Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kusiyanitsa Zinthu N’kothandiza Kwambiri

Kusiyanitsa Zinthu N’kothandiza Kwambiri

Yesu anali Mphunzitsi wabwino kwambiri kuposa munthu aliyense padzikoli. Iye ankagwiritsa ntchito mafunso komanso mafanizo. Mwina inunso mumayesetsa kutsanzira kaphunzitsidwe kake. Koma kodi mukudziwa kuti iye ankakondanso kusiyanitsa zinthu pophunzitsa?

Anthu ambiri akamalankhula amakonda kusiyanitsa zinthu. Mwina nanunso mumachita zimenezi. Mwachitsanzo, mukhoza kunena kuti: “Aja anena kuti nthochi zonsezi ndi zakupsa koma izitu ndi zosapsa.” Kapena mukhoza kunena kuti: “Mtsikanayu ali wamng’ono anali wamantha koma pano ndi wolimba mtima.”

Posiyanitsa zinthu, timagwiritsa ntchito mawu ngati koma, m’malomwake, apo ayi kapena ngakhale zili choncho. Kusiyanitsa zinthu kumasangalatsa ndipo kumathandiza anthu kuti amvetse zimene tikunena.

N’zoona kuti m’zilankhulo zina anthu sakonda kugwiritsa ntchito mawu osiyanitsira zinthu, komabe tonsefe tiyenera kudziwa ubwino wa mawuwa. Tikutero chifukwa chakuti mawu amenewa amapezekapezeka m’Baibulo. Monga tanena kale, Yesu ankakonda kugwiritsa ntchito mawu amenewa. Mwachitsanzo, iye ananena kuti: “Anthu akayatsa nyale, saivundikira ndi dengu, koma amaiika pachoikapo nyale.” “Sindinabwere kudzaziwononga [Chilamulo kapena Zolemba za aneneri] koma kudzazikwaniritsa.” “Inu munamva kuti anati, ‘Usachite chigololo.’ Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense woyang’anitsitsa mkazi . . . “ “Inu munamva kuti anati, ‘Diso kulipira diso, ndi dzino kulipira dzino.’ Koma ine ndikukuuzani kuti: Usalimbane ndi munthu woipa, koma wina akakumenya mbama patsaya lakumanja, umutembenuzirenso linalo.”—Mat. 5:15, 17, 27, 28, 38, 39.

Mabuku ena a m’Baibulo amasiyanitsanso zinthu. Zimenezi zimathandiza kuti timvetse bwino mfundo inayake kapena tidziwe ubwino wochita zinthu zina. Ngati muli ndi ana, mungachite bwino kuganizira mawu akuti: “Inunso abambo, musamapsetse mtima ana anu, koma muwalere m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4) Ngati mtumwi Paulo akanangolemba kuti atate (kapena amayi) ayenera kulera ana awo m’malangizo a Mulungu, zikanakhala zomveka komanso zoona. Koma mfundoyi imamveka bwino kwambiri chifukwa choti ananena kuti: ‘Musamawapsetse mtima, koma muwalere m’malangizo a Yehova.’

M’chaputala chomwechi, Paulo analembanso kuti: “Sitikulimbana ndi anthu athupi la magazi ndi nyama ayi, koma ndi . . . makamu a mizimu yoipa m’malo akumwamba.” (Aef. 6:12) Kalembedwe kameneka kamatithandiza kuona kuti tili pa nkhondo yoopsa kwabasi. Sikuti tikungolimbana ndi anthu koma makamu a mizimu yoipa.

 ZIMENE MUNGACHITE KUTI KUSIYANITSA ZINTHU KUKUTHANDIZENI

M’buku lomweli la Aefeso, timapeza malemba ena amene Paulo anagwiritsa ntchito mawu osiyanitsira zinthu. Tikamaganizira mawu amenewa timamvetsa bwino mfundo ya Paulo komanso kuona zoyenera kuchita.

Mungachite bwino kuwerenga tchati chimene chili patsamba 4 ndi 5 kuti muone malemba enanso a m’buku la Aefeso amene amasiyanitsa zinthu. Mukamawerenga malemba amenewa, muziganizira za moyo wanu. Dzifunseni kuti: ‘Kodi ineyo mtima wanga ndi wotani? Kodi nditakumana ndi zoterezi ndingatani? Kodi anthu ena angaone kuti ndili mbali iti pa zinthu ziwirizi?’ Ngati mukuona kuti pali zina zimene muyenera kusintha, yesetsani kusintha. Lolani kuti mawu osiyanitsa zinthuwo akuthandizeni.

Mwinanso mungagwiritse ntchito tchatichi pa kulambira kwanu kwa pabanja. Choyamba mungawerengere limodzi malemba onsewo. Kenako mmodzi anganene mbali yoyamba ya lemba lina, ndiyeno enawo ayese kukumbukira mfundo ya mbali yachiwiri ya lembalo. Zimenezi zingathandize kuti mukambirane mbali yachiwiriyo ndi kuona mmene mungaigwiritsire ntchito. Kukambirana mawu osiyanitsa zinthu m’njira imeneyi kungathandize ana ndi achikulire omwe kuti akhale ndi makhalidwe abwino.

Ndani akukumbukira mbali yachiwiri?

Mukaona kufunika kwa mawu osiyanitsa zinthu mudzatha kuwazindikira mosavuta m’Baibulo, ndipo mudzaona kuti ndi othandiza mu utumiki. Mwachitsanzo, polalikira munganene kuti: “Anthu ambiri amanena kuti aliyense ali ndi mzimu umene suufa, koma onani zimene Mawu a Mulungu amanena.” Kapena pophunzira Baibulo ndi munthu, mungafunse kuti: “Anthu ambiri kwathu kuno amakhulupirira kuti Yesu ndi Mulungu. Inu maganizo anu ndi otani? Koma kodi mukudziwa zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi?”

Apa taona kuti pali malemba ambiri amene amasiyanitsa zinthu ndipo angatithandize kuyenda m’njira ya Mulungu. Tingathenso kugwiritsa ntchito mawu osiyanitsa zinthu pothandiza anthu ena kuti adziwe mfundo za m’Baibulo.