Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsanzirani Chikhulupiriro cha Mose

Tsanzirani Chikhulupiriro cha Mose

“Mwa chikhulupiriro, Mose atakula anakana kutchedwa mwana wa mwana wamkazi wa Farao.”—AHEB. 11:24.

1, 2. (a) Kodi Mose ali ndi zaka 40 anasankha kuchita chiyani? (Onani chithunzi pamwambapa.) (b) N’chifukwa chiyani Mose anasankha kuvutikira limodzi ndi anthu a Mulungu?

MOSE analeredwa m’banja lachifumu ndipo ankadziwa zinthu zabwino zimene zinali ku Iguputo. Iye ankaona nyumba zikuluzikulu za anthu olemera komanso “anaphunzira nzeru zonse za Aiguputo” monga luso losiyanasiyana, masamu ndi maphunziro ena a sayansi. (Mac. 7:22) Iye akanatha kukhala ndi chuma, udindo komanso zinthu zina zimene Aiguputo ena sakanazipeza.

2 Koma ali ndi zaka 40, Mose anachita zinthu zimene zinadabwitsa kwambiri banja lachifumu limene linkamulera. Iye anasankha kuchoka m’banja lachifumu. Kodi anangokhala ngati munthu wamba wa ku Iguputo? Ayi. Iye anasankha kukhala ndi anthu a mtundu wake amene anali akapolo. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Mose anali ndi chikhulupiriro. (Werengani Aheberi 11:24-26.) Chifukwa cha chikhulupiriro, Mose sankangoona zinthu zooneka. Iye ankakhulupirira Yehova “Wosaonekayo” ndipo ankadziwa kuti malonjezo ake onse adzakwaniritsidwa.—Aheb. 11:27.

3. Kodi tikambirana mafunso ati m’nkhaniyi?

3 Ifenso tisamangoona zinthu zooneka koma tiyenera kukhala “ndi chikhulupiriro.” (Aheb. 10:38, 39) Kukambirana nkhani ya Mose, yomwe ili pa Aheberi 11:24-26, kungalimbitse chikhulupiriro chathu. Tikamakambirana nkhaniyi, tipeza mayankho a mafunso otsatirawa:  Kodi chikhulupiriro chinathandiza bwanji Mose kukana zilakolako za thupi? Pamene ankanyozedwa, kodi chikhulupiriro chinamuthandiza bwanji kuyamikira mwayi wautumiki umene anali nawo? Nanga n’chifukwa chiyani ankayang’anitsitsa “pamphoto imene adzalandire”?

ANAKANA ZILAKOLAKO ZA THUPI

4. Kodi Mose anazindikira chiyani zokhudza ‘zosangalatsa zauchimo’?

4 Chifukwa cha chikhulupiriro, Mose anazindikira kuti ‘zinthu zosangalatsa zauchimo’ ndi zosakhalitsa. Koma anthu ena akanatha kuganiza kuti ngakhale kuti Aiguputo ankalambira mafano komanso kukhulupirira mizimu, ulamuliro wawo unali wamphamvu padziko lonse pamene anthu a Mulungu anali akapolo. Koma Mose ankadziwa kuti Mulungu angasinthe zinthu. Ngakhale kuti anthu ochita zofuna zawo ankaoneka kuti zinthu zikuwayendera, Mose ankadziwa kuti anthu oipa alibe tsogolo. Choncho iye sanakopeke ndi “zinthu zosangalatsa koma zosakhalitsa zauchimo.”

5. N’chiyani chingatithandize kukana “zinthu zosangalatsa koma zosakhalitsa zauchimo”?

5 Kodi mungakane bwanji “zinthu zosangalatsa koma zosakhalitsa zauchimo”? Musaiwale kuti zosangalatsa zauchimo ndi zakanthawi. Chikhulupiriro chanu chingakuthandizeni kuona kuti “dziko likupita limodzi ndi chilakolako chake.” (1 Yoh. 2:15-17) Muziganizira zimene zidzachitikire anthu osalapa. Iwo ali “pamalo oterera . . . kuti awonongeke.” (Sal. 73:18, 19) Tikamayesedwa kuti tichite zoipa, tiyenera kudzifunsa kuti, ‘kodi ndikufuna kuti tsogolo langa lidzakhale lotani?’

