Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zikumbutso za Yehova Ndi Zodalirika

Zikumbutso za Yehova Ndi Zodalirika

“Zikumbutso za Yehova ndi zodalirika, zimapatsa nzeru munthu wosadziwa zinthu.”—SAL. 19:7.

1. (a) Kodi ndi nkhani ziti zimene timaphunzira mobwerezabwereza? (b) Kodi kuchita zimenezi kumatithandiza bwanji?

MWINA nthawi ina mukukonzekera Phunziro la Nsanja ya Olonda munadzifunsapo kuti, ‘Kodi nkhani imeneyi sikufanana ndi imene tinaphunzira m’mbuyomu?’ Ngati mwakhala m’gulu la Yehova kwa nthawi yaitali, muyenera kuti mukudziwa zoti nkhani zina timaziphunzira mobwerezabwereza. Mwachitsanzo, timaphunzira za Ufumu wa Mulungu, dipo, ntchito yophunzitsa anthu ndiponso makhalidwe monga chikondi ndi chikhulupiriro. Kuphunzira nkhani ngati zimenezi mobwerezabwereza kumatithandiza kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba komanso kuti tizichita “zimene mawu [a Mulungu] amanena, osati kungomva chabe.”—Yak. 1:22.

2. (a) Kodi mawu akuti zikumbutso za Mulungu nthawi zambiri amatanthauza chiyani? (b) Kodi malamulo a Yehova amasiyana bwanji ndi a anthu?

2 Mawu achiheberi amene anamasuliridwa kuti “zikumbutso” nthawi zambiri amatanthauza malamulo kapena malangizo amene Mulungu amapatsa anthu ake. Malamulo a anthu amafunika kukonzedwa kapena kusinthidwa nthawi ndi nthawi, koma malamulo a Yehova amakhala odalirika nthawi zonse. Ngakhale kuti Yehova anapereka malamulo ena pa nthawi inayake ndiponso pa zifukwa zinazake, malamulowo amakhalabe othandiza. Wamasalimo anati: “Zikumbutso zanu zidzakhalabe zolungama mpaka kalekale.”—Sal. 119:144.

3, 4. (a) Kodi nthawi zina Yehova angapereke zikumbutso pofuna kutani? (b) Kodi chinkachitika n’chiyani Aisiraeli akamvera zikumbutso za Yehova?

3 Nthawi zina Yehova angapereke zikumbutso pofuna kuchenjeza anthu. Iye ankachenjeza Aisiraeli pogwiritsa ntchito aneneri ake. Mwachitsanzo, Aisiraeli atatsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa, Mose  anawachenjeza kuti: “Samalani kuti mitima yanu isakopeke ndipo musapatuke ndi kupembedza milungu ina n’kumaiweramira. Mukatero mkwiyo wa Yehova udzakuyakirani.” (Deut. 11:16, 17) Baibulo limasonyeza kuti Mulungu ankapatsa anthu ake zikumbutso zambiri pofuna kuwathandiza.

4 Nthawi zambiri, Yehova ankauza Aisiraeli kuti ayenera kumuopa, kumumvera ndiponso kulemekeza dzina lake. (Deut. 4:29-31; 5:28, 29) Aisiraeliwo akamvera zikumbutsozi, ankadalitsidwa kwambiri.—Lev. 26:3-6; Deut. 28:1-4.

KODI AISIRAELI ANKATANI AKALANDIRA ZIKUMBUTSO ZA MULUNGU?

5. N’chifukwa chiyani Yehova anathandiza Mfumu Hezekiya?

5 Pa mavuto onse amene Aisiraeli ankakumana nawo, Mulungu anapitiriza kuthandiza anthu amene ankamumvera. Mwachitsanzo, Senakeribu, yemwe anali mfumu ya Asuri, anaukira Yuda ndipo ankafuna kuchotsa Hezekiya pa udindo wake monga mfumu. Choncho Yehova anatumiza mngelo kuti akathandize Hezekiya, ndipo usiku umodzi wokha, mngeloyo “anapha mwamuna aliyense wamphamvu ndi wolimba mtima” mumsasa wa asilikali a Asuri. Zitatero, Senakeribu anabwerera kwawo ali wamanyazi. (2 Mbiri 32:21; 2 Maf. 19:35) N’chifukwa chiyani Mulungu anathandiza Mfumu Hezekiya? Chifukwa chakuti “Hezekiya anapitiriza kumamatira Yehova. Sanasiye kum’tsatira, koma anapitiriza kusunga malamulo” ake.—2 Maf. 18:1, 5, 6.

