Kodi Tingathandize Bwanji Akhristu Amene Banja Lawo Latha?
Masiku ano mabanja ambiri akutha. Mwinanso inu mukudziwa anthu ena amene mabanja awo anatha. Kafukufuku wina wa ku Poland anasonyeza kuti anthu ambiri azaka 30 amene akhala pa banja zaka zitatu kapena 6 amathetsa mabanja awo. Koma si anthu azaka 30 okha amene amachita zimenezi.
Bungwe lina la ku Spain loona za mabanja linati: “Kafukufuku wasonyeza kuti hafu ya anthu [ku Ulaya] amene akwatirana adzathetsa mabanja awo.” Ndi mmene zililinso kumayiko ena olemera.
AMAVUTIKA MAGANIZO KWAMBIRI
Mlangizi wina wa anthu am’banja ku Ulaya anati: “Banja likafika pakutha zimakhala kuti zinthu zinasokonekera kale. Zinthu ngati zimenezi zikachitika zimakhala zopweteka kwambiri.” Ananenanso kuti: “Munthu amavutika maganizo, amakwiya, amadziimba mlandu, amakhumudwa, amataya mtima ndiponso amachita manyazi.” Ena mpaka amafika pofuna kudzipha. Anapitiriza kuti: “Ndiyeno likatha kubwalo la milandu, mavuto enanso amayamba. Munthu amayamba kuona kuti ali yekhayekha ndipo amadzifunsa kuti: ‘Kodi panopa anthu akundiona bwanji? Kodi ndiye ndizichita chiyani pa moyo wanga?’”
Pokumbukira zimene zinachitika zaka zingapo zapitazo, mlongo wina dzina lake Ewa anati: “Banja lathu litatha, ndinkachita manyazi kwambiri chifukwa aneba anga ndi anzanga akuntchito ankauzana kuti, ‘Awotu banja lawo lija linatha.’ Ndinkakwiya kwambiri ndi zimene zinkandichitikira. Mwamuna wanga anandisiya ndi ana awiri moti ndinkachita zinthu ngati mayi komanso bambo.” * M’bale wina dzina lake Adam, anali mkulu wodalirika kwa zaka 12. Koma banjalo litatha, iye anati: “Munthune ndimamva ngati ndanyozeka kwabasi ndipo nthawi zina ndimakwiya nazo moti ndimangofuna nditamakhala pandekha basi.”
AMAVUTIKA KUTI AYAMBE KUONA ZINTHU MOYENERA
Banja likatha anthu ena amavutika kwambiri kuti ayambenso kuona zinthu moyenera ngakhale patapita zaka zambiri. Mwina angamaganize kuti anthu ena alibe nawonso ntchito. Katswiri wina woona za kutha kwa mabanja ananena kuti: “Anthuwo amayenera kusintha mmene amachitira zinthu n’kuphunzira kulimbana ndi mavuto paokha.”
Stanisław anati: “Banja lathu litatha, mkazi wanga wakale ankandikaniza kuona tiana tanga tiwiri. Izi zinandichititsa kuganiza kuti palibe amene amandikonda komanso kuti ngakhale Yehova wandisiya. Ndinafika poona kuti bola kungofa. Koma kenako ndinazindikira kuti ndinali kuona zinthu molakwika.” Mlongo wina dzina lake Wanda yemwe banja lake linatha n’kusiyidwa ndi ana 4 ankadera nkhawa kwambiri za tsogolo lake ndi anawo. Iye anati: “Ndinkaona kuti pakapita nthawi anzathu, ngakhale abale ndi alongo, adzasiya kutiganizira ndiponso kutithandiza. Koma panopa m’pamene ndikuzindikira kuti abale ankandithandiza kwambiri pamene ndinkayesetsa kulera ana anga ndi kuwaphunzitsa kuti azitumikira Yehova.”
Ndemanga za anthuwa zikusonyeza kuti anthu ena amavutika kwambiri maganizo mabanja awo akatha. Mwina angayambe kuganiza kuti ndi opanda pake ndiponso kuti palibe amene angawakonde. Komanso akhoza kumangotola ena zifukwa. Ndiyeno angayambe kuganiza kuti mumpingo mulibe anthu achikondi. Koma zimene zinachitikira Stanisław ndi Wanda zikusonyeza kuti anthu amene mabanja awo anatha amazindikira patapita nthawi kuti abale ndi alongo awo amawakonda. Akhristu amathandiza m’njira zikuluzikulu ngakhale kuti mwina anthu amene akuthandizidwawo, poyamba sangazindikire.
AMASOWA WOCHEZA NAYE NDIPO AMADZIKAYIKIRA
Koma chimene tiyenera kudziwa n’chakuti ngakhale titayesetsa bwanji kuwathandiza, anthu amene banja lawo latha nthawi zina amavutikabe chifukwa chosowa mnzawo. Nthawi zambiri, alongo osiyidwa amaganiza kuti palibenso amene angawakonde. Mlongo wina dzina lake Alicja anati: “Panopa padutsa zaka 8 kuchokera pamene banja lathu linatha. Koma nthawi zina ndimadzikayikirabe. Maganizo amenewa akandibwerera ndimadzimvera chisoni n’kupita kwandekha kukalira.”
Zimene tanenazi zimachitikira anthu ambiri amene banja lawo latha. Koma Baibulo limanena kuti si bwino kudzipatula. Munthu akayamba kudzipatula akhoza kuyamba kuchita “zosemphana ndi nzeru zonse zopindulitsa.” (Miy. 18:1) Koma munthu amene akusowa mnzakeyo ayenera kusamala kuti asakhale ndi chizolowezi chofunsira nzeru kapena kudandaulira munthu amene si mwamuna kapena mkazi mnzake. Tikutero chifukwa chakuti akhoza kuyamba kukopana.
Akhristu anzathu amene banja lawo linatha akhoza kuvutika kwambiri chifukwa chosowa wocheza nawo, kudera nkhawa za tsogolo lawo komanso kumva kuti palibe amene angawakonde. Zimene anthuwo amaganiza si zachilendo koma n’zovuta kupirira. Choncho tizitsanzira Yehova powamvetsa komanso kupitiriza kuwathandiza. (Sal. 55:22; 1 Pet. 5:6, 7) Dziwani kuti iwo adzayamikira kwambiri chilichonse chimene tingachite powathandiza. Tikachita zimenezi tidzakhala anzawo enieni.—Miy. 17:17; 18:24.
^ ndime 6 Mayina ena asinthidwa.