Tizichita Zinthu Mogwirizana ndi Pemphero la Ambuye—Gawo 2
“Atate wanu amadziwa zimene mukufuna.”—MAT. 6:8.
1-3. N’chiyani chinachititsa mlongo wina kuzindikira kuti Yehova amadziwa zimene akufunikira?
MPAINIYA wina, dzina lake Lana, saiwala zimene zinamuchitikira ku Germany mu 2012. Iye amaona kuti mapemphero ake awiri anayankhidwa. Pemphero loyamba anapereka ali musitima popita kubwalo la ndege. Iye anapempha kuti Yehova amuthandize kulalikira kwa munthu wina. Atafika kubwalo la ndege anamva kuti ndege yake sinyamuka tsikulo koma mawa lake. Zitatero anapempha Yehova kuti amuthandize chifukwa anangotsala ndi ndalama zochepa ndipo analibe malo ogona.
2 Asanamalize pemphero lachiwirili anangomva munthu wina akunena kuti: “Yes Lana, wabwera kudzatani?” Amene ananena zimenezi anali mnyamata wina amene anali naye kusukulu. Mnyamatayo anali pa ulendo wa ku South Africa ndipo anaperekezedwa ndi mayi ake komanso agogo ake kubwalo la ndegelo. Mayi akewo anali a Elke ndipo atamva zoti Lana alibe malo ogona anamutenga kupita naye kunyumba kwawo. Mayiwo ndi agogowo anamusamalira bwino kwambiri ndipo ankamufunsa
mafunso okhudza zimene amakhulupirira komanso utumiki wake.3 Kutacha, anamuphikira chakudya ndipo anakambirana mafunso ena. Kenako anasiyirana ma adiresi kuti adzakambiranenso. Ndiyeno Lana anabwerera kwawo bwinobwino ndipo akupitiriza upainiya. Iye amaona kuti zinthu zinamuyendera bwino chonchi chifukwa chakuti Yehova anayankha mapemphero ake.—Sal. 65:2.
4. Kodi tikambirana chiyani m’nkhaniyi?
4 Anthufe tikakumana ndi vuto ladzidzidzi timakonda kupempha Yehova kuti atithandize. Yehova amasangalala kwambiri akaona atumiki ake akuchita zimenezi. (Sal. 34:15; Miy. 15:8) Koma pemphero la Ambuye likusonyeza kuti pali mfundo zofunika kwambiri zimene sitiyenera kuziiwala popemphera. Tsopano tiyeni tikambirane mfundo 4 zomaliza m’pemphero limeneli. Mfundozi zingatithandize kukhalabe okhulupirika kwa Yehova.—Werengani Mateyu 6:11-13.
“MUTIPATSE IFE LERO CHAKUDYA CHATHU CHALERO”
5, 6. N’chifukwa chiyani tiyenera kupemphererabe chakudya chathu chalero ngakhale kuti tili nacho chakwanira?
5 Yesu anatiphunzitsa kuti tizipempha chakudya “chathu” osati “changa.” Woyang’anira dera wina ku Africa dzina lake Victor anati: “Ndimathokoza kwambiri Yehova chifukwa ine ndi mkazi wanga sitidera nkhawa chakudya kapena ndalama ya lendi. Abale athu amatisamalira bwino tsiku ndi tsiku. Koma ndimapempha Yehova kuti azithandiza abalewa kupeza zinthu zofunika pa moyo.”
6 Ngati tili ndi chakudya chokwanira, tiyenera kuganizira abale athu osauka kapena amene akhudzidwa ndi ngozi inayake. Tiziwapempherera ndiponso kuchita zinthu mogwirizana ndi mapemphero athuwo. Mwachitsanzo, tingawagawire zinthu zomwe tili nazo. Tingaperekenso ndalama zothandiza pa ntchito yapadziko lonse. Paja ndalamazi zimagwiritsidwanso ntchito pothandiza abale ovutika.—1 Yoh. 3:17.
7. Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani pofuna kutithandiza kuti ‘tisamadere nkhawa za tsiku lotsatira’?
