Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chiyani Chimakutsimikizirani Kuti Muli M’gulu la Yehova?

N’chiyani Chimakutsimikizirani Kuti Muli M’gulu la Yehova?

“Muzindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.”—AROMA 12:2.

1. Kodi atsogoleri a matchalitchi achita chiyani pa nthawi ya nkhondo?

PA ZAKA 100 zapitazi, anthu ambiri amene amadzitcha Akhristu akhala akumenya nkhondo n’kumapha anzawo. Mwachitsanzo, atsogoleri achikatolika akhala akudalitsa asilikali ndiponso zida zawo zankhondo kuti akamenyane ndi Akatolika anzawo a m’mayiko ena. Atsogoleri achipulotesitanti akhala akuchitanso zimenezi. Zoterezi zinachitika pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse ndipo anthu ambirimbiri anaphedwa. Koma kodi Mulungu amafuna kuti Akhristu oona azimenya nkhondo n’kumapha anthu a m’mayiko ena?

2, 3. Kodi a Mboni za Yehova anachita chiyani pa nthawi ya nkhondo, ndipo n’chifukwa chiyani?

2 Kodi a Mboni za Yehova anachita chiyani pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse? Iwo sanalowerere chifukwa chakuti amatsatira chitsanzo cha Yesu ndiponso zimene anaphunzitsa. Iye anati: “Onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.” (Yoh. 13:35) Anatsatiranso mfundo ya m’mawu a Paulo m’kalata imene analembera Akhristu a ku Korinto.—Werengani 2 Akorinto 10:3, 4.

3 Choncho Akhristu oona amene amatsatira mfundo za m’Baibulo samenya nawo nkhondo. Chifukwa cha zimenezi, Akhristu ambirimbiri azunzidwa kapena kutsekeredwa m’ndende. Ena a iwo ndi achinyamata, ena okalamba, ena amuna ndipo ena akazi. Pa nthawi ya ulamuliro wa chipani cha Nazi ku Germany, Akhristu ena anaphedwa. Ngakhale kuti anazunzidwa kwambiri, Akhristuwo sanasiye kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Yehova. Iwo anagwira ntchitoyi mokhulupirika atatsekeredwa m’ndende kapena kuthamangitsidwa m’dziko lawo. * Mu 1994, a Mboni sanalowererenso nkhondo yapachiweniweni ku Rwanda. Posachedwapanso, sanamenye nawo nkhondo yoopsa imene inachitika m’dziko limene linkatchedwa Yugoslavia.

4. Kodi anthu azindikira chiyani poona kuti a Mboni salowerera nkhondo?

4 Popeza a Mboni za Yehova salowerera nkhondo, anthu ambiri padziko lonse azindikira kuti a Mboni amakondadi Mulungu ndiponso anzawo. Kapena tinganene kuti iwo azindikira zoti a Mboni ndi Akhristu enieni. Koma pali zinthu zinanso zimene timachita zomwe zathandiza anthu kuzindikira kuti Mboni za Yehova ndi Akhristu enieni.

NTCHITO YAIKULU KWAMBIRI YOPHUNZITSA ANTHU

5. N’chiyani chinachitika Chikhristu chitangoyamba?

5 Pa utumiki wake wonse padzikoli, Yesu ankalimbikitsa anthu kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Iye anasankha ophunzira 12 kuti ayambe nawo ntchito yolalikirayi. Kenako anaphunzitsa anthu ena 70. (Luka 6:13; 10:1) Anthuwa anawathandiza kuti azilalikira uthenga wabwino. Poyamba anawauza kuti azilalikira Ayuda okha koma kenako anafunika kusintha n’kumalalikiranso anthu a mitundu ina. Akhristu achiyuda anafunika kusintha kwambiri maganizo awo kuti athe kuchita zimenezi.—Mac. 1:8.

