Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tumikirani Mulungu Mokhulupirika Ngakhale Kuti Mukukumana ndi “Masautso Ambiri”

Tumikirani Mulungu Mokhulupirika Ngakhale Kuti Mukukumana ndi “Masautso Ambiri”

“Tiyenera kukumana ndi masautso ambiri kuti tikalowe mu ufumu wa Mulungu.”—MAC. 14:22.

1. N’chifukwa chiyani atumiki a Mulungu sadabwa akakumana ndi masautso?

SITIYENERA kudabwa ndi “masautso ambiri” amene tizikumana nawo tisanalandire mphoto ya moyo wosatha. Kaya tangoyamba kumene kutumikira Yehova kapena tamutumikira kwa nthawi yaitali, timadziwa kuti m’dziko la Satanali tonsefe timakumana ndi mavuto.—Chiv. 12:12.

2. (a) Kuwonjezera pa mavuto amene amagwera anthu onse, kodi Akhristu amakumana ndi masautso ati? (Onani chithunzi pamwambapa.) (b) Kodi ndi ndani amene amachititsa kuti tizizunzidwa? (c) Kodi timadziwa bwanji kuti ndi iyeyo amene amachititsa?

2 Kuwonjezera pa mavuto amene amagwera anthu onse, Akhristu amakumana ndi masautso ena. (1 Akor. 10:13) Kodi masautso ake ndi ati? Iwo amazunzidwa kwambiri chifukwa chotsatira malamulo a Mulungu. Yesu anauza otsatira ake kuti: “Kapolo sali wamkulu kuposa mbuye wake. Ngati anazunza ine, inunso adzakuzunzani.” (Yoh. 15:20) Kodi ndi ndani amene amachititsa kuti Akhristu azizunzidwa? Si winanso koma Satana. Baibulo limanena kuti iye ali ngati “mkango wobangula” umene ukufuna kuti “umeze” anthu a Mulungu. (1 Pet. 5:8) Satana amagwiritsa ntchito njira iliyonse imene akuona kuti ingamuthandize kusokoneza Akhristu. Mwachitsanzo, tiyeni tione zimene zinachitikira mtumwi Paulo.

PAULO ANAZUNZIDWA KU LUSITARA

3-5. (a) Kodi Paulo anakumana ndi mavuto ati ku Lusitara? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti mawu ake onena za masautso anali olimbikitsa?

3 Paulo ankazunzidwa chifukwa cha chikhulupiriro chake. (2 Akor. 11:23-27) Kwina kumene anazunzidwa ndi ku Lusitara. Paulo ndi Baranaba ali kumeneku anachiritsa munthu amene anabadwa wolumala. Atangotero, anthu anayamba kuwatamanda ngati kuti iwowo ndi milungu. Atumwiwa anachita kuchonderera anthuwo kuti asawalambire. Koma pasanapite nthawi, kunafika Ayuda ena amene ananena mabodza okhudza atumwiwo. Ndiye zitangotero kunaipiratu. Anthuwo anaponya Paulo miyala n’kumusiya poganiza kuti wafa.—Mac. 14:8-19.

4 Paulo ndi Baranaba atachoka ku Debe “anabwerera ku Lusitara, ku Ikoniyo ndi ku Antiokeya. M’malo onsewa anali kulimbitsa mitima ya ophunzira ndi kuwalimbikitsa kuti akhalebe m’chikhulupiriro. Anali kuwauza kuti: ‘Tiyenera kukumana ndi masautso ambiri kuti tikalowe mu ufumu wa Mulungu.’” (Mac. 14:21, 22) Mwinatu mukudabwa ndi mawu amene ananenawa. Tikutero chifukwa chakuti mfundo yoti tiyenera kukumana ndi “masautso ambiri” ikuoneka kuti ndi yosalimbikitsa. Ndiye zinatheka bwanji kuti Paulo ndi Baranaba ‘alimbitse mitima ya ophunzira’ powauza kuti ayenera kukumana ndi masautso?

5 Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tione bwinobwino mawu a Paulo pa lembali. Iye sanangonena kuti: “Tiyenera kukumana ndi masautso ambiri,” n’kuimira pomwepo. M’malomwake anati: “Tiyenera kukumana ndi masautso ambiri kuti tikalowe mu ufumu wa Mulungu.” Choncho Paulo analimbikitsa anzakewo powauza zinthu zabwino zimene zingachitike akakhalabe okhulupirika. Zimene ankanenazi sizinali nkhambakamwa chabe. Paja Yesu ananenanso kuti: “Yekhayo amene adzapirire mpaka pa mapeto ndi amene adzapulumuke.”Mat. 10:22.