6. (a) N’chifukwa chiyani Mose anakana “kutchedwa mwana wa mwana wamkazi wa Farao”? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Mose anasankha bwino?

6 Chikhulupiriro chimene Mose anali nacho chinamuthandizanso posankha zochita pa moyo wake. Baibulo limati: “Mwa chikhulupiriro, Mose atakula anakana kutchedwa mwana wa mwana wamkazi wa Farao.” (Aheb. 11:24) Mose sanaganize kuti angathe kutumikira Mulungu kunyumba yachifumu komweko ndi kumagwiritsa ntchito chuma chake komanso udindo womwe akanakhala nawo kuthandiza Aisiraeli anzake. M’malomwake, Mose ankakonda Yehova ndi mtima wake wonse, moyo wake wonse, ndi mphamvu zake zonse. (Deut. 6:5) Zimene Mose anasankhazi zinamuthandiza kupewa mavuto aakulu. Chuma chambiri cha Aiguputo chimene Mose anachisiya chinadzatengedwa ndi Aisiraeli. (Eks. 12:35, 36) Farao anachititsidwa manyazi kenako anaphedwa. (Sal. 136:15) Koma Mose sanaphedwe ndipo Mulungu anamugwiritsa ntchito kutsogolera anthu ake kuti atuluke mu Iguputo. Iye anachita zaphindu pa moyo wake.

7. (a) Malinga ndi lemba la Mateyu 6:19-21, n’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira za m’tsogolo osati za moyo uno wokha? (b) Fotokozani zimene mlongo wina anachita, zomwe zikusonyeza kusiyana kwa zinthu zakuthupi ndi chuma chauzimu.

7 Ngati ndinu mtumiki wa Yehova wachinyamata, kodi chikhulupiriro chingakuthandizeni bwanji posankha ntchito? Mungachite bwino kuganizira zimene mukufuna kudzachita m’tsogolo. Kukhulupirira malonjezo a Mulungu n’kumene kungakuthandizeni kuti musunge chuma chosawonongeka osati chakanthawi. (Werengani Mateyu 6:19-21.) Mtsikana wina dzina lake Sophie anali katswiri wovina ndipo anafunika kusankha zochita pa moyo wake. Anali ndi mwayi wolipiriridwa sukulu ndiponso wogwira ntchito yapamwamba m’magulu a zovinavina ku United States. Iye anati: “Ndinkasangalala anthu akamandichemerera. Ndinkaona kuti palibenso angandipose. Koma mumtimamu sindinkamva bwino.” Kenako Sophie anaonera vidiyo ina ya achinyamata. (Young People Ask—What Will I Do With My Life?) Iye anati: “Ndinazindikira kuti ndinasinthanitsa kutumikira Yehova mokhulupirika ndi kutchuka m’dzikoli. Nditapemphera kuchokera pansi pa mtima ndinasiya zovinazo.” Kodi iye amamva bwanji ndi zimene anasankhazi? Iye ananena kuti: “Sindimasiriranso zimene ndinkachita poyamba. Panopa ndine wosangalala kwambiri ndipo ndikuchita upainiya limodzi  ndi mwamuna wanga. Si ife otchuka ndiponso si ife olemera. Koma sindimanong’oneza bondo ngakhale pang’ono chifukwa tikutumikira Yehova. Tilinso ndi anthu omwe timaphunzira nawo Baibulo komanso tili ndi zolinga zauzimu.”

8. Kodi ndi malangizo ati a m’Baibulo omwe angathandize wachinyamata kusankha zochita pa moyo wake?

8 Yehova amadziwa zimene zingatithandize. Mose anati: “Kodi Yehova Mulungu wanu akufuna kuti muzichita chiyani, koposa kuopa Yehova Mulungu wanu kuti muziyenda m’njira zake zonse, kukonda ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, kuti muzisunga malamulo a Yehova ndi mfundo zake zimene ndikukupatsani lero, kuti zinthu zikuyendereni bwino?” (Deut. 10:12, 13) Ngati ndinu wachinyamata, sankhani ntchito imene ingakuthandizeni kukonda Yehova ndiponso kumutumikira ndi “mtima wanu wonse.” Mukatero ‘zinthu zidzakuyenderani bwino.’