Zikumbutso za Yehova zinalimbikitsa Yosiya kuti athandize anthu kuyambanso kulambira Mulungu woona (Onani ndime 6)

6. Kodi Yosiya anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira Yehova?

6 Munthu wina amene anamvera malamulo a Yehova anali Mfumu Yosiya. Kuyambira ali ndi zaka 8 zokha, “iye anachita zoyenera pamaso pa Yehova . . . Sanapatukire mbali ya kudzanja lamanja kapena lamanzere.” (2 Mbiri 34:1, 2) Yosiya anasonyeza kuti ankakhulupirira Yehova. Iye anachita zimenezi pochotsa mafano m’dzikolo ndi kuthandiza anthu kuti ayambenso kulambira Mulungu woona. Chifukwa cha zimenezi, Yosiya komanso anthu onse m’dzikolo anadalitsidwa.Werengani 2 Mbiri 34:31-33.

7. Kodi chinkachitika n’chiyani Aisiraeli akasiya kumvera zikumbutso za Yehova?

7 Koma n’zomvetsa chisoni kuti si nthawi zonse pamene anthu a Mulungu ankakhulupirira zikumbutso za Yehova. Iwo nthawi zina ankamvera, nthawi zina ayi. Chikhulupiriro chawo chitachepa, iwo ‘ankatengeka kupita uku ndi uku ndi mphepo iliyonse ya chiphunzitso.’ (Aef. 4:13, 14) Mogwirizana ndi chenjezo  la Mulungu, iwo akasiya kukhulupirira zikumbutso za Mulungu, ankakumana ndi mavuto aakulu.—Lev. 26:23-25; Yer. 5:23-25.

8. Kodi atumiki a Mulungu masiku ano akufanana bwanji ndi Aisiraeli?

8 Kodi atumiki a Mulungu masiku ano akufanana bwanji ndi Aisiraeli? Iwonso amapatsidwa malangizo. (2 Pet. 1:12) Nthawi iliyonse imene timawerenga Baibulo, timalandira zikumbutso za Mulungu. Tili ndi ufulu wosankha kumvera malangizo a Yehova kapena kuchita zimene timaona kuti ndi zolondola. (Miy. 14:12) N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira zikumbutso za Yehova? Nanga kutsatira zikumbutsozo kungatithandize bwanji? Tiyeni tione.

MUZIMVERA MULUNGU KUTI MUKHALE NDI MOYO

9. Kodi Yehova ankakumbutsa bwanji Aisiraeli kuti iye akuwatsogolera m’chipululu?

9 Pamene Aisiraeli ankayamba ulendo wawo wazaka 40 woyenda ‘m’chipululu chochititsa mantha,’ Yehova sanawauze zimene azidzachita powatsogolera, kuwateteza komanso kuwasamalira. Koma ankawathandiza nthawi ndi nthawi kudziwa kuti zinthu zingawayendere bwino akamamukhulupirira ndiponso kudalira malangizo ake. Masana, Yehova ankagwiritsa ntchito mtambo ndipo usiku ankagwiritsa ntchito moto n’cholinga choti Aisiraeli azikumbukira kuti iye akuwatsogolera podutsa m’chipululumo. (Deut. 1:19; Eks. 40:36-38) Iye ankawapatsanso zofunika pa moyo wawo. Baibulo limati: “Iwo sanasowe kanthu. Zovala zawo sizinathe ndipo mapazi awo sanatupe.”—Neh. 9:19-21.

10. Kodi Yehova amatsogolera bwanji anthu ake masiku ano?

10 Atumiki a Mulungu ali pafupi kulowa m’dziko latsopano lolungama. Kodi timakhulupirira kuti Yehova azitipatsa zinthu zonse zofunika kuti tidzapulumuke “chisautso chachikulu”? (Mat. 24:21, 22; Sal. 119:40, 41) N’zoona kuti Yehova satitsogolera pogwiritsa ntchito mtambo kapena moto. Koma akutitsogolera pogwiritsa ntchito gulu lake. Mwachitsanzo, gululi limatithandiza kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova potiuza kuti tiziwerenga Baibulo, kuchita Kulambira kwa Pabanja, kusonkhana nthawi zonse ndiponso kulalikira. Kodi inuyo mwasintha zinthu zina ndi cholinga choti mutsatire malangizo amenewa? Kuchita zimenezi kungatithandize kukhala ndi chikhulupiriro ndiponso kuti tidzapulumuke n’kulowa m’dziko latsopano.

