Akulu, Kodi Mumalimbikitsa Anthu ‘Olefuka’?
Tiyerekeze kuti pali mlongo wina dzina lake Angela * amene ndi wosakwatiwa ndipo ali ndi zaka za m’ma 30. Iye ali ndi mantha pang’ono chifukwa akuyembekezera kuonana ndi akulu. Akudzifunsa kuti, ‘Kodi iwo akufuna kundiuza chiyani?’ Iye wajomba kangapo ku misonkhano koma amakhala atatopa kwambiri chifukwa chogwira ntchito tsiku lonse yosamalira anthu okalamba. Komanso iye akuda nkhawa kwambiri chifukwa mayi ake akudwala.
Zikanakhala kuti ndinu mkulu amene mukukaonana ndi Angela, kodi mukanamulimbikitsa bwanji? (Yer. 31:25) Choyamba, tiyeni tione zimene mungachite pokonzekera kuti mukachite ulendo waubusa wolimbikitsa.
GANIZIRANI MAVUTO AMENE ABALE ANU AKUKUMANA NAWO
Tonsefe timatopa nthawi zina chifukwa cha ntchito yathu kapena maudindo athu m’gulu la Yehova. Mwachitsanzo, mneneri Danieli ‘anatopa kwambiri’ ataona masomphenya amene sanawamvetse. (Dan. 8:27) Koma analimbikitsidwa ndi mngelo Gabirieli. Mngelo amene Mulungu anatumizayu anathandiza Danieli kumvetsa masomphenyawo ndiponso anamutsimikizira kuti Yehova wamva mapemphero ake. Anamuuzanso kuti Yehova ankamuonabe kuti ndi “munthu wokondedwa kwambiri.” (Dan. 9:21-23) Pa nthawi inanso, Danieli anafooka koma analimbikitsidwa kwambiri ndi mawu a mngelo wina.—Dan. 10:19.
Ifenso tikamakaona Mkhristu mnzathu amene wafooka kapena kutopa, tiyenera kuganizira mavuto amene akukumana nawo. Tiyenera kuganiziranso mmene mavutowo angamukhudzire. Tiziganiziranso makhalidwe abwino amene iye ali nawo. M’bale wina dzina lake Richard, amene wakhala mkulu kwa zaka zoposa 20, anati: “Ndimayesetsa kuganizira makhalidwe abwino amene abale anga ali nawo. Ndimaganiziranso kwambiri mavuto amene akukumana nawo. Izi zimandithandiza kusankha bwino zimene ndinganene powalimbikitsa.” Ngati mukupita ndi m’bale wina pa ulendo waubusa ndi bwino kuti mukambirane za Mkhristu amene mukukaonana nayeyo.
ATHANDIZENI KUKHALA OMASUKA
Munthu akhoza kuchita manyazi kufotokoza zakukhosi kwake. Choncho nthawi zina sangamasuke kuuza akulu mavuto amene akukumana nawo. Kodi akulu angatani kuti munthuyo azimasuka? Choyamba, mukakumana naye mungachite bwino kumwetulira ndiponso kulankhula mawu olimbikitsa. M’bale wina dzina lake Michael wakhala mkulu kwa zaka zoposa 40 ndipo akamachita ulendo waubusa amakonda kuyamba ndi mawu monga akuti: “Ndikuona kuti ntchito yosangalatsa kwambiri ya akulu ndi yoyendera abale ndi alongo n’kumacheza nawo. Lero ndasangalala kwambiri kuti mpata woti ticheze wapezeka.”
Mwina mungasankhe kuyamba ndi pemphero lochokera pansi pa mtima. M’pempherolo mukhoza kutchula makhalidwe abwino amene munthuyo ali nawo monga chikhulupiriro, chikondi kapena kupirira. Izi n’zimene mtumwi Paulo anachita popempherera abale ake. (1 Ates. 1:2, 3) Kuchita zimenezi kumathandiza kuti nonse mukhale ndi maganizo abwino pokambirana. Mawu anu akhozanso kumukhazika mtima m’malo munthuyo. M’bale wina dzina lake Ray, yemwe wakhala mkulu kwa nthawi yaitali, anati: “Nthawi zina anthufe timaiwala zinthu zabwino zimene timachita. Choncho munthu wina akatikumbutsa, timalimbikitsidwa.”
