Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Ndi Mnzathu Weniweni

Yehova Ndi Mnzathu Weniweni

“[Abulahamu] anatchedwa ‘bwenzi la Yehova.’”—YAK. 2:23

1. Popeza tinalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu, kodi timatha kuchita zinthu ziti?

ANA ambiri amafanana ndi makolo awo ndipo si zachilendo kumva anthu akunena kuti: “Uyutu anatengera bambo ake.” Atate wathu wakumwamba, Yehova, ndi amene anatipatsa moyo. (Sal. 36:9) Choncho tinganene kuti ndife ana ake ndipo timafanana naye m’njira zina. Popeza tinalengedwa m’chifaniziro chake, timatha kuganiza, kuzindikira zinthu ndiponso kukhala pa ubwenzi ndi anthu anzathu.—Gen. 1:26.

2. Kodi ubwenzi ndi Yehova umatheka pa zifukwa ziti?

2 Yehova akhoza kukhala Mnzathu weniweni. Ubwenzi umenewu umatheka chifukwa chakuti iye amatikonda. Koma ifenso timafunika kumukhulupirira ndiponso kukhulupirira Mwana wake. Yesu ananena kuti: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yoh. 3:16) Pali anthu ambiri omwe anali mabwenzi a Yehova ndipo m’nkhaniyi tikambirana awiri.

“BWENZI LANGA ABULAHAMU”

3, 4. Pa nkhani yokhala pa ubwenzi ndi Yehova, kodi Abulahamu anasiyana bwanji ndi Aisiraeli?

3 Yehova anatchula kholo la Aisiraeli kuti “bwenzi langa  Abulahamu.” (Yes. 41:8) Lemba la 2 Mbiri 20:7 limasonyezanso kuti Abulahamu anali bwenzi la Mulungu. Kodi Abulahamu anatani kuti akhalebe pa ubwenzi wabwino ndi Mlengi wake? Iye anali ndi chikhulupiriro.—Gen. 15:6; werengani Yakobo 2:21-23.

4 Poyamba, Yehova analinso Atate ndiponso Bwenzi la ana a Abulahamu, omwe anadzakhala mtundu wa Isiraeli. Koma n’zomvetsa chisoni kuti ubwenziwu unasokonekera. Izi zinachitika chifukwa chakuti Aisiraeliwo anasiya kukhulupirira malonjezo a Yehova.

5, 6. (a) Kodi munatani kuti muyambe kukhala pa ubwenzi ndi Yehova? (b) Kodi tingachite bwino kudzifunsa mafunso ati?

5 Mukamaphunzira zambiri zokhudza Yehova, chikhulupiriro chanu chimalimba komanso mumayamba kumukonda kwambiri. Ganizirani zimene zinachitika kuti mukhale pa ubwenzi ndi Mulungu. Choyamba, munazindikira kuti Mulungu ndi Munthu weniweni amene mukhoza kukhala naye pa ubwenzi wabwino. Munaphunziranso kuti tonsefe timabadwa ndi uchimo chifukwa cha kusamvera kwa Adamu. Munazindikiranso kuti anthu m’dzikoli ndi otalikirana ndi Mulungu. (Akol. 1:21) Kenako munazindikira kuti Atate wathu wakumwamba sali kutali ndi ife koma amatikonda ndiponso kutiganizira. Mutaphunzira za nsembe ya dipo ya Yesu n’kumaikhulupirira, munayamba kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu.

6 Panopa tonsefe tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ubwenzi wanga ndi Mulungu ukulimba? Kodi tsiku lililonse ndimasonyeza kuti ndimadalira, kukhulupirira ndiponso kukonda Yehova kuposa kale?’ Munthu wina wakale amene anali pa ubwenzi wolimba ndi Yehova anali Gidiyoni. Tiyeni tikambirane tsopano chitsanzo chake ndi kuona zimene tikuphunzirapo.

“YEHOVA NDI MTENDERE”

7-9. (a) Kodi n’chiyani chinachitikira Gidiyoni, ndipo zotsatira zake zinali zotani? (Onani chithunzi patsamba 21.) (b) Kodi tingatani kuti tikhale pa ubwenzi ndi Yehova?

