Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Sangalalani Chifukwa cha Ukwati wa Mwanawankhosa

Sangalalani Chifukwa cha Ukwati wa Mwanawankhosa

“Tiyeni tisangalale ndipo tikhale ndi chimwemwe chodzaza tsaya . . . chifukwa ukwati wa Mwanawankhosa wafika.”—CHIV. 19:7.

1, 2. (a) Kodi kumwamba kudzakhala chisangalalo chifukwa cha ukwati wa ndani? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

KUKONZEKERA ukwati kumatenga nthawi yaitali. Koma m’nkhani ino tikambirana za ukwati wachifumu, womwe ndi wapadera kwambiri. Kukonzekera ukwati umenewu kwakhala kukuchitika kwa zaka pafupifupi 2,000. Panopa nthawi ya ukwati yayandikira kwambiri. Posachedwapa nyimbo zachisangalalo zidzaimbidwa m’nyumba yachifumu ndipo khamu lakumwamba lidzaimba kuti: “Tamandani Ya, anthu inu, chifukwa Yehova Mulungu wathu, Wamphamvuyonse, wayamba kulamulira monga mfumu. Tiyeni tisangalale ndipo tikhale ndi chimwemwe chodzaza tsaya. Timupatse ulemerero, chifukwa ukwati wa Mwanawankhosa wafika, ndipo mkazi wake wadzikongoletsa.”—Chiv. 19:6, 7.

2 “Mwanawankhosa” amene ali ndi ukwati wosangalatsa kumwambayo ndi Yesu Khristu. (Yoh. 1:29) Kodi iye wavala bwanji pokonzekera ukwatiwu? Kodi mkazi wake ndi ndani? Nanga mkaziyo wakonzekera bwanji? Kodi ukwatiwo uchitika liti? Tanena kale kuti kumwamba kudzakhala chisangalalo chachikulu chifukwa cha ukwatiwu. Koma kodi anthu amene akuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi adzasangalala nawonso?  Nkhaniyitu ndi yochititsa chidwi, choncho kuti tipeze mayankho tiyeni tipitirize kukambirana Salimo 45.

ZOVALA ZAKE NDI ZONUNKHIRA BWINO

3, 4. (a) Kodi Mkwati wavala zovala zotani, nanga n’chiyani chimene chikumusangalatsanso? (b) Kodi “ana aakazi a mafumu” komanso “mkazi wamkulu wa mfumu” amene akusangalala limodzi ndi Mkwatiyu ndi ndani?

3 Werengani Salimo 45:8, 9Mkwati, yemwe ndi Yesu Khristu, wavala zovala zaukwati wachifumu zokongola kwambiri. Zovalazi zikununkhira bwino kwambiri ngati ‘mafuta onunkhira, abwino koposa’ monga mule ndi kasiya. Aisiraeli ankasakaniza mafuta amenewa ndi zinthu zina popanga mafuta ogwiritsa ntchito pa kudzoza kopatulika.—Eks. 30:23-25.

4 M’nyumba yachifumuyi mukumveka nyimbo zomwe Mkwatiyu akusangalala nazo pamene tsiku la ukwatiwu likuyandikira. Nayenso “mkazi wamkulu wa mfumu,” yemwe ndi mbali yakumwamba ya gulu la Mulungu, akusangalala nawo. Mbali imeneyi ya gulu la Mulungu ikuphatikizapo “ana aakazi a mafumu,” kapena kuti angelo oyera. N’zochititsa chidwi kwambiri kumva mawu ochokera kumwamba akuti: “Tiyeni tisangalale ndipo tikhale ndi chimwemwe chodzaza tsaya . . . chifukwa ukwati wa Mwanawankhosa wafika.”

