Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungatani Kuti Muchenjeze Anthu Ambiri?

Kodi Mungatani Kuti Muchenjeze Anthu Ambiri?

Pali filimu ina yakalekale imene imasonyeza mmene zinthu zinalili mumzinda wa San Francisco, ku United States, chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900. Opanga filimuyi anamangirira kamera kutsogolo kwa kabasi kamene kankayenda mumsewu wodutsa anthu ambiri. Mufilimuyi anajambula ngolo zokokedwa ndi mahatchi, magalimoto apanthawiyo, anthu okagula zinthu ndiponso anyamata ogulitsa nyuzi.

Anthu ambiri akaganizira za filimuyi amamva chisoni chifukwa zikuoneka kuti inajambulidwa mu April 1906, kutangotsala nthawi yochepa kuti chivomezi chimene chinayambitsa moto pa April 18 chichitike. Anthu ambiri anafa ndipo mbali imeneyi ya mzindawu inawonongedwa kwambiri. N’kutheka kuti anthu ena amene anajambulidwa mufilimuyi anafa pa ngoziyi. Scott Miles, yemwe ndi mdzukulu wa munthu wina amene anapanga nawo filimuyi, anati: “Anthu amene anajambulidwa ankangodziyendera osadziwa kuti chiwagwere n’chiyani. Ukawaona umangomva chisoni.”

Chivomezi chimene chinayambitsa moto mu 1906 n’kuwononga mbali yaikulu ya mzinda wa San Francisco chinachitika mosayembekezereka

Komatu umu ndi mmene zililinso ndi anthu ambiri masiku ano. Anthuwo amamvetsa chisoni kwambiri chifukwa amangodziyendera osadziwa tsoka limene likubwera. Posachedwapa dziko loipali lidzawonongedwa. Koma mosiyana ndi chivomezi chimene tanena chija, panopa mwayi wochenjeza anthu za tsiku la Yehova limene likubwera udakalipo. Tikudziwa kuti mumayesetsa kulalikira kunyumba ndi nyumba mlungu uliwonse. Koma funso ndi lakuti, kodi mungatani kuti muchenjeze anthu ambiri?

YESU SANKAONA KUTI WAWERUKA MU UTUMIKI

Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri chifukwa sankaona kuti waweruka mu utumiki. Iye ankalalikira munthu aliyense amene wakumana naye. Mwachitsanzo, analalikira wokhometsa msonkho yemwe anamupeza pamsewu komanso mkazi wina amene anakumana naye pachitsime masana. (Luka 19:1-5; Yoh. 4:5-10, 21-24) Ngakhale pamene Yesu ankafuna kupuma, anasiya kupumako kuti aphunzitse anthu. Chifukwa chomvera chisoni anthu, anadzipereka kwambiri polalikira. (Maliko 6:30-34) Kodi anthu ena masiku ano akutengera bwanji chitsanzo cha Yesu?

AMAGWIRITSA NTCHITO MPATA ULIWONSE

Mlongo wina dzina lake Melika amakhala m’nyumba ina yosanja imene ili ndi chitetezo chokhwima. Anthu ena amene amakhala m’zipinda zina za nyumbayo ndi ochokera kumayiko ena ndipo anabwera kudzaphunzira sukulu. Koma mayina awo kapena manambala a mafoni awo sapezeka paliponse  choncho n’zovuta kuti a Mboni awapeze. Melika amaona kuti ali ndi mwayi wapadera wokambirana ndi anthu amenewa nkhani za m’Baibulo akakumana nawo muchikepe kapena pamalo enaake. Iye anati: “Ndimaona kuti limeneli ndi gawo langa.” Melika amayenda ndi mabuku athu a zinenero zosiyanasiyana ndipo anthu ambiri amalandira timapepala ndi magazini. Amawauzanso kuti angawerenge zambiri pa webusaiti yathu ya jw.org. Melika wayamba kuphunzira Baibulo ndi anthu ambiri.

Mlongo wina dzina lake Sonia amakhalanso tcheru kuti alalikire kwa wina aliyense. Iye amagwira ntchito kuchipatala ndipo anali ndi cholinga cholalikira kwa anzake onse amene amagwira nawo ntchito. Kuti akwanitse zimenezi, choyamba anayesetsa kudziwa mavuto a munthu aliyense ndiponso zimene amakonda. Kenako pa nthawi yopuma ankayesetsa kucheza ndi munthu mmodzi ndi kukambirana naye nkhani za m’Baibulo. Zimenezi zinam’thandiza kuyamba kuphunzira Baibulo ndi anthu awiri. Iye wakonzanso zoti pa nthawi yopuma azicheza ndi anthu amene akudikirira kuonana ndi dokotala.

INUNSO MUZIGWIRITSA NTCHITO MPATA ULIWONSE

Munthu wina amene anapulumuka pa ngozi ya mu 1906 ananena kuti: “Ngozi imeneyi inali yoopsa kwambiri kuposa ngozi zonse zimene zinachitikapo mumzinda kapena dera lililonse.” Komatu zimene zidzachitike pa tsiku lopereka chilango kwa anthu “osadziwa Mulungu” zidzakhala zazikulu ndiponso zoopsa kwambiri kuposa ngozi ina iliyonse imene inachitikapo. (2 Ates. 1:8) Yehova akufuna kuti anthu asinthe maganizo ndiponso mitima yawo n’kuyamba kutsatira machenjezo amene Mboni zake zikupereka.—2 Pet. 3:9; Chiv. 14:6, 7.

Muzigwiritsa ntchito mpata uliwonse kuti mulalikire kwa anthu amene mumakumana nawo tsiku ndi tsiku

Ndiyeno inu muli ndi mwayi wothandiza anthu kuti adziwe za tsoka limene likubwerali. Mungawathandize kuti asiye kuchita zofuna zawo n’kuyamba kufunafuna Yehova. (Zef. 2:2, 3) Choncho muzigwiritsa ntchito mpata uliwonse kuti mulalikire kwa anthu amene mumagwira nawo ntchito, aneba anu ndiponso amene mumakumana nawo tsiku ndi tsiku. Kodi inuyo mudzatani kuti muchenjeze anthu ambiri?