“Salaza Njira ya Phazi Lako” Kuti Uyende Bwino
PAMENE anthu a Mulungu ankachoka ku Babulo mu 537 B.C.E., Yehova anawauza kuti akonze bwino njira yawo yopita ku Yerusalemu. Iye anati: “Lambulani njira yodutsa anthu. Konzani msewu. Ukonzeni ndithu. Chotsanimo miyala.” (Yes. 62:10) Mwina Ayuda ena anatsogola kuti akalambule njira ndi kukwirira maenje. Zimenezi zikanathandiza abale awo kuti ayende bwinobwino popita kwawo.
Munthu amafunika kuchita zinthu ngati zimenezi kuti akwaniritse zolinga zake potumikira Yehova. Yehova amafuna kuti tizimutumikira popanda chopinga chilichonse. Mawu ake amatilimbikitsa kuti: “Salaza njira ya phazi lako, ndipo njira zako zonse zikhazikike.” (Miy. 4:26) Kaya ndinu achinyamata kapena achikulire, malangizo amenewa akhoza kukuthandizani.
KONZANI NJIRA POSANKHA BWINO ZOCHITA
Ponena za achinyamata, anthu amakonda kunena kuti, ‘Amene ujatu adzafika patali’ kapena amati, ‘Amene uja ali ndi tsogolo lowala.’ Achinyamata amakhala athanzi, amaganiza mwamsanga ndipo amayesetsa kuti zinthu ziwayendere bwino. M’pake kuti Baibulo limati: “Kukongola kwa anyamata ndiko mphamvu zawo.” (Miy. 20:29) Wachinyamata amene amagwiritsa ntchito luso ndi mphamvu zake potumikira Yehova akhoza kukwaniritsa zolinga zake n’kukhala wosangalala kwambiri.
Anthu m’dzikoli amachitanso chidwi ndi achinyamata ndipo amafuna kuti achite zambiri. Ngati wachinyamata wa Mboni amakhoza bwino kusukulu anthu ena monga aphunzitsi kapena anzake angamuuze kuti apitirize maphunziro n’cholinga choti zinthu zimuyendere bwino m’dzikoli. Achinyamata ena amene ali ndi luso pa masewera enaake amauzidwanso kuti alimbikire kuti adzakhale akatswiri. Kodi zimenezi zakuchitikirani inuyo kapena mnzanu? N’chiyani chingathandize Mkhristu kuti asankhe mwanzeru pa nkhaniyi?
Mfundo za m’Baibulo zingathandize munthu kuti akonze bwino njira yake. Lemba la Mlaliki 12:1 limanena kuti: “Kumbukira Mlengi wako Wamkulu masiku a unyamata wako.” Kodi inuyo kapena mnzanuyo ‘mungakumbukire bwanji Mlengi wanu wamkulu’?
Taganizirani zimene zinachitikira Eric * wa ku West Africa. Iye ankakonda kwambiri mpira. Pamene ankakwanitsa zaka 15, anasankhidwa kuti azisewera mu timu ya dziko lake. Apatu mwayi unamutsegukira woti akaphunzire mpirawo m’mayiko a ku Ulaya n’kufika pokhala katswiri. Ndiyeno kodi malangizo oti ‘ukumbukire mlengi wako wamkulu’ anamuthandiza bwanji? Nanga inuyo kapena mnzanuyo mungaphunzire chiyani pa nkhaniyi?
Eric ali pa sukulu anayamba kuphunzira ndi Mboni za Yehova. Anaphunzira kuti Mlengi wake adzathetsa mavuto onse padzikoli. Iye anazindikira kuti ayenera kugwiritsa ntchito nthawi yake komanso mphamvu zake potumikira Mulungu. Izi zinamuchititsa kuti asiye zoyesetsa kukhala katswiri wa mpira. Iye anabatizidwa n’kuyamba kuchita zambiri potumikira Mulungu. Kenako anadzakhala mtumiki wothandiza ndipo anapita ku Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatira.
Eric akanapitiriza mpira uja mwina akanatchuka komanso kulemera. Koma iye anazindikira mfundo ya m’Malemba yakuti: “Zinthu zamtengo wapatali za munthu wachuma ndizo mzinda wake wolimba, ndipo m’maganizo mwake zili ngati mpanda woteteza.” (Miy. 18:11) Anthu amaganiza kuti chuma chingawateteze koma si zoona. Ndipo amene amangokhalira kusakasaka chuma ‘amadzibweretsera zopweteka zambiri pathupi lawo.’—1 Tim. 6:9, 10.