7 Gidiyoni amene anali woweruza, anatumikira Yehova m’nthawi yovuta kwambiri mtundu wa Isiraeli utalowa m’Dziko Lolonjezedwa. Chaputala 6 cha buku la Oweruza chimanena kuti mngelo wa Yehova anakumana ndi Gidiyoni ku Ofira. Pa nthawiyo, Amidiyani amene ankakhala pafupi ndi Aisiraeli ankawavutitsa. N’chifukwa chake Gidiyoni sankapunthira tirigu poonekera, koma moponderamo mphesa kuti asavutike kumubisa. Iye anadabwa mngelo atamuonekera n’kumunena kuti “munthu wolimba mtima ndi wamphamvuwe.” Ndiyeno Gidiyoni anafunsa ngati Yehova, amene anapulumutsa Aisiraeli ku Iguputo, angawathandizedi pa nthawiyi. Mngelo amene ankaimira Mlengi, anamutsimikizira kuti Yehova amuthandiza.

8 Gidiyoni ankakayikira kuti angathe ‘kupulumutsa Isiraeli m’manja mwa Amidiyani.’ Ndiyeno Yehova anamuuza mosapita m’mbali kuti: “Popeza ndidzakhala ndi iwe, udzaphadi Amidiyani ngati kuti ukupha munthu mmodzi.” (Ower. 6:11-16) Koma Gidiyoni ankafuna umboni wotsimikizira zimenezi, choncho anapempha Yehova kuti amupatse chizindikiro. M’nkhaniyi, n’zoonekeratu kuti Gidiyoni ankaona kuti Yehova ndi Munthu weniweni.

9 Zimene zinachitika pambuyo pake zinalimbitsa chikhulupiriro cha Gidiyoni ndiponso ubwenzi wake ndi Mulungu. Iye anaphikira mngeloyo chakudya ndipo mngeloyo anakhudza chakudyacho ndi ndodo yake n’kuchipsereza mozizwitsa. Izi zinathandiza Gidiyoni kudziwa kuti mngeloyo anatumidwadi ndi Yehova. Iye anachita mantha, ndipo ananena kuti: “Kalanga ine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa! Ndaonana ndi mngelo wa Yehova maso ndi maso.” (Ower. 6:17-22) Kodi zimenezi zinasokoneza ubwenzi wa Gidiyoni ndi Mulungu wake? Ayi, koma zinamuthandiza kuti am’dziwe bwino Yehova n’kumamasuka naye. Tikudziwa zimenezi chifukwa cha dzina lakuti “Yehova-salomu,” limene Gidiyoni anapatsa guwa lansembe limene anamanga pamalowo. Dzinali limatanthauza kuti “Yehova Ndi Mtendere.” (Werengani Oweruza  6:23, 24; mawu a m’munsi) Nafenso tikamaganizira mozama zimene Yehova akutichitira tsiku ndi tsiku, timaona kuti iye ndi Mnzathu weniweni. Tikamapemphera pafupipafupi, timakhala ndi mtendere mumtima ndipo ubwenzi wathu ndi Mulungu umalimba.

NDANI ANGAKHALE ‘MLENDO M’CHIHEMA CHA YEHOVA’?

10. Malinga ndi Salimo 15:3, 5, kodi Yehova amafuna kuti tizichita chiyani ngati tikufuna kuti akhale mnzathu?

10 Koma pali zinthu zina zimene tiyenera kuchita kuti Yehova akhale Mnzathu weniweni. Nyimbo ya Davide pa Salimo 15 imasonyeza zimene tiyenera kuchita kuti tikhale ‘mlendo m’chihema cha Yehova,’ kapena kuti bwenzi lake. (Sal. 15:1) Tiyeni tikambirane zinthu ziwiri zimene tiyenera kuchita. Tiyenera kupewa miseche komanso tiyenera kuchita zinthu moona mtima nthawi zonse. Pa mfundo ziwirizi, David ananena kuti munthu amene angakhale mlendo m’chihema cha Yehova “sanena miseche ndi lilime lake. . . . Ndipo salandira chiphuphu kuti akhotetse mlandu wa munthu wosalakwa.”—Sal. 15:3, 5.

11. N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa miseche?

11 Mu salimo lina, Davide ananena kuti: “Tetezani lilime lanu ku zinthu zoipa.” (Sal. 34:13) Munthu akalephera kutsatira malangizo amenewa, amasokoneza ubwenzi wake ndi Atate wathu wakumwamba yemwe ndi wolungama. Tisaiwale kuti miseche ndi khalidwe la Satana, yemwe ndi mdani wamkulu wa Yehova. Ndipo dzina lakuti “Mdyerekezi” linamasuliridwa ku mawu achigiriki amene amatanthauza “woneneza.” Choncho kuti tikhalebe pa ubwenzi ndi Yehova, tiyenera kusamala kwambiri polankhula za anthu ena. Tiziyesetsa kuchita zimenezi makamaka ponena za oyang’anira mumpingo.—Werengani Aheberi 13:17; Yuda 8.