6. Kodi anthu akapirira adzalandira mphoto iti?

6 Ifenso tikapirira tidzalandira mphoto. Odzozedwa adzalandira mphoto yokalamulira ndi Yesu kumwamba. Koma a “nkhosa zina” adzalandira moyo wosatha padziko lapansi “ndipo mmenemo mudzakhala chilungamo.” (Yoh. 10:16; 2 Pet. 3:13) Koma monga Paulo ananenera, tizikumana ndi masautso ambiri tisanalandire mphotoyo. Tiyeni tikambirane mitundu iwiri ya masautso imene tingakumane nayo.

AKHRISTU AMAZUNZIDWA

7. Kodi masautso ena amene Akhristu angakumane nawo ndi ati?

7 Yesu ananeneratu kuti: “Anthu adzakuperekani kumakhoti aang’ono, ndipo adzakukwapulani m’masunagoge ndi kukuimikani pamaso pa abwanamkubwa ndi mafumu.” (Maliko 13:9) Mawuwa akusonyeza kuti masautso ena amene Akhristu angakumane nawo ndi kuzunzidwa. Ndipo atsogoleri achipembedzo kapena andale ndi amene angayambitse zimenezi. (Mac. 5:27, 28) Koma taganiziraninso za chitsanzo cha Paulo. Kodi iye anabwerera m’mbuyo chifukwa chodziwa kuti azunzidwa? Ayi.—Werengani Machitidwe 20:22, 23.

8, 9. (a) Kodi Paulo anasonyeza bwanji kuti anali wotsimikiza kupirira masautso? (b) Kodi masiku anonso anthu asonyeza bwanji mtima wa Paulowu?

8 Satana anachititsa kuti Paulo azunzidwe. Koma iye analimba mtima n’kunena kuti: “Moyo wanga sindikuuona ngati wofunika kapena wamtengo wapatali kwa ine ayi. Chimene ndikungofuna n’chakuti ndimalize kuthamanga mpikisano umenewu, komanso kuti ndimalize utumiki umene ndinalandira kwa Ambuye Yesu basi. Ndikungofuna kuchitira umboni mokwanira za uthenga wabwino wa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.” (Mac. 20:24) Zikuonekeratu kuti Paulo sankachita mantha chifukwa chodziwa kuti azunzidwa. M’malomwake, anatsimikiza mumtima kuti apirira masautsowo zivute zitani. Zimene ankafunitsitsa kwambiri ndi “kuchitira umboni mokwanira” ngakhale atakumana ndi masautso.

9 Masiku ano, abale ndi alongo ambiri amasonyeza mtima womwewu. Mwachitsanzo, m’dziko lina a Mboni ena anapirira atatsekeredwa m’ndende kwa zaka pafupifupi 20 chifukwa chokana usilikali. Mlandu wawo sunapite kukhoti chifukwa boma la dzikoli linalibe malamulo oteteza anthu okana kulowa usilikali. Ali kundendeko, anzawo ndiponso achibale awo ankakanizidwa kudzawaona. Ndipo ena ankamenyedwa kapena kuzunzidwa m’njira zina.

10. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuopa tikakumana ndi masautso mwadzidzidzi?

10 Abale athu kumadera ena amapirira masautso amene amabwera mwadzidzidzi. Izi zikakuchitikirani, musachite mantha. Taganizirani za Yosefe. Iye anagulitsidwa kuti akhale kapolo koma Yehova “anamulanditsa m’masautso ake onse.” (Mac. 7:9, 10) Yehova angakuthandizeninso. Musaiwale kuti “Yehova amadziwa kupulumutsa anthu odzipereka kwa iye akakhala pa mayesero.” (2 Pet. 2:9) Kodi mupitiriza kudalira Yehova podziwa kuti iye angakupulumutseni m’dziko loipali n’kukupatsani moyo wosatha mu Ufumu wake? Palitu zifukwa zomveka zokuchititsani kumudalira, kupirira ndiponso kulimba mtima mukamazunzidwa.—1 Pet. 5:8, 9.

NJIRA ZINA ZIMENE SATANA AMAGWIRITSA NTCHITO

11. Kodi njira zina zimene Satana amagwiritsa ntchito zimasiyana bwanji ndi kuzunzidwa?

11 Masautso ena amene timakumana nawo amakhala ovuta kuwazindikira. Kodi masautsowa amasiyana bwanji ndi kuzunzidwa? Tikamazunzidwa zimakhala ngati mphepo yamkuntho yabwera n’kuwonongeratu nyumba yathu nthawi imodzi. Koma masautso enawo amakhala ngati chiswe chimene chikudya nyumba yathu pang’onopang’ono mpaka nyumbayo n’kugwa. Vuto ndi lakuti nthawi zina, masautso oterewa timawazindikira zinthu zitavuta kale.

