Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Khalani Maso Kuti Musanyalanyaze Kupemphera”

“Khalani Maso Kuti Musanyalanyaze Kupemphera”

“Khalani oganiza bwino, ndipo khalani maso kuti musanyalanyaze kupemphera.”1 PET. 4:7.

1, 2. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera ‘kukhala maso kuti tisanyalanyaze kupemphera’? (b) Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati pa nkhani ya pemphero?

MUNTHU wina amene ankagwira ntchito usiku anati: “M’bandakucha m’pamene munthu amavutika kwambiri ndi tulo.” Ngati inunso mumagwira ntchito usiku, mukhoza kuvomereza zimenezi. Akhristu masiku ano angavutikenso kukhala maso chifukwa chakuti nthawi imene tikukhalayi ili ngati m’bandakucha wa dziko la Satanali. (Aroma 13:12) Kugona pa nthawi imeneyi kungakhale kwangozi kwambiri. Choncho m’pofunikadi kukhala “oganiza bwino” ndiponso kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti ‘tizikhala maso kuti tisanyalanyaze kupemphera.’—1 Pet. 4:7.

2 Popeza tikukhala m’nthawi yovuta chonchi, ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndimapemphera mwakhama? Kodi mapemphero anga amakhala a mtundu uliwonse? Nanga ndimapemphera nthawi zonse? Kodi ndimakonda kupempherera ena kapena ndimangotchula zimene ineyo ndikufuna? Kodi pemphero ndi lofunika bwanji kuti ndipulumuke?’

MAPEMPHERO ANU AZIKHALA A MTUNDU ULIWONSE

3. Kodi pali mitundu iti ya mapemphero?

3 Mtumwi Paulo anauza Akhristu a ku Efeso kuti azipemphera “mwa mtundu uliwonse wa pemphero.” (Aef. 6:18) Nthawi zambiri tingapemphe Yehova kuti atithandize kupeza zinthu zofunika ndiponso kuthana ndi mavuto athu. Mulungu, yemwe ndi “Wakumva pemphero” ndiponso wachikondi, amamvetsera tikamupempha thandizo. (Sal. 65:2) Komabe mapemphero athu ayenera kukhala a mitundu inanso. Mwachitsanzo, ayenera kukhala otamanda Mulungu, omuyamikira ndiponso opembedzera.

4. N’chifukwa chiyani tiyenera kutamanda Yehova nthawi ndi nthawi m’mapemphero athu?

4 Pali zifukwa zambiri zotichititsa kutamanda Yehova  m’mapemphero athu. Mwachitsanzo, timalimbikitsidwa kumutamanda tikaganizira “ntchito zake zamphamvu” ndiponso “ukulu wake wosaneneka.” (Werengani Salimo 150:1-6.) Mavesi 6 a Salimo 150 amatilimbikitsa nthawi 13 kuti tizitamanda Yehova. Wamasalimo wina anasonyeza kuti amalemekeza kwambiri Mulungu poimba kuti: “Ndimakutamandani maulendo 7 pa tsiku, chifukwa cha zigamulo zanu zolungama.” (Sal. 119:164) Yehova ndi woyeneradi kutamandidwa. Choncho tiyenera kumutamanda “maulendo 7 pa tsiku” kapena kuti nthawi ndi nthawi.

5. Kodi kuyamikira Mulungu popemphera kumatiteteza bwanji?

5 Kuyamikira Yehova n’kofunikanso tikamapemphera. Paulo anauza Akhristu a mumzinda wa Filipi kuti: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.” (Afil. 4:6) Kuyamikira Yehova kuchokera pansi pa mtima tikamapemphera kumatiteteza. M’masiku otsiriza ano zimenezi zikhoza kutitetezadi chifukwa anthu ambiri ndi “osayamika.” (2 Tim. 3:1, 2) Popeza kuti m’dzikoli anthu ambiri ali ndi mtima wosayamika, tiyenera kusamala kuti nafenso tisatengere mtima umenewu. Kuyamikira Mulungu popemphera kumathandiza kuti tizikhutira ndi zimene tili nazo ndiponso kupewa ‘kung’ung’udza kapena kudandaula za moyo wathu.’ (Yuda 16) Bambo akamayamikira Mulungu popemphera limodzi ndi banja lake, amalimbikitsa mkazi wake ndiponso ana ake kukhala ndi mtima woyamikira.

