Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mkazi Wamasiye wa ku Zarefati Anadalitsidwa Chifukwa cha Chikhulupiriro Chake

Mkazi Wamasiye wa ku Zarefati Anadalitsidwa Chifukwa cha Chikhulupiriro Chake

MKAZI wina wamasiye anali ndi mwana mmodzi yekha. Koma tsiku lina mwanayu anamwalira. Kenako anaukitsidwa ndipo mlendo wake anati: “Taona, mwana wako ali moyo.” Mkaziyu anasangalala kwambiri ndipo anakumbatira mwana wakeyo.

Nkhaniyi inachitika zaka pafupifupi 3,000 zapitazo ndipo ili mu chaputala 17 cha 1 Mafumu. Mlendoyo anali mneneri Eliya. Nanga mkaziyu anali ndani? Baibulo silitchula dzina lake koma limangoti anali mkazi wamasiye wa kutauni ya Zarefati. Mwana wake ataukitsidwa, chikhulupiriro chake chinalimba kwambiri. Tiyeni tione zinthu zofunika kwambiri zimene tingaphunzire pa nkhani ya mkaziyu.

ELIYA ANAPITA KWA MKAZI WAMASIYE WACHIKHULUPIRIRO

Mfumu Ahabu ya Isiraeli inali yoipa kwambiri ndipo Yehova anasankha zoti abweretse chilala m’dziko lake kwa zaka zingapo. Eliya atangonena za chilalacho, Mulungu anamubisa kuti Ahabu asamupeze ndipo anagwiritsa ntchito akhwangwala kuti azimubweretsera mkate ndi nyama. Kenako Yehova anauza Eliya kuti: “Nyamuka, upite ku Zarefati m’dziko la Sidoni ukakhale kumeneko. Ine ndikalamula mayi wina wa kumeneko, mkazi wamasiye, kuti azikakupatsa chakudya.”—1 Maf. 17:1-9.

Eliya atafika ku Zarefati anaona mkazi wamasiye wosauka akutola nkhuni. Mwina atamuona ankadzifunsa kuti, ‘Kapena mkazi uja ndi ameneyu? Komatu akuoneka wosauka kwambiri, ndiye angandipatse chakudya?’ Ngakhale kuti mwina Eliya ankakayikira, anayamba kulankhula naye. Iye anati: “Undipatseko madzi pang’ono m’chikho kuti ndimwe.” Ndiyeno mayiyo akupita kukatunga madziwo, Eliya anamuitana n’kumuza kuti: “Undibweretserekonso mkate pang’ono.” (1 Maf. 17:10, 11) Madzi oti mayiyu apereke kwa mlendoyo analipo koma vuto linali chakudya.

Ndiyeno poyankha, mayiyo anati: “Pali Yehova Mulungu wanu wamoyo, ndilibe  mkate, koma ufa pang’ono mumtsuko waukulu ndi mafutanso pang’ono mumtsuko waung’ono. Panopa ndikutola tinkhuni kuti ndipite kukaphika chakudya choti ineyo ndi mwana wanga tidye. Tikadya, tiziyembekezera kufa.” (1 Maf. 17:12) Tsopano tiyeni tione zimene tikuphunzira pa nkhaniyi.

Mkazi wamasiyeyu ankadziwa kuti Eliya anali Mwisiraeli woopa Mulungu. Tikudziwa zimenezi chifukwa cha mawu ake akuti “pali Yehova Mulungu wanu wamoyo.” Zikuoneka kuti ankadziwa ndithu za Mulungu wa Aisiraeli koma anali asanafike pomuona kuti ndi Mulungu wake. Mayiyu ankakhala kutauni ya Zarefati yomwe inali pafupi ndi mzinda wa Sidoni m’chigawo cha Foinike ndipo zikuoneka kuti zinthu zambiri kutauniyi zinkachokera ku Sidoniko. N’zosakayikitsa kuti ku Zarefati kunkakhala anthu olambira Baala. Koma Yehova ayenera kuti anaona mayiyu kukhala wosiyana kwambiri ndi athu a m’deralo.

Ngakhale kuti mayi wamasiyeyu ankakhala ndi anthu olambira mafano, iye anasonyeza chikhulupiriro. Yehova anauza Eliya kuti apite kwa mayiyu n’cholinga choti onse awiriwo athandizike. Apansotu tikhoza kuphunzirapo mfundo ina yofunika.