12. (a) Kodi ndi vuto liti limene Satana amafuna kupezerapo mwayi ndipo zimenezi zingakhudze bwanji chikhulupiriro chathu? (b) N’chifukwa chiyani Paulo ankakhumudwa nthawi zina?

12 Satana amafunitsitsa kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova pogwiritsa ntchito mazunzo. Koma angagwiritsenso ntchito njira zina zovuta kuzizindikira zimene zingawononge chikhulupiriro chathu mwapang’onopang’ono. Mwachitsanzo, tikakhumudwa Satana angapezerepo mwayi. Nayenso mtumwi Paulo ananena kuti nthawi zina ankakhumudwa. (Werengani Aroma 7:21-24.) Tonsefe timadziwa kuti Paulo anali Mkhristu wolimba ndipo mwina anali m’bungwe lolamulira. Ndiye zinatheka bwanji kuti azidziona kuti ndi “munthu wovutika”? Paulo ananena kuti ankadziona choncho chifukwa cha zinthu zina zimene ankalakwitsa. Iye ankafunitsitsa kuchita zabwino koma ankaona mphamvu inayake ikumulepheretsa. Ngati nanunso nthawi zina mumavutika ndi maganizo amenewa, mukhoza kulimbikitsidwa kudziwa kuti Paulo ankavutikanso ndi zimenezi.

13, 14. (a) N’chiyani chimachititsa atumiki a Mulungu ena kukhumudwa? (b) Kodi ndi ndani amene amafuna kuti tifooke, ndipo cholinga chake n’chiyani?

13 Nthawi zina, abale ndi alongo amakhumudwa, kuda nkhawa mwinanso kudziona kuti ndi achabechabe. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina amene tangomupatsa dzina loti Deborah. Iye ndi mpainiya wakhama kwambiri koma ananena kuti: “Ndimangokhalira kuganizira zimene ndinalakwitsa ndipo zimandipweteka koopsa. Ndikamaganizira zonse zimene ndalakwitsa ndimaona kuti munthu aliyense ngakhalenso Yehova sangandikonde.”

14 N’chiyani chimachititsa atumiki a Yehova monga Deborah kuvutika chonchi? Pangakhale zifukwa zambiri. Mwachibadwa, anthu ena amangodziona kuti ndi osayenera ndipo amadandaula kwambiri ndi mavuto awo. (Miy. 15:15) Koma ena amayamba kudziona choncho chifukwa cha matenda. Kaya chayambitsa n’chiyani, tiyenera kukumbukira amene akufuna kupezerapo mwayi pa vuto lathulo. Satana ndi amene amafuna kuti tikhumudwe mpaka kusiya kutumikira Yehova. Amafuna kuti ifeyo tizidziimba mlandu waukulu ngati umene iyeyo anapalamula. (Chiv. 20:10) Choncho tizikumbukira nthawi zonse cholinga cha Satana. Iye amagwiritsa ntchito mazunzo kapena njira zina n’cholinga choti tikhumudwe n’kufooka mpaka kufika posiya kutumikira Yehova. Anthu onse a Mulungu ayenera kumenya nkhondo mwamphamvu kuti zimenezi zisawachitikire.

15. Kodi tingatani kuti zinthu zokhumudwitsa zisatifooketse?

15 Tiyeni tiziyesetsa kuti tisagonje pa nkhondoyi. Tiziganizira kwambiri mphoto imene tingalandire. Paja Paulo anauza Akhristu a ku Korinto kuti: “Sitikubwerera m’mbuyo. Koma ngakhale munthu wathu wakunja akutha, ndithudi munthu wathu wamkati akukhalitsidwanso watsopano tsiku ndi tsiku. Pakuti ngakhale kuti masautso amene tikukumana nawo ndi akanthawi ndipo ndi opepuka, masautsowo akutichititsa kuti tilandire ulemerero umene ukukulirakulira komanso wamuyaya.”—2 Akor. 4:16, 17.

