Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzikumbukira Atumiki a Nthawi Zonse

Muzikumbukira Atumiki a Nthawi Zonse

“Timakumbukira nthawi zonse ntchito zanu zachikhulupiriro, ndi ntchito zanu zachikondi.”—1 ATES. 1:3.

1. Kodi Paulo anati bwanji za anthu otumikira Yehova mwakhama?

MTUMWI Paulo ankakumbukira anthu amene ankathandiza kwambiri pa ntchito yolalikira uthenga wabwino. Iye analemba kuti: “Timakumbukira nthawi zonse ntchito zanu zachikhulupiriro, ndi ntchito zanu zachikondi. Timateronso pokumbukira mmene munapiririra chifukwa cha chiyembekezo chanu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu wathu ndi Atate.” (1 Ates. 1:3) Nayenso Yehova saiwala anthu amene amachita khama pomutumikira. Amatero ngakhale anthuwo atachita zochepa chifukwa cha mmene zinthu zilili pa moyo wawo.—Aheb. 6:10.

2. Kodi tikambirana chiyani m’nkhaniyi?

2 Kuyambira kale, pali anthu ambirimbiri amene amadzipereka kwambiri n’cholinga choti achite utumiki wa nthawi zonse. M’nkhaniyi tikambirana za anthu amene anachita zimenezi m’nthawi ya atumwi komanso amene akuchita utumikiwu masiku ano. Tikambirananso zimene tingachite pothandiza anthu odziperekawa.

AKHRISTU A NTHAWI YA ATUMWI

3, 4. (a)  Kodi anthu ena ankatumikira bwanji Yehova nthawi ya atumwi? (b) Kodi ankapeza bwanji zofunika pa moyo?

3 Yesu atangobatizidwa, anayambitsa ntchito yofunika kugwiridwa mpaka kufika padziko lonse. (Luka 3:21-23; 4:14, 15, 43) Iye ataphedwa, atumwi ake ankatsogolera pa ntchitoyi. (Mac. 5:42; 6:7) Akhristu ena monga Filipo anali amishonale ku Palesitina. (Mac. 8:5, 40; 21:8) Koma Paulo ndiponso anthu ena anakalalikira kumadera akutali. (Mac. 13:2-4; 14:26; 2 Akor. 1:19) Anthu ena monga Silivano (kapena kuti Sila), Maliko ndiponso Luka ankagwira ntchito yolemba kapena yokopera mabuku. (1 Pet. 5:12) Panalinso alongo ena amene ankagwira ntchito ndi abale okhulupirikawa. (Mac. 18:26; Aroma 16:1, 2) Timasangalala kwambiri tikamawerenga m’Malemba Achigiriki nkhani za anthu amenewa. Nkhani zawo zimasonyezanso kuti Yehova amakumbukira zimene atumiki ake amachita.

4 Kodi atumiki a nthawi zonse akale ankapeza bwanji zofunika pa moyo? Nthawi zina, Akhristu anzawo ankawachereza kapena kuwapatsa zinthu koma atumikiwo sankapempha thandizo. (1 Akor. 9:11-15) Mipingo ina komanso anthu ena ankawathandiza mofunitsitsa. (Werengani Machitidwe 16:14, 15; Afilipi 4:15-18.) Koma nthawi zina, Paulo ndi anzake ankagwiranso ntchito kuti azipeza kangachepe.

ATUMIKI A NTHAWI ZONSE A MASIKU ANO

5. Kodi banja lina linati chiyani ponena za utumiki wa nthawi zonse?

5 Masiku anonso, anthu ambiri amachita khama potumikira Yehova m’njira zosiyanasiyana. (Onani bokosi lakuti “ Njira Zina Zochitira Utumiki wa Nthawi Zonse.”) Kodi iwo amamva bwanji akamachita utumikiwu? Mungachite bwino kuwafunsa nokha funso limeneli ndipo zimene angakuuzeni zingakuthandizeni kwambiri. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene m’bale wina ananena. M’baleyu watumikirapo monga mpainiya wokhazikika, mpainiya wapadera, mmishonale ndiponso watumikira ku Beteli ya m’dziko lina. Iye anati: “Ndinachita bwino kwambiri kusankha utumiki wa nthawi zonse. Pamene ndinali ndi zaka 18, ndinkavutika kusankha zochita. Ndinali ndi mwayi wopita kuyunivesite komanso woyamba ntchito yabwino koma ndinasankha upainiya. Ndadzionera ndekha kuti Yehova saiwala zimene timachita pofuna kuti tizimutumikira. Ndakhala ndikugwiritsa ntchito mphamvu zanga komanso luso langa m’njira yabwino kwambiri. Zimenezi sizikanatheka ndikanasankha ntchito zina m’dzikoli.” Mkazi wake anati: “Utumiki uliwonse umene ndakhala ndikuchita wandithandiza kwambiri. Taona Yehova akutiteteza komanso kutitsogolera m’njira zosiyanasiyana. Ngati tikanaopa kuchita utumiki wa nthawi zonse, mwayi umenewu sitikanaupeza. Tsiku lililonse ndimayamikira Yehova chifukwa chotilola kuchita utumiki umenewu.” Kodi inuyo simungakonde kuchita utumikiwu n’kumamva chonchi mumtima mwanu?

