Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’zothekadi Kukwatira Kapena Kukwatiwa “Mwa Ambuye”?

Kodi N’zothekadi Kukwatira Kapena Kukwatiwa “Mwa Ambuye”?

“Sindikupeza m’bale mumpingo ndiye ndikuopa kuti ndikalamba ndisanakwatiwe.”

“Amuna ena m’dzikoli ndi okoma mtima, abwino ndiponso oganizira ena. Satsutsa chipembedzo changa ndipo ndi osangalatsa kuposa abale ena.”

Atumiki a Yehova ena amanena zinthu ngati zimenezi. Iwo amatero ngakhale kuti amadziwa bwino malangizo amene mtumwi Paulo anauza Akhristu onse. Paja iye analemba kuti tiyenera kukwatira kapena kukwatiwa “mwa Ambuye.” (1 Akor. 7:39) Koma n’chifukwa chiyani abale ndi alongowa amanena zinthu ngati zimenezi?

N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHU ENA AMAKAYIKIRA?

Ena amanena zimenezi poona kuti chiwerengero cha alongo n’chachikulu kuposa cha abale. Vutoli ndi la m’mayiko ambiri. Mwachitsanzo, pa Akhristu 100 amene sali pa banja ku Korea, 57 ndi alongo pomwe 43 ndi abale. Ku Colombia, pa Akhristu 100 amene sali pa banja, 66 ndi alongo pomwe 34 ndi abale.

M’mayiko ena vuto limakhala loti makolo omwe si Mboni amafuna ndalama zambiri za malowolo. Ndiyeno abale ena sakwanitsa kupeza ndalamazo. Mavuto amene tatchulawa amachititsa alongo ena kuganiza kuti n’zosatheka kuti “akwatiwe mwa ambuye.” Ndiyeno akhoza kudzifunsa kuti, “Koma n’zothekadi kupeza m’bale mu mpingo?” *

TIYENERA KUDALIRA YEHOVA

Ngati munaganizapo zimenezi, dziwani kuti Yehova amakumvetsani. Iye amadziwa mmene mukumvera mumtima mwanu.—2 Mbiri 6:29, 30.

Komabe Yehova ananena kuti tiyenera kukwatira kapena kukwatiwa mwa Ambuye chifukwa amafunira zabwino atumiki ake. Yehova amafuna kuti atumiki ake azikhala osangalala ndiponso kuti apewe mavuto amene amabwera ngati munthu wasankha njira yolakwika. M’nthawi ya Nehemiya, Ayuda ambiri ankakwatirana ndi anthu a mitundu ina omwe sankatumikira Yehova. Nehemiya anawachenjeza powakumbutsa zimene zinachitikira Solomo. Iye anati ngakhale kuti Solomo “anakondedwa ndi Mulungu wake, . . . akazi achilendo anamuchimwitsa.” (Neh. 13:23-26) Choncho masiku anonso, Mulungu amalangiza atumiki ake kuti azikwatirana ndi Akhristu anzawo okhulupirika n’cholinga choti zinthu ziwayendere bwino. (Sal. 19:7-10; Yes. 48:17, 18) Akhristu okhulupirika amayamikira ndiponso kudalira malangizo anzeru a Yehova. Akhristuwa akamachita zimenezi amasonyeza kuti amakhulupirira zoti Yehova ndi Wolamulira wa Chilengedwe Chonse.—Miy. 1:5.

Kunena zoona, simungafune ‘kumangidwa m’goli’ ndi munthu amene angasokoneze ubwenzi wanu ndi Mulungu. (2 Akor. 6:14) Akhristu ambiri masiku ano atsatira malangizo oteteza amenewa ndipo azindikira kuti ndi othandizadi. Koma ena satsatira.

