Yehova Ndi Wokhulupirika Ndiponso Amakhululuka
“Inu Yehova ndinu Mulungu wabwino ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka. Kukoma mtima kosatha kumene mumawasonyeza onse oitana pa inu ndi kwakukulu.”—SAL. 86:5.
1, 2. (a) N’chifukwa chiyani timasangalala tikakhala ndi anzathu omwe ndi okhulupirika komanso okhululuka? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?
KODI ndi munthu wotani amene munganene kuti ndi mnzanu weniweni? Mlongo wina dzina lake Ashley anati: “Ine ndimaona kuti mnzako weniweni ndi munthu amene amakhala wokonzeka nthawi zonse kukuthandiza ndiponso amene amakukhululukira ukalakwitsa.” Tonsefe timasangalala tikakhala ndi anzathu amene ndi okhulupirika ndiponso amene amatikhululukira. Tikakhala ndi anzathu oterewa, mtima wathu umakhala m’malo ndipo timadziwa kuti timakondedwa.—Miy. 17:17.
2 Yehova ndiye Mnzathu wokhulupirika ndiponso wokhululuka kuposa wina aliyense. M’pake kuti wamasalimo ananena kuti: “Yehova ndinu Mulungu wabwino ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka. Kukoma mtima kosatha kumene mumawasonyeza onse oitana pa inu ndi kwakukulu.” (Sal. 86:5) Kodi munthu wokhulupirika komanso wokhululuka amatani? Kodi Yehova amasonyeza bwanji makhalidwe amenewa? Nanga tingamutsanzire bwanji? Kupeza mayankho a mafunso amenewa kutithandiza kuti tizikonda kwambiri Yehova yemwe ndi Mnzathu wapamtima. Kutithandizanso kuti tizigwirizana kwambiri ndi anthu ena.—1 Yoh. 4:7, 8.
YEHOVA NDI WOKHULUPIRIKA
3. Kodi munthu wokhulupirika amatani?
3 Munthu wokhulupirika amakonda ndiponso kuthandiza munthu wina ndipo sasiya kuchita zimenezi ngakhale pamene zinthu zavuta. Munthu angakhalenso wokhulupirika ku chinthu chinachake. Koma Yehova ndi wokhulupirika kuposa wina aliyense.—Chiv. 16:5.
4, 5. (a) Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti ndi wokhulupirika? (b) Kodi kuganizira mmene Mulungu wasonyezera kuti ndi wokhulupirika kungakulimbikitseni bwanji?
4 Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti ndi wokhulupirika? Njira imodzi ndi yakuti iye sasiya atumiki ake okhulupirika. Davide ndi mmodzi mwa atumiki amenewa. Iye anapereka umboni woti Yehova ndi wokhulupirika. (Werengani 2 Samueli 22:26.) Pamene Davide ankakumana ndi mavuto, Yehova sanamusiye koma anamutsogolera, kumuteteza ndiponso kumupulumutsa. (2 Sam. 22:1) Davide ankadziwa kuti Yehova samangonena ndi pakamwa kuti ndi wokhulupirika. N’chifukwa chiyani Yehova ankachita zinthu mokhulupirika ndi Davide? Chifukwa chakuti nayenso Davide anali wokhulupirika. Yehova amayamikira kwambiri ngati atumiki ake ali okhulupirika ndipo iye amakhalanso wokhulupirika kwa iwo.—Miy. 2:6-8.
5 Timalimbikitsidwa kwambiri tikaganizira mmene Yehova wasonyezera kuti ndi wokhulupirika. M’bale wina dzina lake Reed anati: “Ndimalimbikitsidwa kwambiri ndikaganizira mmene Yehova ankachitira zinthu ndi Davide pa mavuto ake. Ngakhale pamene Davide anali kuthawa n’kumakhala m’mapanga, Yehova ankamuthandiza. Zimenezi zimandikumbutsa kuti Yehova sadzandisiya ndikakhalabe wokhulupirika kwa iye.” Sitikukayikira kuti nanunso mumamva choncho.—Aroma 8:38, 39.
