Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumaona Dzanja la Mulungu Likukuthandizani?

Kodi Mumaona Dzanja la Mulungu Likukuthandizani?

“Dzanja la Yehova lidzadziwika kwa atumiki ake.”—YES. 66:14.

NYIMBO: 65, 26

1, 2. Kodi anthu ena amaganiza zotani zokhudza Mulungu?

ANTHU ambiri amaganiza kuti Mulungu saona zimene iwo amachita. Ena amakhulupirira kuti Mulungu alibe nazo ntchito zimene zikutichitikira. Mwachitsanzo, mu November 2013 mphepo yamkuntho itawononga zinthu zambiri mumzinda wina waukulu m’dziko la Philippines, meya wa mzindawu anati: “Zikuoneka kuti Mulungu kunalibe pa nthawi ya ngoziyi.”

2 Palinso anthu ena amene amachita zinthu ngati kuti Mulungu sakuwaona. (Yes. 26:10, 11; 3 Yoh. 11) Iwo ali ngati anthu amene mtumwi Paulo anawafotokoza ponena kuti: ‘Sanafune kumudziwa Mulungu molondola.’ Anthuwo “anadzazidwa ndi zosalungama zonse, kuipa konse, kusirira konse kwa nsanje, ndi uchimo wonse.”—Aroma 1:28, 29.

3. (a) Kodi tingachite bwino kudzifunsa mafunso ati okhudza Yehova? (b) Kodi nthawi zambiri Baibulo limagwiritsa ntchito mawu oti “dzanja” la Mulungu ponena za chiyani?

3 Mosiyana ndi anthu amenewa, ifeyo timadziwa kuti Yehova amaona zonse zimene timachita. Koma tingachite bwino kudzifunsa kuti, Kodi ndimaona kuti Yehova amandiganizira ineyo? Kodi ndimaona dzanja lake likundithandiza? Nanga kodi ndili m’gulu la anthu amene Yesu ananena kuti “adzaona Mulungu”? (Mat. 5:8) Kuti timvetse tanthauzo la kuona Mulungu kapena kuzindikira dzanja lake, tiyeni tikambirane za anthu otchulidwa m’Baibulo amene anazindikira dzanja la Mulungu ndiponso amene sanalizindikire. Kenako tikambirana zimene tingachite kuti tiziona dzanja la Yehova likutithandiza. Pamene tikukambirana nkhaniyi, tizikumbukira kuti nthawi zambiri Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti “dzanja” la Mulungu ponena za mphamvu zake. Iye amagwiritsa ntchito mphamvu zimenezi pothandiza anthu ake ndiponso pogonjetsa adani.—Werengani Deuteronomo 26:8.

SANAZINDIKIRE MPHAMVU ZA MULUNGU

4. N’chifukwa chiyani adani a Aisiraeli sanazindikire dzanja la Mulungu?

4 M’nthawi ya Aisiraeli, anthu a mitundu ina anali ndi mwayi woona komanso kumva mmene Mulungu anathandizira Aisiraeliwo. Mwachitsanzo, Yehova anapulumutsa anthu ake ku Iguputo komanso kwa mafumu ena ambiri. (Yos. 9:3, 9, 10) Mafumu onse amene anali kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodano anamva komanso kuona zimene Yehova anachitazi. Ngakhale zinali choncho, ambiri a iwo “anasonkhanitsa pamodzi magulu awo ankhondo kuti amenyane ndi Yoswa ndi Isiraeli.” (Yos. 9:1, 2) Atayamba kumenyana nawo, Yehova anasonyeza mphamvu zake. Iye anachititsa kuti ‘dzuwa ndiponso mwezi ziime mpaka Aisiraeli atalanga adani awo.’ (Yos. 10:13) Komabe Yehova analola “mitunduyo kuumitsa mitima yawo kuti ichite nkhondo ndi Aisiraeli.” (Yos. 11:20) Ndiyeno adaniwo anagonjetsedwa chifukwa chakuti sankafuna kuvomereza kuti Mulungu akuwamenyera nkhondo Aisiraeliwo.