Sikuti anthu onse a m’tauni ya Zarefati anali oipa. Potumiza Eliya kwa mkazi wamasiyeyu, Yehova anasonyeza kuti amathandiza anthu oona mtima amene sanayambe kumutumikira. Choncho m’pomveka kunena kuti “[Mulungu] amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”—Mac. 10:35.

Kodi ndi anthu angati m’dera lanu amene ali ngati mkazi wamasiye wa ku Zarefati? Ngakhale kuti amakhala ndi anthu otsatira zipembedzo zonyenga, mwina iwo amafunitsitsa kudziwa choonadi. N’kutheka kuti amangodziwa pang’ono za Yehova kapena samudziwa n’komwe, choncho afunika kuthandizidwa kuti ayambe kumulambira. Kodi inuyo mumafufuza ndiponso kuthandiza anthu oterewa?

“UKAYAMBE WANDIKONZERA MTANDA WAUNG’ONO WA MKATE”

Taganizirani zimene Eliya anapempha mayi wamasiyeyu. Mayiyu anali atangomuuza kumene kuti ufa wake unali wongophika kamodzi kokha chakudya cha iyeyo ndi mwana wake, kenako aziyembekezera kufa. Koma kodi Eliya anati chiyani? Iye anati: “Usachite mantha. Pita ukachite mogwirizana ndi mawu ako. Koma pa zimene uli nazozo, ukayambe wandikonzera mtanda waung’ono wa mkate, n’kubwera nawo kwa ine. Kenako, ukakonze chakudya chako ndi cha mwana wako. Pakuti Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ufa umene uli mumtsuko waukulu siutha, ndipo mafuta amene ali mumtsuko waung’ono saatha, kufikira tsiku limene Yehova adzagwetse mvula padziko lapansi.’”—1 Maf. 17:11-14.

Mwina ena atauzidwa zimenezi, anganene kuti, ‘Sitingachite zimenezo chifukwa chakudya chimene tatsala nacho n’chokhachi.’ Koma mayi wamasiyeyu sananene zimenezo. Ngakhale kuti Yehova sankamudziwa bwinobwino, anakhulupirira Eliya ndipo anachita zimene anamupemphazo. Apatu chikhulupiriro chake chinayesedwa kwambiri, ndipo iye anachita zinthu mwanzeru.

Mkazi wamasiye anakhulupirira Yehova, Mulungu wa Eliya, ndipo izi zinachititsa kuti iye ndi mwana wake apulumuke

Mulungu anathandizadi mayi wamasiyeyu. Zimene Eliya analonjeza zinachitikadi chifukwa Yehova anachulukitsa ufa ndi mafutawo moti Eliya, mayi wamasiyeyo ndi mwana wake anali ndi chakudya chokwanira mpaka chilalacho chitatha. Paja Baibulo limati: “Ufa umene unali mumtsuko waukulu sunathe, ndipo mafuta amene anali mumtsuko waung’ono sanathe,  mogwirizana ndi mawu a Yehova amene ananena kudzera mwa Eliya.” (1 Maf. 17:16; 18:1) Ngati mayiyu akanakana zimene Eliya anamupemphazo, ufa ndi mafutawo akanangophikiradi kamodzi kokha. Koma mayiyu anali ndi chikhulupiriro komanso anadalira Yehova, choncho anakonzera Eliya chakudya.

Apa tikuphunzira kuti Mulungu amadalitsa munthu amene ali ndi chikhulupiriro. Mukasonyeza chikhulupiriro pamene muli pa mayesero, Yehova adzakuthandizani. Adzakupatsani zofuna zanu, adzakutetezani ndiponso adzakhala Mnzanu.—Eks. 3:13-15.

Mu 1898, magazini ya Nsanja ya Olonda inanena za mayi wamasiyeyu kuti: “Popeza kuti mayiyu anasonyeza chikhulupiriro ndipo anamvera, Ambuye anamuthandiza kudzera mwa Mneneri. Koma akanapanda kusonyeza chikhulupiriro, pakanapezeka mayi wina wamasiye amene akanachita zimenezo. Ifenso nthawi zina Ambuye amalola kuti chikhulupiriro chathu chiyesedwe. Tikasonyeza chikhulupiriro amatidalitsa, koma tikapanda kutero timataya mwayiwu.”

