Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Ndi Mulungu Wadongosolo

Yehova Ndi Mulungu Wadongosolo

“Mulungu si Mulungu wachisokonezo, koma wamtendere.”—1 AKOR. 14:33.

1, 2. (a) Kodi Mulungu anayambirira kulenga ndani, nanga anamugwiritsa ntchito bwanji? (b) N’chiyani chikusonyeza kuti angelo amachita zinthu mwadongosolo?

YEHOVA, yemwe analenga zinthu zonse, amachita zinthu mwadongosolo. Iye anayamba ndi kulenga Mwana wake wobadwa yekha. Mwanayo amatchedwa “Mawu” chifukwa ndi amene Mulungu amamugwiritsa ntchito ngati womulankhulira. Iye wakhala akutumikira Yehova kwa zaka zambirimbiri. N’chifukwa chake Baibulo limafotokoza kuti: “Pa chiyambi, panali wina wotchedwa Mawu, ndipo Mawuyo anali ndi Mulungu.” Limanenanso kuti: “Zinthu zonse zinakhalako kudzera mwa iye [Mawuyo], ndipo palibe chinthu ngakhale chimodzi chimene chinakhalapo popanda iyeyo.” Zaka zoposa 2,000 zapitazo, Mulungu anatumiza Mawuyo padziko lapansi. Iye anakhala munthu wangwiro amene anachita chifuniro cha Atate wake mokhulupirika ndipo ankadziwika ndi dzina lakuti Yesu Khristu.—Yoh. 1:1-3, 14.

2 Asanabwere padziko lapansi, Mwanayu ankatumikira Mulungu mokhulupirika monga “mmisiri waluso.” (Miy. 8:30) Yehova anagwiritsanso ntchito Mwana wakeyu polenga angelo ambirimbiri. (Akol. 1:16) Ponena za  angelowa, Baibulo limati: “Panali atumiki okwana miliyoni imodzi amene anali kumutumikira [Yehova] nthawi zonse, ndi atumiki enanso mamiliyoni 100 amene anali kuimirira pamaso pake nthawi zonse.” (Dan. 7:10) Baibulo limasonyezanso kuti angelo a Mulungu ali ngati “makamu” a asilikali omwe amachita zinthu mwadongosolo kwambiri.—Sal. 103:21.

3. Kodi nyenyezi ndi mapulaneti zilipo zochuluka bwanji, nanga n’chiyani chikusonyeza kuti zinasanjidwa mwadongosolo?

3 Nanga bwanji zolengedwa zina monga nyenyezi zosawerengeka komanso mapulaneti? Ponena za nyenyezi, nyuzipepala ina inanena kuti kafukufuku amene asayansi apanga posachedwapa, wasonyeza kuti nyenyezi zilipo zambirimbiri moti nambala yake ndi 3 wotsatizana ndi maziro 23. Nambalayi ikuwirikiza katatu chiwerengero chimene asayansi anapeza poyamba. Nyenyezizi zili mu milalang’amba ndipo mlalang’amba uliwonse uli ndi nyenyezi mabiliyoni kapena mathililiyoni komanso mapulaneti ambiri. Milalang’ambayi imakhalanso mwadongosolo m’magulumagulu.

4. N’chifukwa chiyani tinganene kuti m’pomveka kuti atumiki a Mulungu padzikoli amachita zinthu mwadongosolo?

4 Mofanana ndi angelo, nyenyezi ndi mapulaneti zinalengedwa mwadongosolo. (Yes. 40:26) Choncho m’pomveka kunena kuti Mulungu amathandizanso atumiki ake padziko lapansi kuti azichita zinthu mwadongosolo. Iye amachita zimenezi chifukwa choti wawapatsa ntchito yofunika komanso yambiri yoti agwire. Mbiri ya atumiki a Mulungu akale komanso amasiku ano, imapereka umboni woti Mulungu wakhala akuwathandiza ndipo iye “si Mulungu wachisokonezo, koma wamtendere.”—Werengani 1 Akorinto 14:33, 40.

ANTHU A YEHOVA AKALE ANKACHITA ZINTHU MWADONGOSOLO

5. Kodi dongosolo loti anthu adzaze dziko lapansi linasokonekera bwanji?

5 Yehova atalenga anthu oyamba, anawauza kuti: “Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anire. Muyang’anirenso nsomba zam’nyanja ndi zolengedwa zouluka m’mlengalenga, komanso cholengedwa chilichonse chokwawa padziko lapansi.” (Gen. 1:28) Anthuwo anayenera kuchuluka n’kudzaza dziko lapansi mpaka dziko lonse litakhala paradaiso. Zonsezi zinayenera kuchitika mwadongosolo. Koma zinthu zinakhala ngati zasokonekera chifukwa Adamu ndi Hava sanamvere Mulungu. (Gen. 3:1-6) Patapita nthawi, “Yehova anaona kuti kuipa kwa anthu kwachuluka padziko lapansi, ndipo malingaliro onse a m’mitima ya anthu anali oipa okhaokha nthawi zonse.” Ndipo “dziko lapansi linali litaipa pamaso pa Mulungu woona, ndipo linadzaza ndi chiwawa.” Choncho Mulungu anakonza zoti awononge anthu onse oipa ndi chigumula.—Gen. 6:5, 11-13, 17.

