Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tizigwirizana Kwambiri Pamene Mapeto Akuyandikira

Tizigwirizana Kwambiri Pamene Mapeto Akuyandikira

“Ndife ziwalo za thupi limodzi.”—AEF. 4:25.

1, 2. Kodi Mulungu akufuna kuti atumiki ake onse azichita chiyani?

KODI ndinu wachinyamata? Ngati zili choncho, dziwani kuti ndinu wofunika kwambiri m’gulu la Yehova. M’mayiko osiyanasiyana, anthu ambiri amene akubatizidwa ndi achinyamata. N’zolimbikitsa kuti achinyamata ambiri akusankha kutumikira Yehova.

2 Muyenera kuti mumasangalala kucheza ndi achinyamata anzanu. N’zoona kuti tonse timasangalala kucheza ndi anthu amsinkhu wathu. Koma Mulungu amafuna kuti tonsefe tizigwirizana pomulambira ngakhale kuti timasiyana misinkhu komanso kumene tachokera. Mtumwi Paulo analemba kuti Mulungu akufuna kuti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.” (1 Tim. 2:3, 4) Lemba la Chivumbulutso 7:9 limanenanso kuti atumiki a Mulungu amachokera “m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse.”

3, 4. (a) Kodi achinyamata ambiri m’dzikoli ali ndi mtima wotani? (b) Kodi tingatsatire bwanji mfundo ya pa Aefeso 4:25?

3 Achinyamata amene akutumikira Yehova amasiyana kwambiri ndi achinyamata a m’dzikoli. Ambiri amene satumikira Yehova amangoganizira zofuna zawo zokha. Anthu ena ochita kafukufuku ananena kuti achinyamata a masiku ano ndi odzikonda kwambiri. Kalankhulidwe kawo ndi kavalidwe kawo kamasonyeza kuti amanyoza achikulire ndipo amawaona kuti ndi otsalira.

4 Choncho achinyamata amene akutumikira Yehova ayenera kuchita khama kwambiri kuti asatengere mtima umene wafalawu. Pa nthawi ina, Paulo anauza Akhristu anzake kuti apewe ‘kaganizidwe kamene kakugwira ntchito mwa ana a kusamvera.’ (Werengani Aefeso 2:1-3.) Timayamikira kwambiri achinyamata amene amapewa mtima wodzikondawu n’kumagwirizana ndi Akhristu anzawo. Izi zikugwirizana ndi zimene Paulo ananena. Iye anati: “Ndife ziwalo za thupi limodzi.” (Aef. 4:25) Kugwira ntchito mogwirizana n’kofunika kwambiri pamene mapeto a dzikoli akuyandikira. Tiyeni tione zitsanzo zina za m’Baibulo zimene zingatithandize kudziwa kufunika kokhala ogwirizana.

ZITSANZO ZA ANTHU OGWIRIZANA

5, 6. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Loti ndi ana ake awiri?

5 M’mbuyomu, Yehova ankateteza atumiki ake amene ankachita zinthu mogwirizana pa nthawi ya mavuto. M’Baibulo muli zitsanzo zambiri pa nkhaniyi zimene zingatithandize tonsefe kukhala ogwirizana. Chitsanzo choyamba ndi cha Loti.

6 Loti ndi banja lake ankakhala mumzinda wa Sodomu. Ndiyeno zinthu zinavuta pamene Yehova ankafuna kuwononga mzindawu. Angelo a Yehova anauza Loti kuti athawire kumapiri. Anati: “Thawani mupulumutse moyo wanu!” (Gen. 19:12-22) Loti ndi ana ake awiri anachita zinthu mogwirizana n’kuthawa. N’zomvetsa chisoni kuti anthu ena sanagwirizane nawo. Mwachitsanzo, akamwini a Loti ankaganiza kuti Lotiyo ‘akungonena zocheza’ ndipo anaphedwa. (Gen. 19:14) Koma Loti ndi ana ake awiri anapulumuka chifukwa choti anamvera ndiponso anali ogwirizana.