5. Kodi Ahabu sankafuna kuvomereza chiyani?

5 Ahabu, yemwe anali mfumu yoipa, analinso ndi mwayi woona dzanja la Mulungu. Mwachitsanzo, Eliya anamuuza kuti: “Sikugwa mame kapena mvula zaka zikubwerazi, pokhapokha ine nditalamula.” (1 Maf. 17:1) Zinali zoonekeratu kuti Yehova ndi amene anachititsa kuti mvula isagwe koma Ahabu sankafuna kuvomereza zimenezi. Nthawi inanso Eliya atapemphera, Ahabu anaona moto ukugwa kuchokera kumwamba n’kupsereza nsembe ya Eliyayo. Kenako Eliya ananena kuti Yehova athetsa chilalacho ndipo anauza Ahabu kuti: “Tsetserekani kuti chimvula chisakutsekerezeni.” (1 Maf. 18:22-45) Ngakhale kuti Ahabu anaona zonsezi, sanavomereze kuti Yehova ndi amene ankazichititsa. Zitsanzo zimene takambiranazi zikusonyeza kuti tiyenera kukhala tcheru kuti tizizindikira mphamvu za Yehova.

ANAZINDIKIRA MPHAMVU ZA YEHOVA

6, 7. Kodi anthu ena anazindikira chiyani m’nthawi ya Yoswa?

6 Mitundu yambiri inkafuna kumenyana ndi Aisiraeli koma panali anthu ena amene anazindikira mphamvu za Mulungu. Mwachitsanzo, pa nthawi ya Yoswa, anthu a ku Gibeoni anachita pangano lamtendere ndi Aisiraeli. Iwo anati: “Akapolo anufe . . . tabwera chifukwa tamva za dzina la Mulungu wanu, Yehova. Tamva mbiri yake ndi zonse zimene anachita ku Iguputo.” (Yos. 9:3, 9, 10) Iwo anazindikira kuti Mulungu woona ndi amene akuthandiza Aisiraeli.

7 Nayenso Rahabi anazindikira kuti Mulungu ankathandiza Aisiraeli. Iye anamva mmene Yehova anawapulumutsira, ndipo amuna awiri atabwera kudzazonda mzinda wa Yeriko, anawauza kuti: “Ndikudziwa kuti Yehova akupatsani ndithu dziko lino.” Rahabi analolera kuika moyo wake pa ngozi podziwa kuti Yehova akhoza kumupulumutsa limodzi ndi banja lake.—Yos. 2:9-13; 4:23, 24.

8. Kodi Aisiraeli ena anachita chiyani ataona mphamvu za Mulungu?

8 Pa nthawi ya Ahabu panali Aisiraeli ena amene anaona Yehova akuyankha pemphero la Eliya lokhudza nsembe yake. Iwo ataona moto ukutsika kumwamba n’kupsereza nsembe yake, sanakayikire kuti ndi mphamvu za Mulungu ndipo anafuula kuti: “Yehova ndiye Mulungu woona!”—1 Maf. 18:39.

9. Kodi masiku ano tingaone bwanji Yehova komanso dzanja lake?

9 Zitsanzo zabwino komanso zoipa zimene takambiranazi zikutithandiza kumvetsa tanthauzo la kuona Mulungu komanso kuzindikira mphamvu za dzanja lake. Tikayamba kudziwa bwino Yehova timamvetsa makhalidwe ake komanso zochita zake ndipo zimakhala ngati tikuona Yehovayo komanso dzanja lake. (Aef. 1:18) Choncho tiyeni tiziyesetsa kukhala m’gulu la anthu amene amazindikira mphamvu za dzanja la Yehova. Koma kodi palidi umboni wakuti Yehova amathandizanso anthu masiku ano?

YEHOVA AKUTHANDIZABE ANTHU AKE MASIKU ANO

10. Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti Yehova akuthandiza anthu masiku ano? (Onani chithunzi patsamba 4.)