6, 7. (a) N’chifukwa chiyani Nowa anayanjidwa ndi Mulungu? (Onani chithunzi patsamba 21.) (b) N’chiyani chinachitikira anthu onse oipa m’nthawi ya Nowa?

6 Koma “Nowa anayanjidwa ndi Yehova” chifukwa “anali munthu wolungama” ndipo “anali wopanda cholakwa pakati pa anthu a m’nthawi yake.” Popeza “Nowa anayenda ndi Mulungu woona,” Yehova anamuuza kuti apange chingalawa. (Gen. 6:8, 9, 14-16) Chingalawacho anachipanga m’njira yoti anthu ndi nyama apulumukiremo. Nowa ndi banja lake anagwira ntchitoyi mwadongosolo ndipo ‘anachita zonse motsatira zimene Yehova analamula.’ Atamaliza kulowetsa nyama m’chingalawamo, “Yehova anatseka chitseko.”—Gen. 7:5, 16.

7 Mu 2370 B.C.E, Yehova anabweretsa Chigumula ndipo “anaseseratu chamoyo chilichonse chimene chinali padziko lapansi,” koma anapulumutsa Nowa ndi banja lake chifukwa anali okhulupirika. (Gen. 7:23) Tonsefe ndi zidzukulu za banja la Nowa. Koma anthu onse amene sanamvere zimene Nowa ankalalikira anawonongedwa pa Chigumula.—2 Pet. 2:5.

Kuchita zinthu mwadongosolo kunathandiza anthu 8 kuti apulumuke Chigumula (Onani ndime 6 ndi 7)

8. N’chiyani chikusonyeza kuti Aisiraeli ankachita zinthu mwadongosolo?

8 Patapita zaka zoposa 800 pambuyo pa Chigumula,  Mulungu anakonza zoti Aisiraeli akhale mtundu wake. Anthuwo ankafunika kuchita zinthu mwadongosolo pa moyo wawo, makamaka pa nkhani zokhudza kulambira. Mwachitsanzo, panali ansembe ndi Alevi ambiri komanso akazi “amene anali kutumikira mwadongosolo pachipata cha chihema chokumanako.” (Eks. 38:8) Koma Yehova Mulungu atauza Aisiraeli kuti akalowe m’dziko la Kanani, anthuwo anakhala osakhulupirika. Choncho iye anawauza kuti: “Simudzalowa m’dziko limene ndinachita kukweza dzanja langa polumbira kuti ndidzakhala nanu mmenemo, kupatula Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni.” Anatero chifukwa chakuti anthu awiriwa atapita kukazonda Dziko Lolonjezedwa, anabwera ndi mawu olimbikitsa. (Num. 14:30, 37, 38) Kenako Mulungu anauza Mose kuti asankhe Yoswa kukhala wodzalowa m’malo mwake. (Num. 27:18-23) Yoswa atatsala pang’ono kulowetsa Aisiraeli m’dziko la Kanani, Mulungu anamuuza kuti: “Ukhale wolimba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu. Usachite mantha kapena kuopa, pakuti Yehova Mulungu wako ali nawe kulikonse kumene upiteko.”—Yos. 1:9.

9. Kodi Rahabi ankaona bwanji Yehova komanso Aisiraeli?

9 Yehova Mulungu anatsogolera Yoswa pa chilichonse chimene ankachita. Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinachitika Aisiraeli ali pafupi ndi mzinda wa Yeriko. Mu 1473 B.C.E., Yoswa anatuma amuna awiri kuti akazonde Yeriko ndipo amunawo anakumana ndi Rahabi yemwe anali wachiwerewere. Rahabi anabisa amunawo kudenga la nyumba yake pamene mfumu ya Yeriko inatumiza anthu kuti akawasakesake. Iye anauza amuna awiriwo kuti: “Ndikudziwa kuti Yehova akupatsani ndithu dziko lino. . . .  Tinamva za mmene Yehova anaphwetsera madzi a Nyanja Yofiira pamaso panu . . . Tinamvanso za mmene munaphera mafumu awiri a Aamori.” Iye anatinso: “Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wa kumwamba ndi padziko lapansi.” (Yos. 2:9-11) Pamene Aisiraeli ankawononga mzinda wa Yeriko, Mulungu anapulumutsa Rahabi ndi anthu a  m’banja lakechifukwa choti anagwirizana ndi gulu la Mulungu. (Yos. 6:25) Rahabi anasonyeza chikhulupiriro, ankaopa Yehova komanso ankalemekeza anthu a Mulungu.