ANKAONA KUTI UTUMIKI WAKE NDI WOFUNIKA KWAMBIRI

9. N’chifukwa chiyani mwina Mose anavutika kuti avomere utumiki umene anapatsidwa?

9 Mose ankaona “kutonzedwa kwake monga Wodzozedwa kukhala chuma chochuluka kuposa chuma cha Iguputo.” (Aheb. 11:26) Mose anali “Wodzozedwa” chifukwa chakuti anasankhidwa ndi Mulungu kuti atsogolere Aisiraeli potuluka mu Iguputo. Iye ankadziwa kuti utumiki umenewu ukhala wovuta komanso anthu ena ‘azimutonza.’ Pa nthawi ina, Mwisiraeli wina anamutonza kuti: “Anakuika iwe ndani kukhala kalonga ndi woweruza wathu?” (Eks. 2:13, 14) Nayenso Moseyo pa nthawi ina anafunsa Yehova kuti: “Farao akandimvera bwanji?” (Eks. 6:12) Kuti alimbe mtima, Mose anafotokozera Yehova zonse zimene zinkamuchititsa mantha komanso zimene zinkamudetsa nkhawa. Kodi Yehova anamuthandiza bwanji?

10. Kodi Yehova anathandiza bwanji Mose kuti akwanitse utumiki umene anamupatsa?

10 Choyamba, Yehova anauza Mose kuti: “Ndidzakhala nawe.” (Eks. 3:12) Chachiwiri, Yehova anamufotokozera tanthauzo la dzina lake. Anati: “Ndidzakhala amene ndidzafune kukhala.” * (Eks. 3:14) Chachitatu, Mulungu anapatsa Mose mphamvu yoti azichita zozizwitsa potsimikizira kuti watumidwadi ndi Mulungu. (Eks. 4:2-5) Chachinayi, Yehova anasankha Aroni kuti aziyenda ndi Mose komanso azimulankhulira pogwira ntchitoyi. (Eks. 4:14-16) Chakumapeto kwa moyo wake, Mose anatsimikizira kuti Yehova amathandiza atumiki ake kuti akwanitse utumiki uliwonse umene wawapatsa. N’chifukwa chake anauza Yoswa kuti: “Yehova ndi amene akuyenda patsogolo panu. Iye adzapitiriza kuyenda nanu. Sadzakutayani kapena kukusiyani ngakhale pang’ono. Choncho musaope kapena kuchita mantha.”—Deut. 31:8.

11. N’chifukwa chiyani Mose ankaona kuti utumiki wake ndi wofunika kwambiri?

11 Yehova anathandiza Mose kuona kuti utumiki wake ndi wofunika kwambiri. Ankaona kuti utumikiwo uli ngati “chuma chochuluka kuposa chuma cha Iguputo.” Ndipotu kutumikira Farao kunalibe phindu lililonse tikakuyerekezera ndi kutumikira Mulungu Wamphamvuyonse. N’chimodzimodzinso ndi kukhala kalonga wa Iguputo tikakuyerekezera ndi kukhala “wodzozedwa” wa Yehova. Mose anadalitsidwa chifukwa choona kuti utumiki wake ndi wofunika kwambiri. Yehova anali mnzake weniweni ndipo anam’patsa mphamvu zochita “zinthu zazikulu ndi zoopsa” pamene ankatsogolera Aisiraeli kupita m’Dziko Lolonjezedwa.—Deut. 34:10-12.

12. Kodi Yehova watipatsa utumiki uti umene tiyenera kuuona kuti ndi wofunika kwambiri?

12 Ifenso Yehova watipatsa utumiki kudzera mwa Mwana wake, ngati mmene anachitira ndi mtumwi Paulo ndi ena. (Werengani 1 Timoteyo 1:12-14.) Tonsefe tapatsidwa ntchito yolengeza uthenga wabwino. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Ena akuchita utumiki wa nthawi zonse. Abale ena  obatizidwa akutumikira monga akulu komanso atumiki othandiza mumpingo. Koma achibale anu omwe si Mboni komanso anthu ena angaone ngati kuchita utumiki umenewu n’kungotaya nthawi kapena angakunyozeni chifukwa cha mtima wanu wodzipereka. (Mat. 10:34-37) Zimenezi zingachititse kuti muyambe kuona utumiki wanu ngati wosathandiza kapena kuona kuti simungaukwanitse. Kodi chikhulupiriro chingakuthandizeni bwanji ngati zimenezi zitakuchitikirani?