6. Kodi Yehova amasonyeza kuti ndi wokhulupirika m’njira zinanso ziti? Nanga atumiki ake amapindula bwanji ndi zimenezi?
6 Kodi Yehova amasonyeza kuti ndi wokhulupirika m’njira zinanso ziti? Nthawi zonse iye amatsatira mfundo zake ndipo amatitsimikizira kuti: “Ine sindisintha ngakhale kwa wokalamba.” (Yes. 46:4) Iye amasankha zinthu mogwirizana ndi mfundo zake zosasintha zokhudza chabwino ndi choipa. (Mal. 3:6) Komanso nthawi zonse Yehova amakwaniritsa malonjezo ake. (Yes. 55:11) Atumiki onse a Yehova amapindula ndi kukhulupirika kwake. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti tikamayesetsa kutsatira mfundo za Yehova, sitikayikira kuti iye adzatidalitsa mogwirizana ndi lonjezo lake.—Yes. 48:17, 18.
KHALANI OKHULUPIRIKA NGATI YEHOVA
7. Kodi tingatsanzire bwanji Yehova pa nkhani yokhulupirika?
7 Kodi tingatsanzire bwanji Yehova pa nkhani yokhulupirika? Njira imodzi ndi kuyesetsa kuthandiza anthu amene akuvutika. (Miy. 3:27) Mwachitsanzo, kodi panopa mukudziwa m’bale kapena mlongo amene akuda nkhawa chifukwa cha matenda, kutsutsidwa ndi achibale ake kapena chifukwa cha zimene walakwitsa? Mungachite bwino kulankhula naye kuti mumuuze “mawu abwino ndiponso olimbikitsa.” (Zek. 1:13) * Mukatero, mudzasonyeza kuti ndinu mnzake wokhulupirika amene ‘amamamatira kuposa m’bale wake.’—Miy. 18:24.
8. Kodi tingatsanzire Yehova pa nkhani yokhulupirika m’njira zinanso ziti?
8 Tikhoza kutsanziranso Yehova tikamakhala okhulupirika kwa anthu amene timawakonda. Mwachitsanzo, ngati tili pa banja, tiyenera kukhala okhulupirika kwa mwamuna kapena mkazi wathu. (Miy. 5:15-18) Choncho tiyenera kupewa chilichonse chimene chingatigwetsere mumsampha wa chigololo. (Mat. 5:28) Timasonyezanso kuti ndife okhulupirika kwa Akhristu anzathu popewa nkhani zamiseche. Tiyenera kupewa kulankhula ngakhalenso kumvetsera nkhani zoterezi.—Miy. 12:18.
9, 10. (a) Kodi chofunika kwambiri ndi kukhala okhulupirika kwa ndani? (b) N’chifukwa chiyani kumvera malamulo a Yehova kumakhala kovuta nthawi zina?
9 Koma chofunika kwambiri ndi kukhala okhulupirika kwa Yehova. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tingatero poyesetsa kuona zinthu mmene iye amazionera. Mwachitsanzo, tizikonda zimene amakonda n’kumadana ndi zimene amadana nazo. (Werengani Salimo 97:10.) Pamene tikuyesetsa kuona zinthu mmene Yehova amazionera m’pamenenso timakhala ndi mtima wofunitsitsa kumvera malamulo ake.—Sal. 119:104.
10 N’zoona kuti nthawi zina kumvera malamulo a Yehova kumakhala kovutirapo. Pamafunika khama ndithu kuti tikhalebe okhulupirika. Tiyerekeze kuti pali mlongo wina amene akufunitsitsa kukwatiwa koma sakupeza m’bale womuyenerera. (1 Akor. 7:39) Ndiyeno akakhala kuntchito, anzake omwe si Mboni amamukopa kuti ayambe chibwenzi ndi munthu wina. Koma iye akuyesetsa kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova. Akhristu oterewa timawayamikira kwambiri chifukwa cha kukhulupirika kwawo. Tisaiwale kuti Yehova adzapereka mphoto kwa anthu onse amene amakhalabe okhulupirika akamakumana ndi mavuto.—Aheb. 11:6.
YEHOVA AMAKHULULUKA
11. Kodi munthu wokhululuka amachita chiyani?
11 Yehova ndi wokonzeka kukhululuka ndipo limeneli ndi khalidwe lina losangalatsa kwambiri. Kodi munthu wokhululuka amachita chiyani? Iye amakhululukira munthu wina ngati pali chifukwa chomveka chochitira zimenezi. Izi sizikutanthauza kuti munthu wokhululuka amalekerera kapena kunyalanyaza zinthu zoipa zimene ena amuchitira. M’malomwake, zikutanthauza kuti iye sasunga chakukhosi. Malemba amasonyeza kuti Yehova ndi ‘wokonzeka kukhululukira’ anthu amene amalapa ndi mtima wonse.—Sal. 86:5.
12. (a) Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti ndi wokhululuka? (b) Kodi mawu oti ‘kufafaniza’ machimo amatanthauza chiyani?
