Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Tiziona Ubwino wa Yehova’

‘Tiziona Ubwino wa Yehova’

Nthawi zina tikakumana ndi mavuto timangokhalira kuwaganizira, timafooka komanso moyo susangalatsa. Davide anakumana ndi mavuto ambiri. Kodi anatani atakumana nawo? Iye anafotokoza zimene anachita mu salimo lina logwira mtima. Anati: “Ndinafuulira Yehova kuti andithandize. Ndinafuulira Yehova kuti andikomere mtima. Ndinapitirizabe kumukhuthulira nkhawa zanga. Ndinapitirizabe kumuuza masautso anga. Ndinachita zimenezi pamene mtima wanga unalefuka. Pamenepo, munadziwa njira yanga.” Davide anapemphera modzichepetsa kwa Mulungu.—Sal. 142:1-3.

Davide ankapemphera kwa Yehova modzichepetsa akakumana ndi mavuto

Mu salimo lina, Davide anaimba kuti: “Chinthu chimodzi chimene ndapempha kwa Yehova, chimenecho ndi chimene ndimachikhumba, n’chakuti, ndikhale m’nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kuti ndione ubwino wa Yehova, komanso kuti ndiyang’ane kachisi wake moyamikira.” (Sal. 27:4) Davide sanali Mlevi koma akanatha kuima panja pa bwalo lopatulika n’kumayang’anitsitsa likulu la kulambira Mulungu woona. Davide ankayamikira kwambiri mwayi umenewu moti ankafunitsitsa kukhala kumeneko masiku onse a moyo wake kuti ‘aziona ubwino wa Yehova.’

Mawu oti “ubwino” amanena za zinthu zimene “zimachititsa munthu kusangalala kwambiri kapena kumva bwino mumtima.” Nthawi zonse Davide ankayamikira zimene Mulungu anakonza kuti anthu azimulambira. Tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo, ndimaona zinthu mmene Davide ankazionera?’

‘TIZIYANG’ANA MOYAMIKIRA’ ZIMENE MULUNGU WAKONZA

Masiku ano palibe malo amodzi amene tonse tiyenera kupita kuti tikalambire Yehova. M’malomwake, pali kachisi wamkulu wauzimu yemwe akuimira zimene Mulungu wakonza kuti tizimulambira. * ‘Tikamayang’ana moyamikira’ zimene Mulungu wakonzazi, tikhozanso ‘kuona ubwino wa Yehova.’

Taganizirani za guwa lansembe zopsereza lamkuwa limene linali patsogolo pa khomo la chihema chopatulika. (Eks. 38:1, 2; 40:6) Guwa limeneli likuimira kufunitsitsa kwa Mulungu kulandira moyo wa Yesu monga nsembe. (Aheb. 10:5-10) Kodi zimenezi n’zothandiza bwanji kwa ifeyo? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pamene tinali adani, tinayanjanitsidwa kwa Mulungu kudzera mu imfa ya Mwana wake.” (Aroma 5:10) Tikamakhulupirira magazi a Yesu, tikhoza kukhala pa “ubwenzi wolimba ndi Yehova” n’kumagwirizana naye kwambiri.—Sal. 25:14.

‘Machimo athu amafafanizidwa ndipo nyengo zotsitsimutsa zimabwera kuchokera kwa Yehova.’ (Mac. 3:19) Anthufe tili ngati akaidi amene akuyembekezera kuphedwa koma akumva chisoni ndi zimene anachita ndipo asintha kwambiri. Ndiyeno woweruza wokoma mtima ataona zimenezi, akuwakhululukira n’kunena kuti asaphedwe. Kodi mukuganiza kuti akaidiwo angamve bwanji? Yehova ali ngati woweruza wokoma mtimayu ndipo akaona anthu olapa amawakhululukira n’kuwachotsera chilango cha imfa.

TIZISANGALALA KUTUMIKIRA MULUNGU WOONA

Pali zinthu zingapo zokhudza kulambira Mulungu zimene Davide akanatha kuona panyumba ya Mulungu. Akanatha kuona Aisiraeli anzake atasonkhana, Chilamulo chikuwerengedwa mokweza ndiponso kufotokozedwa, zonunkhira zikufukizidwa  komanso ansembe ndi Alevi akutumikira. (Eks. 30:34-38; Num. 3:5-8; Deut. 31:9-12) Zinthu zonsezi zinkaimira zinthu zimene zikuchitika masiku ano.

Masiku anonso, “ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambiri abale akakhala pamodzi mogwirizana.” (Sal. 133:1) Anthu ambirimbiri atsopano alowa ‘m’gulu lonse la abale.’ (1 Pet. 2:17) Mawu a Mulungu amawerengedwa ndiponso kufotokozedwa pa misonkhano yathu. Yehova amatiphunzitsa zinthu zambiri kudzera m’gulu lake. Tilinso ndi mabuku ambirimbiri ofotokoza Baibulo omwe timatha kugwiritsa ntchito pophunzira patokha kapena limodzi ndi banja lathu. M’bale wina wa m’Bungwe Lolamulira anati: “Kusinkhasinkha Malemba, kuganizira tanthauzo lake komanso kufufuza kuti ndiwamvetse bwino, zimandithandiza kuti ndikhale wosangalala komanso ubwenzi wanga ndi Yehova ulimbe.” N’zoona kuti ‘kudziwa zinthu kumakhala kosangalatsa m’moyo wathu.’—Miy. 2:10.

Tsiku lililonse, atumiki a Yehova amapereka mapemphero. Mapemphero amenewa amakhala ngati fungo labwino la zofukiza lopita kwa Yehova. (Sal. 141:2) N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Yehova Mulungu amasangalala kwambiri tikamapemphera kwa iye modzichepetsa.

Mose anapemphera kuti: ‘Ubwino wa Yehova Mulungu wathu ukhale pa ife, ndipo akhazikitse ntchito ya manja athu.’ (Sal. 90:17) Tikamachita utumiki wathu mwakhama, Yehova amadalitsa ntchito yathu. (Miy. 10:22) N’kutheka kuti tathandizapo anthu ena kuphunzira choonadi. Mwinanso takhala tikulalikira mwakhama kwa zaka zambiri ngakhale kuti timadwala, timakhala ndi nkhawa, timazunzidwa kapenanso anthu ambiri samvetsera uthenga wathu. (1 Ates. 2:2) Koma ngakhale zili choncho, taona “ubwino wa Yehova” ndipo tikudziwa kuti iye amasangalala kwambiri ndi zimene timachita.

Davide anaimba kuti: “Yehova ndiye gawo langa, gawo limene ndinapatsidwa, komanso chikho changa. Inu mukundisungira bwino kwambiri cholowa changa. Zingwe zoyezera zandigwera m’malo abwino.” (Sal. 16:5, 6) Davide ankayamikira kwambiri “gawo” lake, kapena kuti mwayi wokhala pa ubwenzi ndi Yehova komanso womutumikira. Mofanana ndi Davide, ife timakumana ndi mavuto ambiri koma tadalitsidwanso m’njira zambiri. Choncho tiyeni tipitirize kusangalala potumikira Mulungu woona komanso ‘kuyang’ana moyamikira’ kachisi wauzimu wa Yehova.

^ ndime 6 Onani Nsanja ya Olonda ya July 1, 1996, tsamba 14 mpaka 24.