6. N’chifukwa chiyani sitikayikira zoti Yehova amayamikira zimene timachita pomutumikira?

6 N’zoona kuti anthu ena panopa sangakwanitse kuchita utumiki wa nthawi zonse. Koma tiyenera kudziwa kuti Yehova amayamikiranso kwambiri zimene iwo amachita pomutumikira ndi mtima wonse. Taganizirani za anthu amene Paulo anawayamikira pa Filimoni 1 mpaka 3. (Werengani.) Taonani kuti iye ananenanso za anthu onse amene ankasonkhana mumpingo wa Kolose ndipo anawayamikira. Yehova ankawayamikiranso. Dziwani kuti Atate wathu wakumwamba amayamikiranso zimene inuyo mumachita pomutumikira. Koma kodi mungathandize bwanji anthu amene akuchita utumiki wa nthawi zonse?

MUZITHANDIZA APAINIYA

7, 8. (a)  Kodi apainiya amachita zotani? (b) Kodi anthu ena mumpingo angathandize bwanji apainiya?

7 Mofanana ndi atumiki a nthawi ya atumwi, apainiya akhama amalimbikitsa kwambiri anthu mumpingo. Apainiya ambiri amayesetsa kulalikira maola 70 pa mwezi. Koma kodi mungawathandize bwanji?

8 Mlongo wina dzina lake Shari akuchita upainiya ndipo anati: “Apainiya amaoneka kuti ndi olimba chifukwa amakhala mu utumiki tsiku lililonse. Komabe, amafunikira kulimbikitsidwa.” (Aroma 1:11, 12) Mlongo wina amene anali mpainiya kwa zaka zambiri anafotokoza za apainiya mumpingo wawo. Iye anati: “Nthawi zonse amagwira ntchito mwakhama. Iwo amayamikira kwambiri anthu akamayenda nawo mu utumiki, kuwaitanira chakudya kapena kuwapatsa ndalama. Anthu akamachita zimenezi amasonyeza kuti amaganizira apainiyawo.”

9, 10. Kodi anthu ena achita chiyani pothandiza apainiya mumpingo wawo?

9 Kodi mungafune kuthandiza apainiya mu utumiki? Mpainiya wina dzina lake Bobbi anati: “Timasowa anthu oyenda nawo mkati mwa mlungu.” Mpainiya wina mumpingo wawo ananenanso kuti: “Zimavuta kwambiri kupeza anthu oyenda nawo masana.” Mlongo wina amene panopa akutumikira ku Beteli ku Brooklyn anafotokoza za nthawi imene anali mpainiya. Iye anati: “Mlongo wina amene anali ndi galimoto anandiuza kuti, ‘Mukasowa munthu woyenda naye, muzingondiimbira kuti titsagane.’ Iye anandithandiza kwambiri kuti ndipitirize upainiya.” Shari anati: “Apainiya amene sali pa banja nthawi zambiri amakhala okhaokha akaweruka mu utumiki. Mukhoza kuitana abale kapena alongo amenewa kuti adzachite nanu Kulambira kwa Pabanja. Kuwaitana kuti mudzachite nawo zinthu zosiyanasiyana kumawathandiza kukhalabe olimba.”