MALANGIZOWA NDI OTHANDIZABE MASIKU ANO

Mlongo wina wa ku Australia dzina lake Maggy * anafotokoza zimene zinachitika atayamba chibwenzi ndi munthu wosakhulupirira. Iye anati: “Ndinkajomba ku misonkhano yambiri n’cholinga choti ndizicheza naye ndipo ubwenzi wanga ndi Mulungu unasokonekera.” Mlongo wina ku India dzina lake Ratana anayamba chibwenzi ndi mnyamata wa m’kalasi yake yemwe anayamba kuphunzira Baibulo. Kenako zinadziwika kuti mnyamatayo anayamba kuphunzira chifukwa chongofuna kuyamba chibwenzi ndi Ratana. Mlongoyu anasiya kutumikira Yehova ndipo analowa chipembedzo china n’cholinga choti akwatiwe ndi mnyamatayo.

Chitsanzo china ndi cha mlongo wa ku Cameroon dzina lake Ndenguè. Iye anakwatiwa ali ndi zaka 19. Asanakwatirane, mwamuna wake analonjeza kuti adzamulola kutumikirabe Yehova. Koma patangopita milungu iwiri atakwatirana, mwamuna wakeyu anamuletsa kupita ku misonkhano. Mlongoyu anati: “Ndinkamva chisoni kwambiri ndipo ndinkalira. Ndinazindikira kuti ufulu wanga wonse watha ndipo ndinkangokhalira kudandaula.”

N’zoona kuti si amuna onse osakhulupirira amene amachita nkhanza. Koma ngati mukwatiwa ndi munthu wosakhulupirira, kodi ubwenzi wanu ndi Atate wanu wakumwamba sungasokonekere? Kodi mungamve bwanji podziwa kuti munanyalanyaza malangizo amene Mulungu anakupatsani kuti zinthu zikuyendereni? Koma chofunika kwambiri ndi kudzifunsa kuti, Kodi Mulungu angamve bwanji ndikasankha kukwatiwa ndi munthu wosakhulupirira?—Miy. 1:33.

Abale ndi alongo padziko lonse angavomereze kuti kukwatira kapena kukwatiwa “mwa Ambuye” n’kothandiza. Akhristu ambiri amene sali pa banja amafunitsitsa kusangalatsa Mulungu ndipo amayembekezera mpaka atapeza munthu amene amatumikiranso Mulungu. Mlongo wina wa ku Japan dzina lake Michiko ankakakamizidwa ndi achibale ake kuti akwatiwe ndi munthu wosakhulupirira koma anakana. Zinkamuwawa kwambiri akaona anzake akupeza abale mumpingo. Iye anati: “Ndinkadziuza kuti Yehova ndi ‘Mulungu wachimwemwe’ choncho kuti tikhale osangalala sizidalira kukhala pa banja. Ndimakhulupiriranso kuti Mulungu amatipatsa zimene mtima wathu umafuna. Choncho ngati sindikupeza m’bale, ndingachite bwino kukhalabe wosakwatiwa mpaka nditamupeza.” (1 Tim. 1:11) Patapita nthawi, Michiko anakwatiwa ndi m’bale wabwino ndipo akusangalala kwambiri kuti anayembekezera.

Abale ena amayembekezeranso mpaka atapeza mlongo woyenerera. Chitsanzo ndi m’bale wina wa ku Australia dzina lake Bill. Iye ananena kuti nthawi zina ankakopeka ndi akazi osakhulupirira. Koma sankalola kuzolowerana nawo kwambiri. Iye sankafuna kuyamba zinthu zimene zikanamuchititsa ‘kumangidwa m’goli ndi anthu osakhulupirira.’ Panali alongo ena amene ankamusangalatsa koma sizinkatheka kuti akhale nawo pa chibwenzi. Iye anayembekezerabe ndipo patadutsa zaka 30 anapeza mlongo womuyenerera. Bill anati: “Sindikunong’oneza bondo.” Ananenanso kuti: “Ndikuona kuti Yehova wandidalitsa. Ine ndi mkazi wanga timalalikira limodzi, kuphunzira limodzi ndiponso kulambira limodzi. Ndimasangalalanso kucheza ndi anzake a mkazi wanga chifukwa onse ndi atumiki a Yehova. Mfundo za m’Baibulo zimatithandiza kukhala ndi banja losangalala.”

