Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumayamikira Zimene Muli Nazo?

Kodi Mumayamikira Zimene Muli Nazo?

“[Tinalandira] mzimu wochokera kwa Mulungu, kuti tidziwe zinthu zimene Mulungu watipatsa mokoma mtima.”—1 AKOR. 2:12.

1. Kodi anthu ambiri amalephera kuzindikira chiyani?

PALI mwambi wakuti: “Chitsime chimaoneka kuti ndi chakuya pamene chauma.” Mwambiwu umatanthauza kuti zinthu zina timazindikira ubwino wake zinthuzo zitapita. Nthawi zambiri munthu akakhala ndi zinthu zina kuyambira ali mwana saziyamikira kwenikweni. Mwachitsanzo, munthu amene wabadwira m’banja lolemera sayamikira zinthu zabwino zimene ali nazo. Popeza achinyamata sadziwa zambiri, angalepherenso kuzindikira zinthu zamtengo wapatali kwambiri.

2, 3. (a) Kodi Akhristu achinyamata ayenera kupewa chiyani? (b) N’chiyani chingatithandize kuyamikira zimene tili nazo?

2 Ngati ndinu wachinyamata, kodi mumaona kuti chofunika kwambiri n’chiyani? Anthu ambiri m’dzikoli amaona kuti chofunika ndi kukhala ndi ndalama zambiri, nyumba yabwino kapena zipangizo zamakono. Koma ngati mumaona choncho ndiye kuti mwaiwala zinthu zofunika kwambiri. Chofunika kwambiri ndi kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova koma n’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri saganizira n’komwe zimenezi. Achinyamata amene abadwira m’banja la Mboni sayenera kuiwala kufunika kwa zinthu zokhudza Mulungu zimene makolo awo awaphunzitsa. (Mat. 5:3) Ngati munthu sayamikira zinthu zimenezi akhoza kukumana ndi mavuto aakulu pa moyo wake.

3 Komatu n’zotheka kupewa mavutowa. N’chiyani chingakuthandizeni kuyamikira zimene mwaphunzira zokhudza Yehova? Tiyeni tikambirane zitsanzo za m’Baibulo zimene zingatithandize kuzindikira ubwino woyamikira zinthuzo. Zitsanzozi zingatithandize tonsefe kuyamikira zinthu zimene tili nazo.

ANTHU ENA SANAYAMIKIRE

4. Kodi lemba la 1 Samueli 8:1-5 limasonyeza kuti ana a Samueli anali otani?

4 Pali zitsanzo za m’Baibulo za anthu ena amene sankayamikira zinthu zokhudza Yehova. Zoterezi zinachitika m’banja la mneneri Samueli ngakhale kuti iye anatumikira Yehova mokhulupirika kuyambira ali mwana. (1 Sam. 12:1-5) Iye anali ndi ana ndipo mayina awo anali Yoweli ndi Abiya. Anawo anayenera kuyamikira chitsanzo cha bambo awo. Koma sanawatsanzire ndipo ankachita zoipa. Mwachitsanzo, Baibulo limati iwo ‘ankapotoza chiweruzo.’—Werengani 1 Samueli 8:1-5.

5, 6. Kodi ana a Yosiya komanso chidzukulu chake anali anthu otani?

5 Ndi mmene zinalilinso ndi ana a Mfumu Yosiya. Mfumuyi inapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yolambira Yehova. Pa nthawi ina, buku la Chilamulo linapezeka ndipo iye atamva zimene zinali m’bukulo anayesetsa kutsatira malangizo a Mulungu. Anagwira ntchito mwakhama pochotsa mafano ndi kukhulupirira mizimu mu Isiraeli. Iye analimbikitsa anthu kuti azimvera Yehova. (2 Maf. 22:8; 23:2, 3, 12-15, 24, 25) Apatu ana ake anayenera kuphunzirapo kanthu. Atatu mwa anawo anadzakhala mafumu koma palibe ngakhale mmodzi amene anatengera chitsanzo cha Yosiya.

6 Woyamba kulowa ufumu wa bambo ake anali Yehoahazi koma ‘ankachita zoipa pamaso pa Yehova.’ Iye anangolamulira miyezi itatu kenako n’kumangidwa ndi Farao wa ku Iguputo moti anafera ku ukapolo. (2 Maf. 23:31-34) Kenako m’bale wake dzina lake Yehoyakimu analamulira kwa zaka 11. Nayenso sanatengere bambo ake. Chifukwa cha zoipa zimene Yehoyakimu ankachita, Yeremiya analosera kuti: “Adzaikidwa m’manda ngati mmene amaikira bulu wamphongo.” (Yer. 22:17-19) Ndiyeno anadzalowedwa m’malo ndi mwana wina dzina lake Zedekiya kenako mdzukulu wake dzina lake Yehoyakini. Koma onsewa sanatsatire chitsanzo cha Yosiya.—2 Maf. 24:8, 9, 18, 19.