Kumvera zikumbutso za Yehova kumatithandiza kusamalira Nyumba ya Ufumu kuti tipewe ngozi (Onani ndime 11)

11. Kodi Mulungu amasonyeza bwanji kuti amatifunira zabwino?

11 Malangizo amene timalandira amatithandizanso pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Mwachitsanzo, timalangizidwa kuti tingachepetse nkhawa tikamapewa kukonda chuma ndiponso tikamakhala moyo wosalira zambiri. Tapindulanso potsatira malangizo okhudza kavalidwe kathu, zosangalatsa komanso maphunziro apamwamba. Taganiziraninso za malangizo otithandiza kukonzekera zakugwa mwadzidzidzi komanso kupewa ngozi kunyumba kwathu, pagalimoto ndiponso pa Nyumba ya Ufumu. Malangizo onsewa amasonyeza kuti Mulungu amatifunira zabwino.

ZIKUMBUTSO ZINATHANDIZA AKHRISTU OYAMBIRIRA KUTI AKHALEBE OKHULUPIRIKA

12. (a) Kodi Yesu analangiza ophunzira ake mobwerezabwereza pa nkhani iti? (b) Kodi ndi phunziro liti limene Petulo sanaiwale ndipo liyenera kutilimbikitsa kukhala anthu otani?

12 Anthu a Mulungu ankalandiranso zikumbutso nthawi ya atumwi. Mwachitsanzo, Yesu ankauza ophunzira ake mobwerezabwereza kuti afunika kukhala odzichepetsa. Iye anawapatsanso chitsanzo pa nkhani ya kudzichepetsayi. Tsiku loti aphedwa mawa lake, Yesu ndi atumwi ake anasonkhana kuti achite Pasika. Atumwi akewo akudya, Yesu anadzuka n’kuyamba kuwasambitsa mapazi. Koma  nthawi zambiri wantchito ndi amene ankachita zimenezi. (Yoh. 13:1-17) Phunziro limene Yesu anapereka pamenepa linali losaiwalika. Mtumwi Petulo analipo pa nthawiyo ndipo patapita zaka pafupifupi 30, analangiza Akhristu anzake kuti azikhala odzichepetsa. (1 Pet. 5:5) Chitsanzo cha Yesu chiyenera kutilimbikitsa tonsefe kukhala odzichepetsa kwambiri.—Afil. 2:5-8.

13. Kodi Yesu ankakumbutsa ophunzira ake kuti akhale ndi khalidwe liti?

13 Yesu ankauzanso ophunzira ake mobwerezabwereza kuti ayenera kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Mwachitsanzo, ophunzira atalephera kutulutsa chiwanda, anafunsa Yesu kuti: “N’chifukwa chiyani ife tinalephera kutulutsa chiwanda chija?” Poyankha, Yesu ananena kuti: “Chifukwa cha kuchepa kwa chikhulupiriro chanu. Pakuti ndithu ndikukuuzani, ngati mutakhala ndi chikhulupiriro chofanana ndi kanjere ka mpiru kuchepa kwake, . . . palibe chimene chidzakhala chosatheka kwa inu.” (Mat. 17:14-20) Choncho pa utumiki wake wonse, Yesu ankauza ophunzira ake kuti chikhulupiriro n’chofunika kwambiri. (Werengani Mateyu 21:18-22.) Malangizo amene timalandira pa misonkhano yachigawo, yadera komanso yampingo amatithandiza kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba. Kodi timayesetsa kupezekapo ndiponso kumvetsera? N’zoona kuti timasonkhana kuti tisangalale ndi anzathu, koma timachitanso zimenezi posonyeza kuti timakhulupirira Yehova.

14. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kukhala ndi chikondi ngati cha Khristu?

14 M’Malemba Achigiriki timakumbutsidwa mobwerezabwereza kuti tizikondana. Yesu ananena kuti pa malamulo akuluakulu, lachiwiri ndi lakuti: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.” (Mat. 22:39) Nayenso Yakobo, amene anali m’bale wa Yesu, ananena kuti limeneli ndi “lamulo lachifumu.” (Yak. 2:8) Mtumwi Yohane analembanso kuti: “Okondedwa, sindikukulemberani lamulo latsopano, koma lamulo lakale limene mwakhala nalo kuyambira pa chiyambi.” (1 Yoh. 2:7, 8) Kodi ndi lamulo liti limene Yohane ankanena kuti ndi “lakale”? Apa Yohane ankanena za lamulo loti tizikondana. Lamuloli linali “lakale” chifukwa chakuti Yesu anali atapereka lamuloli zaka zambiri m’mbuyomo kapena kuti “pa chiyambi.” Koma linalinso “latsopano” chifukwa chakuti ophunzirawo ankafunika kukhala ndi chikondi chololera kuvutikira ena akakumana ndi mavuto atsopano. Masiku ano, mtima wodzikonda wafala kwambiri m’dzikoli ndipo ukuchititsa kuti anthu asamakondane. Koma ife timayamikira kwambiri malangizo amene timalandira otichenjeza kuti tipewe mtima umenewu.