6, 7. (a) Kodi kupembedzera kumatanthauza chiyani? (b) Kodi tingapembedzere Yehova pa nkhani ziti?

6 Kupembedzera kumatanthauza kupemphera mochonderera kwambiri komanso ndi mtima wonse. Kodi tingachonderere Yehova pa nkhani ziti? Tikhoza kuchita zimenezi tikamazunzidwa kapena tikamadwala mwakayakaya. N’zomveka kuti pa nthawi ngati zimenezi munthu amafuna kupemphera kwa Mulungu mopembedzera. Koma kodi ndi pa nthawi zimenezi zokha pamene tingapembedzere Yehova?

7 Taganizirani zimene Yesu ananena m’pemphero lake lachitsanzo pa nkhani ya dzina la Mulungu, Ufumu wake ndiponso chifuniro chake. (Werengani Mateyu 6:9, 10.) Dzikoli ladzaza ndi zinthu zoipa ndipo maboma akulephera kuthandiza anthu awo kupeza zinthu zofunika pa moyo. Choncho tiyenera kupemphera kuti dzina la Atate wathu wakumwamba liyeretsedwe ndiponso kuti Ufumu wake uchotse ulamuliro wa Satana padzikoli. Tiyeneranso kupembedzera Yehova kuti chifuniro chake chichitike padzikoli ngati mmene zilili kumwamba. Tiyeni tikhalebe maso n’kumapemphera mapemphero a mitundu yonse.

“PEMPHERANI KOSALEKEZA”

8, 9. N’chifukwa chiyani si bwino kuweruza Petulo ndi atumwi ena amene anagona m’munda wa Getsemane?

8 Mtumwi Petulo anauza Akhristu kuti ‘akhale maso kuti asanyalanyaze kupemphera.’ Koma iyeyo pa nthawi ina analephera kuchita zimenezi. Iye anali mmodzi wa ophunzira amene anagona pamene Yesu ankapemphera m’munda wa Getsemane. Ngakhale Yesu atabwera n’kuwauza kuti “khalani maso ndipo pempherani kosalekeza,” anagonanso.—Werengani Mateyu 26:40-45.

9 Komatu si bwino kufulumira kuweruza Petulo ndi anzakewo. Tiyenera kukumbukira kuti anali atatopa chifukwa cha zinthu zambirimbiri zimene anachita pa tsikulo. Iwo anagwira ntchito yokonzekera Pasika ndipo anachita mwambowu madzulo a tsiku limenelo. Kenako Yesu anayambitsa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye kuti apereke chitsanzo cha zimene ophunzira ake azidzachita  pokumbukira imfa yake. (1 Akor. 11:23-25) Ndiyeno “atatha kuimba nyimbo zotamanda Mulungu, anatuluka n’kupita kuphiri la Maolivi.” (Mat. 26:30, 36) Iwo anadutsa m’tinjira ta ku Yerusalemu ndipo n’kutheka kuti anafika ku Getsemane 12 koloko ya usiku itadutsa. Mwina ifenso tikanakhalapo, tikanagona. M’malo modzudzula atumwiwo, Yesu anawauza mwachikondi kuti “mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.”

Ngakhale kuti Petulo anakana Yesu, anaphunzira ‘kukhala maso kuti asanyalanyaze kupemphera’ (Onani ndime 10 ndi 11)

10, 11. (a) Kodi Petulo anaphunzirapo chiyani pa zimene zinamuchitikira? (b) Nanga inuyo mukuphunzirapo chiyani?

10 Petulo anaphunzirapo kanthu pa zimene zinachitika usiku umene anagona m’munda wa Getsemane. Koma anaphunzira m’njira yowawa kwambiri. Pa tsiku lomweli, Yesu anali atanena kuti: “Nonsenu muthawa ndi kundisiya ndekha usiku uno.” Petulo atamva zimenezi ananena kuti: “Ngakhale ena onse atathawa kukusiyani, ine ndekha sindingathawe!” Pomuyankha, Yesu ananena kuti iye adzamukana katatu. Koma Petulo anachita makani n’kunena kuti: “Ngati kuli kufa, ine ndifa nanu limodzi, sindingakukaneni.” (Mat. 26:31-35) Koma zimene Yesu ananenazo zinachitikadi. Petulo atakana Yesu kachitatuko anamva chisoni moti ‘analira mopwetekedwa mtima kwambiri.’—Luka 22:60-62.