MKWATIBWI WAKONZEKERA UKWATI

5. Kodi “mkazi wa Mwanawankhosa” ndi ndani?

5 Werengani Salimo 45:10, 11. Mkwati ndiye tamudziwa, koma kodi mkwatibwi ndi ndani? Ndi gulu la anthu ena amene ali mumpingo umene mutu wake ndi Yesu Khristu. (Werengani Aefeso 5:23, 24.) Anthu amene ali m’gululi adzalamulira limodzi ndi Khristu mu Ufumu wa Mesiya. (Luka 12:32) Iwo ndi Akhristu odzozedwa okwana 144,000 ndipo “amatsatira Mwanawankhosa kulikonse kumene akupita.” (Chiv. 14:1-4) Popeza iwo ndi “mkazi wa Mwanawankhosa,” adzakhala naye kumwamba kumene iye amakhala.—Chiv. 21:9; Yoh. 14:2, 3.

6. (a) N’chifukwa chiyani odzozedwa amatchedwa “mwana wamkazi wa mfumu”? (b) Nanga n’chifukwa chiyani amauzidwa kuti ‘aiwale anthu awo’?

6 Mkazi wa Mwanawankhosayu akutchedwa ‘mwana wamkazi’ komanso “mwana wamkazi wa mfumu.” (Sal. 45:13) Ndiyeno kodi ‘mfumuyo’ ndi ndani? Ndi Yehova, amene amatenga Akhristu odzozedwawa kukhala “ana” ake. (Aroma 8:15-17) Popeza Akhristuwa amakhala mkwatibwi wakumwamba, iwo amauzidwa kuti: “Uiwale anthu ako ndi nyumba ya bambo ako” pansi pano. Amafunika ‘kuika maganizo awo pa zinthu zakumwamba osati pa zinthu zapadziko.’—Akol. 3:1-4.

7. (a) Kodi Khristu wakhala akukonzekeretsa bwanji mkazi wake? (b) Kodi mkaziyo amaona bwanji mwamuna wake wam’tsogoloyu?

7 Khristu wakhala akukonzekeretsa mkazi wakeyu kwa zaka zambirimbiri. Mtumwi Paulo anafotokoza kuti Khristu anakonda “mpingo n’kudzipereka yekha chifukwa cha mpingowo, ndipo anauyeretsa pousambitsa m’madzi a mawu a Mulungu. Anatero kuti iyeyo alandire mpingowo uli wokongola ndiponso waulemerero, wopanda banga kapena makwinya kapenanso chilichonse cha zinthu zotero, koma kuti ukhale woyera ndi wopanda chilema.” (Aef. 5:25-27) Paulo anauzanso Akhristu odzozedwa ku Korinto kuti: “Ndikukuchitirani nsanje, ngati imene Mulungu amakuchitirani, popeza ndine ndinakuchititsani kulonjezedwa ukwati ndi mwamuna mmodzi, Khristu, ndipo ndikufuna kukuperekani ngati namwali woyera kwa iye.” (2 Akor. 11:2) Mfumu Yesu Khristu, yemwe ndi Mkwati, amanyadira akaona mkazi wakeyu chifukwa amamuona kuti ndi ‘wokongola’ mwauzimu. Mkaziyonso amaona kuti Khristu ndi “mbuye” wake ndipo ‘amamuweramira’ monga mwamuna wake wam’tsogolo.

MKWATIBWI “ADZAMUBWERETSA KWA MFUMU”

8. N’chifukwa chiyani m’pomveka kunena kuti mkwatibwiyu “ali pa ulemerero waukulu”?

8 Werengani Salimo 45:13, 14a. Mkwatibwiyu wakonzekera ukwati wake ndipo  akuoneka kuti “ali pa ulemerero waukulu.” Pa Chivumbulutso 21:2, mkwatibwiyu akumuyerekezera ndi mzinda wa Yerusalemu Watsopano, ndipo ‘wakongoletsedwera mwamuna wake.’ Mzinda wakumwamba umenewu uli ndi “ulemerero wa Mulungu” ndipo ukunyezimira “ngati mwala wamtengo wapatali kwambiri, ngati mwala wa yasipi wowala mbee! ngati galasi.” (Chiv. 21:10, 11) Buku la Chivumbulutso limafotokoza bwino ulemerero wa Yerusalemu Watsopanoyu. (Chiv. 21:18-21) M’pake kuti wamasalimo ananena kuti mkwatibwiyu “ali pa ulemerero waukulu.” Alidi pa ulemerero chifukwa ukwatiwu ukuchitikiranso kumwamba.