10 Mlongo wina amene wakhala mu utumiki wa nthawi zonse kwa zaka pafupifupi 50 ankachita upainiya ndi alongo ena osakwatiwa. Ponena za nthawi imeneyo, iye anati: “Akulu mumpingo wathu ankayendera apainiya pakangopita miyezi yochepa. Iwo ankatifunsa za moyo wathu komanso ntchito yathu kapena ngati tinali ndi nkhawa zina. Zinkaonekeratu kuti amatiganizira. Iwo ankabwera kudzaona nyumba yathu n’cholinga choti adziwe ngati angatithandize chilichonse.” Zimenezi zikufanana ndi zimene anachita Onesiforo. Iye ankasamalira banja lake komanso kuthandiza mtumwi Paulo.—2 Tim. 1:18.

11. Kodi apainiya apadera amachita zotani?

11 Mipingo ina ili ndi mwayi wokhala ndi apainiya apadera. Ambiri a apainiyawa amayesetsa kuti akwanitse maola 130 pa mwezi. Chifukwa cha kutanganidwa mu utumiki komanso pothandiza mumpingo, nthawi yogwira ntchito imakhala yochepa kapena sipezeka n’komwe. Ofesi ya nthambi imawapatsa ndalama zochepa n’cholinga choti utumiki wawo usasokonezeke.

12. Kodi akulu komanso anthu ena angathandize bwanji apainiya apadera?

12 Kodi tingathandize bwanji apainiya apadera? Mkulu wina amene amatumikira ku ofesi ya nthambi amalankhulana ndi apainiya apadera ambiri. Iye anati: “Akulu ayenera kucheza nawo kuti adziwe mavuto awo ndiponso zimene angachite powathandiza. Abale ndi alongo ena amaganiza kuti apainiya apadera sasowa kanthu chifukwa amalandira ndalama. Koma zoona zake n’zakuti amafunika kuwathandizabe m’njira zosiyanasiyana.” Mofanana ndi apainiya okhazikika, apainiya apadera amayamikira kwambiri akakhala ndi anthu oyenda nawo mu utumiki. Kodi nanunso mungamayende nawo?

MUZITHANDIZA OYANG’ANIRA MADERA

13, 14. (a)  Kodi tiyenera kukumbukira chiyani za oyang’anira madera? (b) Kodi inuyo mukufuna kuchita chiyani powathandiza?

13 Anthu ambiri amaona kuti oyang’anira madera ndi akazi awo ndi olimba kwambiri. N’zoona kuti amakhala olimba koma amafunanso kuti tiziwalimbikitsa, kuyenda nawo mu utumiki komanso kucheza nawo. Nthawi zina angadwale, kugonekedwa kuchipatala kapena kuchitidwa opaleshoni. Abale ndi alongo akamawaona pa nthawi imeneyi kapena kuwathandiza m’njira zina amayamikira kwambiri. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Luka yemwe analemba buku la Machitidwe. Iye anali “dokotala wokondedwa” ndipo ayenera kuti ankathandiza kwambiri Paulo ndi anzake amene ankayenda nawo.—Akol. 4:14; Mac. 20:5–21:18.

14 Oyang’anira madera ndi akazi awo amafunanso kukhala ndi anzawo apamtima. Woyang’anira dera wina analemba kuti: “Anzanga amadziwa ngati ndikufunika kulimbikitsidwa. Amandifunsa mafunso mwanzeru ndipo izi zimandithandiza kuti ndifotokoze zimene zikundidetsa nkhawa. Iwo amamvetsera bwino ndikamafotokoza ndipo zimenezi zimandilimbikitsa kwambiri.” Oyang’anira madera ndi akazi awo amayamikira kwambiri ngati abale ndi alongo amasonyeza kuti amawakonda.

MUZITHANDIZA OTUMIKIRA PA BETELI

15, 16. Kodi anthu otumikira pa Beteli amagwira ntchito ziti, nanga tingawathandize bwanji?

15 Padziko lonse, anthu otumikira pa Beteli amathandiza kwambiri pa ntchito za Ufumu m’gawo la nthambi yawo. Kodi mumpingo wanu kapena m’dera lanu muli anthu otumikira pa Beteli? Kodi anthu amenewa mungawathandize bwanji?

16 Anthuwa akangofika kumene pa Beteli, amasowa achibale awo komanso anzawo. Choncho zimakhala bwino ngati anthu ena pa Betelipo kapena kumpingo umene amapita amacheza nawo. (Maliko 10:29, 30) Otumikira pa Beteli amakhala ndi mpata wopezeka pa misonkhano komanso kulalikira mlungu uliwonse. Koma nthawi zina amapatsidwa ntchito zina moti sangapite kumpingo. Zingakhale zolimbikitsa ngati abale ndi alongo mumpingo amamvetsa zimenezi komanso kuyamikira atumikiwa chifukwa cha ntchito zimene amagwira.—Werengani 1 Atesalonika 2:9.