7. Kodi Yehova anathandiza bwanji Aisiraeli amene ankayenda mogwirizana pochoka ku Iguputo?

7 Chitsanzo china ndi cha Aisiraeli. Pa nthawi imene ankachoka ku Iguputo, iwo ankayenda monga gulu limodzi. Sanali m’timagulu tosiyanasiyana toyenda m’njira zawozawo. Atafika panyanja, ‘Mose anatambasula dzanja lake kuloza panyanjapo’ ndipo Yehova anachititsa kuti igawikane. Ndiyeno Mose anawoloka ndi gulu lonse la Aisiraeli osati yekha kapena ndi Aisiraeli ochepa okha. (Eks. 14:21, 22, 29, 30) Anthu onse anachita zinthu mogwirizana ndipo panali “khamu la anthu a mitundu yosiyanasiyana” limene linatsagana nawo. (Eks. 12:38) Kodi chikanachitika n’chiyani ngati kagulu kenakake, mwina ka achinyamata, kakanatengana n’kumadutsa njira ina? Kumenekutu kukanakhala kusaganiza bwino chifukwa Yehova sakanawateteza.—1 Akor. 10:1.

8. Kodi anthu a Mulungu anasonyeza bwanji kugwirizana m’nthawi ya Yehosafati?

8 M’nthawi ya Mfumu Yehosafati, anthu a Mulungu anakumananso ndi mavuto. Kunabwera “khamu lalikulu” la adani ochokera m’madera ozungulira. (2 Mbiri 20:1, 2) Chosangalatsa n’chakuti Aisiraeliwo anadalira Yehova osati mphamvu zawo. (Werengani 2 Mbiri 20:3, 4.) Iwo anachita zinthu mogwirizana osati mmene aliyense ankafunira. Baibulo limati: “Anthu onse a ku Yuda anali ataimirira pamaso pa Yehova, kuphatikizapo akazi awo ndi ana awo, ngakhalenso ana awo ang’onoang’ono.” (2 Mbiri 20:13) Anthu a misinkhu yonse anamvera Yehova mogwirizana ndipo iye anawateteza. (2 Mbiri 20:20-27) Nafenso tiyenera kuchita zimenezi tikakumana ndi mavuto.

9. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Akhristu oyambirira?

9 Akhristu oyambirira ankagwirizananso kwambiri. Mwachitsanzo, pamene Ayuda ndi anthu ena olowa Chiyuda anakhala Akhristu, onse ‘anapitiriza kulabadira zimene atumwi anali kuphunzitsa. Iwo anali kugawana zinthu, kudya chakudya komanso kupemphera.’ (Mac. 2:42) Mgwirizanowu unaonekera kwambiri pamene ankazunzidwa chifukwa ankafunika kuthandizana. (Mac. 4:23, 24) Kunena zoona, kugwirizana kumathandiza kwambiri pakagwa mavuto.

TIZIGWIRIZANA KWAMBIRI PAMENE TSIKU LA YEHOVA LIKUYANDIKIRA

10. Kodi ndi liti pamene kugwirizana kudzakhala kofunika kwambiri?

10 Nthawi yovuta koopsa ikuyandikira ndipo mneneri Yoweli anafotokoza kuopsa kwake. (Yow. 2:1, 2; Zef. 1:14) Pa nthawiyo, anthu a Mulungu adzayenera kukhala ogwirizana kwambiri chifukwa Yesu anati: “Ufumu uliwonse wogawanika umatha.”—Mat. 12:25.

11. Kodi tikuphunzira chiyani pa Salimo 122:3, 4? (Onani chithunzi patsamba 22.)

11 Pa nthawi yovutayi, tidzayenera kukhala ogwirizana kwambiri ngati mmene zinalili mumzinda wa Yerusalemu. Nyumba za mumzindawu zinali zoyandikana kwambiri moti wamasalimo anati Yerusalemu ali ngati “chinthu chimodzi chogwirizana.” Izi zinathandiza kuti anthu ake azitetezana. Kuyandikana kwa nyumbazo kunkaimiranso kugwirizana kwa Aisiraeli pamene mafuko onse ankasonkhana pofuna kulambira Yehova. (Werengani Salimo 122:3, 4.) Choncho ifenso tiyenera kukhala ogwirizana kwambiri masiku ano komanso m’nthawi yovuta imene ikubwerayi.