7, 8. (a) Kodi Solomo anasonyeza bwanji kuti sanayamikire zimene anaphunzitsidwa? (b) Kodi tikuphunzira chiyani kwa anthu amene sanayamikire zimene anaphunzitsidwa?

7 Nayenso Solomo anaphunzitsidwa zinthu zambiri ndi Davide. Poyamba, Solomo anali munthu wabwino kwambiri koma kenako anasiya kuyamikira zimene anaphunzitsidwa. Baibulo limati: “Pamene iye anali kukalamba, akazi ake anali atapotoza mtima wake moti iye anali kutsatira milungu ina. Sanatumikire Yehova Mulungu wake ndi mtima wathunthu monga mmene anachitira Davide bambo ake.” (1 Maf. 11:4) Izi zinasokoneza ubwenzi wake ndi Yehova.

8 N’zomvetsa chisoni kuti anthu onse amene takambiranawa anaphunzitsidwa bwino ndi makolo awo koma sanayamikire zimene anaphunzitsidwazo. Koma pali ana ena amene ankayamikira zimene anaphunzitsidwa. Masiku anonso ana oterowo alipo. Tiyeni tsopano tikambirane za anthu ena amene achinyamata angachite bwino kuwatsanzira.

ANTHU ENA ANAYAMIKIRA

9. Kodi ana a Nowa anapereka bwanji chitsanzo chabwino? (Onani chithunzi patsamba 27.)

9 Ana a Nowa anapereka chitsanzo chabwino kwambiri. Nowa anauzidwa kuti apange chingalawa choti alowemo limodzi ndi banja lake. Zikuoneka kuti ana a Nowa anazindikira kufunika kochita zimene Yehova ananena ndiponso kugwirizana ndi bambo awo. Iwo anawathandiza kupanga chingalawacho ndipo analowamo. (Gen. 7:1, 7) Onse analowa m’chingalawamo kuti apulumuke. Komanso lemba la Genesis 7:3 limati analowetsamo zinyama “kuti zisungike padziko lonse lapansi.” Ana a Nowa ankayamikira zimene bambo awo anawaphunzitsa. Chifukwa cha zimenezi, anali ndi mwayi wothandiza kuti anthu apulumuke komanso kuti kulambira koona kuyambirenso pambuyo poti dziko layeretsedwa.—Gen. 8:20; 9:18, 19.

10. Kodi anyamata 4 achiheberi anasonyeza bwanji kuti ankayamikira zimene anaphunzira zokhudza Yehova?

10 Patapita zaka zambiri, panali anyamata 4 achiheberi omwe anasonyeza kuti ankayamikira zimene anaphunzitsidwa ndi makolo awo. Hananiya, Misayeli, Azariya ndi Danieli anatengedwa kupita ku Babulo mu 617 B.C.E. Iwo anali anyamata ooneka bwino komanso anzeru ndipo zinali zosavuta kuti zinthu ziziwayendera bwino ku Babulo. Koma iwo ankakumbukira zimene makolo awo anawaphunzitsa. Anyamatawa anadalitsidwa kwambiri chifukwa chotsatira zinthu zimene anaphunzira zokhudza Yehova.—Werengani Danieli 1:8, 11-15, 20.

11. Kodi Yesu anathandiza bwanji anthu ndi zimene iye anaphunzira?

11 Tiyeni tsopano tikambirane chitsanzo chabwino kwambiri cha Yesu. Iye anaphunzira zinthu zambiri kwa Atate wake ndipo ankaziyamikira kwambiri. Yesu anasonyeza zimenezi pamene anati: “Ndimalankhula zinthu izi ndendende mmene Atate anandiphunzitsira.” (Yoh. 8:28) Ankafunanso kuti athandize anthu ena ndi zimene anaphunzirazo. Iye anauza anthu kuti: “Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu kumizinda inanso, chifukwa ndi zimene anandituma kudzachita.” (Luka 4:18, 43) Anathandizanso anthu kudziwa kuti sayenera kukhala “mbali ya dzikoli.” Anatero chifukwa anthu ambiri m’dzikoli sayamikira zinthu zokhudza Yehova.—Yoh. 15:19.

