Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Ubwerere Ukalimbikitse Abale Ako’

‘Ubwerere Ukalimbikitse Abale Ako’

PETULO atakana Yesu, analira koopsa. Zimenezi zinamufooketsa ndithu koma Yesu ankafuna kumugwiritsabe ntchito kuti akathandize anzake. Choncho anamuuza kuti: “Ukabwerera, ukalimbikitse abale ako.” (Luka 22:32, 54-62) Petulo anadzakhala mmodzi mwa mizati ya mpingo wachikhristu. (Agal. 2:9) Masiku anonso, pali abale amene anali akulu koma anaima kaye. Iwo akhoza kutumikiranso monga akulu n’kumalimbikitsa Akhristu anzawo.

Anthu ena amene anali oyang’anira anauzidwa kuti aime kaye ndipo amadziona kuti ndi olephera. Chitsanzo ndi m’bale wina wa ku South America dzina lake Julio. * Iye anali mkulu kwa zaka zoposa 20 ndipo anati: “Ndinkatanganidwa kukonzekera nkhani, kuyendera abale ndiponso kuchita maulendo aubusa. Koma zonsezi zinatha nthawi imodzi. Kunena zoona zinthu sizinkandiyendera pa nthawiyo.” Koma panopa Julio akutumikiranso monga mkulu.

“SANGALALANI PAMENE MUKUKUMANA NDI MAYESERO”

Yakobo analemba kuti: “Abale anga, sangalalani pamene mukukumana ndi mayesero osiyanasiyana.” (Yak. 1:2) Yakobo ankanena za mayesero amene timakumana nawo chifukwa chozunzidwa komanso chifukwa cha uchimo. Popeza ndife ochimwa tikhoza kuvutika chifukwa cha zilakolako zoipa, mtima wokondera komanso zinthu zina. (Yak. 1:14; 2:1; 4:1, 2, 11) Yehova akatilanga zimakhala zopweteka. (Aheb. 12:11) Koma tikhoza kukhalabe osangalala ngakhale kuti takumana ndi mayesero oterewa.

Ngati tauzidwa kuti tiime kaye pa udindo wina mumpingo tikhoza kulimbitsabe chikhulupiriro chathu ndiponso kusonyeza kuti timakonda kwambiri Yehova. Tingachitenso bwino kudzifufuza kuti tione cholinga chathu pamene tinkayesetsa kuti tikhale woyang’anira. Kodi tinkafuna kukhala ndi udindo chifukwa chofuna kupeza kenakake? Kapena tinatero chifukwa chokonda Mulungu ndiponso kudziwa  kuti mpingo ndi wake ndipo anthu ake akufunikira kusamaliridwa mwachikondi? (Mac. 20:28-30) Kodi chingachitike n’chiyani ngati m’bale apitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika atauzidwa kuti aime kaye pa udindo? Anthu onse ngakhalenso Satana amaona kuti iye amakondadi Yehova.

Davide atachita machimo akuluakulu anamvera uphungu umene anapatsidwa ndipo anakhululukidwa. Iye anaimba kuti: “Wodala ndi munthu amene wakhululukidwa zolakwa zake, amene machimo ake aphimbidwa. Wodala ndi munthu amene Yehova sanamusungire cholakwa chake, amene alibe mtima wachinyengo.” (Sal. 32:1, 2) Chilango chimene Davide analandira chinamuthandiza kusintha ndi kukhala m’busa wabwino kwambiri wa anthu a Mulungu.

Nthawi zambiri, abale amene amayambanso kutumikira monga akulu amakhala abusa abwino kwambiri kuposa poyamba. M’bale wina amene akutumikiranso monga mkulu anati: “Panopa ndimadziwa bwino kuthandiza anthu amene alakwitsa zinthu.” Mkulu wina anati: “Tsopano ndimayamikira kwambiri mwayi wanga wotumikira abale.”

KODI NANUNSO MUNGABWERERE?