12 Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti ndi wokhululuka? Yehova amakhululuka “ndi mtima wonse” ndipo akatero sakumbutsanso nkhaniyo. (Yes. 55:7) Kodi tikudziwa bwanji kuti Yehova amakhululuka ndi mtima wonse? Tangoganizirani mawu a pa Machitidwe 3:19. (Werengani.) Mtumwi Petulo anauza omvera ake kuti: “Lapani ndi kutembenuka.” Munthu wochimwa amene walapadi amamva chisoni kwambiri ndi zimene anachita. Amayesetsanso kuti asadzachitenso tchimolo. (2 Akor. 7:10, 11) Munthu wotereyu ‘amatembenuka’ kapena kuti kusiya machimo akewo n’kuyamba kuchita zinthu zosangalatsa Mulungu. Kodi Petulo anauza anthuwo kuti akalapadi ndi kutembenuka, zotsatira zake zikhala zotani? Ananena kuti machimo awo ‘adzafafanizidwa.’ Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti ‘kufafanizidwa’ akutanthauza ‘kufufuta kapena kupukuta.’ Yehova akakhululuka, zimakhala ngati watenga labala ndi kufufuta zolakwikazo. Iye amakhululuka ndi mtima wonse.—Aheb. 10:22; 1 Yoh. 1:7.
13. Kodi mawu akuti “machimo awo sindidzawakumbukiranso” amatitsimikizira za chiyani?
13 Kodi tikudziwa bwanji kuti Yehova sakumbutsanso machimo amene wakhululuka? Tiyeni tione mawu a Yeremiya okhudza pangano latsopano limene Yehova anapanga ndi Akhristu odzozedwa. Panganoli limachititsa kuti anthu amene amakhulupirira dipo akhululukidwe machimo awo. (Werengani Yeremiya 31:34.) Yehova anati: “Ine ndidzawakhululukira zolakwa zawo ndipo machimo awo sindidzawakumbukiranso.” Choncho Yehova amatitsimikizira kuti akatikhululukira, sadzakumbutsanso za machimowo. Iye sakumbukiranso machimowo n’kuganiza zoti atiimbe mlandu kapena kutilanga. M’malomwake, Yehova akakhululuka machimo, amasiyiratu kuwaganizira.—Aroma 4:7, 8.
14. Kodi kuganizira mfundo yakuti Yehova ndi wokhululuka kungatilimbikitse bwanji? Perekani chitsanzo.
14 Kuganizira mfundo yakuti Yehova amakhululuka kumatilimbikitsa kwambiri. Tiyeni tione chitsanzo cha mlongo wina amene tangomupatsa dzina loti Elaine. Zaka zambiri zapitazo, iye anachotsedwa mu mpingo ndipo patapita nthawi, anabwezeretsedwa. Elaine anati: “Ndinkadziuza mumtima kuti Yehova wandikhululukira ndipo ndinkauzanso anthu ena kuti ndikukhulupirira zimenezi. Komabe mumtimamu ndinkaona kuti anthu ena ali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova kusiyana ndi ineyo.” Koma Elaine analimbikitsidwa kwambiri atawerenga ndiponso kuganizira mawu a m’Baibulo amene amafotokoza mmene Yehova amakhululukira. Iye anati: “M’mbuyo monsemu, sindinamvepo kuti Yehova amandikonda ngati mmene ndikumvera panopa.” Iye analimbikitsidwa kwambiri ndi mfundo yakuti: “Yehova akatikhululukira machimo athu, tisamaganize kuti timakhala othimbirira ndi machimowo kwa moyo wathu wonse.” * Elaine anati: “Ndinazindikira kuti sindinkakhulupirira kuti Yehova angandikhululukire ndi mtima wonse. Ndinkaganiza kuti chikumbumtima changa chidzapitiriza kundivutitsa kwa moyo wanga wonse. Ndikudziwa kuti zitengabe nthawi kuti zonse zikhale bwinobwino. Koma panopa ndikuona kuti ndayamba kuyandikira kwa Yehova ndipo ndayambanso kusangalala.” Kunena zoona, timatumikira Mulungu wachikondi ndiponso wokhululuka.—Sal. 103:9.
KHALANI OKHULULUKA NGATI YEHOVA
15. Kodi tingatsanzire bwanji Yehova pa nkhani ya kukhululuka?
15 Ifenso tingatsanzire Yehova ngati timakhululukira anthu ena pakakhala zifukwa zomveka. (Werengani Luka 17:3, 4.) Tisamaiwale kuti Yehova akakhululuka, sakumbutsanso machimowo. Ifenso tikakhululukira anthu ena, tiziiwala nkhaniyo ndipo tisamawakumbutsenso.