6. Kodi Petulo anazindikira bwanji kuti Yehova alibe tsankho?

6 Mtumwi Petulo anauzidwa kuti apite kwa Koneliyo. Munthuyu sanali Myuda ndipo anali wosadulidwa. Petulo anazindikira kuti Mulungu alibe tsankho. Koneliyo ndi anthu amene anali m’nyumba mwake anabatizidwa ndipo ichi chinali chiyambi choti uthenga wabwino ulalikidwe kwa anthu a mitundu yonse padziko lonse lapansi.—Mac. 10:9-48.

7, 8. Kodi gulu la Mboni za Yehova likuchita zotani? (Onani chithunzi patsamba 7.)

7 Masiku anonso, anthu amene akutsogolera gulu la Yehova amalimbikitsa kwambiri ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu padziko lonse. Panopa, a Mboni pafupifupi 8 miliyoni akugwira ntchitoyi mwakhama m’zilankhulo zoposa 600 ndipo adzayambanso m’zilankhulo zina posachedwapa. A Mboni za Yehova amadziwika kuti amalalikira kunyumba ndi nyumba ndiponso mumsewu. Nthawi zina akamalalikira amaika mabuku awo m’matebulo kapena m’mashelefu amatayala.

8 Pali anthu oposa 2,900 amene aphunzitsidwa ntchito yomasulira Baibulo ndiponso mabuku m’zilankhulo zosiyanasiyana. Zilankhulo zina n’zosadziwika kwa anthu ena koma zimalankhulidwa ndi anthu ambiri. Mwachitsanzo, ku Spain kuli anthu mamiliyoni amene chilankhulo chawo ndi Chikatalani. Posachedwapa, anthu ayamba kugwiritsa ntchito kwambiri chilankhulochi ku Alicante ndi Valencia, kuzilumba za Balearic ndiponso m’dziko la Andorra. Masiku ano, a Mboni za Yehova amafalitsa mabuku a Chikatalani ndipo misonkhano imachitikanso m’chilankhulochi moti anthu akusangalala kwambiri.

9, 10. N’chiyani chikusonyeza kuti gulu la Mulungu limafuna kuti anthu onse amve uthenga wabwino?

9 Ntchito yomasulira mabuku komanso kuphunzitsa anthu m’zilankhulo zawo ikuchitika m’mayiko osiyanasiyana. Mwachitsanzo, chilankhulo chachikulu ku Mexico ndi Chisipanishi koma kuli anthu ambiri ndithu a zilankhulo zina. M’dzikoli muli anthu ena amene chilankhulo chawo ndi Chimaya. Ofesi ya nthambi ya kumeneku inakonza zoti omasulira m’chilankhulochi azikakhala kudera limene chimalankhulidwa kwambiri. Chitsanzo china ndi cha ku Nepal. M’dzikoli muli anthu oposa 29 miliyoni ndipo kuli zilankhulo zoposa 120. Chilankhulo cha anthu oposa 10 miliyoni m’dzikoli ndi Chinepali ndipo pali enanso ambiri amene amachilankhula. Mabuku athu akumasuliridwanso m’chilankhulochi.

10 Zimene omasulirawa akuchita zikusonyezeratu kuti gulu la Yehova limaona kuti ntchito yolalikira padziko lonse ndi yofunika kwambiri. Anthu padziko lonse akhala akupatsidwa kwaulere timapepala, timabuku ndiponso magazini ambirimbiri. Ndalama zoyendetsera ntchitoyi ndi zimene a Mboni za Yehova amapereka mwakufuna kwawo. Iwo amatsatira malangizo a Yesu akuti: “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.”—Mat. 10:8.

Omasulira mabuku m’chilankhulo cha kumpoto kwa Germany(Onani ndime 10)

Mabuku a m’chilankhulo cha kumpoto kwa Germany akuthandiza kwambiri m’dziko la Paraguay (Onaninso chithunzi patsamba 7)

11, 12. Kodi ntchito imene a Mboni za Yehova akugwira padziko lonse yathandiza bwanji anthu?

11 A Mboni za Yehova amachita khama kwambiri polalikira ndiponso kuphunzitsa. Iwo amadziwa kuti gulu la Yehova ndi lomweli ndipo amachita zonse zimene angathe kuti azilalikira kwa anthu a mitundu yonse. Ena ayamba moyo wosalira zambiri, ena aphunzira chilankhulo china ndipo ena asamukira m’mayiko ena n’cholinga choti achite zambiri pa ntchitoyi. Ntchito yolalikira padziko lonse yathandizanso anthu ambiri kudziwa kuti a Mboni za Yehova ndi Akhristu enieni.