Wamasalimo analemba kuti: “[Yehova] sadzakhalira kutiimba mlandu nthawi zonse chifukwa cha zolakwa zathu.” (Sal. 103:9) Choncho tisamaganize kuti Mulungu sangakhulupirirenso munthu amene analakwitsa zinazake. M’bale wina dzina lake Ricardo anauzidwa kuti aime kaye atatumikira monga mkulu kwa zaka zambiri. Iye anati: “Zinkandipweteka kwambiri ndikaganizira zimene ndinalakwitsa. Ndinkangodziona kuti ndine wosayeneranso kutumikira abale monga woyang’anira. Ndinkadzikayikira ndipo ndinkaona kuti anthu sangandikhulupirirenso. Koma popeza ndimakonda kuthandiza ena, ndinkachititsabe maphunziro a Baibulo, kulimbikitsa abale pa Nyumba ya Ufumu komanso kulalikira limodzi ndi ena. Zinthu zimenezi zinandithandiza kuti ndisiye kudzikayikira ndipo ndinayambiranso kutumikira monga mkulu.”

Yehova wathandiza abale ena kuti ayambirenso kusangalala komanso kukhala ndi mtima wofuna kutumikiranso

Kukwiya kungalepheretse munthu kuti ayambirenso kutumikira. Choncho ndi bwino kutengera chitsanzo cha Davide. Iye anathawa pamene Sauli ankafuna kumupha chifukwa cha nsanje. Koma Davide anakana kupha Sauli mpata utapezeka.  (1 Sam. 24:4-7; 26:8-12) Sauli atafa kunkhondo, Davide analira. Iye ananena kuti Sauliyo ndiponso mwana wake Yonatani, anali anthu “okondeka ndi osangalatsa.” (2 Sam. 1:21-23) Izi zikusonyezeratu kuti sanamusungire zifukwa.

Kodi mumaona kuti nkhani yanu sinasamaliridwe mwachilungamo? Ngati ndi choncho, musalole mkwiyo kukusokonezani. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi William wa ku Britain, amene anauzidwa kuti aime kaye atatumikira monga mkulu kwa zaka pafupifupi 30. Iye anasungira zifukwa akulu ena. N’chiyani chinamuthandiza? Iye anati: “Kuwerenga buku la Yobu kunandilimbikitsa kwambiri. Yehova anathandiza Yobu kuti akhazikitse mtendere ndi anzake osathandiza aja. Choncho ndinkaona kuti ngati anathandiza Yobu, akhoza kundithandizanso kuti ndikhale pa mtendere ndi akulu mumpingo.”—Yobu 42:7-9.

YEHOVA AMADALITSA AKULU AMENE AYAMBIRANSO KUTUMIKIRA

Ngati munasiya nokha kutumikira monga mkulu, muyenera kudzifufuza kuti muone zifukwa zimene zinakuchititsani kusiya. Kodi munakumana ndi mavuto enaake? Kapena munayamba kuona zinthu zina kukhala zofunika kwambiri? Kodi mwina pali amene anakukhumudwitsani? Kaya chinachititsa n’chiyani, dziwani kuti pamene munali mkulu, munali ndi mwayi wothandiza anthu kwambiri. Munkawalimbikitsa ndi nkhani zanu ndiponso chitsanzo chanu. Maulendo anu aubusa ankawathandizanso kuti apirire mavuto awo. Pamene munkatumikira mokhulupirika monga mkulu munkasangalatsa Yehova komanso inuyo munkasangalala.—Miy. 27:11.

Mukamapitiriza kutumikira Yehova mosangalala mudzasonyeza kuti mumamukonda kwambiri

Yehova wathandiza abale ena kuti ayambirenso kusangalala komanso kukhala ndi mtima wofuna kutumikira mumpingo. Kaya munasiya nokha kapena anachita kukuuzani kuti muime kaye, mukhoza ‘kuyesetsanso kuti mukhale woyang’anira.’ (1 Tim. 3:1) Paulo ‘sanaleke kupempherera’ Akhristu a ku Kolose kuti akhale odziwa molondola chifuniro cha Mulungu n’cholinga choti ‘aziyenda mogwirizana ndi zimene Yehova amafuna, kuti azimukondweretsa pa chilichonse.’ (Akol. 1:9, 10) Mukayambiranso kutumikira monga mkulu, muzidalira Yehova kuti akuthandizeni kupeza mphamvu, kukhala oleza mtima komanso osangalala. M’masiku otsiriza ano, anthu a Mulungu akufuna kulimbikitsidwa ndi abusa achikondi. Kodi inuyo muyesetsa kuti mulimbikitse abale anu?

^ ndime 3 Mayina ena asinthidwa.