12. Kodi tidzayenera kuchita chiyani kuti tidzapulumuke tikadzaukiridwa ndi Gogi?

12 M’tsogolomu tidzafunika kukhala ogwirizana kwambiri. Ulosi wa m’chaputala 38 cha Ezekieli umasonyeza kuti “Gogi wa kudziko la Magogi” adzaukira anthu a Mulungu. Pa nthawiyo tisadzalole kuti chilichonse chitilepheretse kukhala ogwirizana. Sidzakhala nthawi yofufuza thandizo kwa anthu a m’dzikoli koma kwa abale athu. Koma sikuti tidzapulumuka chifukwa chongokhala m’gulu la Yehova. Anthu okhawo amene akuitana pa dzina la Yehova ndi amene adzapulumutsidwe. (Yow. 2:32; Mat. 28:20) Ngakhale zili choncho, n’zokayikitsa kuti Yehova angapulumutse anthu amene asiya kugwirizana ndi gulu lake.—Mika 2:12.

13. Kodi achinyamata angaphunzire chiyani pa zimene takambiranazi?

13 Choncho si bwino kutengera mtima wa achinyamata a m’dzikoli amene amangoganizira zawo zokha. Nthawi imene ikubwerayi, tonsefe tidzafunika kudalirana kwambiri. Choncho tiyeni tiyambiretu kukhala ogwirizana kwambiri.

“NDIFE ZIWALO ZA THUPI LIMODZI”

14, 15. (a) N’chifukwa chiyani Yehova amatilimbikitsa kuti tikhale ogwirizana? (b) Kodi Yehova watipatsa malangizo ati otilimbikitsa kukhala ogwirizana?

14 Yehova akutithandiza kuti ‘tizimutumikira mogwirizana.’ (Zef. 3:8, 9) Iye akutiphunzitsa kuti zochita zathu zizigwirizana ndi cholinga chake ‘chosonkhanitsanso zinthu zonse pamodzi mwa Khristu.’ (Werengani Aefeso 1:9, 10.) Iye akufuna kuti anthu onse komanso angelo akhale banja limodzi logwirizana ndipo zimenezi sizingalephereke. Ngati ndinu wachinyamata, kodi mukuona ubwino wochita zinthu mogwirizana ndi gulu la Yehova?

15 Yehova akufuna kuti tiyambe kugwirizana panopa n’cholinga choti tidzakhale ogwirizana mpaka muyaya. Paja Malemba amatilimbikitsa mobwerezabwereza kuti tizisamalirana, tizikondana ndiponso tizilimbikitsana. (1 Akor. 12:25; Aroma 12:10; 1 Ates. 4:18; 5:11) Yehova amadziwa kuti si zapafupi kuti anthu ochimwafe tizigwirizana. N’chifukwa chake amanena kuti tiziyesetsa ‘kukhululukirana ndi mtima wonse.’—Aef. 4:32.

16, 17. (a) Kodi cholinga china cha misonkhano n’chiyani? (b) Kodi achinyamata angaphunzire chiyani kwa Yesu?

16 Yehova watipatsanso misonkhano kuti izitithandiza kukhala ogwirizana. Lemba la Aheberi 10:24, 25 limasonyeza kuti misonkhano imatithandiza kuti “tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino.” Koma lembali limanena kuti tiyenera ‘kuwonjezera kuchita zimenezi makamaka pamene tikuona kuti tsikulo likuyandikira.’

17 Yesu ali kamnyamata ankayamikira kwambiri misonkhano. Iye ali ndi zaka 12 anapita ku msonkhano waukulu limodzi ndi makolo ake. Ndiyeno pa nthawi ina anasowa. Koma sikuti anapita kukasewera ndi anzake. Tikutero chifukwa chakuti makolo ake anamupeza akukambirana mfundo za m’Malemba ndi aphunzitsi a kukachisi.—Luka 2:45-47.

