Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Amadalitsa Anthu Opereka ndi Mtima Wonse

Yehova Amadalitsa Anthu Opereka ndi Mtima Wonse

YEHOVA watilemekeza kwambiri potipatsa ufulu wosankha. Iye amadalitsa kwambiri anthu amene amagwiritsa ntchito bwino ufuluwu. Iwo amagwiritsa ntchito zinthu zawo pomutumikira, pothandiza kuti dzina lake liyeretsedwe komanso pochita zinthu mogwirizana ndi cholinga chake. Yehova safuna kuti tizingomumvera chifukwa cha mantha kapena kunyengereredwa. Iye amafuna kuti tizidzipereka chifukwa chomukonda komanso kuyamikira zimene watichitira.

Mwachitsanzo, Aisiraeli ali m’chipululu cha Sinai, Yehova anawauza kuti amange chihema kuti azimulambiramo. Anati: “Nonse mupereke zopereka kwa Yehova. Aliyense amene ali ndi mtima wofunitsitsa apereke kwa Yehova.” (Eks. 35:5) Mwisiraeli aliyense anayenera kupereka zimene akanakwanitsa. Kaya zoperekazo zinali zochepa kapena zambiri, zikanathandiza pa ntchitoyi. Kodi Aisiraeliwo anatani?

“Aliyense amene anali ndi mtima wofunitsitsa” anapereka zinthu zake. Anthu anabweretsa zinthu monga ndolo, mphete, golide, siliva, mkuwa, ulusi, nsalu, ubweya wa mbuzi, zikopa za nkhosa, zikopa za akatumbu, matabwa a mthethe, miyala yamtengo wapatali ndiponso mafuta. Zinthu zimene anaperekazo “zinali zokwanira pa ntchito yonse yoyenera kuchitika, ndipo zinaposanso zinthu zofunikira pa ntchitoyo.”—Eks. 35:21-24, 27-29; 36:7.

Chimene chinasangalatsa kwambiri Yehova si kuchuluka kwa zinthuzo koma mtima wofunitsitsa umene operekawo anali nawo. Iwo anagwiritsanso ntchito nthawi yawo ndi mphamvu zawo pa ntchitoyi. Baibulo limati: “Akazi onse aluso anawomba nsalu ndi manja awo.” Limanenanso kuti: “Akazi onse aluso amene anali ndi mtima wofunitsitsa anawomba nsalu za ubweya wa mbuzi.” Yehova anathandizanso Bezaleli kuti “akhale wanzeru, wozindikira, wodziwa zinthu, ndi kuti akhale mmisiri waluso pa ntchito ina iliyonse.” Tingati Yehova anapatsa Bezaleli ndi Oholiabu luso limene linkafunika kuti ntchito yonseyo itheke.—Eks. 35:25, 26, 30-35.

Pamene Yehova ankapempha Aisiraeli kuti apereke zinthu zawo, ankadziwa kuti aliyense amene ali ndi “mtima wofunitsitsa” adzathandiza pa ntchito yokhudza kulambirayo. Iwo atapereka, Yehova anawadalitsa kwambiri powatsogolera komanso kuwathandiza kukhala osangalala. Nkhaniyi ikusonyeza kuti Yehova amadalitsa atumiki ake ngati apereka zinthu ndi mtima wonse. Izi zimachititsa kuti pasasowe zinthu kapena anthu aluso othandiza kuti cholinga chake chikwaniritsidwe. (Sal. 34:9) Yehova adzakudalitsaninso mukamadzipereka ndi mtima wonse pomutumikira.