7 Pamene Yesu ananena za kupempha chakudya chalero, ankatanthauzanso kuti tisamadere nkhawa za m’tsogolo. Iye anasonyeza kuti Mulungu amaveka maluwa akutchire ndipo anati: “Kodi iye sadzakuvekani kuposa pamenepo, achikhulupiriro chochepa inu? Choncho musamade nkhawa n’kumanena kuti, . . . ‘Tivala chiyani?’” Pomaliza, Yesu anabwereza malangizo ofunika kwambiri akuti: “Musamade nkhawa za tsiku lotsatira.” (Mat. 6:30-34) Zimenezi zikusonyeza kuti m’malo mofunafuna chuma, tizikhutira ndi zinthu zofunika za tsiku lililonse. Apa tikunena zinthu monga nyumba, ntchito yotithandiza kusamalira banja lathu ndiponso nzeru zotithandiza kusankha bwino zochita ngati tadwala. Koma tiyenera kupemphereranso zinthu zokhudza kutumikira Yehova, chifukwa ndi zofunika kwambiri.
8. Kodi mawu a Yesu akuti tizipempha chakudya chathu chalero ayenera kutikumbutsanso chiyani? (Onani chithunzi patsamba 25.)
8 Nkhani yopempha chakudya chathu chalero ikutikumbutsanso mawu ena amene Yesu ananena. Iye anati: “Munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu onse otuluka pakamwa pa Yehova.” (Mat. 4:4) Choncho tiyenera kumapemphera kuti Yehova apitirize kutipatsa chakudya pa nthawi yake.
“MUTIKHULULUKIRE ZOLAKWA ZATHU”
9. N’chifukwa chiyani tinganene kuti zolakwa zathu zili ngati ngongole?
9 Mawu a m’munsi a pa Mateyu 6:12 akusonyeza kuti mawu amene anamasuliridwa kuti “zolakwa” kwenikweni amatanthauza “ngongole.” (Luka 11:4) Mu 1951, Nsanja ya Olonda inafotokoza chifukwa chimene Yesu anagwiritsira ntchito mawuwo. Magaziniyo inati tikachimwira Yehova zimakhala ngati tili naye ngongole. Anthufe tiyenera kukonda ndiponso kumvera Yehova. Koma tikachimwa timalephera kupatsa Mulungu zinthu zimene amayenera kulandira. Timalephera kusonyeza kuti timamukonda. Ndiyeno Yehova ali ndi ufulu wothetsa ubwenzi wake ndi anthu amene achimwa chifukwa ali ndi ngongole yomwe malipiro ake ndi imfa.—1 Yoh. 5:3.
10. (a) Kodi Yehova anachita chiyani n’cholinga choti azitikhululukira? (b) Kodi tiyenera kuona bwanji zimene Yehova watichitirazi?
10 Tsiku lililonse timalakwira Mulungu. Choncho timayamikira kwambiri kuti iye anapereka nsembe ya dipo ya Yesu kuti athe kutikhululukira. Yesu anatifera zaka pafupifupi 2,000 zapitazo koma nsembeyo imatithandizabe panopa. Palibe munthu wina amene akanakwanitsa kupereka dipo limeneli. (Werengani Salimo 49:7-9; 1 Petulo 1:18, 19.) Choncho tiyenera kuyamikira kwambiri kuti Mulungu anatipatsa mphatso imeneyi. Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu oti “mutikhululukire zolakwa zathu” osati “zanga”? Mawuwa ayenera kutikumbutsa kuti tonsefe m’gulu la Yehova timafunikira dipoli. Zikusonyezanso kuti Yehova amafuna kuti tiziganizira anzathu n’kumafuna kuti akhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Tiyenera kuganiziranso ngakhale anthu amene atilakwira. Nthawi zambiri zinthu zimene anthu ena amatilakwira zimakhala zazing’ono ndipo tikawakhululukira timasonyeza kuti timawakonda. Timasonyezanso kuti timayamikira Yehova chifukwa chotikhululukira.—Akol. 3:13.
11. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhululukira anthu ena?