9. Kodi mkwatibwi ‘akumubweretsa’ kwa “mfumu” iti, ndipo wavala bwanji?

9 Mkwatibwiyu akumubweretsa kwa Mkwati, yemwe ndi Mfumu ya Ufumu wa Mesiya. Mfumuyi yakhala ikumukonzekeretsa ‘pomusambitsa m’madzi a mawu a Mulungu.’ Choncho ndi “woyera ndi wopanda chilema.” (Aef. 5:26, 27) Zovala za mkwatibwiyu ziyeneranso kukhala zokongola zogwirizana ndi mwambo wa ukwati. Ndipo ndi mmene zililidi chifukwa “zovala zake ndi zagolide,” ndipo “adzamubweretsa kwa mfumu atavala chovala choluka.” Pa ukwati wa Mwanawankhosawu, mkwatibwi “waloledwa kuvala zovala zapamwamba, zonyezimira ndi zoyera bwino, pakuti zovala zapamwambazo zikuimira ntchito zolungama za oyera.”—Chiv. 19:8.

‘UKWATI WAFIKA’

10. Kodi ukwati wa Mwanawankhosa udzachitika liti?

10 Werengani Chivumbulutso 19:7. Kodi ukwati wa Mwanawankhosayu udzachitika liti? Ngakhale kuti “mkazi wake wadzikongoletsa” pokonzekera ukwati, zimene zili m’mavesi otsatira sizikufotokoza nkhani ya ukwatiwu. M’malomwake, zikufotokoza mbali yomaliza ya chisautso chachikulu. (Chiv. 19:11-21) Kodi izi zikutanthauza kuti ukwatiwo udzachitika Mfumuyi isanamalize kugonjetsa adani ake? Ayi. Masomphenya a m’buku la Chivumbulutso safotokoza zinthu motsatira nthawi imene zidzachitike. Koma Salimo 45 limasonyeza kuti ukwati wachifumuwu udzachitika pambuyo poti Mfumu Yesu Khristu wamangirira lupanga lake ndipo ‘wapambana’ pa nkhondo yolimbana ndi adani ake.—Sal. 45:3, 4.

11. Kodi Khristu adzagonjetsa bwanji adani ake?

11 Choncho tinganene kuti zinthu zidzachitika motere: Choyamba, “hule lalikulu,” kapena kuti Babulo Wamkulu, yemwe ndi zipembedzo zonse zonyenga, adzawonongedwa. (Chiv. 17:1, 5, 16, 17; 19:1, 2) Kenako, Khristu adzapita kukapereka chiweruzo cha Mulungu ku dziko loipa la Satanali ndi kuliwononga pa Aramagedo, yomwe ndi ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.’ (Chiv. 16:14-16; 19:19-21) Pamapeto pake, Mfumuyi idzamaliza kugonjetsa adani ake poponya Satana ndi ziwanda zake kuphompho ndipo iwo adzakhala ngati afa.—Chiv 20:1-3.

12, 13. (a) Kodi ukwati wa Mwanawankhosa udzachitika liti? (b) Kodi kumwamba ndi ndani amene adzasangalale pa ukwati wa Mwanawankhosa?

