KALE LATHU
“Ndinali Ngati Kamba Woyenda Ndi Chigoba Chake”
M’MWEZI wa August ndi September 1929, abale ndi alongo oposa 10,000 anagwira ntchito yapadera yolalikira m’dziko la United States. Iwo anayenda mbali zosiyanasiyana kwa masiku 9 akugwira ntchito imeneyi ndipo anagawira mabuku pafupifupi 250,000. Pagululi panalinso akopotala oposa 1,000. Izi zikusonyeza kuti akopotalawo anali atachuluka kwambiri. Utumiki Wathu wa Ufumu * unanena kuti “n’zodabwitsa” kuti chiwerengero cha apainiya chinawonjezeka kuwirikiza katatu kuchokera m’chaka cha 1927 kudzafika mu 1929.
Chakumapeto kwa chaka cha 1929 chuma chinasokonekera kwambiri ku United States. Lachiwiri pa October 29, 1929, zinthu zinasokonekera kwambiri m’makampani ndipo izi zinakhudza chuma cha padziko lonse. Mabanki ambiri anatsekedwa. Ntchito zambiri zaulimi ndiponso za mafakitale zinaima. Anthu mamiliyoni ambiri anachotsedwa ntchito. Mu 1933, tsiku lililonse ku United States, anthu pafupifupi 1,000 ankalandidwa nyumba.
Kodi n’chiyani chinathandiza atumiki a nthawi zonse pa nthawi yovutayi? Ambiri ankakhala m’makalavani. Iwo sankawononga ndalama zambiri chifukwa sankalipira lendi kapena msonkho wa nyumba. * Pa nthawi ya msonkhano, sankavutikanso kulipira malo ogona kuhotelo. Mu 1934, Utumiki Wathu wa Ufumu unafotokoza mmene abale angamangire kalavani yabwino yokhala ndi zonse zofunika monga madzi, zophikira, bedi ndi zina.
Abale ambiri anamanga makalavani awo. M’bale wina dzina lake Victor Blackwell, yemwe anakwanitsa kumanga kalavani yake, anati: “Nowa sankadziwa ntchito yomanga chombo. Inenso sindinkadziwa kumanga kalavani.”
Nayenso Avery Bristow ndi mkazi wake Lovenia anamanga kalavani yawo. Avery anati: “Ndinali ngati kamba woyenda ndi chigoba chake chifukwa nthawi zonse ndinkayenda ndi nyumba yanga.” M’bale ndi mlongoyu ankachita upainiya limodzi ndi Harvey ndi Anne Conrow. Kalavani ya banja la a Conrow inali ndi makoma opangidwa ndi mapepala olimba opakidwa phula. Koma nthawi iliyonse akamayenda mapepala ena ankayoyoka. Avery anati: “Kalavani ya anzathuwo inali yapadera. Sindinaonepo yangati imeneyi moti ndingati inali yoyamba ndi yomaliza.” Koma Avery ananenanso kuti m’bale ndi mlongo Conrow ndi ana awo awiri anali “osangalala kwambiri.” Harvey Conrow analemba kuti: “Sitinasowepo kanthu. Potumikira Yehova, tinkaona kuti akutisamalira bwino ndipo ndife otetezeka m’manja mwake.” Banja lonse la a Conrow linadzapita ku Sukulu ya Giliyadi ndipo linatumizidwa kukakhala amishonale ku Peru.
Giusto Battaino ndi mkazi wake Vincenza ankachitanso upainiya. Poyamba ankagona mu tenti koma atazindikira kuti mlongoyo ndi woyembekezera anasintha galimoto yawo kuti ikhale kalavani. Iwo ankaona kuti kalavaniyo “inali ngati hotelo yokongola kwambiri” akaiyerekezera ndi tenti ija. Iwo ankachitabe upainiya limodzi ndi kamwana kawo kakakazi. Anapemphedwa kuti azilalikira kwa anthu ochokera ku Italy ndipo ankasangalala kwambiri kuchita zimenezi.
Anthu ankamvetsera uthenga wabwino koma popeza ambiri anali osauka ndipo sankagwira ntchito, zinkawavuta kupereka ndalama akapatsidwa mabuku. M’malomwake, ankangopereka chilichonse chimene ali nacho. Alongo awiri amene ankachita upainiya analemba zinthu 64 zosiyanasiyana zimene analandira mu utumiki. Zimene analembazo “zinali ngati katundu wa musitolo.”
Fred Anderson anakumana ndi mlimi wina amene ankafuna mabuku athu ndipo ananena kuti apereka magalasi amene anali a mayi ake. Atafika pa famu ina, anapeza bambo amene ankafuna kwambiri mabuku athu koma anati: “Ndilibe magalasi owerengera.” Ndiye zinangochitika kuti atayesa magalasi aja, ankaona bwinobwino. Choncho anapereka ndalama za mabuku athu komanso za magalasiwo.
Herbert Abbott ankayenda ndi chikwere cha nkhuku m’galimoto yake. Akasinthanitsa mabuku ndi nkhuku zitatu kapena zinayi ankapita nazo kumsika kukagulitsa n’kugula mafuta a galimoto yake. Iye analemba kuti: “Nthawi zina tinalibe ndalama iliyonse. Komabe zimenezi sizinatilepheretse kuchita utumiki wathu. Tikakhala ndi mafuta m’galimoto, tinkapita kukalalikira podalira ndi kukhulupirira kuti Yehova atidalitsa.”
Anthu a Yehova anapirira m’nthawi yovutayo chifukwa ankamudalira ndipo anali ofunitsitsa kumutumikira ndi mtima wonse. Nthawi ina kunagwa mvula yamkuntho ndipo Maxwell Lewis ndi mkazi wake Emmy anathawa m’kalavani yawo. Atangotuluka, mtengo unagwera pakalavaniyo n’kuidula pakati. Maxwell analemba kuti: “Tinkaona kuti zinthu ngati zimenezi zinali zing’onozing’ono ndipo sitinaganizepo zosiya utumiki. Panali ntchito yambiri ndipo tinkafuna kuigwira.” Maxwell ndi Emmy sanabwerere m’mbuyo ndipo mothandizidwa ndi anzawo, anamanganso kalavani yawo.
M’nthawi yovuta ino palinso a Mboni za Yehova mamiliyoni ambiri omwe amadzipereka kwambiri pa ntchito yolalikira. Ndipo mofanana ndi apainiya amene takambiranawa, tikufunitsitsa kupitiriza ntchito yolalikira mpaka Yehova atanena kuti basi tisiye.