Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MBIRI YA MOYO WATHU

Tinapeza Ntchito Yofunika Kwambiri

Tinapeza Ntchito Yofunika Kwambiri

INE ndi Gwen tinayamba kuphunzira kuvina tili ndi zaka 5. Pa nthawiyo sitinkadziwana. Aliyense ankafuna kuti adzakhale katswiri wovina. Koma titatsala pang’ono kukhaladi akatswiri enieni, tinasiya zovinazo. N’chifukwa chiyani tinasiya?

David: Ndinabadwa mu 1945 m’dera lina la ku England. Bambo anga anali ndi famu yawo m’kadera kena kakumidzi. Ndikaweruka kusukulu ndinkakonda kuwathandiza kudyetsa nkhuku, kutolera mazira komanso kusamalira ng’ombe ndi nkhosa. Ndikakhala pa holide ndinkawathandiza kukolola mbewu ndipo nthawi zina ndinkayendetsa mathalakitala.

Koma ndinayamba kukonda zovinavina ndili wamng’ono. Bambo anga anazindikira kuti ndinkakonda kuvina ndikangomva nyimbo. Ndiyeno ndili ndi zaka 5, anauza mayi anga kuti azindiperekeza kokaphunzira kuvina. Mphunzitsi wangayo anaona kuti ndilidi ndi luso, choncho ankandiphunzitsa kavinidwe kotchedwa ballet. Nditakwanitsa zaka 15, ndinapeza mwayi wolipiriridwa kusukulu ina yapamwamba ku London yophunzitsa kavinidweka. Uku n’kumene ndinakumana ndi Gwen ndipo tinkavina awiri.

Gwen: Ndinabadwa mu 1944 mumzinda waukulu wa London. Kuyambira ndili wamng’ono ndinkakhulupirira kwambiri Mulungu. Ndinkayesa kuwerenga Baibulo koma linkandivuta kumvetsa. Ndili ndi zaka 5, ndinayamba kupita kukaphunzira zovinavina. Patapita zaka 6 ndinapezanso mwayi wopita kusukulu yapamwamba yophunzitsa zovinavina. Sukuluyi inali pamalo okongola kwambiri pafupi ndi mzinda wa London. Kusukuluyi ndinkaphunzira maphunziro ena komanso ndinkaphunzitsidwa kuvina ndi aphunzitsi otchuka. Pofika zaka 16, ndinapita kusukulu yophunzitsa zovinavina kumene David anapita kuja. Pasanapite miyezi yambiri tinkapemphedwa kukavina limodzi kuholo yotchuka kwambiri mumzinda wa London.

Tinkapita kukavina m’mayiko ambiri

David: Monga wanenera Gwen, tinali ndi mwayi wovina limodzi m’malo otchuka kwambiri ku London. Katswiri wina wa zovinavina anayambitsa gulu lovina ku Germany ndipo anatisankha kuti tipite naye n’cholinga choti tizikatsogolera povina. Tinkayenda m’mayiko osiyanasiyana ndipo tinkavina ndi anthu otchuka kwambiri padziko lonse. Ntchito yathuyi inkachititsa kuti tikhale okonda kupikisana ndiponso odzikonda. Pa moyo wathu tinkangoganizira zovina basi.

Gwen: Nkhani yovinayi inandilowerera kwambiri. Ine ndi David tinkafunitsitsa kukhala akatswiri enieni. Tinkasangalala anthu akamatichemerera, kutipatsa maluwa komanso kutipatsa zinthu zawo kuti tisainepo mayina athu. Mofanana ndi anthu ambiri, ndinkadalira zithumwa. Ndinaonanso kuti anthu ambiri amene tinkakhala nawo anali achiwerewere, osuta komanso oledzera.

MOYO WATHU UNASINTHIRATU

Tsiku la ukwati wathu

David: Patapita zaka zambiri, ndinatopa ndi moyo woyendayenda. Ndinayamba kufuna moyo wosalira zambiri kudera lakumidzi ngati umene tinkakhala ndili mwana. Choncho ndinasiya zovina mu 1967 n’kumakagwira ntchito kufamu ina yaikulu pafupi ndi kumene makolo anga ankakhala. Mwini famuyi anandilola kuti ndichite lendi kanyumba kena. Kenako ndinaimbira foni Gwen kumene ankagwira ntchito n’kumufunsira. Iye anali atakwezedwa pa ntchito yake yovina ndipo zinthu zinkamuyendera kwambiri. Choncho sizinali zapafupi kuti andivomere. Koma anavomera ndipo anabwera kudzakhala nane ngakhale kuti moyo wakumidzi sankaudziwa bwino.