12 Akhristu odzozedwa akamwalira pa nthawi ino ya kukhalapo kwa Khristu, amaukitsidwa n’kupita kumwamba. Pambuyo poti Babulo Wamkulu wawonongedwa, Yesu adzasonkhanitsa odzozedwa onse amene adzakhale adakali padziko lapansi. (1 Ates. 4:16, 17) Choncho nkhondo ya Aramagedo isanayambe, Akhristu onse amene ali m’gulu la “mkwatibwi” adzakhala ali kumwamba. Pambuyo pa nkhondoyi, ukwati wa Mwanawankhosa udzachitika. Ukwati umenewu udzakhala wosangalatsa kwambiri. Lemba la Chivumbulutso 19:9 limati: “Odala ndiwo amene aitanidwa ku phwando la chakudya chamadzulo la ukwati wa Mwanawankhosa.” Akhristu 144,000 omwe ndi mkwatibwi wa Khristu adzasangalala kwambiri.  Nayenso Mkwatiyo adzasangalala kwambiri kukhala limodzi ndi olamulira anzake onse ndipo mophiphiritsa ‘adzadya ndi kumwa nawo patebulo la Ufumu wake.’ (Luka 22:18, 28-30) Koma si Mkwati ndi mkwatibwi okha amene adzasangalale pa ukwati wa Mwanawankhosawu.

13 Taona kale kuti khamu lakumwamba lidzaimba mogwirizana kuti: “Tiyeni tisangalale ndipo tikhale ndi chimwemwe chodzaza tsaya. Timupatse [Yehova] ulemerero, chifukwa ukwati wa Mwanawankhosa wafika, ndipo mkazi wake wadzikongoletsa.” (Chiv. 19:6, 7) Nanga bwanji atumiki a Yehova a padziko lapansi? Kodi nawonso adzasangalala nawo?

“ADZAWABWERETSA AKUSANGALALA”

14. Kodi “anamwali anzake” a mkwatibwi otchulidwa mu Salimo 45 ndi ndani?

14 Werengani Salimo 45:12, 14b, 15. Mneneri Zekariya analosera kuti m’nthawi yamapeto, anthu amitundu ina adzagwirizana ndi otsalira a Isiraeli wauzimu. Iye analemba kuti: “M’masiku amenewo, amuna 10 ochokera m’zilankhulo zonse za anthu a mitundu ina adzagwira chovala cha munthu amene ndi Myuda ndi kunena kuti: ‘Anthu inu tipita nanu limodzi, chifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.’” (Zek. 8:23) Pofotokoza za “amuna 10” ophiphiritsawa, lemba la Salimo 45:12 limagwiritsa ntchito mawu akuti “mwana wamkazi wa ku Turo” komanso “olemera pakati pa anthu.” Iwo amapita ndi mphatso kwa odzozedwa amene ali padzikoli pofuna kuti agwirizane nawo komanso athandizidwe mwauzimu. Kuyambira mu 1935, anthu mamiliyoni ambiri alola kuti odzozedwawo ‘awathandize kukhala olungama.’ (Dan. 12:3) Anthu amene agwirizana ndi Akhristu odzozedwawa asintha zambiri pa  moyo wawo ndipo ali ngati anamwali osadetsedwa. “Anamwali anzake” a mkwatibwiyu adzipereka kwa Yehova ndipo asonyeza kuti ndi okhulupirika kwa Mfumu Yesu Khristu.

15. Kodi “anamwali” akugwira ntchito yotani pamodzi ndi anthu omwe ali m’gulu la mkwatibwi padziko lapansi?

15 Anthu a m’gulu la mkwatibwi omwe adakali padzikoli amayamikira kwambiri ‘anamwaliwo’ chifukwa chowathandiza mwakhama polalikira ‘uthenga wabwino wa ufumu’ padziko lonse lapansi. (Mat. 24:14) “Mzimu ndi mkwatibwi akunenabe kuti, ‘Bwera!’ ndipo onse akumva akunenanso kuti, ‘Bwera!’” (Chiv. 22:17) Izi zikutanthauza kuti a “nkhosa zina” anamva odzozedwa omwe ali m’gulu la mkwatibwi akunena kuti “Bwera!” ndipo nawonso akuuza aliyense wokhala padziko lapansi kuti “Bwera!”—Yoh. 10:16.