13. Kodi Yehova amatithandiza bwanji kuti tikwanitse utumiki wathu?

13 Muzipemphera kwa Yehova ndipo muzikhulupirira kuti akuthandizani. Muuzeni zinthu zonse zimene zikukudetsani nkhawa. Pajatu Yehova ndi amene wakupatsani utumikiwo, ndipo mofanana ndi Mose adzakuthandizani kuti muukwanitse. Choyamba, Yehova akukutsimikizirani kuti: “Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza. Ndikugwira mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lachilungamo.” (Yes. 41:10) Chachiwiri, akukukumbutsani kuti malonjezo ake ndi odalirika. Iye akuti: “Ineyo ndalankhula ndipo ndidzazichita. Ndakonza zimenezi ndipo ndidzazichitadi.” (Yes. 46:11) Chachitatu, Yehova adzakupatsani “mphamvu yoposa yachibadwa” kuti mukwanitse utumiki wanu. (2 Akor. 4:7) Chachinayi, Yehova wakupatsani abale ndi alongo padziko lonse kuti akuthandizeni kupirira pamene mukuchita utumiki wanu. Abale ndi alongo amenewa ‘adzakutonthozani ndi kukulimbikitsani.’ (1 Ates. 5:11) Mukaona mmene Yehova akukuthandizirani kuti mukwanitse utumiki wanu, mudzayamba kumukhulupirira kwambiri ndipo utumiki wanu mudzauona kuti ndi wofunika kuposa chilichonse m’dzikoli.

“ANAYANG’ANITSITSA PAMPHOTO IMENE ADZALANDIRE”

14. N’chifukwa chiyani Mose sankakayikira zoti adzalandira mphoto?

14 Mose ‘ankayang’anitsitsa pamphoto imene adzalandire.’ (Aheb. 11:26) Iye ankachita zinthu moganizira za m’tsogolo ngakhale kuti sankadziwa zonse. Mofanana ndi Abulahamu, Mose ankadziwa kuti Mulungu akhoza kuukitsa akufa. (Luka 20:37, 38; Aheb. 11:17-19) Chifukwa choganizira mphoto imene adzalandire, Mose sankaona ngati wangotaya nthawi kukhala zaka 40 ku Midiyani komanso zaka zina 40 m’chipululu. N’zoona kuti sankadziwa zonse zimene Mulungu adzachite pokwaniritsa malonjezo ake koma chikhulupiriro chinamuthandiza kuti athe kuona zosaonekazo.

15, 16. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira kwambiri mphoto imene tidzalandire? (b) Kodi ndi zinthu ziti zimene inuyo mukuyembekezera mwachidwi m’dziko latsopano?

 15 Kodi inunso ‘mumayang’anitsitsa pamphoto imene mudzalandire’? Ifenso sitidziwa zonse zimene Mulungu adzachite pokwaniritsa malonjezo ake. Mwachitsanzo, sitidziwa “nthawi yoikidwiratu” ya chisautso chachikulu. (Maliko 13:32, 33) Koma tikayerekezera ndi Mose, ifeyo tikudziwa zambiri za Paradaiso. N’zoona kuti pali zinthu zina zimene sitikudziwa zomwe Yehova walonjeza kuti zidzachitika mu Ufumu wake. Koma ‘timaziyang’anitsitsa’ kapena kuti kuziyembekezera mwachidwi. Kuona m’maganizo mwathu zimene zidzachitike m’dziko latsopano kungatithandize kuti tizifunafuna Ufumu choyamba. N’chifukwa chiyani tikutero? Tiyerekeze chonchi: Kodi inuyo mungagule nyumba yomwe simukuidziwa bwinobwino? Mwina mwayankha kale kuti ayi. N’chimodzimodzi ndi zimene tikuyembekezera. Sitingapereke moyo wathu wonse kuchita zinthu zokhudza Ufumu ngati sitikuudziwa bwinobwino. Tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro n’kumaona m’maganizo mwathu mmene moyo udzakhalire mu Ufumuwo.