ZIMENE MUNGACHITE POYEMBEKEZERA YEHOVA

Kodi mungachite chiyani poyembekezera kuti Yehova akuthandizeni? Choyamba, muziganizira zimene zikuchititsa kuti musakhale pa banja. Ngati simuli pa banja chifukwa chotsatira lamulo la Mulungu loti tizikwatira kapena kukwatiwa “mwa Ambuye” ndiye kuti mukuchita bwino kwambiri. Dziwani kuti Yehova amasangalala kukuonani mukumumvera chonchi. (1 Sam. 15:22; Miy. 27:11) Pitirizani kupemphera kwa iye ‘n’kumamukhuthulira za mumtima mwanu.’ (Sal. 62:8) Mapemphero anu akhoza kukhala abwino kwambiri ngati mumapemphera kuchokera mumtima komanso mosalekeza. N’zoona kuti mukhoza kuvutika chifukwa cholakalaka kukhala pa banja kapena chifukwa cha mavuto ena. Koma tsiku lililonse mukamapirira zonsezi, ubwenzi wanu ndi Yehova udzalimba kwambiri. Kumbukirani kuti Yehova amakonda atumiki ake okhulupirika ndipo amaona kuti ndinu wamtengo wapatali. Iye amadziwa mavuto anu komanso zimene mumalakalaka. N’zoona kuti salonjeza zoti azipezera munthu mwamuna kapena mkazi. Koma popeza amadziwa zimene mukufunikira, adzakuthandizani m’njira yoyenerera.—Sal. 145:16; Mat. 6:32.

Nthawi zina mungakhale ndi maganizo amene Davide anali nawo. Iye anapemphera kuti: “Fulumirani, ndiyankheni inu Yehova. Mphamvu zanga zatha. Musandibisire nkhope yanu.” (Sal. 143:5-7, 10) Mukamamva chonchi, muyenera kuyembekezerabe kuti muone zimene Yehova akufuna kuti muchite. Poyembekezerapo muziwerenga Mawu ake n’kumaganizira kwambiri zimene mukuwerengazo. Mukatero mudzadziwa bwino malamulo a Yehova komanso mudzaona mmene ankathandizira anthu ake m’mbuyomu. Mukamamumvera mudzazindikira ubwino wotsatira malangizo ake.

Anthu amene sali pa banja amathandiza kwambiri anthu ena mumpingo

Kodi mungatani kuti muzisangalala komanso kugwiritsa ntchito bwino nthawi imene simuli pa banja? Pa nthawi imeneyi, muziyesetsa kukhala munthu wozindikira, wopatsa, wakhama, wochezeka ndiponso wodzipereka kwa Mulungu. Muziyesetsanso kuti mukhale ndi mbiri yabwino. Zinthu zimene tatchulazi zidzathandiza kuti mudzakhale ndi banja losangalala. (Gen. 24:16-21; Rute 1:16, 17; 2:6, 7, 11; Miy. 31:10-27) Kuti mukhale otetezeka, muyenera kuika patsogolo zinthu zokhudza Ufumu monga kulalikira ndi kusonkhana. Bill amene tamutchula kale uja anafotokoza bwino za nthawi imene sanali pa banja. Iye anati: “Nthawi imeneyi sindinaione kuchedwa. Ndinaigwiritsa ntchito potumikira Yehova chifukwa ndinkachita upainiya.”

Choncho n’zothekadi kukwatira kapena kukwatiwa “mwa Ambuye.” Mukamvera malangizo amenewa mudzalemekeza Yehova komanso mudzakhala osangalala. Paja Baibulo limati: “Wodala ndi munthu woopa Yehova, munthu amene amasangalala kwambiri ndi malamulo ake. Zinthu zamtengo wapatali ndiponso chuma zili m’nyumba yake, ndipo chilungamo chake chidzakhalapo kwamuyaya.” (Sal. 112:1, 3) Choncho tiyeni tiyesetse ndi mtima wonse kumvera lamulo la Mulungu lakuti tizikwatira kapena kukwatiwa “mwa Ambuye.”

^ ndime 7 M’nkhaniyi tikufotokoza mmene alongo amamvera koma mfundo zake zikukhudzanso abale.

^ ndime 13 Mayina ena asinthidwa.