Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungapereke Chiyani pa Ntchito ya Ufumu?

Kodi Mungapereke Chiyani pa Ntchito ya Ufumu?

“Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.”—2 AKOR. 9:7.

1. Kodi anthu amadzipereka kwambiri pochita zinthu ziti, ndipo n’chifukwa chiyani?

ANTHU amadzipereka kwambiri pa zinthu zimene amaona kuti ndi zofunika. Mwachitsanzo, makolo amagwiritsa ntchito nthawi, ndalama ndiponso mphamvu zawo pothandiza ana awo. Achinyamata ena amadzipereka kwambiri pokonzekera kuti akaimire dziko lawo pa mpikisano. Iwo amachita zimenezi kwa maola ambiri pomwe anzawo akungosewera ndi kusangalala. Nayenso Yesu anadzipereka kwambiri pa zinthu zimene ankaona kuti n’zofunika. Sankafunafuna chuma komanso sanakwatire n’kukhala ndi ana. M’malomwake, ankadzipereka pogwira ntchito ya Ufumu. (Mat. 4:17; Luka 9:58) Ophunzira ake analoleranso kusiya zinthu zambiri kuti agwire ntchito ya Ufumu wa Mulungu. Iwo ankaona kuti Ufumu wa Mulungu ndi wofunika kwambiri choncho anachita zonse zimene akanatha kuti athandize pa ntchitoyi. (Mat. 4:18-22; 19:27) Ifenso tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ndimaona kuti chofunika kwambiri n’chiyani?’

2. (a) Kodi Akhristu oona onse ayenera kudzipereka pochita zinthu ziti? (b) Kodi Akhristu ena amatha kudzipereka pochita zinthu zinanso ziti?

2 Akhristu oona onse ayenera kudzipereka pochita zinthu zina zimene zimathandiza kuti akhalebe pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Iwo ayenera kugwiritsa ntchito nthawi yawo ndiponso mphamvu zawo popemphera, kuwerenga Baibulo, kuchita kulambira kwa pabanja, kusonkhana ndiponso kulalikira. * (Yos. 1:8; Mat. 28:19, 20; Aheb. 10:24, 25) Ntchito yolalikira ikuyenda bwino kwambiri ndipo anthu ambiri akukhamukira ‘kuphiri  la nyumba ya Yehova.’ (Yes. 2:2) Izi zikuchitika chifukwa chakuti tikuchita khama pa ntchitoyi ndipo Yehova akuidalitsa. Masiku ano, anthu ambiri akudzipereka pothandiza pa ntchito zosiyanasiyana za Ufumu. Ena amatumikira pa Beteli, ena amamanga nawo Nyumba za Ufumu ndiponso malo a misonkhano, ena amathandiza pokonzekera misonkhano ikuluikulu ndipo ena amapereka chithandizo kumene kwagwa masoka a chilengedwe. Sikuti munthu ayenera kugwira ntchito zimenezi kuti akapulumuke, komabe n’zofunika kuti ntchito ya Ufumu iziyenda bwino.

3. (a) Kodi kudzipereka pogwira ntchito ya Ufumu kumatithandiza bwanji? (b) Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati?

3 Akhristu ayenera kudzipereka kwambiri panopa pa ntchito ya Ufumu. N’zosangalatsa kuti anthu ambiri akudzipereka ndi mtima wonse potumikira Yehova. (Werengani Salimo 54:6.) Tikamakhala ndi mtima wodzipereka timakhala osangalala pamene tikudikira Ufumu wa Mulungu. (Deut. 16:15; Mac. 20:35) Koma tonsefe tiyenera kudzifufuza pa nkhani imeneyi. Tizidzifunsa kuti: ‘Kodi pali zinthu zina zimene ndingachite kuti ndithandize pa ntchito ya Ufumu? Kodi ndimagwiritsa ntchito bwanji zinthu monga nthawi, ndalama, mphamvu ndiponso luso langa? Koma kodi ndiyenera kusamala ndi chiyani?’ Tiyeni tikambirane chitsanzo chimene chingatithandize pa nkhani ya kudzipereka. Tikamatsatira chitsanzo chimenechi tikhoza kukhala osangalala.

NSEMBE ZIMENE AISIRAELI ANKAPEREKA

4. Kodi nsembe zimene Aisiraeli ankapereka zinkawathandiza bwanji?

4 Aisiraeli ankayenera kupereka nsembe kuti akhululukidwe machimo. Choncho nsembezi zinkathandiza kuti iwo akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Nsembe zina zinali zoti aliyense azipereka koma zina zinali zaufulu, zomwe anthu ankasankha kupereka kapena ayi. (Lev. 23:37, 38) Aisiraeli ankapereka nsembe zopsereza zathunthu monga nsembe zaufulu kapena kuti mphatso kwa Yehova. Aisiraeli anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yopereka nsembe pamene ankatsegulira kachisi mu ulamuliro wa Solomo.—2 Mbiri 7:4-6.

5. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti ankaganizira anthu osauka?

5 Yehova ankamvetsa kuti anthu sangapereke nsembe zofanana, choncho ankalola kuti aliyense azipereka zimene angathe. Yehova analamula kuti magazi a nyama ayenera kukhetsedwa  ndipo izi zinali “mthunzi chabe wa zinthu zabwino zimene zikubwera” kudzera mwa Mwana wake Yesu. (Aheb. 10:1-4) Koma Yehova ankachita zinthu moganizira anthu pa nkhani ya lamuloli. Mwachitsanzo, iye ankalola munthu kupereka njiwa ziwiri ngati sangakwanitse kupereka nyama zikuluzikulu. Choncho ngakhale anthu osauka ankatha kupereka nsembe kwa Yehova mosangalala. (Lev. 1:3, 10, 14; 5:7) Ngakhale kuti nyama zimene anthuwo ankapereka zinkakhala zosiyana, panali zinthu ziwiri zimene Yehova ankafuna kwa aliyense amene ankapereka nsembe zaufulu.

6. (a) Tchulani zinthu zimene munthu aliyense ankafunika kuchita popereka nsembe. (b) N’chifukwa chiyani kuchita zinthu zimenezi kunali kofunika kwambiri?

6 Choyamba, munthuyo ankafunika kupereka zinthu zabwino kwambiri zimene angakwanitse. Yehova anauza Aisiraeli kuti nsembe iliyonse iyenera kukhala yopanda chilema kuti ‘Mulungu awayanje.’ (Lev. 22:18-20) Yehova sakanalandira nsembe iliyonse ya nyama yokhala ndi chilema. Chachiwiri, munthu wopereka nsembeyo ankafunika kukhala woyera. Munthu wodetsedwa, amene ankafuna kupereka nsembe yaufulu, ankafunika kupereka kaye nsembe yamachimo kapena nsembe ya kupalamula kuti akhalenso pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. (Lev. 5:5, 6, 15) Zimenezitu zinali zofunika kwambiri. Yehova ananena kuti munthu wodetsedwa amene wadya nawo nsembe yachiyanjano, yomwe inkaphatikizapo nsembe zaufulu, aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu ake. (Lev. 7:20, 21) Koma munthu amene anali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova akapereka nsembe yopanda chilema, ankasangalala kwambiri.—Werengani 1 Mbiri 29:9.

ZIMENE TINGAPEREKE MASIKU ANO

7, 8. (a) Kodi anthu ambiri amadalitsidwa bwanji chifukwa chodzipereka pa ntchito ya Ufumu? (b) Kodi tili ndi zinthu ziti zimene tingapereke kwa Yehova?

7 Masiku anonso anthu ambiri amadzipereka ndi mtima wonse potumikira Yehova ndipo iye amasangalala kwambiri ndi zimenezi. Timadalitsidwa kwambiri tikamatumikira abale athu. M’bale wina amene amathandiza kumanga Nyumba za Ufumu ndiponso kupereka chithandizo kumene kwachitika masoka a chilengedwe, ananena kuti amakhala ndi chisangalalo chosaneneka. Iye anati: “Kuona kuti abale ndi alongo akusangalala kwambiri akakhala ndi Nyumba ya Ufumu yatsopano kapena akathandizidwa pambuyo pokumana ndi  tsoka la chilengedwe, kumatichititsa kuona kuti ntchitoyi ndi yofunika kwambiri.”

Timapereka zinthu mwaufulu ngati mmene Aisiraeli ankaperekera nsembe zaufulu (Onani ndime 7 mpaka 13)

8 Masiku ano, gulu la Yehova limayesetsa nthawi zonse kuona mmene lingathandizire pa ntchito ya Yehova. Mu 1904, M’bale C. T. Russell analemba kuti: “Aliyense ayenera kudziwa kuti Ambuye amupatsa udindo woonetsetsa kuti akugwiritsa ntchito bwino nthawi yake, mphamvu zake, ndalama zake ndi zina zotero. Ndipo ayenera kuyesetsa kugwiritsa ntchito zinthu zimenezi mmene angathere polemekeza Ambuye.” N’zoona kuti timadalitsidwa kwambiri tikapereka nsembe kwa Yehova, koma kuti tichite zimenezi tiyenera kulolera kuti tisakhale ndi zinthu zina. (2 Sam. 24:21-24) Kodi pali zinthu zimene tingapereke kwa Yehova?