TIZIYAMIKIRA ZIMENE TILI NAZO

12. (a) Malinga ndi 2 Timoteyo 3:14-17, kodi achinyamata ambiri akufanana bwanji ndi Timoteyo? (b) Kodi achinyamata ayenera kudzifunsa mafunso ati?

12 Mwina inunso makolo anu amatumikira Yehova mokhulupirika ndipo akuphunzitsani zambiri. Ngati ndi choncho ndiye kuti mukufanana ndi Timoteyo. (Werengani 2 Timoteyo 3:14-17.) Makolo anuwo ‘anakuphunzitsani’ za Mulungu woona komanso zimene mungachite kuti muzimusangalatsa. N’kutheka kuti anayamba kuchita zimenezi kuyambira muli wakhanda. Mfundo zimene anakuphunzitsanizo zingachititse kuti mukhale ndi “nzeru zokuthandizani kuti mudzapulumuke kudzera m’chikhulupiriro chokhudza Khristu Yesu.” Zingachititsenso kuti mukhale ‘okonzeka mokwanira’ kutumikira Mulungu. Komano funso ndi lakuti: Kodi mudzayamikira zimene akuphunzitsanizo? Ndi bwino kudzifufuza bwinobwino pa nkhaniyi. Mwina mungadzifunse kuti: ‘Kodi ndimamva bwanji ndikaganizira za atumiki a Mulungu okhulupirika a m’mbuyomu? Kodi ndimayamikira mwayi wokhala wa Mboni za Yehova? Kodi ndimayamikira kukhala m’gulu la anthu ochepa amene Mulungu amawaona kuti ndi anzake? Kodi ndimaona kuti zimene ndili nazo panopa ndi zamtengo wapatali kwambiri?’

Kodi mumamva bwanji mukaganizira mwayi wokhala m’gulu la anthu a Yehova okhulupirika?(Onani ndime 9, 10 ndi 12)

13, 14. (a) Kodi achinyamata ena amasirira chiyani? (b) N’chifukwa chiyani si nzeru kutengeka ndi dzikoli? Perekani chitsanzo.

13 Achinyamata ena a m’banja la Mboni sazindikira mwayi umene ali nawo chifukwa chokhala m’gulu la Yehova moti amasirira zochitika za m’dziko loipali. Ndiye mwina tifunse chonchi: Kodi inuyo mungathamangire galimoto kuti ikugundeni pongofuna kuona ngati ingakuvulazeni kapena kukuphani? Ngati mwayankha kuti ayi, ndiye palibenso chifukwa choti ‘muzithamanga nawo m’chithaphwi cha makhalidwe oipa’ a m’dzikoli pongofuna kuona ngati zingabweretsedi mavuto.—1 Pet. 4:4.

14 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mnyamata wina dzina lake Gener. Iye amakhala ku Asia ndipo anabadwira m’banja la Mboni. Anabatizidwa ali ndi zaka 12 koma kenako anayamba kusirira moyo wa m’dzikoli. Iye anati: “Ndinkaona kuti m’dzikoli muli ufulu ndiye ndinkafuna kuulawa.” Gener anayamba moyo wachiphamaso. Pamene ankakwanitsa zaka 15, anali atayamba kutengera zochita za anzake. Iye ankamwa mowa komanso kutukwana. Ankapita kocheza ndi anzake ndipo ankachita masewera achiwawa apakompyuta moti ankafika kwawo usiku kwambiri. Koma anadzazindikira kuti zinthu za m’dzikoli ndi zachabechabe ndipo sizithandiza munthu kukhala wosangalala. Iye atabwerera mumpingo anati: “N’zoona kuti ndimakumana ndi mavuto ena koma ndi ochepa kwambiri ndikawayerekezera ndi madalitso amene Yehova wandipatsa.”

