Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwawerenga mosamala magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:

Kodi Nkhosa ya pa Pasika pa Nisani 14 inkaphedwa nthawi yanji?

Mabaibulo ena amanena kuti nkhosayo inayenera kuphedwa “pakati pa madzulo awiri.” Izi zikutanthauza kuti inkaphedwa kumayambiriro kwa tsiku la Nisani 14 nthawi ya madzulo kuli chisisira kapena kuti dzuwa litangolowa kumene. (Eks. 12:6)—12/15, tsamba 18-19.

Kodi achinyamata angagwiritse ntchito mfundo ziti za m’Baibulo kuti asankhe bwino zochita?

Pali mfundo zitatu (1) Kufunafuna ufumu choyamba ndi chilungamo chake. (Mat. 6:19-34) (2) Mumakhala osangalala mukamathandiza ena. (Mac. 20:35) (3) Kutumikira Mulungu mudakali achinyamata. (Mlal. 12:1)—1/15, tsamba 19-20.

Kodi ndani akwera pamahatchi 4 kuyambira mu 1914?

Pa hatchi yoyera pali Yesu ndipo anachotsa Satana ndi ziwanda zake kumwamba. Wokwera pa hatchi yofiira akuimira nkhondo zimene zakhala zikusautsa anthu padzikoli. Ndipo amene wakwera pahatchi yakuda akuimira njala. Pomwe wokwera pahatchi yotuwa akubweretsa imfa pogwiritsa ntchito miliri imene yapha anthu mamiliyoni. (Chiv. 6:2-8)—2/1, tsamba 6-7.

Kodi “ukwati wa Mwanawankhosa” udzachitika liti? (Chiv. 19:7)

Ukwatiwu udzachitika pambuyo poti Mfumu Yesu Khristu ‘wapambana’ pa nkhondo yolimbana ndi adani ake. Izi zikutanthauza kuti udzachitika pambuyo poti Babulo wamkulu wawonongedwa komanso nkhondo ya Aramagedo yamenyedwa.—2/15, tsamba 10.

N’chifukwa chiyani Ayuda m’nthawi ya Yesu “anali kuyembekezera” Mesiya? (Luka 3:15)

Palibe umboni wotsimikizira kuti Ayuda pa nthawiyo ankadziwa zolondola pa ulosi wa Danieli wokhudza nthawi yoti Mesiya afike. (Dan. 9:24-27) Koma ayenera kuti anamva uthenga umene mngelo anauza abusa kapena zimene mneneri wamkazi dzina lake Anna ananena atangoona Yesu kukachisi. Okhulupirira nyenyezi nawonso atafika ananena kuti abwera kudzaona “mfumu ya Ayuda imene yabadwa.” (Mat. 2:1, 2) Pa nthawi ina, zimene Yohane M’batizi ananena zinasonyeza kuti Khristu watsala pang’ono kuonekera.—2/15, tsamba 26-27.

Kodi tingatani kuti mawu athu asakhale inde kenako ayi? (2 Akor. 1:18)

N’zoona kuti nthawi zina tikhoza kusintha pulogalamu yathu pa zifukwa zomveka. Koma tikalonjeza zinazake, tiyenera kuchita zonse zimene tingathe kuti tikwaniritse lonjezolo.—3/15, tsamba 32.

Kodi tingapewe bwanji kuonera zolaula?

Mfundo zitatu izi zingathandize: (1) Ngati mwaona zolaula, mwamsanga yang’anani kumbali. (2) Mukayamba kuganizira zoipa, nthawi yomweyo yesetsani kusiya kuganizira zimenezo ndipo kenako pempherani. (3) Muzipewa mafilimu kapena mawebusaiti oonetsa zolaula.—4/1, tsamba 10-12.

Kodi Mkhristu angakumane ndi mavuto ati amene sankawayembekezera akasiya banja lake n’kukagwira ntchito kudziko lina?

Makolo akamakhala kosiyana, ana awo amavutika kwambiri. Mwina anawo angasiye kukonda makolo awo. Komanso mwamuna ndi mkazi wake amene akukhala kosiyana akhoza kugwera m’msampha wochita chigololo.—4/15, tsamba 19-20.

N’chifukwa chiyani zigawenga ankazithyola miyendo akamazipha pamtengo?

Aroma ankapha zigawenga zina pozipachika pamtengo. Ayuda anapempha kuti miyendo ya anthu amene anapachikidwa limodzi ndi Yesu ithyoledwe. Zimenezi zinachititsa kuti anthuwo afe msanga chifukwa cholephera kupuma mokwanira. Ndiyeno sankayenera kukhala pamtengo usiku wonse. (Deut. 21:22, 23)—5/1, tsamba 11.

Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso anayi ati tikamalalikira?

Kodi munthu amene ndilankhule naye ndi wotani? Kodi ndizichita chiyani ndikafika panyumba ya munthu? Kodi ndizilalikira pa nthawi iti? Nanga ndiziyamba bwanji kulankhula ndi anthu?—5/15, tsamba 12-15.

Kodi ndi anthu angati amene amafa chifukwa chosuta fodya?

Zaka 100 zapitazo, anthu okwana 100 miliyoni anafa chifukwa cha kusuta. Anthu pafupifupi 6 miliyoni amamwalira chaka chilichonse chifukwa cha vutoli.—6/1, tsamba 3.