KONZEKERANI MASAUTSO PANOPA

Akhristu onse amakonzekera kufotokoza zimene amakhulupirira (Onani ndime 16)

16. N’chifukwa chiyani tiyenera kukonzekera masautso panopa?

16 Taona kuti Satana amagwiritsa ntchito “zochita zachinyengo” zosiyanasiyana. (Aef. 6:11) Choncho tonsefe tiyenera kutsatira malangizo a pa 1 Petulo 5:9 akuti: “Khalani olimba m’chikhulupiriro ndipo mulimbane naye.” Kuti tichite zimenezi, tiyenera kudziphunzitsa panopa kuchita zinthu zoyenera. Mwachitsanzo, asilikali amayambiratu kuchita zambiri mwinanso zopweteka n’cholinga choti akhale okonzeka nkhondo ikayamba. Ifenso tiyenera kuchita zimenezi chifukwa ndife asilikali a Yehova. Nafenso sitikudziwa kuti tidzalimbana ndi zinthu zotani m’tsogolo. Choncho ndi nzeru kukonzekera kwambiri panopa chifukwa mpata ndi womwewu. Paulo analembera Akhristu a ku Korinto kuti: “Pitirizani kudziyesa kuti muone ngati mukadali olimba m’chikhulupiriro. Pitirizani kudziyesa kuti mudziwe kuti ndinu munthu wotani.”—2 Akor. 13:5.

17-19. (a) Kodi tingadzifufuze bwanji? (b) Kodi achinyamata angakonzekere bwanji kufotokoza zimene amakhulupirira?

17 Kuti titsatire malangizo a Paulo amenewa tiyenera kudzifufuza. Tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndimapemphera nthawi zonse? Anthu akandikakamiza kuchita zinthu zosayenera, kodi ndimamvera Mulungu kapena anthuwo? Kodi ndimapezeka pa misonkhano yonse? Kodi ndimafotokoza molimba mtima zimene ndimakhulupirira? Kodi ndimayesetsa kumvetsa Akhristu anzanga akalakwitsa zinthu podziwa kuti nanenso ndimalakwitsa? Kodi ndimagonjera anthu amene akutsogolera mumpingo ndiponso m’gulu la Yehova padziko lonse?

18 Pa mafunso apamwambapa, lina ndi lokhudza kufotokoza molimba mtima zimene timakhulupirira ndipo lina ndi lokhudza kusatengera anzathu. Akhristu achinyamata ambiri ayenera kuchita zimenezi kusukulu. Iwo amayesetsa kuti asachite manyazi kapena mantha pouza anthu zimene amakhulupirira. Magazini athu ali ndi mfundo zimene zingathandize pa nkhaniyi. Mwachitsanzo, Galamukani! ya July 2009 imafotokoza zimene wachinyamata angayankhe ngati anzake kusukulu amufunsa mafunso pa nkhani zosiyanasiyana. Makolo ayenera kuyeseza nkhani ngati zimenezi ndi ana awo kuti akhale okonzeka akakumana nazo kusukulu.

19 N’zoona kuti nthawi zina zimakhala zovuta kufotokoza maganizo athu kapena kuchita zimene Yehova amafuna. Tikamaweruka kuntchito timatopa kwambiri ndipo mwina timachita kudzikakamiza kupita kumisonkhano. Kapena timaona kuti n’zovuta kudzuka msanga kuti tikalalikire. Koma kumbukirani kuti ngati mwazolowera kuchita zinthu ngati zimenezi, sizingakuvuteni mukadzakumana ndi mayesero akuluakulu.

20, 21. (a) Kodi kuganizira kwambiri za dipo kungatithandize bwanji? (b) Kodi tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani?

20 Nanga tingatani kuti zinthu zokhumudwitsa zisatifooketse? Chinthu chimodzi chimene chingatithandize ndi kuganizira kwambiri za dipo. Mtumwi Paulo anachita zimenezi. Nthawi zina ankavutika kwambiri maganizo koma ankadziwanso kuti Khristu anafera anthu ochimwa osati angwiro. Ndiye ankaona kuti iye ndi mmodzi mwa ochimwawo ndipo analemba kuti: “Ndikukhala mokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene anandikonda ndi kudzipereka yekha chifukwa cha ine.” (Agal. 2:20) Paulo ankakhulupirira dipo ndipo ankaona kuti linaperekedwa chifukwa cha iye.

21 Kuona kuti dipo ndi mphatso imene Yehova wapereka kwa inuyo kungakuthandizeninso kwambiri. Koma sikuti kukhumudwa kudzatheratu nthawi yomweyo. Mwina ena a ife tizilimbana ndi vutoli mpaka mapeto a dziko loipali. Koma musaiwale kuti anthu amene sataya mtima ndi amene adzalandire mphoto. Nthawi imene Ufumu wa Mulungu udzakhazikitsa mtendere ndiponso kuchotsa uchimo ikuyandikira kwambiri. Choncho yesetsani kuti mudzalowe mu Ufumuwo ngakhale kuti mukukumana ndi masautso ambiri.