Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukulandira “Chakudya pa Nthawi Yoyenera?”

Kodi Mukulandira “Chakudya pa Nthawi Yoyenera?”

TIKUKHALA m’nthawi yovuta kuposa nthawi ina iliyonse. (2 Tim. 3:1-5) Tsiku lililonse timakumana ndi zinthu zimene zingasokoneze makhalidwe athu abwino komanso ubwenzi wathu ndi Yehova. Yesu anadziwiratu za nthawi yovutayi ndipo anauza ophunzira ake kuti iye aziwalimbikitsa kuti athe kupirira mpaka mapeto. (Mat. 24:3, 13; 28:20) Pofuna kuwalimbikitsa, iye anasankha kapolo wokhulupirika kuti aziwapatsa “chakudya pa nthawi yoyenera.”—Mat. 24:45, 46.

Kuyambira mu 1919 pamene kapolo wokhulupirika anasankhidwa, “antchito ake apakhomo” mamiliyoni, olankhula zilankhulo zosiyanasiyana, asonkhanitsidwa m’gulu la Mulungu ndipo akulandira chakudya pa nthawi yoyenera. (Mat. 24:14; Chiv. 22:17) Koma mabuku ndi mavidiyo ena sapezeka m’zilankhulo zina. Mwachitsanzo, ambiri sangaone mavidiyo ndi nkhani zimene zimaikidwa pa jw.org. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti anthuwo sakulandira chakudya chokwanira ndipo ubwenzi wawo ndi Yehova sungakhale wolimba? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tikambirane kaye mafunso 4 ofunika.

 1 Kodi kwenikweni Yehova amagwiritsa ntchito chiyani potiphunzitsa?

Satana atauza Yesu kuti asandutse miyala kukhala mkate, Yesuyo anayankha kuti: “Munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu onse otuluka pakamwa pa Yehova.” (Mat. 4:3, 4) Mawu a Yehova ali m’Baibulo. (2 Pet. 1:20, 21) Choncho kwenikweni Yehova amagwiritsa ntchito Baibulolo potiphunzitsa.—2 Tim. 3:16, 17.

Gulu la Yehova lakonza zoti Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika kapena mabuku ake ena apezeke m’zilankhulo 120 ndipo chaka chilichonse Baibuloli likumasuliridwa m’zilankhulo zinanso. Komanso makope mabiliyoni angapo a Mabaibulo ena amapezeka m’zilankhulo masauzande. Izi zikugwirizana ndi cholinga cha Yehova chakuti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.” (1 Tim. 2:3, 4) Popeza kuti “palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona” tikudziwa kuti iye adzathandiza anthu onse amene “amazindikira zosowa zawo zauzimu” kuti alowe m’gulu lake ndipo adzawaphunzitsa.—Aheb. 4:13; Mat. 5:3, 6; Yoh. 6:44; 10:14.

2 Kodi mabuku athu amathandiza bwanji anthu?

Munthu ayenera kuchita zinthu zambiri kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba osati kungowerenga Baibulo basi. Iye ayenera kumvetsa bwino zimene akuwerengazo ndiponso kuzigwiritsa ntchito pa moyo wake. (Yak. 1:22-25) M’nthawi ya atumwi, munthu wina wa ku Itiyopiya ankadziwa bwino zimenezi. Iye ankawerenga Mawu a Mulungu ndipo Filipo anamufunsa kuti: “Kodi mukumvetsa zimene mukuwerengazo?” Ndipo iye anayankha kuti: “Ndingamvetse bwanji popanda wondimasulira?” (Mac. 8:26-31) Ndiyeno Filipo anamuthandiza kuti amvetse bwino Mawu a Mulungu. Munthuyo anakhudzidwa kwambiri ndi zimene anaphunzirazo moti anabatizidwa. (Mac. 8:32-38) Ifenso mabuku athu ofotokoza Baibulo amatithandiza kudziwa Malemba molondola. Mabukuwo amatifika pa mtima ndipo amatilimbikitsa kutsatira zimene tikuphunzira.—Akol. 1:9, 10.

Yehova amagwiritsa ntchito mabukuwo kuti atumiki ake asamamve njala kapena ludzu mwauzimu. (Yes. 65:13) Mwachitsanzo, magazini ya Nsanja ya Olonda imapezeka m’zilankhulo zoposa 210. Imafotokoza maulosi a m’Baibulo, imatithandiza kumvetsa mfundo zozama komanso imatilimbikitsa kutsatira mfundo za m’Baibulo. Magazini ya Galamukani! imapezeka m’zilankhulo 100. Imatithandiza kudziwa zinthu zimene Yehova analenga ndipo imatithandiza kugwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo. (Miy. 3:21-23; Aroma 1:20) Kapolo wokhulupirika amatipatsa mabuku m’zilankhulo zoposa 680. Kodi inuyo mumawerenga Baibulo tsiku lililonse? Nanga magazini atsopano kapena mabuku atsopano omwe ali m’chilankhulo chanu mumawawerenga?

Gulu la Yehova limakonzanso nkhani zochokera m’Baibulo zimene zimakambidwa pa misonkhano yampingo ndiponso ikuluikulu. Kodi mumasangalala ndi nkhani, masewero, zitsanzo ndiponso mbali zofunsa zimene zimapezeka pa misonkhano imeneyi? Yehova amatikonzeradi phwando lauzimu.—Yes. 25:6.

 3. Kodi ngati mabuku ena sanamasuliridwe m’chilankhulo chanu ndiye kuti chakudya chanu n’choperewera?

Ayi. Sitiyenera kudabwa kuti atumiki a Yehova ena amakhala ndi mabuku ndiponso nkhani zambiri kuposa ena. Tikutero chifukwa chakuti ndi mmene zinalili ndi atumwi. Iwo ankalandira malangizo ambiri kuposa ophunzira ena. (Maliko 4:10; 9:35-37) Ngakhale zinali choncho, sikuti chakudya cha ophunzira enawo chinali choperewera ayi. Iwonso ankalandira chakudya chokwanira.—Aef. 4:20-24; 1 Pet. 1:8.

Tisaiwalenso kuti zinthu zambiri zimene Yesu anachita ndiponso kunena ali padzikoli sizinalembedwe m’Baibulo. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Pali zinthu zinanso zambiri zimene Yesu anachita. Zikanakhala kuti zonse zinalembedwa mwatsatanetsatane, ndikuganiza kuti mipukutu yolembedwayo sikanakwana m’dzikoli.” (Yoh. 21:25) Ngakhale kuti Akhristu oyambirira ankadziwa zambiri zokhudza Yesu kuposa ifeyo, sitinganene kuti zimene tikudziwa n’zoperewera. Yehova amatithandiza kuti tidziwe mfundo zokwanira zokhudza Yesu zimene zingatithandize kutsatira mapazi ake.—1 Pet. 2:21.

Taganiziraninso za makalata amene atumwi ankatumizira mipingo. Kalata ina imene Paulo analemba sipezeka m’Baibulo. (Akol. 4:16) Kodi tinganene kuti zimene tikudziwa n’zoperewera chifukwa choti sitinawerenge kalatayo? Ayi. Yehova amadziwa zimene timafunikira ndipo amaonetsetsa kuti tili ndi zonse zimene zingatithandize kukhalabe olimba.—Mat. 6:8.

Yehova amadziwa zimene timafunikira ndipo amaonetsetsa kuti tili ndi zonse zimene zingatithandize kukhalabe olimba

Masiku anonso, Akhristu ena amakhala ndi mabuku kapena zinthu zina zimene ena alibe. Kodi muli ndi mabuku ochepa m’chilankhulo chanu? Ngati ndi choncho, musamakayikire zoti Yehova amakukondani. Chofunika n’chakuti muziwerenga zimene muli nazo n’kumapezeka ku misonkhano ya chilankhulo chimene mumamva. Yehova adzakuthandizani kuti mupitirize kukhala naye pa ubwenzi wolimba.—Sal. 1:2; Aheb. 10:24, 25.

4. Kodi ubwenzi wanu ndi Yehova sungalimbe ngati simuona zinthu zimene gulu lathu lafalitsa pa webusaiti yathu?

Pa webusaiti yathu pamapezeka magazini, mabuku ndiponso zinthu zina zothandiza pophunzira Baibulo. Palinso nkhani zothandiza mabanja, achinyamata komanso makolo amene ali ndi ana aang’ono. Mabanja ambiri amagwiritsa ntchito zimenezi pa Kulambira kwa Pabanja ndipo zimawathandiza. Pa webusaitiyi amaikaponso malipoti a zochitika zapadera monga mwambo womaliza maphunziro a Sukulu ya Giliyadi ndi msonkhano wapachaka. Pamapezekanso malipoti a masoka achilengedwe komanso milandu ina yokhudza anthu a Yehova. (1 Pet. 5:8, 9) Uthenga wa Ufumu ukulalikidwanso kudzera pa webusaitiyi ngakhale m’mayiko amene ntchito yathu ndi yoletsedwa.

Komabe, kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova sikudalira pa kukhala ndi mwayi woona zinthu zimenezi. Kapolo amatulutsa mabuku ndi magazini okwanira kuti azidyetsa bwino antchito apakhomo onse. Choncho simuyenera kukakamizika kuti mugule zipangizo zamakono n’cholinga choti muziona zinthu pa jw.org. Akhristu ena amasindikiza zinthu zimene zili pa webusaitiyi n’kumapatsa anzawo amene alibe mwayi woziona koma si lamulo loti mpingo uzichita zimenezi.

Timayamikira kwambiri kuti Yesu akukwaniritsa lonjezo lake loti azitisamalira. Panopa dzikoli langotsala pang’ono penipeni kuti liwonongedwe koma sitikayikira kuti Yehova apitiriza kutipatsa “chakudya pa nthawi yoyenera.”