ALIMBIKITSENI NDI MAWU A MULUNGU
Mofanana ndi Paulo, mukhoza kugawira abale anu “mphatso inayake yauzimu” pokambirana nawo ngakhale vesi limodzi lokha. (Aroma 1:11) Mwachitsanzo, m’bale amene walefuka akhoza kumadziona kuti ndi wachabechabe. Nayenso wamasalimo ankadziona choncho ndipo anadziyerekezera ndi “thumba lachikopa mu utsi” limene lakwinyikakwinyika. Ngakhale kuti iye ankadziona choncho, ananenanso kuti: “Sindinaiwale malamulo anu.” (Sal. 119:83, 176) Mukhoza kufotokozera m’baleyo pang’ono mavesiwa kenako n’kumuuza kuti simukukayikira zoti nayenso ‘sanaiwale’ malamulo a Mulungu.
Mukakumana ndi mlongo wina amene wafooka, mwina mungamulimbikitse ndi fanizo lonena za dalakima imodzi imene inatayika. (Luka 15:8-10) N’kutheka kuti dalakimayi inali yofunika kwambiri chifukwa inali imodzi mwa madalakima ambiri asiliva omwe ankapanga nekilesi yamtengo wapatali kwambiri. Mukakambirana naye fanizoli, mungamuthandize kuona kuti iye ndi wofunika kwambiri mu mpingo. Mutamufotokozera zimenezi, mungamuuzenso kuti Yehova amamukonda kwambiri ndipo amamuona kuti ndi kankhosa kake kamtengo wapatali.
Abale ndi alongo athu amakonda kufotokoza zimene akudziwa pa malemba enaake. Choncho si bwino kuti muzingolankhula nokha. Mutawerenga lemba lokhudza vuto lawo, mungasankhe mawu enaake n’kuwapempha kuti anene maganizo awo pa mawuwo. Mwachitsanzo, mutawerenga lemba la 2 Akorinto 4:16, mungafunse kuti, “Kodi inuyo mwaona Yehova akukuthandizani ‘kukhalanso watsopano,’ kapena kuti kupezanso mphamvu, m’njira ziti?” Mukamachita zimenezi, mukhoza kulimbikitsana kwambiri.—Aroma 1:12.
Mungalimbikitsenso Mkhristu mnzanu mukamakambirana naye za munthu wina wa m’Baibulo amene anakumana ndi mavuto ofanana ndi ake. Mwachitsanzo, ngati iye akuvutika maganizo mukhoza kukambirana naye za anthu ngati Hana kapena Epafurodito. Anthu amenewo ankavutikanso maganizo nthawi zina koma Mulungu ankawaona kuti ndi amtengo wapatali kwambiri. (1 Sam. 1:9-11, 20; Afil. 2:25-30) Pali zitsanzo za anthu ambiri otchulidwa m’Baibulo zimene mukhoza kugwiritsa ntchito polimbikitsa anthu.
MUSASIYE KUWALIMBIKITSA
Mutapanga ulendo waubusa, muyenera kupitiriza kulimbikitsa anthu amene mwawayenderawo. (Mac. 15:36) Mwachitsanzo, pa mapeto pa ulendo waubusawo, mukhoza kugwirizana zoti mudzayendere limodzi mu utumiki. M’bale wina dzina lake Bernard, yemwe wakhala mkulu kwa nthawi yaitali, akakumananso ndi m’bale kapena mlongo amene anamuyendera amamufunsa kuti, “Kodi zijazi zikuyenda?” Mukamachita zimenezi, mudzadziwa ngati akufunika thandizo lina.
Masiku ano, abale ndi alongo athu amafuna kwambiri kudziwa kuti timawakonda, kuwamvetsa ndiponso kuwaganizira. (1 Ates. 5:11) Choncho musanapange ulendo waubusa, muziganizira kaye mavuto amene m’bale kapena mlongoyo akukumana nawo. Muzipemphera kuti ulendowo ukhale wolimbikitsa ndipo muzisankha malemba oyenerera. Mukatero, mudzapeza mfundo zimene mungagwiritse ntchito polimbikitsa anthu ‘olefuka.’
^ ndime 2 Names have been changed.