12, 13. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zinthu zonse moona mtima? (b) Kodi chimachitika n’chiyani tikakhala oona mtima?

12 Atumiki a Yehova amadziwika ndi kuchita zinthu moona mtima osati kudyera ena masuku pamutu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pitirizani kutipempherera, pakuti tikukhulupirira kuti tili ndi chikumbumtima choona, popeza tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.” (Aheb. 13:18) Akhristufe timafunitsitsa “kuchita zinthu zonse moona mtima,” choncho timapeweratu kulima Akhristu anzathu pamsana. Mwachitsanzo, ngati talemba ntchito abale athu timawachitira zinthu mwachilungamo komanso kuwapatsa malipiro amene tinagwirizana. Timayesetsa kuchita zinthu moona mtima ndi anthu amene akutigwirira ntchito komanso anthu ena onse. Tikalembedwanso ntchito ndi Mkhristu mnzathu, timapewa mtima wofuna kuti azitichitira zinthu zina mwapadera.

13 Anthu ambiri m’dzikoli amayamikira Mboni za Yehova. Mwachitsanzo, bwana wa kampani ina yaikulu ya zomangamanga anaona kuti a Mboni za Yehova akanena zinthu zimakhala zomwezo. Iye anati: “A Mboninu nthawi zonse tikapangana zinthu, simusintha.” (Sal. 15:4) Kuchita zinthu moona mtima kumathandiza kuti tikhalebe pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Zimathandizanso kuti Atate wathu wakumwamba atamandidwe.

THANDIZANI ENA KUTI AKHALE MABWENZI A YEHOVA

Timathandiza anthu ena kukhala mabwenzi a Yehova (Onani ndime 14, 15)

14, 15. Kodi mu utumiki tingathandize bwanji anthu kuti akhale mabwenzi a Yehova?

14 Anthu ambiri amene timakumana nawo mu utumiki amakhulupirira zoti kuli Mulungu koma samuona ngati Mnzawo weniweni. Kodi tingawathandize bwanji? Tiyeni tiganizire malangizo amene Yesu anapatsa ophunzira ake 70 amene anawatumiza awiriawiri kuti akalalikire. Iye anati: “Mukafika panyumba, choyamba muzinena kuti, ‘Mtendere ukhale panyumba pano.’ Ndipo ngati pakhomopo pali munthu wokonda mtendere, mtendere wanu udzakhala pa iye. Koma ngati palibe, udzabwerera kwa inu.” (Luka 10:5, 6) Tikamalankhula ndi anthu mokoma  mtima, iwo angafune kumvetsera uthenga wathu. Zimenezi zingathandizenso kuti anthu otsutsa asamadane nafe ndiponso kuti adzamvetsere pa nthawi ina.

15 Timalankhulabe mwamtendere ndiponso mokoma mtima kwa anthu amene amakhulupirira kwambiri chipembedzo chonyenga kapena amene amatsatira miyambo yosemphana ndi Malemba. Timalandiranso bwino anthu amene afika ku misonkhano yathu. N’kutheka kuti anthuwa sakusangalala ndi zimene zikuchitika m’dzikoli ndipo akufunitsitsa kuphunzira za Mulungu wathu. M’nkhani zakuti “Baibulo Limasintha Anthu” muli zitsanzo zambiri za anthu oterewa.

TIMAGWIRA NTCHITO LIMODZI NDI MNZATHU WENIWENI

16. Kodi tingatani kuti tikhale mabwenzi a Yehova komanso “antchito anzake”?

16 Kawirikawiri, anthu amene amagwira ntchito limodzi amagwirizana kwambiri. Atumiki onse amene anadzipereka kwa Yehova ali ndi mwayi wokhala mabwenzi ake komanso “antchito anzake.” (Werengani 1 Akorinto 3:9.) Tikamalalikira ndi kuphunzitsa anthu Baibulo, timamvetsa bwino kwambiri makhalidwe osangalatsa a Atate wathu wakumwamba. Timaona mmene mzimu wake woyera umatithandizira kuti tizigwira bwino ntchito yolalikira uthenga wabwino.

