Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

M’bale Watsopano M’Bungwe Lolamulira

M’bale Watsopano M’Bungwe Lolamulira

Tsiku Lachitatu m’mawa pa September 5, 2012, analengeza ku banja la Beteli ku United States ndi ku Canada kuti pali m’bale watsopano m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. M’bale Mark Sanderson anayamba kutumikira m’bungweli pa September 1, 2012.

M’bale Sanderson analeredwa ndi makolo a Mboni za Yehova mumzinda wa San Diego ku California m’dziko la United States. Iye anabatizidwa pa February 9, 1975 ndipo anayamba kuchita upainiya kudera la Saskatchewan m’dziko la Canada pa September 1, 1983. Mu December 1990, anamaliza maphunziro a Sukulu Yophunzitsa Utumiki (yomwe panopa ikuchedwa Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatira) ku United States. M’bale Sanderson anaikidwa kukhala mpainiya wapadera pachilumba cha Newfoundland m’dziko la Canada mu April 1991. Kenako anadzakhala woyang’anira dera wogwirizira. Ndiyeno mu February 1997, anaitanidwa kuti azikatumikira ku Beteli ya ku Canada. Mu November 2000, anaitanidwa kuti azikatumikira ku nthambi ya ku United States. Kumeneko ankagwira ntchito mu Dipatimenti Yoyang’anira Zachipatala ndipo kenako anayamba kugwira ntchito mu Dipatimenti ya Utumiki.

Mu September 2008, M’bale Sanderson analowa Sukulu ya Abale a M’komiti ya Nthambi. Kenako anatumizidwa kukatumikira m’Komiti ya Nthambi ku Philippines. Mu September 2010, anauzidwa kuti abwerere ku United States kuti azikathandizira m’Komiti ya Utumiki ya Bungwe Lolamulira.