11 Koma anthu ochimwafe nthawi zina timasungira ena zifukwa. (Lev. 19:18) Tikauza anthu ena zimene wina watilakwira, tingachititse kuti anthuwo azitiikira kumbuyo. Ndiyeno izi zingasokoneze mgwirizano mumpingo. Tikalola zimenezi kuchitika timasonyezanso kuti sitiyamikira kwenikweni chifundo cha Mulungu ndiponso dipo. Mulungu sadzatikhululukira ngati ifeyo sitikhululukira anzathu. (Mat. 18:35) Yesu anafotokoza zimenezi pambuyo ponena pemphero lachitsanzo. (Werengani Mateyu 6:14, 15.) Komanso kuti Mulungu azitikhululukira tiyenera kuyesetsa kuti tisamachite machimo aakulu. Tiyeni tsopano tikambirane mfundo ina ya m’pemphero lija.—1 Yoh. 3:4, 6.
“MUSATILOWETSE M’MAYESERO”
12, 13. (a) N’chiyani chinachitikira Yesu atangobatizidwa? (b) N’chifukwa chiyani sitiyenera kuimba mlandu munthu wina ngati tagonja poyesedwa? (c) Kodi kukhulupirika kwa Yesu kunasonyeza chiyani?
12 Tikaganizira zimene zinachitikira Yesu atangobatizidwa, tikhoza kuona ubwino wopempha Mulungu kuti ‘asatilowetse m’mayesero.’ Paja Yesu atangobatizidwa, mzimu unamutsogolera kuchipululu “kuti akayesedwe ndi Mdyerekezi.” (Mat. 4:1; 6:13) Ndiyeno funso n’kumati, N’chifukwa chiyani Mulungu analola kuti zimenezi zichitike? Choyamba, tiyenera kukumbukira kuti Adamu ndi Hava anakana ulamuliro wa Mulungu ndipo Satana anayambitsa nkhani yaikulu. Panali mafunso amene anafunika nthawi yaitali kuti ayankhidwe. Mwachitsanzo, kodi Mulungu analenga bwino anthu kapena ayi? Kodi munthu wangwiro akhoza kukhala wokhulupirika kwa Mulungu ngakhale atayesedwa kwambiri ndi “woipayo”? Kodi zimene Satana ananena zoti anthu akhoza kudzilamulira okha bwinobwino zinali zoona? (Gen. 3:4, 5) Ndiyeno kukhulupirika kwa Yesu kunasonyeza kuti Mdyerekezi ndi wabodza. M’tsogolomu mafunso onsewa akadzayankhidwa bwinobwino, anthu onse ndiponso angelo adzadziwa kuti Yehova ndi amene amalamulira bwino kwambiri.
13 Yehova ndi woyera choncho sangayese munthu kuti achite zoipa. Koma Satana ndi amene amayesa anthu. (Mat. 4:3) Amachita zimenezi m’njira zosiyanasiyana. Koma munthu aliyense angasankhe yekha kukopeka ndi mayeserowo kapena ayi. (Werengani Yakobo 1:13-15.) Yesu anakana mayesero onse pogwiritsa ntchito malemba oyenerera. Apatu Yesu anasonyeza kuti Mulungu ndi woyenera kulamulira. Koma Satana sanasiyire pomwepo. Anangomudikira kaye “kufikira nthawi ina yabwino.” (Luka 4:13) Satana anachita zonse zimene akanatha kuti alepheretse Yesu kukhala wokhulupirika koma Yesu sanalole. Nthawi zonse, Khristu ankamvera Mulungu ndipo anasonyeza kuti munthu wangwiro akhoza kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova ngakhale atayesedwa koopsa. Koma Satana amayesabe Akhristu onse ndipo inuyo muli m’gulu loyesedwalo.
14. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tisagonje poyesedwa?