Tidzasangalala kwambiri kucheza ndi anthu okhulupirika monga Mose (Onani ndime 16)

16 Ndiyeno kuti mukhale ndi chithunzi chabwino, muyenera kuganizira kwambiri mmene moyo wanu udzakhalire m’Paradaiso. Mukamawerenga nkhani za anthu ena m’Baibulo, muziganizira mafunso amene mungadzawafunse akadzaukitsidwa. Muziganiziranso mafunso amene angadzakufunseni okhudza zimene zikuchitika m’masiku otsiriza ano. Muziyerekezera mutakumana ndi azigogo anu akalekale ndipo mukuwaphunzitsa zonse zimene Mulungu wawachitira. Muziyerekezeranso mukuona zinyama zina zimene panopa simungaziyandikire zikukhala mwamtendere ndipo inuyo mukuyamba kuzidziwa bwinobwino. Ganiziraninso mmene ubwenzi wanu ndi Yehova udzakhalira mukadzayamba kukhala angwiro.

17. Kodi kuganizira mphoto imene tidzalandire kungatithandize bwanji?

17 Kuganizira mphoto imene tidzalandire kungatithandize kuti tisafooke, tizikhala osangalala komanso kuti tizisankha zinthu moganizira zam’tsogolozo. Paulo analembera Akhristu odzozedwa kuti: “Ngati tikuyembekezera chimene sitikuchiona, timachidikirabe mopirira.” (Aroma 8:25) Mfundo imeneyi imagwiranso ntchito kwa Akhristu amene akuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha padzikoli. Panopa sitinalandire mphoto yathu koma chikhulupiriro chimatithandiza kuti tiziyembekezera moleza mtima ‘mphoto imene tidzalandireyo.’ Mofanana ndi Mose, sitiona kuti tangotaya nthawi yathu pa zaka zonse zimene tatumikira Yehova. Timadziwa kuti “zooneka n’zakanthawi, koma zosaoneka n’zamuyaya.”—Werengani 2 Akorinto 4:16-18.

18, 19. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita khama kuti chikhulupiriro chathu chisachepe? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

18 Chikhulupiriro chimatithandiza kuti tiziona “umboni wooneka wa zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.” (Aheb. 11:1) Munthu amene amangoganizira zam’dzikoli saona ubwino wotumikira Yehova. Munthu wotereyu amaona kuti zinthu zokhudza kutumikira Mulungu ndi “zopusa.” (1 Akor. 2:14) Anthu m’dzikoli saona m’maganizo mwawo zinthu zimene tikuyembekezera monga moyo wosatha komanso kuuka kwa akufa. Iwo ali ngati anthu ena amene ankaonedwa kuti ndi anzeru nthawi ya Paulo, omwe ankati Pauloyo ndi “wobwetuka.” Masiku anonso anthu ambiri amangoona kuti zimene timalalikira ndi zoduka mutu.—Mac. 17:18.

19 Popeza anthu ambiri m’dzikoli ndi opanda chikhulupiriro, tiyenera kuchita khama kuti chikhulupiriro chathu chisachepe. Tiyeni tizichonderera Yehova kuti ‘chikhulupiriro chathu chisathe.’ (Luka 22:32) Tiziganizira ubwino wotumikira Yehova komanso mavuto amene angabwere ngati titachita tchimo. Tiziganiziranso chiyembekezo cha moyo wosatha chimene tili nacho. Komatu chikhulupiriro chinathandiza Mose kuonanso zina. M’nkhani yotsatira tidzaona mmene chikhulupiriro chinamuthandizira kuti azikhala ngati “akuona Wosaonekayo.”—Aheb. 11:27.

^ ndime 10 Pofotokoza mawu a Mulungu a pa Ekisodo 3:14, katswiri wina analemba kuti: “Palibe chimene chingamulepheretse kuchita zimene akufuna . . . Dzina limeneli [lakuti Yehova] linali ngati mpanda wolimba wa Aisiraeli ndipo likanawathandiza kukhala ndi chiyembekezo komanso kuti asamade nkhawa.”