Tikakumana ndi mayesero, tizifufuza malangizo a Mulungu kuchokera m’Malemba komanso mabuku athu. Tikapeza malangizowo, tizichita zimene Yehova akufuna ngakhale zitakhala zovuta kwambiri. Mulungu adzatidalitsa tikatsatira malangizo anzeru akuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalire luso lako lomvetsa zinthu. Uzim’kumbukira m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola njira zako.”—Miy. 3:5, 6.

KODI ‘MWABWERA KUDZAPHA MWANA WANGA’?

Koma mayi wamasiyeyu anakumananso ndi mayesero ena. Baibulo limati: “Pambuyo pa zimenezi, mwana wamwamuna wa mayi wa m’nyumbamo, anadwala. Matenda ake anakula kwambiri mpaka anamwalira.” Mayiyo anadabwa nazo zimenezi ndipo polira anafunsa Eliya kuti: “Ndili nanu chiyani inu munthu wa Mulungu woona? Mwabwera kwa ine kudzandikumbutsa cholakwa changa ndi kudzapha mwana wanga.” (1 Maf. 17:17, 18) Kodi mayiyu ankatanthauza chiyani ponena zimenezi?

Kodi mwina anakumbukira zinthu zina zimene analakwitsa m’mbuyomo zomwe zinkavutitsa chikumbumtima chake? Kodi ankaganiza kuti imfa ya mwana wakeyo ndi chilango chochokera kwa Mulungu ndipo Eliyayo anatumidwa kudzapereka chilangocho? Baibulo silinena chilichonse pa nkhaniyi koma mfundo ndi yakuti: Mayi wamasiyeyu sanaimbe mlandu Mulungu pa vuto lakeli.

Eliya ayenera kuti anamva chisoni kwambiri kuona mwanayo atamwalira komanso kumva mayiyo akunena kuti iye anabwera kudzapha mwana wake. Ndiyeno Eliya anatenga mwana wakufayo n’kupita naye m’chipinda chapamwamba komwe anakafuulira Yehova kuti: “Inu Yehova Mulungu wanga, kodi mukuchitiranso zoipa mkazi wamasiye amene ndikukhala naye monga mlendo wake, mwa kupha mwana wake?” Eliya ankadera nkhawa kuti dzina la Mulungu likhoza kunyozeka ngati Mulunguyo atalola kuti vuto la mayi wokoma mtimayu lipitirire. Choncho anachonderera Mulungu kuti: “Inu Yehova Mulungu wanga, chonde chititsani kuti moyo wa mwanayu ubwerere mwa iye.”—1 Maf. 17:20, 21.

“TAONA, MWANA WAKO ALI MOYO”

Yehova anayankha pempheroli. Anatero chifukwa chakuti mkazi wamasiyeyu anapereka chakudya kwa mneneri wa Mulungu ndipo anasonyeza chikhulupiriro. Zikuoneka kuti Mulungu analola kuti mwanayu amwalire podziwa kuti adzamuukitsa ndipo ngati atatero zidzapereka chiyembekezo kwa anthu ena m’tsogolo. Ndipotu m’Baibulo, imeneyi ndi nkhani yoyamba yofotokoza za kuuka kwa akufa. Choncho Eliya atachonderera kwambiri, Yehova anaukitsa mwanayo. Kodi mukuganiza kuti mayiyo anamva bwanji pamene Eliya anamuuza kuti “Taona, mwana wako ali moyo”? Zitatero, mayiyu anauza Eliya kuti: “Tsopano ndadziwadi kuti ndinu munthu wa Mulungu ndipo mawu a Yehova amene ali m’kamwa mwanu ndi oona.”—1 Maf. 17:22-24.

Nkhani ya mkazi wamasiyeyu imathera pomwepa. Koma popeza Yesu anamutchulanso, ayenera kuti ankatumikira Yehova mokhulupirika pa zaka zomaliza za moyo wake. (Luka 4:25, 26) Nkhani imeneyi ikusonyeza kuti Yehova amadalitsa anthu amene amachitira atumiki ake zabwino. (Mat. 25:34-40) Ikusonyezanso kuti Yehova amapereka zinthu zofunika kwa atumiki ake ngakhale pamene zinthu zafika poipa kwambiri. (Mat. 6:25-34) Imatithandizanso kudziwa kuti Yehova ali ndi mphamvu zoukitsa akufa ndipo amafunitsitsa kuchita zimenezi. (Mac. 24:15) Izitu ndi zifukwa zomveka zotichititsa kukumbukira mkazi wamasiye wa ku Zarefati.