15. Kaya makolo athu ndi Mboni kapena ayi, kodi tiyenera kuganizira kwambiri za chiyani?

15 Palinso achinyamata ena mumpingo amene makolo awo si Mboni. Kodi ndinu mmodzi mwa iwo? Dziwani kuti muli ndi mwayi waukulu kwambiri chifukwa chodziwa Mlengi wathu komanso kumutumikira. Kumbukirani kuti padzikoli pali anthu mabiliyoni ambiri koma ndi ochepa amene Yehova wawakoka kuti adziwe mfundo za m’Baibulo. (Yoh. 6:44, 45) Pa anthu 1,000 alionse m’dzikoli, mmodzi yekha ndi amene amadziwa bwino mfundo za m’Malemba. Choncho kaya mwaphunzira Malemba kuchokera kwa makolo anu kapena kwa anthu ena, muyenera kuyamikira kwambiri mwayi wokhala m’gulu la Yehova. (Werengani 1 Akorinto 2:12.) Gener amene tamutchula uja anati: “Zimandivuta kumvetsa ndikaganizira kuti Yehova, yemwe ndi Mwini chilengedwe chonse, amandidziwa ineyo.” (Sal. 8:4) Mlongo wina wa ku Asia komweko anati: “Ana ambiri amasangalala kwambiri ngati amadziwidwa ndi aphunzitsi awo. Ndiye kuli bwanji kudziwidwa ndi Yehova, yemwe ndi Mlangizi wathu wamkulu.”

KODI MUDZACHITA CHIYANI?

16. Kodi achinyamata ayenera kuchita chiyani?

16 Muyenera kutsatira chitsanzo cha atumiki a Yehova okhulupirika a m’mbuyomu. Muziganizira kwambiri mwayi wanu wodziwa Yehova n’kukhala ndi cholinga chomutumikira moyo wanu wonse. Musamangotsatira zimene achinyamata a m’dzikoli akuchita chifukwa akungoyenda dzandidzandi limodzi ndi dziko limene likukawonongekali.—2 Akor. 4:3, 4.

17-19. N’chifukwa chiyani ndi nzeru kukhala osiyana ndi anthu a m’dzikoli?

17 N’zoona kuti kukhala osiyana ndi anthu a m’dzikoli si kophweka koma n’kothandiza. Taganizirani zimene munthu amachita kuti akhale katswiri pa masewera enaake. Iye amayenera kukhala wosiyana ndi anzake. Amapewa zinthu zambiri zomwe zingamuwonongere nthawi yake yophunzira masewerawa. Kulolera kuti akhale wosiyana ndi anzake kumamuthandiza kuti aphunzire kwambiri n’kufika pokhala katswiri.

18 Anthu ambiri m’dzikoli saona patali. Koma mungachite bwino kuganizira za m’tsogolo n’kulolera kukhala osiyana ndi anthuwo. Muzipewa makhalidwe awo oipa komanso zochita zawo zimene zingasokoneze ubwenzi wanu ndi Yehova. Mukatero ‘mudzagwira mwamphamvu moyo weniweniwo.’ (1 Tim. 6:19) Mlongo amene tamutchula kale uja anati: “Ukamayendera mfundo zimene umakhulupirira umakhala wosangalala. Zimasonyeza kuti sutengeka ndi mafunde a m’dziko la Satanali. Koma chofunika kwambiri n’chakuti umadziwa kuti ukusangalatsa Yehova. Ukazindikira zimenezi umasangalala kukhala osiyana ndi anzako.”

19 Munthu amene amangoganizira zapanopa sakhala wosangalala. (Mlal. 9:2, 10) Popeza tikudziwa cholinga cha moyo komanso tikuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha, tiyenera kusankha bwino zochita. Tizipewa kuchita zinthu ngati anthu a m’dzikoli. Tikamatero tidzakhala osangalala kwambiri.—Aef. 4:17; Mal. 3:18.

20, 21. (a) Kodi tikamasankha bwino zochita tingayembekezere chiyani?

20 Tikamasankha bwino zochita tingakhale ndi moyo wosangalala panopa komanso tingayembekezere kudzakhala ndi moyo wosatha. Pali madalitso ambiri amene tikuwayembekezera kuposa amene tingawaganizire. (Mat. 5:5; 19:29; 25:34) Mulungu amapereka madalitso kwa anthu okhawo amene amamumvera. (Werengani 1 Yohane 5:3, 4.) Choncho ndi nzeru kumutumikira mokhulupirika panopa.

21 Mulungu watipatsa madalitso ambiri. Watithandiza kudziwa molondola mfundo za m’Mawu ake zokhudza iye komanso zolinga zake. Tilinso ndi mwayi wodziwika ndi dzina lake komanso wokhala Mboni zake. Mulungu walonjezanso kuti adzatithandiza. (Sal. 118:7) Choncho tiyeni tonsefe tiziyamikira zimene watichitira n’kumasonyeza kuti timafuna kumulemekeza mpaka muyaya.—Aroma 11:33-36; Sal. 33:12.