Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Micronesia
KATHERINE anakulira ku United States ndipo anabatizidwa kukhala wa Mboni za Yehova ali ndi zaka 16. Iye ankalalikira mwakhama kwambiri m’dera lawo koma sankapeza anthu ofuna kuphunzira. Mlongoyu anati: “Ndinkawerenga za anthu amene ankapemphera kwa Mulungu kuti awatumizire munthu woti azikawaphunzitsa Baibulo. Ndinkalakalaka nditapeza munthu wotero koma sizinkatheka.”
Atalalikira kwa zaka zingapo m’deralo, Katherine anaganiza zosamukira kumene anthu angafune kumva uthenga wa Ufumu. Koma ankakayikira zoti angakwanitse kukakhala kwayekha. Pa nthawi ina imene anachoka kwawo kwa milungu iwiri yokha, ankasowa kwambiri achibale ake tsiku lililonse. Koma anaganizabe zosamuka chifukwa chofunitsitsa kuthandiza anthu kuti adziwe Yehova. Atafufuza za mayiko osiyanasiyana oti n’kusamukirako, analembera kalata ku ofesi ya nthambi ya ku Guam. Abale a kumeneko anamuyankha n’kumufotokozera zonse zofunika. Ndiyeno mu July 2007, Katherine ali ndi zaka 26, anasamukira kuchilumba china m’nyanja ya Pacific chotchedwa Saipan. Chilumbachi chili pa mtunda wa makilomita pafupifupi 10,000 kuchokera kwawo. Kodi zinamuyendera bwanji atasamuka?
MAPEMPHERO AWIRI ANAYANKHIDWA
Atangofika kumpingo wake watsopano, Katherine anakumana ndi mayi wina dzina lake Doris. Mayiyu anali wazaka za m’ma 40 ndipo anavomera kuphunzira Baibulo. Koma atangophunzira naye mitu itatu yoyambirira ya buku lakuti Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, Katherine anayamba kuda nkhawa. Iye anati: “Phunziro langa ndi Doris linkayenda bwino kwambiri ndipo sindinkafuna kuti ndimusokoneze. Ndinali ndisanachititsepo phunziro kwa nthawi yaitali. Choncho ndinkaona kuti Doris akufunikira mlongo waluso komanso wokulirapo kuti amuthandize bwinobwino.” Katherine anapemphera kwa Yehova kuti amuthandize kupeza mlongo woyenerera woti apitirize kuphunzira ndi Doris. Kenako anaganiza zouza Doris kuti amupezera munthu wina kuti aziphunzira naye.
Katherine anati: “Ndisanafotokoze maganizo angawa, Doris ananena kuti akufuna kundiuza za vuto linalake. Nditamvetsera vutolo, ndinamufotokozera mmene Yehova anandithandizira nditakumana ndi vuto ngati lomwelo. Mayiyu anathokoza kwambiri.” Kenako Doris anauza Katherine kuti: “Ukudziwa, Mulungutu akukugwiritsa ntchito kuti undithandize. Tsiku limene unayamba kufika lija ndinali nditawerenga Baibulo kwa maola ambiri. Ndiyeno ndinapemphera kwa Mulungu, uku ndikulira, kuti anditumizire munthu woti azindiphunzitsa Baibulo. Kenako ndi mmenenso iweyo unkagogoda pakhomo. Ndimaona kuti Mulungu anayankha pemphero langa.” Katherine akamafotokoza zimene zinachitika pa nthawiyi misozi imayamba kulengeza m’maso mwake. Iye anati: “Zimene Doris ananenazi zinali ngati yankho la pemphero langanso. Ndinamva ngati Yehova akundiuza kuti ndipitirize phunzirolo.”
Doris anabatizidwa mu 2010 ndipo panopa amaphunzitsa Baibulo anthu ambiri. Katherine anati: “Ndinkafunitsitsa nditathandiza winawake kukhala mtumiki wa Mulungu. Ndimathokoza Yehova kuti anandithandiza kuti zimene ndinkalakalaka kwa nthawi yaitali zitheke.” Masiku ano, Katherine ndi mpainiya wapadera kuchilumba cha Kosrae m’nyanja ya Pacific.
ZIMENE MUNGACHITE POTHANA NDI MAVUTO ATATU
Abale ndi alongo oposa 100 ochokera kumayiko ena atumikirapo kuzilumba za ku Micronesia. Iwo anali azaka za pakati pa 19 ndi 79. Abale ndi alongo akhamawa amamva ngati Erica, yemwe anasamukira ku Guam mu 2006 ali ndi zaka 19. Iye anati: “Kuchita upainiya m’dera limene anthu ambiri amamvetsera kumasangalatsa kwambiri. Ndikuyamikira kuti Yehova anandithandiza kuti ndichite utumiki wabwino kwambiri umenewu.” Masiku ano, Erica akuchita upainiya wapadera pachilumba cha Ebeye ku Marshall Islands. Komabe kutumikira kudziko lina kumakhala ndi mavuto ake. Tiyeni tikambirane mavuto atatu amene anthu ambiri omwe asamukira ku Micronesia akumana nawo.
Kuzolowera moyo watsopano. M’bale wina wazaka 22 dzina lake Simon anasamukira kuchilumba cha Palau mu 2007. Iye anaona kuti malipiro amene angapeze kumeneko ndi ochepa kwambiri powayerekezera ndi amene ankapeza kwawo ku England. Simon anati: “Ndinayenera kuzolowera kuti ndisamangogula chilichonse chimene ndikufuna. Panopa ndimafunika kusankha bwino chakudya choti ndigule komanso ndimayesetsa kupeza mitengo yabwino ya zinthu. Chinthu china chikawonongeka ndimayesa kupeza munthu amene angandithandize kuchikonza.” Kodi moyo watsopanowu unamukhudza bwanji? Iye anati: “Zandithandiza kuzindikira zinthu zofunika kwambiri komanso kugwiritsa ntchito bwino zinthu zochepa zomwe ndili nazo. Nthawi zambiri ndaona kuti Yehova akundithandiza. Pa zaka 7 zimene ndatumikira kunoko, sindinasowepo chakudya kapena malo ogona.” Yehova amathandizadi anthu amene amakhala moyo wosalira zambiri n’cholinga choti aike zinthu za Ufumu patsogolo.—Mat. 6:32, 33.
