Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mtengo Ukadulidwa Umaphukanso?

Mtengo Ukadulidwa Umaphukanso?

MTENGO wa maolivi suoneka bwino tikauyerekezera ndi wa mkungudza. Koma mtengo wa maolivi umapirira nyengo zovuta kwambiri. Ena apezapo mitengo yotereyi yomwe yakhala zaka 1,000. Mtengowu umakhala ndi mizu italiitali ndipo izi zimachititsa kuti ukadulidwa uphukenso.

Yobu ankakhulupirira kuti akafa adzaukanso. (Yobu 14:13-15) Posonyeza kuti amakhulupirira zoti Mulungu adzaukitsa anthu iye ananena kuti: “Ngakhale mtengo umakhala ndi chiyembekezo. Ukadulidwa umaphukanso.” N’kutheka kuti Yobu analemba zimenezi akuganizira za mtengo wa maolivi. Kukachitika chilala, mtengowu ukhoza kuuma koma mizu yake siifa. Ndipo mvula ikabwera nthambi zimaphuka “ngati mtengo watsopano.”—Yobu 14:7-9.

Mlimi amalakalaka kuona mtengo wa maolivi umene unadulidwa ukuphuka. Nayenso Yehova amalakalaka kuukitsa anthu amene amwalira. (Mat. 22:31, 32; Yoh. 5:28, 29; Mac. 24:15) Tidzasangalala kwambiri kuona anzathu atauka.