12 A Mboni amachita zonsezi chifukwa chokhulupirira ndi mtima wonse kuti zimene aphunzira m’Baibulo ndi zoona. Koma kodi ndi zinthu zinanso ziti zimene zachititsa anthu kukhulupirira kuti a Mboni za Yehova ndi Akhristu enieni?—Werengani Aroma 14:17, 18.

ZIMENE ZIMACHITITSA ANTHU ENA KUKHULUPIRIRA

13. Kodi a Mboni amachita chiyani kuti gulu lawo likhale loyera?

13 Akhristu ambiri odzipereka amakhulupirira ndi mtima wonse kuti ali m’gulu la Yehova ndipo zimene iwo ananena zingatithandize. M’bale wina amene watumikira Yehova kwa nthawi yaitali anati: “A Mboni amayesetsa kwambiri kuti gulu la Yehova likhale loyera. Amapereka malangizo kapena kudzudzula aliyense amene sakuchita bwino.” Amachita zimenezi chifukwa chotsatira mfundo za m’Mawu a Mulungu komanso chitsanzo cha Yesu ndi ophunzira ake. Anthu ena ochepa achotsedwa m’gulu la Yehova chifukwa chokana kutsatira mfundo za Mulungu. Koma anthu ambiri amapitiriza kukhala ndi makhalidwe abwino. Ena a iwo poyamba sanali ndi makhalidwe abwino koma anasintha n’kumatsatira mfundo za Mulungu.—Werengani 1 Akorinto 6:9-11.

14. (a) Kodi anthu ambiri amene anachotsedwa achita chiyani? (b) Kodi zotsatira zake n’zotani?

14 Kodi anthu ambiri amene anachotsedwa achita chiyani? Ambiri alapa ndipo alandiridwanso mumpingo. (Werengani 2 Akorinto 2:6-8.) Kutsatira mfundo zapamwamba za m’Baibulo kwathandiza kuti mpingo ukhale woyera ndiponso wosakayikitsa. Chifukwa cha zimenezi, anthu ambiri akhulupirira kuti a Mboni ndi Akhristu enieni ndipo ndi osiyana kwambiri ndi anthu a m’matchalitchi amene amalekerera makhalidwe oipa.

15. N’chiyani chathandiza m’bale wina kutsimikizira kuti ali m’gulu la Yehova?

15 N’chiyani chimachititsa a Mboni ena kudziwa kuti ali m’gulu la Yehova? M’bale wina wazaka za m’ma 50 anati: “Pali zinthu zitatu zimene ndakhala ndikuzikhulupirira kuyambira ndili wachinyamata. Zinthu zake n’zakuti: (1) Mulungu alipo, (2) Baibulo ndi lochokera kwa Mulungu ndiponso (3) Mulungu akugwiritsa ntchito mpingo wa Mboni za Yehova ndipo akuudalitsa. Ndikamaphunzira Baibulo ndimayesetsa kuonanso ngati ndili ndi zifukwa zomveka zoti ndizikhulupirirabe zinthu zitatuzi. Ndiyeno chaka chilichonse ndimapeza umboni winanso wondithandiza kukhulupirira kwambiri zinthuzi ndipo sindikayikira kuti gulu la Yehova ndi lomweli.”

16. N’chifukwa chiyani mlongo wina anayamikira gulu la Yehova?

16 Mlongo wina amene akutumikira kulikulu lathu ku New York anayamikira gulu la Yehova. Iye ananena kuti ndi gulu lokhali limene limalengeza za dzina la Yehova. Anati izi n’zomveka chifukwa chakuti dzinali limapezeka m’Baibulo maulendo oposa 7,000. Anafotokozanso kuti amalimbikitsidwa akamva mfundo ya pa 2 Mbiri 16:9 yakuti: “Maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.” Mlongoyu anati: “Mfundo zimene ndaphunzira zimandithandiza kukhala wokhulupirika n’cholinga choti Yehova aonetse mphamvu zake kwa ineyo. Ndimaona kuti ubwenzi wanga ndi Yehova ndi chinthu chofunika kwambiri. Ndimayamikiranso kwambiri zimene Yesu amachita potithandiza kuti tidziwe bwino Mulungu.”