Gwen: Zinandivuta kwambiri kuzolowera moyo wakumidzi. Sindinkadziwa kudyetsa nkhumba ndi nkhuku tsiku ndi tsiku, kaya nyengo ili bwino kapena ayi. David anayamba kupita kukoleji ina kukaphunzira ulimi wamakono ndipo ankabwerako usiku. Akachoka ndinkasowa wocheza naye. Pa nthawiyi, tinali ndi mwana mmodzi wamkazi dzina lake Gilly. David anandiuza kuti ndiphunzire kuyendetsa galimoto ndipo tsiku lina ndikupita kutauni ina ndinakumana ndi mtsikana wina dzina lake Gael. Tinadziwana ndi mtsikanayu pa nthawi imene ankagwira ntchito mushopu inayake.

Tili kufamu yathu titangokwatirana kumene

Gael anandiitana kuti tsiku lina ndikacheze kwawo. Nditapita tinayamba kuonetsana zithunzi za ukwati. Chithunzi chake china chinali cha anthu ataima pafupi ndi Nyumba ya Ufumu. Ndinamufunsa kuti, “Kodi tchalitchichi ndi cha chipembedzo chiti?” Ndinasangalala kwambiri atandiuza kuti iye ndi mwamuna wake ndi a Mboni za Yehova. Ndinakumbukira kuti azakhali anga ena anali a Mboni. Koma bambo anga anawakwiyira kwambiri n’kufika potaya mabuku awo onse. Sindinamvetse zimene anachitazi chifukwa bambo anga anali munthu wokoma mtima.

Pasanapite nthawi yaitali, ndinazindikira chimene chinkasiyanitsa zikhulupiriro za azakhali angawo ndi za m’matchalitchi ena. Gael anandisonyeza zimene Baibulo limaphunzitsa. Ndinadabwa kuona kuti zinthu zimene zimaphunzitsidwa m’matchalitchi n’zosagwirizana ndi Malemba. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi utatu ndiponso zoti anthu ali ndi mzimu umene suufa. (Mlal. 9:5, 10; Yoh. 14:28; 17:3) Ndinaonanso dzina la Mulungu lakuti Yehova m’Baibulo.—Eks. 6:3.

David: Gwen anandiuza zimene ankaphunzira. Ndinakumbukira kuti ndili mwana, bambo anga ankakonda kundiuza kuti ndiziwerenga Baibulo. Choncho tinavomera kuti tiziphunzira Baibulo ndi Gael ndi mwamuna wake dzina lake Derrick. Patapita miyezi 6, tinasamukira kutauni ina n’kumachita lendi kafamu kena. Kumeneko, mlongo wina dzina lake Deirdre ankapitiriza kutiphunzitsa moleza mtima. Poyamba zinkativuta kugwiritsa ntchito zimene tinkaphunzira chifukwa tinkatanganidwa kwambiri ndi ziweto zathu. Komabe pang’ono ndi pang’ono zimene tinkaphunzirazo zinayamba kutifika pamtima.

Gwen: Vuto langa lalikulu linali lokhudza kukhulupirira matsenga. Lemba la Yesaya 65:11 linandithandiza kuzindikira mmene Yehova amaonera anthu amene ‘amayalira tebulo mulungu wa Mwayi.’ Ndinkapemphera kwambiri koma zinatenga nthawi yaitali kuti nditaye zithumwa zanga zonse. Nditaphunzira kuti “aliyense wodzikweza adzatsitsidwa, koma aliyense wodzichepetsa adzakwezedwa” ndinazindikira kuti Mulungu amakonda odzichepetsa. (Mat. 23:12) Ndinkafunitsitsa kutumikira Mulungu amene amatikonda kwambiri moti anapereka Mwana wake wokondedwa monga dipo. Pa nthawiyi, tinali ndi mwana wina wamkazi ndipo ndinasangalala kwambiri kuphunzira kuti banja lathu likhoza kudzakhala m’Paradaiso padzikoli mpaka kalekale.

David: Nditaphunzira ndinazindikira kuti ulosi wa m’Baibulo monga wopezeka pa Mateyu chaputala 24 ndiponso wa m’buku la Danieli ukukwaniritsidwa. Zimenezi zinandithandiza kuona kuti ndapeza chipembedzo choona. Ndinaona kuti palibe chilichonse m’dzikoli chimene chingapose kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Choncho ndinayamba kusiya kufunafuna zinthu zambiri m’dzikoli. Ndinazindikira kuti mkazi wanga ndiponso ana anga ndi ofunika kwambiri. Lemba la Afilipi 2:4 linandithandiza kusintha mtima wodzikonda komanso wofuna kukhala ndi famu yaikulu kapena zinthu zina zondisangalatsa. Ndinaona kuti ndiyenera kuika kutumikira Yehova patsogolo. Choncho ndinasiya kusuta. Koma tinkavutika kupita ku misonkhano imene inkachitika Loweruka madzulo. Tinkayenera kuyenda mtunda wa makilomita 10 pa nthawi imene tinkayeneranso kukama mkaka wa ng’ombe. Koma Gwen ankandithandiza ndipo sitinkaphonya misonkhano. Lamlungu lililonse tikamaliza kukama mkaka tinkapitanso mu utumiki ndi ana athu.