Kusowa achibale anu. Erica anati: “Ndimakonda kwambiri achibale anga ndipo ndinkadera nkhawa kuti sindingakwanitse kutumikira kutali.” Kodi anakonzekera bwanji kuti athane ndi vutoli? Iye anati: “Ndisanasamuke ndinawerenga nkhani za mu Nsanja ya Olonda zokhudza kusowana ndi achibale. Zimenezi zinandithandiza kuti ndilimbe mtima. M’nkhani ina, mayi wina analimbikitsa mwana wake wamkazi pomuuza kuti, ‘Yehova angakusamalire bwino kuposa ineyo.’ Mawu amenewa anandilimbikitsa kwambiri.” Hannah ndi mwamuna wake, dzina lake Patrick, amatumikira pachilumba cha Majuro ku Marshall Islands. Kuti asamasowe achibale, Hannah amaganizira kwambiri ndiponso kucheza ndi abale ndi alongo mumpingo wawo. Iye anatinso: “Nthawi zonse ndimathokoza Yehova kuti ndili ndi abale a padziko lonse amene ali ngati am’banja langa. Sindikanakwanitsa kutumikira kudera lina popanda thandizo lawo.”
Chilendo. Simon anati: “Mukafika m’dziko lina pafupifupi chilichonse chimakhala chachilendo. Nthawi zina ndimadandaula kuti anthu sandimvetsa ndikamacheza nawo nkhani zanthabwala.” Erica anati: “Poyamba, ndinkaona kuti anthu akundisala. Koma zimenezi zinandithandiza kuti ndiganizirenso zimene zinandichititsa kuti ndisamukire kumeneko. Sindinasamuke pofuna kupeza zondisangalatsa koma kuti ndichite zambiri potumikira Yehova.” Ananenanso kuti: “Patapita nthawi, ndinayamba kugwirizana kwambiri ndi anthu ena.” Simon anachita khama pophunzira Chipalawu ndipo zimenezi zinamuthandiza kuti azimasukirana ndi abale ndi alongo. (2 Akor. 6:13) Komanso abale anayamba kumukonda kwambiri chifukwa cha khama lake pophunzira chilankhulo chawo. Anthu amene asamukira m’dziko lina akamachita zinthu mogwirizana kwambiri ndi abale a kumeneko, onse amasangalala chifukwa chokhala pa ubwenzi wabwino kwambiri. Kodi anthu amene amadzipereka kukatumikira kudera lina amasangalalanso ndi zinthu zotani?
‘AMAKOLOLA ZOCHULUKA’
Mtumwi Paulo ananena kuti: “Wobzala mowolowa manja adzakololanso zochuluka.” (2 Akor. 9:6) Izi n’zimene zimachitikiranso anthu amene amayesetsa kuchita zambiri potumikira Yehova. N’chifukwa chiyani tinganene kuti abale ndi alongo amenewa ‘akolola zambiri’ kuzilumba za ku Micronesia?
Ku Micronesia, anthu ambiri amafunabe kuphunzira Baibulo ndipo abale ndi alongo ali ndi mwayi woona anthu ena akuyamba kusintha n’kumatsatira mfundo za m’Mawu a Mulungu. Patrick ndi Hannah analalikiranso kukachilumba kotchedwa Angaur, komwe kuli anthu 320. Atalalikira kumeneko kwa miyezi itatu, anakumana ndi mayi wina amene ankalera yekha ana. Nthawi yomweyo mayiyo anavomera kuphunzira Baibulo ndipo anayamba kusinthiratu moyo wake. Hannah anati: “Nthawi zonse tikamaliza kuphunzira ndi mayiyu, pobwerera ine ndi mwamuna wanga tinkayang’anizana n’kunena pamodzi kuti: ‘Zikomo Yehova.’” Hannah ananenanso kuti: “Ndikudziwa kuti Yehova akanapeza njira ina yokokera mayiyu. Koma chifukwa chosamukira kuderali, ifeyo takhala ndi mwayi womupeza n’kumuthandiza. Ichi ndi chimodzi mwa zinthu zosangalatsa kwambiri pa moyo wathu.” Erica anati, “Kuthandiza munthu kuti adziwe Yehova kumasangalatsa kwambiri.”
KODI INUNSO MUNGAKATHANDIZE KWINA?
Kumayiko ambiri kulibe ofalitsa okwanira. Kodi inuyo mungapite kukathandiza kumadera ngati amenewo? Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala wofunitsitsa kuchita zambiri mu utumiki. Mukambirane ndi akulu mumpingo wanu, woyang’anira dera wanu komanso anthu ena amene anatumikirapo kudera lina. Mukayamba kukonzekera kuti musamukire kwina, muyenera kulembera kalata nthambi imene imayang’anira dera limene mukufuna kupita kuti mudziwe zina ndi zina. * Mukhoza kukhalanso ndi mwayi ‘wokolola zambiri’ chifukwa chodzipereka ndi mtima wonse ngati mmene achitira abale ndi alongo osiyanasiyana.
^ ndime 17 Onani nkhani yakuti “Kodi ‘Mungawolokere ku Makedoniya’?” mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa August 2011.