Yehova tikamasonyeza makhalidwe ake? (b) N’chiyani chimakulimbikitsani kukhalabe odzipereka pa ntchito zabwino?

17 Koma anthu amafuna kuphunzira za Mulungu akamva mfundo zoona za m’Baibulo ndiponso akaona zinthu zabwino zimene timachitira anzathu. Mwachitsanzo, mpainiya wina amene anali mu utumiki anafika panyumba ya mayi wina wachikulire yemwe anali wamasiye. Mpainiyayo anafika pa nthawi imene mayiyo anali pamakwerero kuti asinthe babu la magetsi. Choncho mayiyo sanafune kulankhula naye. Koma m’baleyo anati: “Iii mugwatu mayi. Si bwino kuti mupange nokha zimenezo.” M’baleyo anamuthandiza kusintha babulo n’kumapita. Mwana wa mayiyo atamva, anadabwa kwambiri ndipo anafufuza m’baleyo kuti amuthokoze. Kenako mwanayo anayamba kuphunzira Baibulo.

18 N’chifukwa chiyani inuyo mukufuna kukhalabe odzipereka pa ntchito zabwino? Mwina n’chifukwa chodziwa kuti tikakhala odzipereka mu utumiki ndiponso kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna, timalemekeza Yehova komanso timathandiza anthu kuti adzapulumuke. (Werengani 1 Akorinto 10:31-33.) Timadzipereka pa ntchito yolalikira ndiponso kuyesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino chifukwa chokonda Yehova ndi anzathu. (Mat. 22:37-39) Tikakhala odzipereka pa ntchito zabwino, timakhala anthu osangalala kwambiri ngakhale panopa. Tikuyembekezera nthawi imene anthu onse adzakhala odzipereka polambira Yehova ndiponso kulemekeza Mlengi wathuyu.