Kodi Ndi Bwino Kusintha Maganizo Anu?
TIYEREKEZE kuti Akhristu achinyamata akufuna kukaonera filimu inayake. Anzawo kusukulu aionera ndipo akuti ndi yabwino kwambiri. Koma atangoona pachikuto cha filimuyo akupeza zithunzi za zida zoopsa komanso za azimayi osavala bwino. Kodi aionerabe kapena ayi?
Chitsanzochi chikusonyeza kuti zimene timasankha pa nkhani zambiri zimakhudza ubwenzi wathu ndi Yehova. Nthawi zina timafuna kuchita zinthu zina koma pambuyo poziganizira bwinobwino timasintha maganizo. Kodi ndi bwino kuchita zimenezi?
Pa Zinthu Zina si Bwino Kusintha
Tinasankha kudzipereka kwa Yehova ndiponso kubatizidwa chifukwa choti timamukonda kwambiri. Timafunitsitsanso kumutumikira mokhulupirika nthawi zonse. Koma Satana Mdyerekezi akuyesetsa kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova. (Chiv. 12:17) Popeza kuti tasankha kutumikira Yehova ndiponso kumumvera, zingakhale zomvetsa chisoni kwambiri ngati titasintha maganizo athu. Tikutero chifukwa chakuti sitidzapeza moyo wosatha.
Zaka zoposa 2,600 zapitazo, Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo inaimika fano lalikulu kwambiri lagolide ndipo inalamula anthu onse kuti agwade n’kulilambira. Iye anati munthu amene samvera adzaponyedwa m’ng’anjo yoyaka moto. Koma Sadirake, Mesake ndi Abedinego sanagwadire fanolo. Iwo analolera kuika moyo wawo pa ngozi chifukwa anali atasankha kutumikira Yehova mokhulupirika. Choncho anaponyedwa m’ng’anjoyo koma Yehova anawapulumutsa.—Dan. 3:1-27.
Pa nthawi ina, panali lamulo loti munthu wopemphera kwa Mulungu adzaponyedwa m’dzenje la mikango. Koma mneneri Danieli sanasiye chizolowezi chake chopemphera kwa Yehova katatu pa tsiku. Sanasinthe maganizo ake pa nkhani yolambira Mulungu. Ndiyeno Yehova anamupulumutsa m’dzenje la mikango.—Masiku anonso, anthu amene analonjeza kuti adzatumikira Mulungu sasintha maganizo awo. Mwachitsanzo, pasukulu ina ku Africa, achinyamata ena a Mboni za Yehova anakana kulambira mbendera. Aphunzitsi anawaopseza kuti adzawachotsa sukulu. Kenako nduna ya zamaphunziro inafika m’tauniyo n’kukambirana ndi ena mwa achinyamatawo. Iwo anafotokoza mwaulemu koma molimba mtima zimene amakhulupirira ndipo nkhaniyo inathera pomwepo. Panopa abale ndi alongo achinyamata amapita kusukulu popanda kukakamizidwa kuti achite zinthu zosokoneza ubwenzi wawo ndi Yehova.
Chitsanzo china ndi cha Joseph. Mkazi wake anamwalira mwadzidzidzi atadwala khansa. Achibale a Joseph anamvetsa ndiponso analemekeza zimene iye anasankha zokhudza miyambo ya maliro. Koma achibale a mkazi wake si Mboni ndipo ankafuna kuchita miyambo ina imene Mulungu sasangalala nayo. Joseph anati: “Ataona kuti sindikulola, anayesetsa kunyengerera ana anga koma nawonso anakana. Achibalewo ankadziwa kuti sindingalole kuchita mwambo wochezera chifukwa cha zimene ndimakhulupirira. Ankadziwanso kuti mkazi wanga sakanagwirizana ndi mwambowu. Choncho titakambirana kwa nthawi yaitali, anasankha kuti akachitire kwina mwambowu.
Joseph ananenanso kuti: “Pa nthawi yovutayi, ndinachonderera Yehova kuti atithandize kukhalabe okhulupirika. Iye anayankha mapemphero anga ndipo anatithandiza.” Joseph ndi ana ake sanaganize ngakhale pang’ono zosintha maganizo awo.
Pa Zinthu Zina Mukhoza Kusintha
Pambuyo pa Pasika mu 32 C.E., Yesu anafika kuchigawo cha Sidoni ndipo mayi wina wa ku Foinike anabwera ndi dandaulo lake. Anamupempha mobwerezabwereza kuti achiritse mwana wake wamkazi amene anali ndi chiwanda. Poyamba, Yesu sanamuyankhe. Kenako anauza ophunzira ake kuti: “Ine sananditumize kwa wina aliyense koma kwa nkhosa zotayika za nyumba ya Isiraeli.” Mayiyo atapitiriza kupempha, Yesu anati: “Si bwino kutenga chakudya cha ana n’kuponyera tiagalu.” Koma mayiyo anasonyeza kuti ali ndi chikhulupiriro champhamvu ponena kuti: “Inde Ambuye, komatu tiagalu timadya nyenyeswa zakugwa patebulo la ambuye awo.” Zitatero, Yesu anasintha maganizo n’kuchiritsa mwana wa mayiyo.—Mat. 15:21-28.