GULU LA YEHOVA M’NTHAWI YA ATUMWI

10. (a) N’chiyani chimene Yesu anauza atsogoleri a chipembedzo chachiyuda? (b) N’chifukwa chiyani ananena zimenezi?

10 Yoswa anatsogolera Aisiraeli powononga mizinda yambiri m’dziko la Kanani n’kukhazikika m’dzikolo. Koma kenako n’chiyani chinachitika? Aisiraeli anayamba kuphwanya malamulo a Mulungu mobwerezabwereza. Pofika nthawi imene Yehova anatumiza Mwana wake padziko lapansi, Aisiraeliwo sankamvera Mulungu ndi aneneri ake moti Yesu ananena za Yerusalemu kuti ndi “wakupha aneneri.” (Werengani Mateyu 23:37, 38.) Mulungu anakana atsogoleri a chipembedzo chachiyuda chifukwa chakuti anali osakhulupirika. Choncho Yesu anawauza kuti: “Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu n’kuperekedwa kwa mtundu wobala zipatso zake.”—Mat. 21:43.

11, 12. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova anayamba kugwiritsa ntchito gulu lina atakana mtundu wachiyuda? (b) Kodi m’gulu latsopanoli munali anthu ati?

11 Yehova anakana mtundu wa Aisiraeli chifukwa anali osakhulupirika. Komabe izi sizikutanthauza kuti Mulungu sanakhalenso ndi gulu la anthu ake padzikoli. Iye anayamba kugwiritsa ntchito gulu latsopano la anthu okhulupirira Yesu Khristu ndiponso zimene iye anaphunzitsa. Izi zinayamba pa Pentekosite mu 33 C.E. Pa tsikuli panali ophunzira 120 a Yesu amene anasonkhana ku Yerusalemu ndipo “mwadzidzidzi kumwamba kunamveka mkokomo ngati wa mphepo yamphamvu, ndipo unadzaza m’nyumba yonse imene iwo anakhalamo.” Kenako “anaona malawi amoto ooneka ngati malilime, ndipo anagawanika ndi kukhala pa aliyense wa iwo limodzilimodzi. Ndiyeno onsewo anadzazidwa ndi mzimu woyera ndipo anayamba kulankhula zinenero zosiyanasiyana, monga mmene mzimuwo unawachititsira kulankhula.” (Mac. 2:1-4) Zimenezi zinapereka umboni wakuti Yehova anali kugwiritsa ntchito gulu latsopanoli la ophunzira a Khristu.

12 Pa tsiku lapaderali, “chiwerengero cha ophunzirawo chinawonjezeka ndi anthu pafupifupi 3,000.” Komanso “Yehova anapitiriza kuwawonjezera anthu amene anali kuwapulumutsa.” (Mac. 2:41, 47) Ophunzirawo ankagwira bwino ntchito yolalikira moti “mawu a Mulungu anapitiriza kufalikira ponseponse. Chiwerengero cha ophunzira chinali kuwonjezeka kwambiri mu Yerusalemu.” Ngakhale “ansembe ambirimbiri anakhala okhulupirira.” (Mac. 6:7) Anthu ambiri ofunitsitsa kudziwa Mulungu anakhulupirira mfundo zoona zimene anthu a m’gulu latsopanoli ankaphunzitsa. Yehova anasonyezanso kuti ankagwiritsa ntchito gululi pamene anayamba kuthandiza “anthu a mitundu ina” kuti alowe mumpingo wachikhristu.—Werengani Machitidwe 10:44, 45.

13. Kodi ntchito ya gulu latsopano la Mulungu inali iti?

13 Akhristu ankadziwa bwino ntchito imene Mulungu ankafuna kuti agwire. Tikutero chifukwa chakuti Yesu anawapatsa chitsanzo. Iye atangobatizidwa, anayamba kulalikira za “ufumu wakumwamba.” (Mat. 4:17) Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuti agwirenso ntchitoyi. Iye anawauza kuti: “Mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Choncho Akhristu oyambirira ankadziwa bwino zimene ankayenera kuchita. Mwachitsanzo, ku Antiokeya wa ku Pisidiya, Paulo ndi Baranaba anauza molimba mtima Ayuda omwe anali otsutsa kuti: “Kunali koyenera kuti inu mukhale oyamba kuuzidwa mawu a Mulungu. Koma popeza kuti mukuwatayira kumbali ndipo mukudziweruza nokha kukhala osayenera moyo wosatha, ifeyo  tikutembenukira kwa anthu a mitundu ina. Ndipotu Yehova anatiikira lamulo lakuti, ‘Ndakuikani monga kuwala kwa anthu a mitundu ina, kuti mukhale chipulumutso mpaka kumalekezero a dziko lapansi.’” (Mac. 13:14, 45-47) Kuyambira nthawi ya atumwi, atumiki a Mulungu akhala akudziwitsa anthu zimene Mulunguyo wakonza kuti apulumutse anthu.