Akutumikira ku Beteli ya ku Australia

9. Kodi ndi mfundo iti pa Luka 10:2-4 imene ingatithandize kugwiritsa ntchito bwino nthawi?

9 Nthawi yathu. Pamafunika nthawi yambiri ndiponso khama pomasulira mabuku athu, pomanga Nyumba za Ufumu ndi malo a misonkhano, pokonzekera misonkhano ikuluikulu, pothandiza pakagwa masoka ndiponso pochita zinthu zina zofunika. Koma timakhala ndi maola ochepa pa tsiku. Yesu anapereka malangizo amene akhoza kutithandiza kugwiritsa ntchito bwino nthawi. Potumiza ophunzira ake kukalalikira, iye anawauza kuti ‘asamachedwe akamapereka moni panjira.’ (Luka 10:2-4) N’chifukwa chiyani Yesu anapereka malangizowa? Katswiri wina wa Baibulo anati: “Moni wa anthu a ku Isiraeli ndi mayiko ozungulira sunali wongogwirana chanza n’kuwerama pang’ono ngati mmene ife timachitira. Koma ankakumbatirana ndi kuwerama mobwerezabwereza, ndipo nthawi zina ankagona pansi chafufumimba. Zonsezi zinkafuna nthawi yambiri.” Yesu sanali kulimbikitsa ophunzira ake kuti azikhala achipongwe. Koma anali kuwathandiza kuzindikira kuti anali ndi nthawi yochepa ndipo ankayenera kuigwiritsa ntchito pa zinthu zofunika. (Aef. 5:16) Ifenso tingachite bwino kutsatira mfundoyi kuti tikhale ndi nthawi yambiri yogwira ntchito ya Ufumu.

Abale ndi alongo ali m’Nyumba ya Ufumu ku Kenya

10, 11. (a) Kodi zopereka zathu pa ntchito ya padziko lonse zimagwiritsidwa ntchito bwanji? (b) Kodi ndi mfundo iti pa 1 Akorinto 16:1, 2 imene ingatithandize?

10 Ndalama zathu. Pamafunika ndalama zambiri kuti ntchito ya Ufumu iziyenda bwino. Chaka chilichonse ndalama zokwana madola mamiliyoni ambiri zimagwiritsidwa ntchito posamalira oyang’anira oyendayenda, apainiya apadera ndiponso amishonale. Kuchokera mu 1999, Nyumba za Ufumu 24,500 zamangidwa m’mayiko osauka. Koma pakufunikabe Nyumba za Ufumu 6,400 m’mayikowa. Mwezi uliwonse magazini okwana 100 miliyoni a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! amasindikizidwa. Ntchito zonsezi zimatheka chifukwa cha zopereka zaufulu.

11 Mtumwi Paulo ananena mfundo ina imene tiyenera kutsatira pa nkhani ya zopereka. (Werengani 1 Akorinto 16:1, 2.) Iye analimbikitsa abale a ku Korinto kuti asamangodikira kuti aone ndalama zimene atsala nazo pa mapeto a mlungu. Koma anawauza kuti kumayambiriro kwa mlungu, aziika pambali ndalama zimene angakwanitse kupereka. Masiku anonso, abale ndi alongo amakonzekera pasadakhale ndalama zimene angakwanitse ndipo amapereka mowolowa manja. (Luka 21:1-4; Mac. 4:32-35) Yehova amayamikira kwambiri mtima wopereka umenewu.

Akutumikira m’komiti ya zomangamanga ku Tuxedo, New York, m’dziko la United States

12, 13. (a) Kodi ndi maganizo ati amene angalepheretse ena kuchita zambiri? (b) Kodi Yehova angawathandize bwanji anthu oterewa?

12 Luso ndi mphamvu zathu. Yehova amatithandiza tikamagwiritsa ntchito luso ndiponso mphamvu zathu pa ntchito ya Ufumu. Iye walonjeza kuti azitithandiza tikatopa. (Yes. 40:29-31) Kodi mumaona kuti mulibe luso lokwanira kuti muthandize pa ntchito ya Ufumu? Kodi mumaganiza kuti ntchito zimenezi n’zoyenera  abale ndi alongo ena? Ngati ndi choncho, kumbukirani kuti Yehova amatha kukulitsa luso la munthu ngati mmene anachitira ndi Bezaleli ndi Oholiabu.—Eks. 31:1-6; onani chithunzi patsamba 11.