MUZITHANDIZA ATUMIKI OCHOKERA M’MAYIKO ENA

17, 18. Kodi anthu amene asamukira m’mayiko ena amagwira ntchito ziti?

17 Abale ndi alongo amene amakatumikira m’mayiko ena amakumana ndi mavuto ena. Tikutero chifukwa chakuti zinthu monga zakudya, zilankhulo ndi zikhalidwe zimakhala zosiyana. Ndiyeno n’chifukwa chiyani abale ndi alongo amalolera kupita kumayiko ena?

18 Ena amakhala amishonale ndipo amagwira ntchito kwambiri mu utumiki n’kumathandiza anthu ndi zimene anaphunzira. Ofesi ya nthambi imapatsa amishonale malo ogona komanso ndalama zogulira zinthu zofunika pa moyo. Anthu ena akapita m’mayiko ena amakatumikira pa nthambi. Ena amathandiza pa ntchito yomanga maofesi a nthambi, maofesi a omasulira mabuku, malo a misonkhano komanso Nyumba za Ufumu. Anthu amenewanso amapatsidwa chakudya, malo ogona komanso zinthu zina zofunika pa moyo. Mofanana ndi otumikira pa Beteli, iwo amasonkhana komanso kulalikira ndi mipingo ya kumene akutumikirako. Choncho tingati amathandiza m’njira zambiri.

19. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timaganizira anthu ochokera m’mayiko ena?

19 Kodi tingasonyeze bwanji kuti timaganizira anthu ochokera m’mayiko ena? Choyamba, tiyenera kukumbukira kuti chakudya chimene tinazolowera chingakhale chachilendo kwa iwo. Choncho tikawaitana kuti adzadye kunyumba kwathu, ndi bwino kuwafunsa zimene amakonda kapena zimene angafune kulawa. Tiyeneranso kuleza nawo mtima ngati akuvutika kuphunzira chilankhulo kapena kuzolowera chikhalidwe. Mwina poyamba sangamvetse zimene tikunena komanso angavutike kutchula mawu ena, choncho tiyenera kuwathandiza. Chofunika n’kukumbukira kuti anthuwo ali ndi mtima wofuna kuphunzira.

20. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakumbukira atumiki a nthawi zonse komanso makolo awo?

20 Atumiki a nthawi zonse kapena makolo awo amakalamba. Ndiyeno makolo omwe ndi Mboni amafuna kuti ana awo asasiye utumiki wawo. (3 Yoh. 4) N’zoona kuti atumiki a nthawi zonse amachita zonse zimene angathe makolo awo akafunika thandizo ndipo amayesetsa kupita kukawasamalira pafupipafupi. Koma anthu akwawo angathandize atumikiwa kusamalira makolo awo. Muzikumbukira kuti atumiki a nthawi zonsewa akuthandiza kwambiri pa ntchito yofunika kuposa ina iliyonse. (Mat. 28:19, 20) Kodi inuyo kapena mpingo wanu mungathandize kusamalira makolo a atumiki ena a nthawi zonse?

21. Kodi atumiki a nthawi zonse amamva bwanji akathandizidwa kapena kulimbikitsidwa?

21 Anthu amayamba utumiki wa nthawi zonse kuti atumikire Yehova komanso athandize anthu osati kuti apeze ndalama. Choncho amayamikira mukamawathandiza. Mlongo wina amene akutumikira m’dziko lina anati: “Kungolandira kakalata kokuyamikira kumasonyeza kuti anthu ena amakuganizira komanso amasangalala ndi zimene ukuchita.”

22. N’chifukwa chiyani tinganene kuti utumiki wa nthawi zonse ndi wabwino?

22 Kuchita utumiki wa nthawi zonse ndi kosangalatsa kuposa chilichonse chimene munthu angachite m’dzikoli. N’zoona kuti si zophweka koma munthu amaphunzira zambiri komanso amakhala wosangalala. Tingati munthu amakhala akukonzekera utumiki wosangalatsa umene tonsefe tizidzachita m’dziko latsopano. Tiyeni ‘tizikumbukira nthawi zonse ntchito zachikhulupiriro ndi ntchito zachikondi’ zimene atumiki a nthawi zonse amagwira.—1 Ates. 1:3.