NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) September 2014
Magaziniyi ili ndi nkhani zophunzira kuyambira pa October 27 mpaka November 30, 2014.
Kodi ‘Mukuyesetsa Kuti Mukhale Woyang’anira’?
Kodi mungatani kuti muyesetse kukhala woyang’anira?
N’chiyani Chimakutsimikizirani Kuti Muli M’gulu la Yehova?
Nkhaniyi ikufotokoza zinthu zina zimene zimachititsa anthu ambiri kukhulupirira kuti Mboni za Yehova ndi Akhristu enieni. Ikufotokozanso zinthu zina zimene zathandiza a Mboni ena kudziwa kuti ali m’gulu la Yehova.
Tumikirani Mulungu Mokhulupirika Ngakhale Kuti Mukukumana ndi “Masautso Ambiri”
Anthu onse amakumana ndi mavuto m’dziko la Satanali. Kodi Satana amagwiritsa ntchito njira ziti pofuna kusokoneza anthu? Kodi tingakonzekere bwanji?
Makolo, Muzisamalira Bwino Ana Anu
Makolo ali ndi udindo wolera ana awo “m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aefeso 6:4) Nkhaniyi ikufotokoza zinthu zitatu zimene zingathandize makolo kusamalira bwino ana awo n’cholinga choti azikonda Yehova.
Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Kodi mawu a pa Salimo 37:25 komanso a pa Mateyu 6:33 amasonyeza kuti Yehova sadzalola kuti Mkhristu avutike ndi njala?
Mdani Wathu Womalizira Adzawonongedwa
Imfa imavutitsa kwambiri anthu. N’chifukwa chiyani anthu amafa? Kodi imfa idzawonongedwa bwanji? (1 Akorinto 15:26) Werengani kuti mupeze mayankho osonyeza kuti Yehova ndi wachilungamo, wanzeru komanso wachikondi.
Muzikumbukira Atumiki a Nthawi Zonse
Anthu a Yehova ambiri amachita khama mu utumiki wa nthawi zonse. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakumbukira ‘ntchito zachikhulupiriro ndi ntchito zachikondi’ zimene amagwira?—1 Atesalonika 1:3.