13 Yehova amatilimbikitsa kuti tisamakhale oumira koma tizipereka zonse zimene tingathe. (Miy. 3:27) Pamene Ayuda ankamanganso kachisi ku Yerusalemu, Yehova anawauza kuti aziganizira mozama zimene anali kuchita pa ntchitoyo. (Hag. 1:2-5) Iwo anali atasokonezeka n’kuiwala zinthu zofunika. Tingachite bwino kuona ngati timaika patsogolo zimene Yehova amaona kuti n’zofunika. Tiyenera ‘kuganizira mofatsa’ kuti tione ngati tingawonjezere zimene timachita pa ntchito ya Ufumu m’masiku otsiriza ano.

TIZIPEREKA ZIMENE TINGATHE

14, 15. (a) Kodi zimene abale athu osauka amachita zimatilimbikitsa bwanji? (b) Kodi tiyenera kuyesetsa kukhala ndi mtima wotani?

14 Abale ndi alongo ambiri amakhala m’mayiko osauka ndipo amakumana ndi mavuto ambiri. Gulu lathu limayesetsa kuthandiza abale amenewa. (2 Akor. 8:14) Ngakhale zili choncho, abale a m’mayikowa amakondanso kupereka. Yehova amasangalala kwambiri akaona kuti anthu osauka ali ndi mtima wopereka mokondwera.—2 Akor. 9:7.

15 M’dziko lina losauka ku Africa, abale ena amasankha kachigawo kena ka munda wawo kuti ndalama zimene angapeze pamenepo azipereke pa ntchito ya Ufumu. M’dziko lomweli panafunika kumanga Nyumba ya Ufumu. Abale ndi alongo a kumeneko ankafunitsitsa kuthandiza. Koma ntchitoyi inafunika kuchitika nthawi yobzala. Chifukwa cha mtima wofuna kuthandiza, iwo ankagwira nawobe ntchitoyi kenako n’kupita kumunda madzulo. Apatu abalewa anadzipereka kwambiri. Izi zikutikumbutsa za abale a ku Makedoniya m’nthawi ya atumwi. Iwo anali pa umphawi wadzaoneni koma anapempha kuti athandize nawo pa ntchito imene inkafunika. (2 Akor. 8:1-4) Choncho tiyeni tonse tiziyesetsa kupereka mogwirizana ndi ‘madalitso amene Yehova watipatsa.’—Werengani Deuteronomo 16:17.

16. Kodi tingatani kuti tizipereka nsembe zimene Yehova amakondwera nazo?

16 Komabe tiyenera kukhala osamala. Mofanana ndi Aisiraeli, tiyenera kuonetsetsa kuti nsembe zathu n’zovomerezeka kwa Mulungu. Choncho ndi bwino kusamaliranso maudindo ena amene tili nawo m’banja komanso okhudza kulambira Yehova. Kodi chingachitike n’chiyani ngati tikulephera kusamalira banja lathu pa nkhani yolambira komanso kupeza zofunika chifukwa chakuti tikuthandiza anthu ena? Tikatero ndiye kuti tikupereka zinthu ‘zimene sitingathe.’ (Werengani 2 Akorinto 8:12.) Tiyeneranso kuyesetsa kuti ubwenzi wathu ndi Mulungu ukhalebe wabwino. (1 Akor. 9:26, 27) Tikamatsatira mfundo za m’Baibulo, timakhala osangalala popereka nsembe zathu ndipo Yehova “amakondwera” ndi nsembezo.

TIMAYAMIKIRA KWAMBIRI ZIMENE MUMAPEREKA

17, 18. (a) Kodi mumaona bwanji anthu onse amene akudzipereka kwambiri pa ntchito ya Ufumu? (b) Kodi tonsefe tiyenera kuganizira chiyani?

17 Abale ndi alongo ambiri ‘akudzipereka ngati nsembe yachakumwa’ pogwira ntchito ya Ufumu. (Afil. 2:17) Timayamikira kwambiri anthu amene amasonyeza mtima wopereka umenewu. Timayamikiranso akazi ndi ana a abale amene amatsogolera pa ntchito ya Ufumu chifukwa cha mtima wawo wodzipereka.

18 Pamafunika khama kwambiri kuti ntchito ya Ufumu iziyenda bwino. Tiyeni tonse tiziganizira ndiponso kupemphera kuti tione zina zimene tingachite kuti tithandize pa ntchito ya Ufumu. Musakayikire kuti mudalitsidwa panopa komanso mudzapeza madalitso ambiri “m’nthawi imene ikubwerayo.”—Maliko 10:28-30.

^ ndime 2 Onani nkhani yakuti “Tizipereka Nsembe kwa Yehova ndi Moyo Wathu Wonse” mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 2012, tsamba 21 mpaka 25.