Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwawerenga mosamala magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:

Kodi ndi liti pamene Yesu ‘analalikira kwa mizimu imene inali m’ndende’? (1 Pet. 3:19)

Zikuoneka kuti nthawi inayake Yesu ataukitsidwa, analalikira kwa mizimu yoipayi n’kuiuza za chilango chimene idzalandire.6/15, tsamba 23.

Kodi anthu amene akwatiwa kapena kukwatiranso amakumana ndi mavuto atatu ati?

Mavuto ake ndi awa: zimavuta kuiwala mkazi kapena mwamuna wanu woyamba; zimavuta kuchita zinthu ndi anzanu amene sanazolowerane ndi banja lanu latsopano; zimavuta kukhulupirira mkazi kapena mwamuna wanu watsopano ngati woyamba anali wosakhulupirika.—7/1, tsamba 9-10.

Kodi Yesu adzaweruza liti anthu kuti ndi nkhosa kapena mbuzi? (Mat. 25:32)

Adzachita zimenezi akadzabwera kudzaweruza anthu pa nthawi ya chisautso chachikulu, pambuyo poti zipembedzo zonyenga zawonongedwa.7/15, tsamba 6.

Kodi ndi liti pamene anthu osamvera malamulo otchulidwa m’fanizo la tirigu ndi namsongole adzalira ndi kukukuta mano? (Mat. 13:36, 41, 42)

Adzachita zimenezi pa chisautso chachikulu akadzazindikira kuti awonongedwa basi chifukwa sangathe kuthawa.7/15, tsamba 13.

Kodi mawu a Yesu onena za kapolo wokhulupirika ndi wanzeru anayamba kukwaniritsidwa liti? (Mat. 24:45-47)

Anayamba kukwaniritsidwa pambuyo pa chaka cha 1914 osati pa Pentekosite mu 33 C.E. Mu 1919, kapoloyu anaikidwa kuti aziyang’anira antchito apakhomo omwe akuimira Akhristu onse amene akudyetsedwa mwauzimu.7/15, tsamba 21-23.

Kodi Yesu adzaika liti kapolo wokhulupirika kuti aziyang’anira zinthu zake zonse?

Izi zidzachitika m’tsogolomu pa nthawi ya chisautso chachikulu pamene kapolo wokhulupirikayu adzalandira mphoto yake kumwamba.7/15, tsamba 25.

Kodi anthu amene mayina awo sanatchulidwe m’Baibulo anali oipa kapena osafunika?

Ayi si choncho. Baibulo silitchula mayina a anthu ena omwe anali abwino komanso ena omwe anali oipa. (Rute 4:1-3; Mat 26:18) Pa angelo onse okhulupirika, Baibulo limangotchula mayina a angelo awiri okha.8/1, tsamba 10.

Kuwonjezera pa mphamvu imene Mulungu anawapatsa, kodi n’chiyaninso chinathandiza a Mboni okwana 230 kuti asafe pa ulendo umene anawayendetsa kuchokera ku ndende ya ku Germany?

Iwo anali atafooka ndi njala komanso matenda koma sanasiye kulimbikitsana kuti apirire.8/15, tsamba 18.

Kodi zimene zinachitika pamene Aisiraeli ankawoloka mtsinje wa Yorodano kuti alowe m’Dziko Lolonjezedwa zingatilimbikitse bwanji?

Ngakhale kuti mtsinjewo unali utasefukira, Yehova anaimitsa madziwo kuti anthu ake awoloke. Izi ziyenera kuti zinawathandiza kukhulupirira kwambiri Yehova. Ifenso nkhaniyi ingatilimbikitse kwambiri.9/15, tsamba 16.

N’chifukwa chiyani nthawi zambiri Baibulo limatchula mitundu ya zinthu (monga zofiira, zobiriwira kapena zoyera)?

Mmene Baibulo limagwiritsira ntchito mitundu ya zinthu zimasonyeza kuti Mulungu amadziwa zoti anthu amakhudzidwa kwambiri ndi mitundu ya zinthu. Zimasonyezanso kuti mitundu ingathandize anthu kukumbukira zinthu.10/1, tsamba 14-15.

Kodi ulosi wa pa Mika 5:5 wokhudza atsogoleri ndi abusa ukukwaniritsidwa bwanji masiku ano?

‘Abusa 7 ndi atsogoleri 8’ amene atchulidwa pa Mika 5:5 akuimira akulu mumpingo. Akuluwo akulimbikitsa anthu a Mulungu kuti asadzagonje akadzaukiridwa m’tsogolo.11/15, tsamba 20.

N’chifukwa chiyani tiyenera kudalira Mulungu?

Timafunikira malangizo abwino ndiponso kudziwa chifukwa chake timakumana ndi mavuto. Ndiye Mulungu ndi amene angatithandize pa nkhani imeneyi. Iye amatithandizanso kukhala ndi moyo wabwino ndiponso wosangalala. Komanso m’tsogolo adzakwaniritsa malonjezo a m’Mawu ake kuti tidzakhale ndi moyo wabwino kwambiri.12/1, tsamba 4-6.