Pochita zimenezi, Yesu anatsanzira Yehova. Tikutero chifukwa chakuti Yehova amasintha maganizo ngati pali zifukwa zomveka. Mwachitsanzo, Aisiraeli atapanga fano la mwana wang’ombe, Yehova ankafuna kuwapha onse. Koma analolera zimene Mose ananena pochonderera kuti asawaphe.—Eks. 32:7-14.
Nayenso mtumwi Paulo ankatsanzira Yehova ndi Yesu. Pa nthawi ina, iye ankaganiza kuti si bwino kuyenda ndi Yohane Maliko chifukwa chakuti pa ulendo wina waumishonale anawasiya panjira. Koma kenako anadzazindikira kuti Maliko wasintha ndipo akhoza kumuthandiza kwambiri. Choncho Paulo anauza Timoteyo kuti: “Pobwera utengenso 2 Tim. 4:11.
Maliko, pakuti iye ndi wofunika kwa ine chifukwa amandithandiza pa utumiki wanga.”—Kodi ifenso timatsanzira Atate wathu wakumwamba yemwe ndi wachifundo, woleza mtima komanso wachikondi? Nthawi zina ndi bwino kusintha mmene timaonera anthu ena. Yehova ndi Yesu ndi angwiro koma amalolera kusintha maganizo. Ndiye kuli bwanji ifeyo? Tiyeneranso kuganizira mmene zinthu zilili pa moyo wa anthu ena n’kusintha mmene timawaonera.
Nthawi zina timafunika kusintha zolinga zathu potumikira Mulungu. Anthu ena anayamba kalekale kuphunzira Baibulo ndipo amapezeka pa misonkhano koma saganiza zoti abatizidwe. Ena akhoza kukwanitsa upainiya koma sachita. Ndiye pali abale ena amene sayesetsa kuti akhale pa udindo. (1 Tim. 3:1) Kodi inuyo ndi mmodzi mwa anthu amene tatchulawa? Kodi simungasinthe maganizo anu? Yehova akufuna kuti muzisangalala chifukwa chomutumikira komanso kutumikira anzanu.
Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Ella amene akutumikira ku ofesi ina ya nthambi ku Africa. Iye anati: “Nditangofika ku Beteli, sindinkaganiza kuti ndikhalitsa. Ndinkafunitsitsa kutumikira Yehova ndi mtima wonse koma ndinkasowa kwambiri achibale anga. Koma mlongo amene ndinkakhala naye ankandilimbikitsa kwambiri moti ndinaganiza zoti ndikhazikike basi. Panopa ndatumikira kwa zaka 10 ndipo ndikufunitsitsa kukhalabe pa Beteli n’kumatumikira abale ndi alongo anga.”
Pa Zinthu Zina Muyenera Kusintha
Kodi mukukumbukira zimene Mulungu anachita Kaini atakwiya chifukwa cha nsanje? Anamuuza kuti ayenera kusintha n’kuyamba kuchita zabwino. Anamuuzanso kuti agonjetse uchimo umene ‘unamyata pakhomo n’kumamudikirira.’ Kaini sanamvere malangizo a Yehova ndipo sanasinthe maganizo. Iye anapha m’bale wake ndipo tingati anali munthu woyamba kupha mnzake.—Gen. 4:2-8.
Taganiziraninso za Mfumu Uziya. Poyamba, ankamvera Mulungu ndipo anali naye pa ubwenzi wabwino. Koma kenako anayamba kudzikuza. Iye sanali wansembe koma analowa m’kachisi n’kukapereka nsembe. Ansembe anamuuza kuti asachite zimenezo. Koma m’malo mosintha maganizo, “anakwiya kwambiri.” Pamapeto pake, Yehova anamudwalitsa khate.—2 Mbiri 26:3-5, 16-20.
Zimene takambiranazi zikusonyeza kuti pa zinthu zina tiyenera kusintha maganizo. Izi n’zimene M’bale Joachim anayenera kuchita. Iye anabatizidwa mu 1955 koma anadzachotsedwa mu 1978. Analapa pambuyo pa zaka 20 ndipo anabwezeretsedwa. Posachedwapa, mkulu wina anamufunsa chimene chinkamulepheretsa kupempha zoti abwezeretsedwe pa zaka zonsezo. Iye anati: “Ndinali wokula mtima ndipo ndinakwiya. Panopa zimandiwawa kwambiri kuti ndinachita zimenezi. Nthawi yonseyi ndinkadziwa kuti zimene Mboni za Yehova zimaphunzitsa ndi zoona.” Iye anachita bwino kusintha maganizo ake n’kulapa.
Mwina nafenso nthawi zina tiyenera kusintha maganizo athu komanso zochita zathu. Tikalolera kuchita zimenezi tidzasangalatsa Yehova.—Sal. 34:8.