11 Apatu Petulo anaphunzirapo kanthu ndipo anasiya kukhala ndi mtima wodzidalira. Zikuoneka kuti pemphero ndi limene linamuthandiza kuti asinthe. N’zochititsa chidwi kuti Petulo ndi amene anapereka malangizo akuti “khalani maso kuti musanyalanyaze kupemphera.” Kodi ifeyo tikutsatira malangizo amenewa? Nanga ‘timapemphera kosalekeza’ posonyeza kuti timadalira Yehova? (Sal. 85:8) Tiyeni tisaiwalenso mawu a mtumwi Paulo akuti: “Amene akuyesa kuti ali chilili asamale kuti asagwe.”—1 Akor. 10:12.

YEHOVA ANAYANKHA MAPEMPHERO A NEHEMIYA

12. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Nehemiya ndi chitsanzo chabwino?

12 Taganiziraninso zimene zinachitikira Nehemiya cha m’ma 400 B.C.E. Iye ankagwira ntchito yoperekera chikho kwa Mfumu Aritasasita ya ku Perisiya. Nehemiya anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yopemphera mopembedzera. Kwa masiku angapo iye anali “kusala kudya ndi kupemphera pamaso pa Mulungu” chifukwa cha mavuto amene Ayuda ankakumana nawo ku Yerusalemu. (Neh. 1:4) Nehemiya atafunsidwa ndi Mfumu Aritasasita chifukwa chimene ankaonekera wachisoni, ‘nthawi yomweyo anapemphera kwa Mulungu wakumwamba.’ (Neh. 2:2-4) Ndiyeno Yehova anayankha mapemphero ake  ndipo anatsogolera zinthu kuti anthu ake athandizidwe. (Neh. 2:5, 6) Zimenezi ziyenera kuti zinalimbitsa kwambiri chikhulupiriro cha Nehemiya.

13, 14. Kodi tingatani kuti tikhalebe ndi chikhulupiriro cholimba ndiponso kuti Satana asatifooketse?

13 Ifenso tingalimbitse chikhulupiriro chathu tikamapemphera nthawi zonse. Satana alibe chifundo ndipo amatiyesa akaona kuti tafooka. Mwachitsanzo, ngati tikudwala kapena tikuvutika maganizo, tingayambe kuganiza kuti Mulungu sasangalala ndi zimene timachita mu utumiki. Enafe tikhoza kuvutika chifukwa chokumbukira zinthu zoipa zimene zinatichitikira m’mbuyomu. Satana amafuna kuti tizidziona kuti ndife opanda pake. Nthawi zambiri iye amayesetsa kusokoneza maganizo athu n’cholinga choti chikhulupiriro chathu chifooke. Koma tikakhala maso n’kumapemphera nthawi zonse, chikhulupiriro chathu chimakhalabe cholimba. Ndiyeno ‘chishango chachikulu chachikhulupiriro chidzatithandiza kuzimitsa mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.’—Aef. 6:16.

Kukhala maso n’kumapemphera nthawi zonse kumatithandiza kulimbana ndi mayesero (Onani ndime 13 ndi 14)

14 Tikamakhala maso n’kumapemphera nthawi zonse, sitidzagonja tikakumana ndi mayesero mosayembekezereka. Ngati takumana ndi mayesero, tiyenera kupemphera kwa Mulungu nthawi yomweyo ngati mmene Nehemiya anachitira. Popanda thandizo la Yehova sitingathe kupirira ndiponso kulimbana ndi mayesero.

MUZIPEMPHERERA ANTHU ENA

15. Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati okhudza kupempherera anthu ena?

15 Yesu anapempherera Petulo kuti chikhulupiriro chake chisathe. (Luka 22:32) Mkhristu wokhulupirika dzina lake Epafura ankatsanzira Yesu pa nkhani imeneyi. Iye ankapempherera  mwakhama abale ake a ku Kolose. Paulo analembera abalewo kuti: “Iye amakupemphererani mwakhama nthawi zonse, kuti . . . mukhale okhwima mwauzimu ndi osakayika ngakhale pang’ono za chifuniro chonse cha Mulungu.” (Akol. 4:12) Tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimapempherera mwakhama abale anga padziko lonse? Kodi ndimatchula m’mapemphero anga Akhristu anzanga amene akuvutika chifukwa cha masoka achilengedwe? Kodi ndi liti pamene ndinapempherera abale amene ali ndi udindo waukulu m’gulu la Yehova? Nanga kodi posachedwapa ndapempherera anthu mumpingo amene akukumana ndi mavuto?