ANTHU AMBIRI ANAPHEDWA KOMA ATUMIKI A MULUNGU ANAPULUMUKA

14. N’chiyani chinachitika ku Yerusalemu, nanga ndi ndani amene anapulumuka?

14 Ayuda ambiri sanamvere uthenga wabwino ndipo tsogolo lawo silinali labwino. Yesu anachenjeza ophunzira ake kuti: “Mukadzaona magulu ankhondo atazungulira Yerusalemu, mudzadziwe kuti chiwonongeko chake chayandikira. Pamenepo amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawira kumapiri, ndipo amene ali mkati mwa mzindawo adzatulukemo. Amene ali m’madera akumidzi asadzalowe mumzindawo.” (Luka 21:20, 21) Zimene Yesu analoserazi zinachitikadi. Ayuda atagalukira Aroma, Seshasi Galasi ndi asilikali achiroma anazungulira mzinda wa Yerusalemu mu 66 C.E. Koma kenako asilikaliwo anabwerera mosayembekezereka ndipo izi zinapereka mpata woti Akhristu athawe ku Yerusalemu ndi ku Yudeya. Malinga ndi zimene katswiri wa mbiri yakale dzina lake Eusebius analemba, Akhristu ambiri atathawa anawoloka Yorodano n’kupita kumzinda wa Pela m’dera la Pereya. Ndiyeno mu 70 C.E., asilikali achiroma otsogoleredwa ndi Tito anabweranso n’kuwonongeratu Yerusalemu. Koma Akhristu okhulupirika anapulumuka chifukwa chomvera chenjezo la Yesu.

15. Kodi n’chiyani chikanalepheretsa kuti anthu ambiri alowe mumpingo wachikhristu?

15 Akhristu oyambirira ankakumana ndi mavuto osiyanasiyana ndiponso kuzunzidwa koma anthu ambiri ankalowabe mumpingo wachikhristu. (Mac. 11:19-21; 19:1, 19, 20) Akhristuwo zinkawayenderabe bwino mwauzimu chifukwa chakuti Yehova ankawadalitsa.—Miy. 10:22.

16. Kodi Mkhristu aliyense anafunika kuchita chiyani kuti zinthu zimuyendere bwino?

16 Mkhristu aliyense anafunika kuchita khama kuti zinthu zimuyendere bwino. Ankafunika kuphunzira Malemba mosamala, kupezeka pa misonkhano yonse komanso kulalikira mwakhama. Zonsezi zinkathandiza kuti munthu akhale pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu komanso ndi Akhristu anzake ndipo zimatithandizanso masiku ano. Gulu la Yehova pa nthawiyo linkachita zinthu mwadongosolo ndipo anthu ankapindula kwambiri chifukwa chakuti oyang’anira ndi atumiki othandiza anali akhama komanso odzipereka. (Afil. 1:1; 1 Pet. 5:1-4) Abale ankasangalalanso akachezeredwa ndi oyang’anira oyendayenda monga Paulo. (Mac. 15:36, 40, 41) Zimene zinkachitika m’gulu la Yehova kalelo n’zofanana kwambiri ndi zimene zikuchitika masiku ano. Timayamikira kwambiri kuti Yehova ankathandiza anthu ake akale kuti azichita zinthu mwadongosolo ndipo amatithandizanso ifeyo. *

17. Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

17 Panopa dziko la Satanali latsala pang’ono kutha koma mbali yapadziko lapansi ya gulu la Yehova ikuyenda mosabwerera m’mbuyo. Kodi inuyo mukuyenda limodzi ndi gulu la Yehova? Kodi panopa mukuchita zotani kuti mulimbitse ubwenzi wanu ndi Yehova? Tidzaphunzira mmene tingachitire zimenezi m’nkhani yotsatira.

^ ndime 16 Onani nkhani zakuti “Akristu Amalambira Mumzimu ndi M’choonadi” ndiponso yakuti “Amayendabe M’choonadi” mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 2002. Mbiri ya mbali ya padziko lapansi ya gulu la Yehova masiku ano yafotokozedwa mwatsatanetsatane m’buku lakuti Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom.