KALE LATHU
Sewero Limene Linathandiza Ambiri Kuphunzira Baibulo
SEWERO limene linathandiza ambiri kuphunzira Baibulo linkatchedwa “Sewero la Eureka.” Mawu akuti “eureka” amatanthauza kuti “ndapeza.” M’ma 1800 ku California m’dziko la United States, anthu ankanena mofuula mawuwa akapeza golide. Koma Charles Taze Russell ndi Ophunzira Baibulo anzake anapeza mfundo zoona za m’Baibulo zomwe zinali zamtengo wapatali kwambiri kuposa golide. Ndiyeno iwo ankafunitsitsa kuuza anthu ena mfundozo.
Pofika chapakati pa chaka cha 1914, anthu mamiliyoni m’mizinda ikuluikulu anali atapita kukaona “Sewero la Pakanema la Chilengedwe.” Seweroli linapangidwa ndi Ophunzira Baibulo ndipo linali la maola 8. Linali ndi zithunzi zokongola, mawu ofotokozera komanso nyimbo zabwino. Linasonyeza nkhani za m’Baibulo kuchokera pamene zinthu zinalengedwa mpaka kumapeto kwa Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Yesu Khristu.—Chiv. 20:4. *
Koma zinkavuta kuti akaonetse seweroli kumadera a kumidzi. Choncho mu August 1914, Ophunzira Baibulo anatulutsa “Sewero la Eureka.” Seweroli linali chidule cha “Sewero la Pakanema” ndipo silinkaoneka ngati filimu. Panali mitundu itatu ya sewero lachiduleli ndipo inkapezeka m’zilankhulo zingapo. Mtundu woyamba unkatchedwa kuti “Eureka X” ndipo unali ndi mawu ofotokozera komanso nyimbo. Mtundu wachiwiri unkatchedwa “Eureka Y” ndipo unali ndi mawu onse a anthu komanso zithunzi zokongola. Ndipo mtundu wachitatu unali sewero loti anthu azionera kunyumba lomwe linali ndi mawu ena ofotokozera ndiponso nyimbo. Anthu ankatha kugulanso galamafoni komanso pulojekita pa mtengo wabwino kuti azigwiritsa ntchito poonetsa masewerowa.
Ophunzira Baibulo ankaonetsa seweroli kwaulere m’madera akutali chifukwa chakuti sankayenera kugwiritsa ntchito mapulojekita akuluakulu kapena zimasikirini. Izi zinathandiza kuti uthenga wa Ufumu ufalitsidwe kwambiri. Sewero la “Eureka X” linkatha kuonetsedwa masana kapena usiku chifukwa linali la mawu okha. Sewero la “Eureka Y” linkaonetsedwa ndi pulojekita pogwiritsa ntchito mtundu winawake wa nyali ngati panalibe magetsi. Lipoti lina mu Nsanja ya Olonda yachifinishi linati: “Tikhoza kuonetsa seweroli kulikonse.” Zimenezi zinalidi zoona.
Nthawi zambiri, Ophunzira Baibulo sankachita lendi malo ochitira masewero koma ankangopempha malo m’masukulu, makhoti, m’masiteshoni a sitima kapena m’mabalaza a nyumba zikuluzikulu. Nthawi zina ankaonetsa pamtetete ndipo ankangoyala chinsalu choyera pakhoma la nyumba ina yaikulu. Anthony Hambuch analemba kuti: “Alimi ankamanga kasitediyamu m’minda yawo ya zipatso ndipo ankayala mitengo kuti anthu akhalire.” Gulu lina loonetsa seweroli linali ndi ngolo yonyamulira zipangizo, zikwama, matenti ndi zophikira.
Kumalo ena kunkabwera anthu ochepa kudzaonera koma kwina kunkabwera ambirimbiri. M’tauni ina ya ku United States, kumene kunkakhala anthu 150 okha, anthu 400 anafika kudzaonera seweroli pasukulu ina. Kumalo ena, anthu anayenda makilomita 8 kuti adzaonere. Ku Sweden, anthu apafupi ndi nyumba ya Charlotte Ahlberg anasonkhana m’kanyumba kake ndipo anasangalala kwambiri atamvetsera seweroli. Mumzinda wina ku Australia, anthu 1,500 anafika kudzaonera. Nsanja ya Olonda inanena kuti aphunzitsi ndiponso ophunzira a m’masekondale komanso m’makoleji ankachita nalo chidwi kwambiri. Seweroli linkakondedwa ngakhale m’madera amene anthu anazolowera kuonera mafilimu.
ANAFESA MBEWU ZA CHOONADI
Abale amene ankatumidwa kukayambitsa makalasi atsopano ophunzira Baibulo ankakonda kugwiritsa ntchito seweroli. Sitingadziwe chiwerengero cha anthu amene anaonera. Koma anthu ena ankalionetsa kambirimbiri. Mu 1915 magulu 14 okha pa magulu 86 omwe ankaonetsa seweroli anachitira lipoti mwezi ndi mwezi. Koma malipoti ochepawo anasonyeza kuti m’chakachi anthu oposa 1 miliyoni analionera. Komanso anthu oposa 30,000 anapempha mabuku ofotokoza Baibulo.
Mwina panopa palibe anthu ambiri amene amadziwa za “Sewero la Eureka.” Koma anthu mamiliyoni ochokera m’madera osiyanasiyana padziko lonse analionera. Ambiri mwa iwo anapeza mfundo zoona za m’Baibulo zomwe zinali zamtengo wapatali kuposa golide ndipo anatha kunena kuti “Eureka.”
^ ndime 4 Onani nkhani ya “Kale Lathu” ya mutu wakuti “Padutsa Zaka 100 Tsopano” mu Nsanja ya Olonda ya February 15, 2014, tsamba 30 mpaka 32.