16. Kodi kupempherera anthu ena kumathandizadi? Fotokozani.

16 Kutchula anthu ena m’mapemphero athu kungawathandize kwambiri. (Werengani 2 Akorinto 1:11.) Sikuti Yehova amakakamizika kuthandiza ena ngati atumiki ake ambiri amupempha mobwerezabwereza kuchita zimenezi. Koma iye amaona chikondi ndiponso nkhawa ya anthu amene akupemphera ndipo amaganizira zimenezi poyankha mapemphero awo. Choncho tiyenera kuona kuti tili ndi mwayi ndiponso udindo wopempherera anthu ena. Mofanana ndi Epafura, tiyenera kusonyeza kuti timakonda kwambiri ndiponso kudera nkhawa Akhristu anzathu powapempherera mwakhama. Tikatero tidzakhala osangalala chifukwa “kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.”—Mac. 20:35.

“CHIPULUMUTSO CHATHU CHILI PAFUPI”

17, 18. Kodi ‘kukhala maso kuti tisanyalanyaze kupemphera’ kungatithandize bwanji?

17 Paulo asananene kuti “usiku uli pafupi kutha, usana wayandikira,” anati: “Nyengo ino mukuidziwa, kuti tili kale mu ola lakuti mudzuke ku tulo, pakuti chipulumutso chathu chili pafupi kwambiri tsopano kusiyana ndi nthawi imene tinakhala okhulupirira.” (Aroma 13:11, 12) Dziko latsopano la Mulungu lili pafupi kubwera ndipo nthawi yoti tipulumuke yayandikira kwambiri kuposa mmene tingaganizire. Choncho tisagone mwauzimu ndipo tisalole kuti zinthu za m’dzikoli zizitilepheretsa kupeza nthawi yopemphera kwa Yehova. M’malomwake, ‘tizikhala maso kuti tisanyalanyaze kupemphera.’ Izi zingatithandize ‘kukhala anthu akhalidwe loyera ndiponso kuchita ntchito zosonyeza kuti ndife odzipereka kwa Mulungu’ pamene tikuyembekezera tsiku la Yehova. (2 Pet. 3:11, 12) Tikatero tidzasonyeza kuti tikukhalabe maso mwauzimu komanso kuti timakhulupiriradi zoti dziko loipali latsala pang’ono kutha. Choncho tiyeni ‘tizipemphera mosalekeza.’ (1 Ates. 5:17) Komanso tizitsanzira Yesu poyesetsa kupeza nthawi yokhala patokha kuti tipemphere kwa Yehova. Tikamapemphera kwa Yehova n’kumamufotokozera zonse zamumtima mwathu, tidzamuyandikira kwambiri. (Yak. 4:7, 8) Ndiyeno tikakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova tidzapeza madalitso osaneneka.

18 Malemba amati: “Pamene anali munthu, Khristu anapereka mapemphero opembedzera ndi opempha, kwa amene anali wokhoza kumupulumutsa ku imfa. Anapereka mapempherowa mofuula komanso akugwetsa misozi, ndipo anamumvera chifukwa chakuti anali kuopa Mulungu.” (Aheb. 5:7) Yesu ankapereka mapemphero opembedzera ndiponso opempha ndipo anakhalabe wokhulupirika mpaka mapeto a moyo wake padzikoli. Chifukwa cha zimenezi, Yehova anapulumutsa Mwana wake wokondedwa. Anamuukitsa ndi kumupatsa moyo wosafa kumwamba. Ifenso tikhoza kukhalabe okhulupirika kwa Atate wathu wakumwamba ngakhale kuti tingakumane ndi mayesero aakulu m’tsogolo. Ndithudi tikhoza kudzapeza mphoto ya moyo wosatha ngati tipitiriza ‘kukhala maso kuti tisanyalanyaze kupemphera.’