14 Popeza nkhani yokhudza ulamuliro wa Mulungu ija sinathe, Yehova amalola kuti Satana azigwiritsa ntchito dzikoli potiyesa. Koma sitinganene kuti Mulungu ndi amene amatilowetsa m’mayesero. Iye amatikhulupirira kwambiri ndipo amafunitsitsa kutithandiza. Ngakhale zili choncho, amalemekeza ufulu wathu wosankha ndipo satikakamiza kuti tizimumvera. Choncho amalola kuti tisankhe tokha kumumvera kapena kukopeka ndi mayesero. Kuti tisagonje poyesedwa, tiyenera kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova ndiponso kupemphera mosalekeza. Kodi Yehova amayankha bwanji tikamupempha kuti tisagonje poyesedwa?
15, 16. (a) Tchulani mayesero ena amene tiyenera kupewa. (b) Kodi munthu akagonja poyesedwa ndiye kuti vuto ndi ndani?
15 Yehova amatipatsa mphamvu ya mzimu woyera kuti itithandize kupewa mayesero. Mulungu amagwiritsanso ntchito Mawu ake ndiponso mpingo potichenjeza. Mwachitsanzo,
amanena kuti tiyenera kupewa kugwiritsa ntchito nthawi, ndalama kapena mphamvu zathu pofufuza chuma kapena zinthu zosafunika kwenikweni. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Espen ndi mkazi wake Janne. Anthuwa amakhala m’dziko lotukuka ku Europe. Kwa zaka zambiri, ankachita upainiya kudera limene kunkafunika ofalitsa ambiri. Koma atakhala ndi mwana anasiya upainiyawo ndipo pano ali ndi mwana wachiwiri. Espen anati: “Popeza sitingachite zambiri mu utumiki, timapempha Yehova kuti azitithandiza kuti tisalowe m’mayesero. Timapempha kuti atithandize kukhalabe pa ubwenzi wolimba ndi iye komanso kuti tizichita khama mu utumiki.”16 Kuonera zolaula ndi vuto lina limene lafika poipa masiku ano. Kodi munthu amene amaonera zolaula ayenera kuimba mlandu Satana kuti ndi amene wamuchititsa? Ayi. Tikutero chifukwa chakuti sitingakakamizidwe ndi Satana komanso dziko loipali kuti tichite zimene sitikufuna. Ena amayamba kuonera zolaulazi chifukwa chakuti sadziletsa akayamba kuganizira zinthu zoipa. Koma pali abale ndi alongo ambirimbiri amene amapeweratu zimenezi ndipo inunso mukhoza kukwanitsa.—1 Akor. 10:12, 13.
“MUTILANDITSE KWA WOIPAYO”
17. (a) Kodi tingachite bwanji zinthu mogwirizana ndi pemphero lakuti mutilanditse kwa woipayo? (b) Kodi tidzasangalala Yehova akachita chiyani posachedwapa?
17 Kuti tichite zinthu mogwirizana ndi pemphero lakuti “mutilanditse kwa woipayo,” tiyenera kupewa kukhala ‘mbali ya dziko la Satanali.’ Tiyeneranso kupewa ‘kukonda dziko kapena zinthu za m’dzikoli.’ (Yoh. 15:19; 1 Yoh. 2:15-17) Koma kuchita zimenezi si kophweka. Tidzasangalala kwambiri Yehova akadzayankha pempheroli n’kuchotsa Satana ndi dziko loipali. Tisaiwale kuti Satana akudziwa zoti wangotsala ndi nthawi yochepa. Iye ndi wokwiya kwambiri ndipo akuchita zonse zimene angathe kuti asokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. Choncho tiyenera kupemphera nthawi zonse kuti Yehova atilanditse kwa woipayo.—Chiv. 12:12, 17.
18. Kodi tiyenera kupitiriza kuchita chiyani kuti tidzapulumuke?
18 Kodi mukulakalaka kukhala m’dziko lopanda Satana? Ngati zili choncho, pitirizani kupemphera kuti Mulungu ayeretse dzina lake ndiponso chifuniro chake chichitike padzikoli. Pitirizani kupempha Yehova kuti azikuthandizani kupeza zofunika pa moyo ndiponso kulimbitsa ubwenzi wanu ndi iye. Tiyeni tonse tiziyesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi pemphero la Ambuye.