16. (a) Kodi munthu wokhululuka amalekerera zoipa kapena kulola kuti anthu ena azimupezerera? Fotokozani. (b) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Mulungu atikhululukire?
16 Sikuti munthu wokhululuka amangolekerera zoipa kapena kulolera kuti anthu ena azimupezerera. M’malomwake, iye amasankha kuti asasunge chakukhosi. Koma tizikumbukira kuti Mulungu amatikhululukira pokhapokha ngati nafenso timakhululukira anthu ena. (Mat. 6:14, 15) Pajatu Yehova amatimvera chisoni ndipo amakumbukira kuti “ndife fumbi.” (Sal. 103:14) Choncho nafenso tiyenera kumvera anthu ena chisoni n’kumawakhululukira ndi mtima wonse.—Aef. 4:32; Akol. 3:13.
17. N’chiyani chingatithandize ngati Mkhristu mnzathu watikhumudwitsa?
17 N’zoona kuti kukhululuka kumavuta nthawi zina. Ngakhale Akhristu ena odzozedwa a m’nthawi ya atumwi ankavutika kuti azikhululukirana. (Afil. 4:2) Ngati Mkhristu mnzathu watikhumudwitsa, kodi n’chiyani chingatithandize kuti timukhululukire? Tiyeni tiganizire chitsanzo cha Yobu. Iye atakumana ndi mavuto, Elifazi, Bilidadi ndi Zofari, omwe ankati ndi anzake, anabwera kudzamuona. Koma m’malo momulimbikitsa, anangomuimba milandu yabodza. Zimenezi zinamupweteka kwambiri Yobu. (Yobu 10:1; 19:2) Koma kenako Yehova anadzudzula anzake achinyengowo. Mulungu anawauza kuti apite kwa Yobu kuti iye awaperekere nsembe chifukwa cha machimo awowo. (Yobu 42:7-9) Koma Yehova anauzanso Yobu kuti achite zinthu zina. Anamuuza kuti apempherere anthu amene ankamuimba mlanduwo. Yobu anamvera Yehova ndipo Yehova anamudalitsa chifukwa chokhala ndi mtima wokhululuka. (Werengani Yobu 42:10, 12, 16, 17.) Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Kupempherera mochokera pansi pa mtima munthu amene watikhumudwitsa kungatithandize kumukhululukira ndi mtima wonse.
PITIRIZANI KUONA KUTI MAKHALIDWE A YEHOVA NDI AMTENGO WAPATALI
18, 19. Kodi tingatani kuti tiziona makhalidwe a Yehova kukhala amtengo wapatali kwambiri?
18 Talimbikitsidwa kwambiri kukambirana makhalidwe abwino a Yehova. Taona kuti iye amathandiza anthu kuti azimasuka naye, alibe tsankho, ndi wowolowa manja, wololera, wokhulupirika ndiponso amakhululuka. Komatu kutereku tangoyepula pamwamba chabe. Tidzakhala ndi mwayi wophunzira za Yehova mpaka muyaya. (Mlal. 3:11) Tikugwirizana ndi mfundo ya mtumwi Paulo yakuti: “Ndithudi, madalitso amene Mulungu amapereka ndi ochuluka kwambiri. Nzeru zake n’zozama, ndiponso iye ndi wodziwa zinthu kwambiri.” Kuwonjezera pamenepo, Yehova ndi wachikondi komanso ali ndi makhalidwe 6 amene takambiranawa.—Aroma 11:33.
19 Tiyeni tonsefe tiziyesetsa kudziwa bwino makhalidwe a Yehova, kuwaganizira mozama komanso kumutsanzira. (Aef. 5:1) Zimenezi zingathandize kuti tiziwaona kuti ndi amtengo wapatali. Komanso tidzafika pogwirizana kwambiri ndi wamasalimo amene anaimba kuti: “Kwa ine kuyandikira kwa Mulungu ndi chinthu chabwino.”—Sal. 73:28.
^ ndime 7 Kuti mupeze malangizo ena, onani nkhani yakuti “Kodi Mwalimbikitsapo Aliyense Posachedwapa?” mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 1995 ndiponso yakuti “Fulumizanani ku Chikondano ndi Ntchito Zabwino—Motani?” mu Nsanja ya Olonda ya April 1, 1995.