17. Kodi munthu wina amene sankakhulupirira zoti kuli Mulungu anati chiyani?

17 Munthu wina amene kale sankakhulupirira zoti kuli Mulungu ananena kuti: “Zimene Mulungu analenga zimapereka umboni wakuti iye amafuna kuti anthufe tizisangalala ndipo sangalole kuti mavuto azingopitirirabe. Panopa dzikoli likuipiraipirabe koma chikhulupiriro cha anthu a Yehova chikulimbabe, chikondi chawo chikuwonjezereka ndipo akuchita khama kwambiri. Mzimu wa Yehova ndi umene ukuthandiza kuti zimenezi zichitike.”—Werengani 1 Petulo 4:1-4.

18. Kodi inuyo mukumva bwanji ndi zimene abale awiriwa ananena?

18 M’bale wina amene watumikira Yehova kwa nthawi yaitali sakayikira zoti mfundo zimene timalalikira ndi zoona. Iye anati: “Zimene ndaphunzira pa zaka zonsezi zanditsimikizira kuti Mboni za Yehova zimayesetsa kutsanzira Akhristu oyambirira. Ndayenda m’mayiko osiyanasiyana ndipo ndadzionera ndekha umboni wakuti a Mboni za Yehova ndi ogwirizana pa dziko lonse. Mfundo zimene ndaphunzira m’Baibulo zandithandiza kukhala wosangalala.” M’bale wina wa zaka zoposa 60 anapemphedwa kuti anene zimene zimamutsimikizira kuti alidi m’gulu la Yehova. Poyankha, ananena kuti chifukwa chakuti a Mboni za Yehovafe timakhulupirira kwambiri Yesu Khristu. Iye anafotokoza kuti: “Taphunzira za moyo wa Yesu komanso utumiki wake. Taonanso kuti iye anatisiyira chitsanzo chabwino kwambiri. Tayesetsa kwambiri kusintha moyo wathu kuti tiyandikane ndi Mulungu kudzera mwa Yesu Khristu. Tikudziwa kuti tidzapulumuka chifukwa cha nsembe ya dipo ya Khristu. Tikudziwanso kuti Yesu anaukitsidwa chifukwa pali umboni wa anthu ambiri amene anamuona atauka.”—Werengani 1 Akorinto 15:3-8.

KODI TIYENERA KUCHITA CHIYANI?

19, 20. (a) Kodi Paulo analimbikitsa abale a ku Roma kuchita chiyani? (b) Kodi Akhristufe tili ndi mwayi wotani?

19 Akhristufe timakonda anzathu, choncho timayesetsa kuuza ena mfundo zoona zimene taphunzira. Paulo anauza abale a mumpingo wa ku Roma kuti: “Ngati ukulengeza kwa anthu ‘mawu amene ali m’kamwa mwakowo,’ akuti Yesu ndiye Ambuye, ndipo mumtima mwako ukukhulupirira kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka. Munthu amakhala ndi chikhulupiriro mumtima mwake kuti akhale wolungama, koma ndi pakamwa pake amalengeza poyera chikhulupiriro chake kuti apulumuke.”—Aroma 10:9, 10.

20 Tonsefe amene tadzipereka kwa Yehova sitikayikira kuti tili m’gulu lake ndipo tili ndi mwayi wouza ena uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Choncho tikamalalikira tiyenera kusonyeza kuti timakhulupirira kwambiri mfundo za m’Baibulo zimene timaphunzitsa anthu. Tikamatero, anthu ambiri adzachita chidwi ndi uthenga wathu.

^ ndime 3 Onani buku lakuti Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom, tsamba 191 mpaka 198 ndiponso tsamba 448 mpaka 454.