Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Pa Luka 20:34-36, Yesu anauza Asaduki kuti anthu oukitsidwa sadzakwatira kapena kukwatiwa. Kodi pamenepa ankanena za anthu odzakhala padziko lapansi?
Funso limeneli ndi lofunika makamaka kwa anthu amene mwamuna kapena mkazi wawo anamwalira. Anthu oterewa angafunitsitse kudzakhalabe pa banja ndi mnzawoyo m’dziko latsopano. M’bale wina anati: “Ine ndi mkazi wanga sitinasankhe zoti tisiyane. Tonse tinkafunitsitsa kuti tizitumikira Yehova monga banja mpaka muyaya. Sindinasinthe maganizowa mpaka pano.” Koma kodi munthu angachite bwino kuyembekezera kuti anthu oukitsidwa adzakhalanso pa banja? Panopa sitinganene motsimikiza kuti inde kapena ayi.
Kwa zaka zambiri, mabuku athu akhala akunena kuti mawu a Yesu pa Luka 20:34-36 amasonyeza kuti anthu amene adzaukitsidwe n’kukhala padziko lapansi sadzakwatira kapena kukwatiwa. * (Mat. 22:29, 30; Maliko 12:24, 25) Ngakhale kuti sitinganene motsimikiza, kodi mwina Yesu ankanena za anthu amene adzapite kumwamba? Tiyeni tione bwinobwino zimene ananena.
Taganizirani zimene zinachitika kuti Yesu anene mawuwa. (Werengani Luka 20:27-33.) Asaduki, omwe sankakhulupirira zoti akufa adzauka ankafuna kukola Yesu. Iwo anamufunsa za kuuka kwa mkazi komanso anthu 7 apachibale amene anamukwatira. * Yesu anawayankha kuti: “Ana a m’nthawi ino amakwatira ndi kukwatiwa. Koma amene ayesedwa oyenerera kudzapeza moyo pa nthawi imeneyo ndi kudzaukitsidwa kwa akufa sadzakwatira kapena kukwatiwa. Ndiponso iwo sadzafanso, chifukwa adzakhala ngati angelo. Iwo adzakhalanso ana a Mulungu mwa kukhala ana a kuuka kwa akufa.”—Luka 20:34-36.
N’chifukwa chiyani mabuku athu ankanena kuti Yesu ankafotokoza za anthu amene adzakhale padzikoli? Kwenikweni panali zifukwa ziwiri. Choyamba, tinkaona kuti Asadukiwo ayenera kuti ankaganizira za anthu amene adzakhale padzikoli ndiye Yesu ankayankha mogwirizana ndi zimene ankaganizazo. Chachiwiri, Yesu anamaliza yankho lake ponena za anthu akale okhulupirika amene adzakhale padzikoli monga Abulahamu, Isaki ndi Yakobo.—Luka 20:37, 38.
Komabe n’kutheka kuti Yesu ankanena za anthu amene adzapite kumwamba. N’chifukwa chiyani tikutero? Tiyeni tikambirane mfundo ziwiri zimene anatchula.
Mfundo yoyamba ndi yakuti: “Amene ayesedwa oyenerera . . . kudzaukitsidwa kwa akufa.” Odzozedwa okhulupirika ndi amene amaonedwa kuti ndi “oyenerera ufumu wa Mulungu.” (2 Ates. 1:5, 11) Iwo amayesedwa olungama chifukwa cha dipo ndipo pamene amwalira amakhala opanda mlandu. (Aroma 5:1, 18; 8:1) Odzozedwawa amatchedwanso ‘odala ndi oyera’ ndipo amaonedwa kuti ndi oyenerera kuukitsidwa kuti apite kumwamba. (Chiv. 20:5, 6) Koma m’gulu la anthu amene adzaukitsidwe kuti akhale padzikoli mudzakhalanso anthu “osalungama.” (Mac. 24:15) Ndiye Yesu sakananena kuti anthuwo ndi “amene ayesedwa oyenerera” kuti aukitsidwe.
Mfundo yachiwiri ndi yakuti: “Iwo sadzafanso.” Mawu a Yesu amenewa akutanthauza kuti n’zosatheka kuti anthu amenewa afenso. M’Mabaibulo ena, mawuwa amawamasulira kuti “sangathe kufanso” kapena kuti “imfa ilibenso mphamvu pa iwo.” Choncho odzozedwa amene amakhala okhulupirika mpaka imfa, amaukitsidwa kupita kumwamba n’kupatsidwa moyo umene sungafe kapena kuwonongeka. (1 Akor. 15:53, 54) Imfa imakhala kuti ilibenso mphamvu pa anthu amene apita kumwamba. *
Ndiye malinga ndi zimene takambiranazi, kodi tinganene kuti chiyani? N’kutheka kuti pamene Yesu ankanena zoti oukitsidwa sadzakwatira kapena kukwatiwa ankanena za anthu opita kumwambawa. Ngati ndi choncho, ndiye kuti mawu akewa akutithandiza kudziwa zinthu zingapo zokhudza anthu opita kumwamba. Anati iwo sadzakwatira kapena kukwatiwa, sangafe komanso adzakhala ngati angelo kumwamba. Koma mfundo yoti ankanena za opita kumwamba ingabweretsenso mafunso ena.