15. Kodi ntchito yaikulu ya Yesu padzikoli inali iti?

 15 Yesu ankakonda ndiponso kuganizira kwambiri anthu. Iye anasonyeza zimenezi pochiritsa odwala komanso kuukitsa akufa. Koma ntchito yake yaikulu sinali yochiritsayo. Ntchito yake imene inathandiza kwambiri anthu inali yolalikira ndi kuphunzitsa. N’chifukwa chiyani tikutero? Pajatu anthu amene anawachiritsa komanso kuwaukitsa anakalamba n’kufa. Koma amene anatsatira zimene Yesu ankaphunzitsa anali ndi mwayi wodzalandira moyo wosatha.—Yoh. 11:25, 26.

16. Kodi ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu yafika pati masiku ano?

16 Ntchito yolalikira imene Yesu anaiyambitsa kalelo ikugwirika kwambiri masiku ano padziko lonse. Iye anauza ophunzira ake kuti: “Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga.” (Mat. 28:19) Ndipotu izi n’zimene ophunzira ake akhala akuchita. Panopa a Mboni za Yehova oposa 7 miliyoni akulalikira mwakhama za Ufumu wa Mulungu m’mayiko oposa 230. Iwo amaphunzira Baibulo ndi anthu mamiliyoni ambiri. Ntchito yolalikirayi imapereka umboni wakuti tili m’masiku otsiriza.

NAFENSO TIZIKHULUPIRIRA YEHOVA

17. Kodi Paulo ndi Petulo anapereka malangizo ati?

17 Taona kuti zikumbutso zinkathandiza Akhristu oyambirira kuti akhalebe okhulupirika. Mtumwi Paulo ali m’ndende ku Roma, analangiza Timoteyo kuti: “Gwiritsitsabe chitsanzo cha mawu olondola amene unawamva kwa ine.” (2 Tim. 1:13) Mawu amenewa ayenera kuti analimbikitsa kwambiri Timoteyo. Nayenso Petulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti akhale ndi makhalidwe monga kupirira, kukonda abale ndiponso kudziletsa. Kenako anawauza kuti: “Nthawi zonse ndizikukumbutsani zinthu zimenezi, ngakhale kuti mukuzidziwa kale ndipo ndinu olimba m’choonadi chimene munachilandira.”—2 Pet. 1:5-8, 12.

18. Kodi Akhristu a m’nthawi ya atumwi ankaona bwanji zikumbutso?

18 Makalata amene Paulo ndi Petulo analemba anakumbutsa Akhristu oyambirira “mawu amene aneneri oyera ananena kale.” (2 Pet. 3:2) Kodi abale athu a m’nthawi ya atumwi ankadandaula akalandira malangizowa? Ayi. Tikutero chifukwa chakuti malangizowo ankasonyeza kuti Mulungu amawakonda. Ankawathandizanso ‘kupitiriza kulandira kukoma mtima kwakukulu ndi kumudziwa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.’—2 Pet. 3:18.

19, 20. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira zikumbutso za Yehova?

19 Masiku ano, tili ndi zifukwa zambiri zotichititsa kukhulupirira zikumbutso za Yehova zomwe zili m’Baibulo, lomwe ndi Mawu ake odalirika. (Werengani Yoswa 23:14.) M’Mawu akewo timaona mmene Mulungu ankachitira zinthu ndi anthu opanda ungwiro kwa zaka masauzande ambiri. Nkhani zimenezi zinalembedwa kuti zitithandize. (Aroma 15:4; 1 Akor. 10:11) Taona maulosi ambiri a m’Baibulo akukwaniritsidwa. Maulosi ali ngati zikumbutso zimene Mulungu anatiuziratu. Mwachitsanzo, anthu mamiliyoni ambiri ayamba kulambira Yehova “m’masiku otsiriza” ano ndipo izi zikugwirizana ndi ulosi wa m’Baibulo. (Yes. 2:2, 3) Zinthu zikuipiraipira padzikoli ndipo izinso zikukwaniritsa ulosi wa m’Baibulo. Komanso ntchito yolalikira imene ikugwiridwa padziko lonse ikukwaniritsa mawu a Yesu.—Mat. 24:14.

20 Mlengi wathu wachita zinthu zambiri zotichititsa kumukhulupirira. Tiyenera kukhulupirira ndiponso kumvera zikumbutso zake chifukwa n’zothandiza. Mlongo wina dzina lake Rosellen anati: “Nditayamba kukhulupirira Yehova ndi mtima wonse m’pamene ndinaona kuti iye akundithandiza kwambiri ndiponso kundipatsa mphamvu.” Tiyeni ifenso tizimvera zikumbutso za Yehova kuti atidalitse.