Chosangalatsa n’chakuti achinyamata ambiri ayamba utumiki wa nthawi zonse ndipo akusangalala komanso ndi otetezeka. Eric anati: “Panopa ndinganene kuti ndalowa timu ya atumiki a nthawi zonse. Timu imeneyi ndi yabwino kwambiri ndipo ndikuyamikira Yehova chifukwa chondithandiza kuti ndikhale ndi moyo wabwino komanso wosangalatsa.”
Nanga bwanji inuyo? M’malo moyesetsa kuti mukhale ochita bwino m’dzikoli, muyenera ‘kukhazikitsa njira yanu’ potumikira Yehova. Mungachite zimenezi poyamba upainiya.—Onani bokosi lakuti “ Zinthu Zabwino Zimene Simungazipeze ku Yunivesite.”
CHOTSANI CHOPINGA CHILICHONSE
Mlongo wina ndi mwamuna wake anapita kukaona ofesi ya nthambi ya ku United States ndipo anaona kuti anthu otumikira kumeneko ndi osangalala kwambiri. Mlongoyu analemba kuti: “Tinali titazolowera kwambiri zimene tinkachita pa moyo wathu.” Koma banjali linasankha kuti lisinthe zinthu zina ndi zina kuti liyambe kuchita zambiri mu utumiki.
Poyamba, iwo anaona kuti mwina sangakwanitse kuchita zimenezi. Koma tsiku lina atachita lemba la tsiku anaganizira kwambiri mfundo yake. Lembalo linali pa Yohane 8:31 pamene Yesu anati: “Mukamasunga mawu anga nthawi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga.” Choncho malinga ndi lembali anaona kuti angachite bwino kwambiri kusintha zinthu kuti ayambe kukhala moyo wosalira zambiri. Ndiyeno anagulitsa nyumba yawo yaikulu komanso kusintha zinthu zina kuti asamukire kumpingo umene unalibe ofalitsa ambiri. Panopa iwo akuchita upainiya, amathandiza nawo pomanga Nyumba za Ufumu ndiponso amadzipereka kuthandiza pa misonkhano yachigawo. Kodi iwo amamva bwanji ndi zomwe anachitazi? Iwo anati: “Tikusangalala kwambiri chifukwa chokhala moyo wosalira zambiri ndiponso kutsatira malangizo a gulu la Yehova.”
MUSAPATUKE PANJIRA YOKUTHANDIZANI
Solomo analemba kuti: “Maso ako aziyang’ana patsogolo. Maso ako owala aziyang’anitsitsa patsogolo pako.” (Miy. 4:25) Munthu amene akuyendetsa galimoto amayang’ana kutsogolo kuti asachite ngozi. Kuti ifenso tikwaniritse zolinga zathu potumikira Yehova tiyenera kuyang’ana kutsogolo, osatengeka ndi zilizonse.
Kodi mungakhale ndi zolinga ziti? Mwina mungayesetse kuti muyambe utumiki wa nthawi zonse. Apo ayi, mungapite kukathandiza kumpingo umene ulibe ofalitsa okwanira. Mwinanso mungasamukire mumpingo umene ulibe akulu ndi atumiki othandiza okwanira. Mungakambirane ndi woyang’anira dera kuti akuuzeni zimene mungachite. Ngati mukufuna kupita kugawo lakutali, mungachite bwino kufufuza kuti mudziwe kumene kukufunika thandizo. *
Tiyeni tikambiranenso mfundo ya pa Yesaya 62:10 ija. Ayuda ena ayenera kuti anagwira chintchito cholambula njira yopita kwawo kuti anthu a Mulungu ayende bwino. Ngati mukuyesetsa kukwaniritsa zolinga zinazake potumikira Yehova musabwerere m’mbuyo. Yehova akuthandizani kuti zolinga zanuzo zitheke. Pitirizani kupempha nzeru kwa Yehova kuti muchotse chopinga chilichonse. Mudzaona iye akukuthandizani ‘kusalaza njira ya mapazi anu.’—Miy. 4:26.
^ ndime 8 Dzina lasinthidwa.
^ ndime 18 Onani buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova, tsamba 111 ndi 112.