Funso loyamba ndi lakuti: N’chifukwa chiyani Yesu ankanena za anthu opita kumwamba pamene Asaduki omwe ankafunsawo ayenera kuti ankaganizira za anthu odzakhala padziko lapansi? Kumbukirani kuti nthawi zina Yesu sankayankha anthu mogwirizana ndi maganizo awo. Mwachitsanzo, Ayuda atamuuza kuti awapatse chizindikiro, iye ananena kuti: “Gwetsani kachisi uyu, ndipo ine ndidzamumanga m’masiku atatu.” Yesu ayenera kuti ankadziwa kuti anthuwo aganiza za kachisi weniweni koma “iye anali kunena za kachisi wa thupi lake.” (Yoh. 2:18-21) Choncho mwina pamene Asaduki ongofuna kumukolawo anamufunsa, Yesu anaona kuti palibe chifukwa chowayankhira mogwirizana ndi maganizo awo. Iwo sankakhulupirira zoti akufa adzauka komanso zoti kuli angelo. (Miy. 23:9; Mat. 7:6; Mac. 23:8) Koma n’kutheka kuti iye ankafuna kufotokozera ophunzira ake okhulupirika mfundo zoona zokhudza anthu amene adzapite kumwamba podziwa kuti iwowo akhoza kudzapeza mwayiwu.
Funso lachiwiri ndi lakuti: N’chifukwa chiyani m’mawu ake omaliza, Yesu anatchula Abulahamu, Isaki ndi Yakobo, omwe adzakhale padzikoli? (Werengani Mateyu 22:31, 32.) Onani kuti Yesu asanatchule anthuwo, ananena mawu akuti “kunena za kuuka kwa akufa.” Mwina mawuwa akusonyeza kuti Yesu ankafuna kusiya nkhani ya opita kumwamba n’kuyamba kufotokoza za amene adzaukitsidwe kuti akhale padzikoli. Ndiyeno, anagwiritsa ntchito mawu amene Yehova anauza Mose, omwe Asadukiwo ankawakhulupirira. Iye anachita zimenezi kuti apereke umboni woti Yehova ali ndi cholinga choukitsa anthu kuti akhale padziko lapansi.—Eks. 3:1-6.
Funso lachitatu ndi lakuti: Ngati mawu a Yesu pa Luka 20:34-36 akunena za anthu amene adzapite kumwamba, kodi zikutanthauza kuti anthu amene adzaukitsidwe kuti akhale padzikoli adzakwatira kapena kukwatiwa? Mawu a Mulungu sayankha funsoli mwachindunji. Ngati Yesu ankanena za anthu amene adzapite kumwamba ndiye kuti mawu ake sakutiuza chilichonse za anthu amene adzaukitsidwe kuti akhale padziko lapansi.
Komabe timadziwa kuti Mawu a Mulungu amanena kuti mwamuna kapena mkazi akamwalira, wotsalayo amamasuka. Choncho wotsalayo sayenera kudziimba mlandu ngati akufuna kukwatiranso kapena kukwatiwanso. Aliyense ayenera kusankha yekha pa nkhaniyi. Ngati munthu wasankha kulowanso m’banja, anthu ena sayenera kumutsutsa.—Aroma 7:2, 3; 1 Akor. 7:39.
N’zoona kuti tingakhale ndi mafunso ambiri okhudza zimene zidzachitike m’dziko latsopano. Koma m’malo mongopereka mayankho oyerekezera, tiyeni tingoyembekezera. Koma chimene sitikukayikira n’chakuti: Anthu omvera Yehova adzakhala osangalala chifukwa iye adzawapatsa zonse zimene amakhumba.—Sal. 145:16.
^ ndime 4 Onani Nsanja ya Olonda ya June 1, 1987, tsamba 30 ndi 31.
^ ndime 5 Kalelo mwamuna akamwalira opanda mwana wamwamuna, m’bale wake ankachita chokolo kapena kuti ukwati wa pachilamu. Ankachita zimenezi n’cholinga choti abereke mwana wamwamuna woti apitirize dzina la m’bale wakeyo.—Gen. 38:8; Deut. 25:5, 6.
^ ndime 9 Koma anthu amene adzaukitsidwe kuti akhale padzikoli adzakhala ndi moyo wosatha osati moyo umene sungafe kapena kuwonongeka. Kuti muone kusiyana pakati pa moyo wosatha ndi moyo umene sungafe kapena kuwonongeka, werengani Nsanja ya Olonda yachingelezi ya April 1, 1984, tsamba 30 ndi 31.