16. Kodi Yehova wapatsa a nkhosa zina mwayi wotani?

16 Odzozedwa amakonda kwambiri anzawowa ndipo amasangalala kuona kuti Yehova, yemwe ndi Atate a Mkwati, wapatsa anzawowo mwayi wosangalala nawo chifukwa cha ukwati wa Mwanawankhosa. Ulosi unanena kuti “anamwali anzake” a mkwatibwiyu “adzawabweretsa akusangalala ndi kukondwera.” Choncho a nkhosa zina, omwe akuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi, adzasangalalanso chifukwa cha ukwati wa Mwanawankhosa kumwamba. Buku la Chivumbulutso limasonyeza kuti ‘a khamu lalikulu akuimirira pamaso pa mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa.’ Zili choncho chifukwa chakuti iwo amatumikira Yehova m’bwalo lapadziko lapansi la kachisi wauzimuyu.—Chiv. 7:9, 15.

“Anamwali anzake” a mkwatibwi adzasangalala chifukwa cha ukwati wa Mwanawankhosa (Onani ndime 16)

“ANA ANU ADZATENGA MALO A MAKOLO ANU”

17, 18. (a) Kodi ndi madalitso otani amene adzabwere chifukwa cha ukwati wa Mwanawankhosa? (b) Kodi Khristu adzakhalanso atate wa ndani mu Ulamuliro wa Zaka 1,000?

17 Werengani Salimo 45:16. “Anamwali anzake” a mkwatibwi adzasangalalanso akadzaona madalitso amene adzabwere m’dziko latsopano chifukwa cha ukwati wa Mwanawankhosa. Mkwati, yemwenso ndi Mfumu, adzayamba kukonza zinthu padziko lapansi ndipo adzaukitsa “makolo” akale kuti akhale “ana” ake padzikoli. (Yoh. 5:25-29; Aheb. 11:35) Ndiyeno pa anthu amenewa, adzasankha ena kuti akhale “akalonga padziko lonse lapansi.” N’zosakayikitsa kuti Khristu adzasankhanso ena mwa akulu okhulupirika a masiku ano kuti azidzatsogolera m’dziko latsopano.—Yes. 32:1.

18 Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000, Khristu adzakhalanso atate wa anthu ena. Anthu onse amene adzalandire moyo wosatha padziko lapansi adzapeza mwayiwu chifukwa chokhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu. (Yoh. 3:16) Choncho Yesu adzakhala ‘Atate wawo wosatha.’—Yes. 9:6, 7.

AMAFUNITSITSA ‘KUDZIWITSA ENA DZINA LAKE’

19, 20. Kodi nkhani ya mu Salimo 45 imakhudza bwanji Akhristu onse oona masiku ano?

19 Werengani Salimo 45:1, 17. Choncho, nkhani ya mu Salimo 45 ikukhudza Mkhristu aliyense. Odzozedwa amene adakali padzikoli amasangalala chifukwa chakuti akuyembekezera kukakhala limodzi ndi abale awo komanso Khristu kumwamba. A nkhosa zina amagonjeranso ndi mtima wonse Mfumu yawo yaulemerero ndipo amaona kuti kutumikira limodzi ndi anthu a m’gulu la mkwatibwi wake ndi mwayi wamtengo wapatali. Ndiyeno ukwati ukadzachitika, Khristu ndi mafumu anzake adzapereka madalitso osaneneka kwa anthu padziko lapansi.—Chiv. 7:17; 21:1-4.

20 Pamene tikuyembekezera kukwaniritsidwa kwa “nkhani yosangalatsa” yonena za Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, tiyeni tizidziwitsa ena dzina la Mfumuyi. Tiyeni tiyesetsenso kuti tidzakhale m’gulu la anthu amene ‘adzatamanda Mfumuyi mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.’