17. Kodi chakudya chauzimu chimene timalandira pa misonkhano ikuluikulu chimasonyeza bwanji kuti Yehova ndi Mnzathu?

17 Tikamachita zambiri pa ntchito yolalikira, timalimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Mwachitsanzo, timaona zimene iye amachita polepheretsa zolinga za anthu otsutsa. M’zaka zapitazi, taonanso bwino zimene Mulungu akuchita potitsogolera. Akutipatsa chakudya chauzimu chamwanaalirenji. Misonkhano ikuluikulu imasonyeza kuti Atate wathu ndi wachikondi ndipo amadziwa mavuto athu ndi zofuna zathu. Banja lina linalemba kalata yoyamikira msonkhano wina. Iwo analemba kuti: “Msonkhanowu watilimbikitsa kwabasi. Taona kuti Yehova amatikonda kwambiri, aliyense payekha, ndipo amafuna kuti zinthu zitiyendere bwino.” Banja lina lochokera ku Germany litapita ku msonkhano wachigawo wapadera ku Ireland, linayamikira kuti abale kumeneko anawalandira ndi kuwasamalira bwino. Iwo ananenanso kuti: “Koma tikuthokoza kwambiri Yehova ndi Mfumu yathu Yesu Khristu. Iwo atiitana kuti tikhale m’gulu logwirizana kwambiri padziko lonse. Sikuti timangonena kuti ndife ogwirizana, koma tsiku ndi tsiku timasangalala ndi mgwirizano umenewu. Zimene taona pa msonkhano wachigawo wapadera umenewu, zidzatithandiza kuti nthawi zonse tizikumbukira mwayi wapadera umene tili nawo wotumikira Mulungu wathu wamkulu limodzi ndi abale athu.”

 ANTHU AMENE AMAGWIRIZANA AMALANKHULANA

18. Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati pa nkhani yolankhulana ndi Yehova?

18 Anthu amagwirizana kwambiri ngati amalankhulana. Masiku ano, anthu amakonda kutumizirana mameseji kapena kucheza pa Intaneti. Ndiyeno funso ndi lakuti, Kodi ifeyo timakondanso kulankhulana ndi Yehova, yemwe ndi Mnzathu weniweni? N’zoona kuti iye ndi “Wakumva pemphero.” (Sal. 65:2) Koma kodi ifeyo timalankhula naye pafupipafupi?

19. Kodi pali thandizo liti ngati timasowa chonena pofotokozera Atate wathu wakumwamba mmene tikumvera mumtima?

19 Atumiki ena a Mulungu zimawavuta kufotokoza maganizo awo kapena mmene akumvera mumtima mwawo. Komatu Yehova amafuna kuti tizifotokoza zimenezi tikamapemphera. (Sal. 119:145; Maliro 3:41) Koma ngati tikusowa chonena m’pemphero sitiyenera kuda nkhawa chifukwa thandizo lilipo. Paulo anauza Akhristu a ku Roma kuti: “Pakuti chimene tiyenera kupempherera monga mmene tiyenera kupemphera sitikuchidziwa, koma mzimu umachonderera m’malo mwathu ndi madandaulo amene sitinathe kuwafotokoza. Koma iye amene amasanthula mitima amadziwa zimene mzimu ukutanthauza, chifukwa umachonderera m’malo mwa oyera mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.” (Aroma 8:26, 27) Kuganizira mawu a m’mabuku a m’Baibulo monga Yobu, Masalimo ndi Miyambo kungatithandize kuti tizipeza zonena pofotokozera Yehova mmene tikumvera mumtima mwathu.

20, 21. Kodi mawu a Paulo pa Afilipi 4:6, 7 ndi olimbikitsa bwanji?

20 Ngati vuto linalake likutisowetsa mtendere, tiyenera kutsatira malangizo amene Paulo anauza Afilipi. Iye anati: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.” Tikafotokoza mavuto athu kwa Yehova, yemwe ndi Mnzathu weniweni, timayamba kumva bwino mumtima. Tikutero chifukwa chakuti Paulo anapitiriza kuti: “Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.” (Afil. 4:6, 7) Choncho tiyeni tizipemphera nthawi zonse kuti “mtendere wa Mulungu” uziteteza mitima yathu ndi maganizo athu.

Kodi pemphero limathandiza bwanji kuti tikhalebe pa ubwenzi ndi Mulungu?(Onani ndime 21)

21 Kupemphera kumatithandiza kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. Choncho tiyeni ‘tizipemphera mosalekeza.’ (1 Ates. 5:17) Zimene taphunzira m’nkhani ino ziyenera kutithandiza kulimbitsa kwambiri ubwenzi wathu ndi Mulungu komanso kukhala ndi mtima wofuna kutsatira mfundo zake zolungama. Tiyeninso tizipeza nthawi yoganizira madalitso amene tili nawo chifukwa chakuti Yehova ndi Atate wathu, Mulungu wathu komanso Mnzathu weniweni.