Achibale athu sankasangalala ndi kusinthaku. Bambo a Gwen sankalankhula nafe kwa zaka 6. Makolo anganso anayesetsa kutiletsa kusonkhana ndi a Mboni.

Gwen: Yehova ankatithandiza kwambiri kupirira mavutowa. Tinayamba kuona abale ndi alongo mumpingo wathu kuti ndi achibale athu chifukwa ankatilimbikitsa kwambiri. (Luka 18:29, 30) Tinadzipereka kwa Yehova ndipo tinabatizidwa mu 1972. Ndinkafunitsitsa kwambiri kuthandiza anthu kudziwa Yehova choncho ndinayamba upainiya.

NTCHITO YABWINO KWAMBIRI

David: Tinkayenera kugwira ntchito mwakhama pafamu yathu. Koma tinkayesetsa kupereka chitsanzo chabwino kwa ana athu pa zinthu zokhudza kulambira. Patapita nthawi, tinayenera kuchoka pafamuyo chifukwa boma linasiya kupereka chithandizo china. Tinalibe nyumba kapena ntchito ndipo mwana wathu wachitatu anali ndi chaka chimodzi chokha. Tinapempha Yehova kuti atithandize ndi kutitsogolera. Tinasankha zotsegula malo ophunzitsira kuvina n’cholinga choti tizipeza kangachepe. Zimene tinkachita poika patsogolo zinthu zokhudza kulambira, zinathandiza kwambiri ana athu. Onse atamaliza sukulu anayamba upainiya. Nayenso Gwen anayamba upainiya ndipo ankathandiza kwambiri ana athuwo.

Ana athu awiri oyamba aja atakwatiwa, tinatseka sukulu yophunzitsa kuvina ija. Ndiyeno tinalemba kalata ku ofesi ya nthambi kuti tidziwe gawo limene tingapite kukathandiza. Iwo anatiuza kuti tingapite kumatauni ena a kum’mwera chakum’mawa kwa England. Poti tinkakhala ndi mwana mmodzi yekha, nanenso ndinayamba upainiya. Patapita zaka 5, tinapemphedwa kuti tikathandizenso kumipingo ina ya kumpoto. Kenako, mwana wathu womaliza atakwatiwanso, tinagwira ntchito ya zomangamanga kwa zaka 10. Tinagwira ntchitoyi ku Zimbabwe, ku Moldova, ku Hungary ndi ku Côte d’Ivoire. Ndiyeno tinakathandiza pa ntchito ya zomangamanga ku Beteli ya ku London. Popeza ndimadziwa zaulimi, anandipempha kuti ndizikagwira ntchito kufamu ya Beteli, imene inalipo pa nthawiyo. Panopa tikuchita upainiya kumpoto chakumadzulo kwa England.

Tinkasangalala kwambiri pogwira ntchito ya zomangamanga m’mayiko osiyanasiyana

Gwen: Poyamba tinkadzipereka pa zovinavina koma tinaona kuti n’zosakhalitsa. Ndiyeno titadzipereka kuti tizitumikira Yehova, tinaona kuti tasankha ntchito yabwino kwambiri komanso yamuyaya. M’malo movina limodzi, tikuchita upainiya limodzi. Timasangalala kwambiri kuthandiza anthu kudziwa mfundo za m’Baibulo zimene zingawathandize kupulumuka. Anthuwa ali ngati ‘makalata abwino kwambiri otichitira umboni’ ndipo izi sizingafanane ndi kutchuka m’dzikoli. (2 Akor. 3:1, 2) Tikanapanda kuphunzira Baibulo, bwenzi titangotsala ndi zithunzi zakalekale n’kumangokumbukira kuti kale tinkavina m’maholo apamwamba.

David: Kutumikira Yehova kwatithandiza kwambiri pa moyo wathu. Ineyo kwandithandiza kusamalira bwino mkazi wanga komanso ana anga. Baibulo limanena kuti Miriamu, Davide ndiponso anthu ena anavina chifukwa chosangalala. Ifenso tidzavina ndi anzathu chifukwa chosangalala m’dziko latsopano limene Yehova watilonjeza.—Eks. 15:20; 2 Sam. 6:14.