18. Kodi mapemphero amathandiza bwanji kuti tizigwirizana?

18 Kuwonjezera pa kukondana komanso kulimbikitsana pa misonkhano, tiyenera kupemphererana. Kupempherera abale athu kumathandiza kuti tiziwaganizira. Koma si Akhristu achikulire okha amene ayenera kuchita zimenezi. Nanunso achinyamata muyenera kumachita zimenezi kuti muzigwirizana ndi abale ndi alongo anu. Mukatero simudzakhala mbali ya dziko loipa limene likupita posachedwapa.

Tonsefe tiyenera kupempherera abale athu (Onani ndime 18)

TIZISONYEZA KUTI “NDIFE ZIWALO ZA THUPI LIMODZI”

19-21. (a) Kodi timasonyeza bwanji kuti ndife ziwalo za thupi limodzi? Perekani zitsanzo. (b) Kodi mukuphunzira chiyani pa zimene abale ena amachita pakagwa masoka?

19 Anthu a Yehova amachita zinthu mogwirizana ndi mfundo ya pa Aroma 12:5 yakuti tili ngati ziwalo za thupi limodzi. Umboni wake umaonekera pakagwa masoka. Mu December 2011, mphepo yamkuntho inachititsa kuti madzi asefukire kwambiri pachilumba cha Mindanao ku Philippines. Tsiku lina usiku, madziwo anawononga zinthu zambiri m’nyumba zoposa 40,000. Katundu wa m’nyumba za abale ambiri anawonongekanso. Ofesi ya nthambi ya kumeneko inanena kuti: “Tisanakonze makomiti opereka chithandizo, abale ndi alongo ochokera m’madera ena anayamba kuthandiza anzawo”

20 Ku Japan kunachitikanso chivomezi ndipo madzi ambiri anasefukira. Katundu wa abale ndi alongo ambiri anawonongeka ndipo ena katundu wawo yense anawonongeka. Nyumba ya mlongo wina dzina lake Yoshiko inawonongedwanso. Iye ankakhala pa mtunda wa makilomita pafupifupi 40 kuchokera ku Nyumba ya Ufumu. Mlongoyu anati: “Tinadabwa kumva kuti pa tsiku la chivomezichi, woyang’anira dera ndi m’bale winanso anabwera kudzatifufuza.” Iye anamwetulira n’kunenanso kuti: “Tinayamikira kwambiri kuti abale a mumpingo anatilimbikitsa. Komanso tinalandira zovala, nsapato ndi zikwama.” M’bale wina wa m’komiti yopereka chithandizo anati: “Abale ochokera m’madera onse ku Japan ankagwirizana poyesetsa kuthandizana. Abale ena anachoka ku United States kudzathandiza. Atafunsidwa chifukwa chake anabwera kuchokera kutali anati: ‘Timagwirizana ndi abale athu ku Japan ndipo akufunikira thandizo.’” Kodi simunyadira kuti muli m’gulu limene limasamalira kwambiri anthu ake? Tisakayikire kuti Yehova amasangalala kwambiri kuona kuti ndife ogwirizana.

21 M’tsogolomu tikhoza kukumana ndi mavuto aakulu ndipo mwina sitidzatha kulankhulana ndi abale athu m’mayiko ena. Choncho kugwirizana panopa kudzatithandiza kukhala ogwirizana kwambiri pa nthawi imeneyo. Katundu wa mlongo wina dzina lake Fumiko anawonongedwa ndi mvula yamkuntho ku Japan ndipo anati: “Mapeto ali pafupi kwambiri ndipo tiyenera kupitiriza kuthandizana mpaka nthawi imene sipadzakhalanso masoka.”

22. Kodi kukhala ogwirizana ndi Akhristu anzathu kungatithandize bwanji?

22 M’dziko loipali, anthu ndi ogawikana. Koma achinyamata ndi achikulire amene amayesetsa kukhala ogwirizana panopa akukonzekera kuti adzapulumuke dzikoli likamadzawonongedwa. Mulungu wathu adzapulumutsa anthu ake ngati mmene anachitira m’mbuyomu. (Yes. 52:9, 10) Dziwani kuti mukhozanso kudzapulumuka ngati mumayesetsa kukhala ogwirizana ndi anthu a Mulungu. Kuyamikira kwambiri zinthu zimene tili nazo panopa kungatithandizenso kuti tidzapulumuke. Tidzakambirana zimenezi m’nkhani yotsatira.