10 Pali umboni wotsimikizira kuti Yehova akuthandizabe anthu masiku ano. Anthu ambiri amene amapemphera kuti Mulungu awathandize amaona kuti akuwathandizadi. (Sal. 53:2) Mwachitsanzo, m’bale wina dzina lake Allan ankalalikira pachilumba chinachake ku Philippines. Ndiyeno atakumana ndi mayi wina anangodabwa kuti mayiyo wayamba kulira. Allan anati: “Mayiyu ali mtsikana ankaphunzira ndi a Mboni koma atakwatiwa anasamukira kuchilumbachi ndipo sanakumanenso nawo. Ndiyeno patsikuli m’mawa anapempha Yehova kuti amuthandize kukumana ndi a Mboni. Choncho ataona kuti Mulungu anayankha pemphero lake mwamsanga, zinamukhudza kwambiri moti analira.” Pasanathe chaka, anadzipereka kwa Yehova.

Kodi mumaona umboni wakuti Yehova akuthandiza anthu ake masiku ano? (Onani ndime 11 mpaka 13)

11, 12. (a) Kodi Yehova akuthandiza bwanji atumiki ake masiku ano? (b) Perekani chitsanzo cha munthu wina amene Mulungu anamuthandiza.

11 Akhristu ambiri anaona Mulungu akuwathandiza pamene ankayesetsa kusiya makhalidwe oipa monga kusuta, kumwa mankhwala osokoneza ubongo kapena kuonera zolaula. Ena a iwo anayesetsa mobwerezabwereza kuti asiye zinthu zoipazo paokha koma analephera. Ndiyeno atapempha Yehova kuti awathandize, iye anawapatsa “mphamvu yoposa yachibadwa” yomwe inawathandiza kusiya makhalidwewo.—2 Akor. 4:7; Sal. 37:23, 24.

12 Yehova amathandiza atumiki ake ambiri kuti alimbane ndi mavuto awo. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina dzina lake Amy. Iye anapemphedwa kuti akathandize kumanga Nyumba ya Ufumu ndiponso nyumba ya amishonale pachilumba china cha m’nyanja ya Pacific. Amy ankavutika chifukwa chakuti chikhalidwe chinali chosiyana ndi cha kwawo, nthawi zambiri kunkakhala kopanda magetsi ndi madzi ndipo misewu inkasefukira ndi madzi. Iye ankakhala m’kachipinda kakang’ono kuhotelo ndipo ankasowana ndi achibale ake. Amy anati: “Kuwonjezera pa mavuto enawa, tsiku lina ndinakalipira mlongo wina amene tinkagwira naye ntchito. Tsiku limenelo ndinapita kunyumba ndikumva kuti ndine wachabechabe ndipo ndinakapezanso magetsi atazima. Ndiyeno ndinapempha Yehova mochokera pansi pa mtima kuti andithandize.” Magetsi atayaka, Amy anayamba kuwerenga nkhani yokhudza mwambo womaliza Sukulu ya Giliyadi mu Nsanja ya Olonda. Nkhaniyo inafotokoza zinthu zina zimene iyenso ankavutika nazo monga kuzolowera chikhalidwe chatsopano, anthu atsopano komanso kusowa anthu akwawo. Iye anati: “Ndinaona kuti Yehova ankalankhula nane tsikulo ndipo zinandithandiza kuti ndizigwirabe ntchito kumeneko.”—Sal. 44:25, 26; Yes. 41:10, 13.

13. N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova amathandiza anthu ake “kuteteza uthenga wabwino ndi kukhazikitsa mwalamulo” ntchito yolalikira?

13 Yehova wakhala akuthandizanso anthu ake “kuteteza uthenga wabwino ndi kukhazikitsa mwalamulo ntchito ya uthenga wabwino.” (Afil. 1:7) Maboma ena akhala akuyesetsa kuti aletse ntchito yathu yolalikira. Koma tawina milandu yoposa 268 kumakhoti akuluakulu. Mwachitsanzo, kuyambira m’chaka cha 2000, tawina milandu 24 ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya. Izi zikusonyeza kuti palibe amene angalepheretse Mulungu kuti azithandiza anthu ake.—Yes. 54:17; werengani Yesaya 59:1.

14. Perekani umboni wina wosonyeza kuti Mulungu akuthandiza anthu ake.

14 Ntchito yolalikira uthenga wabwino ikuyenda bwino padziko lonse chifukwa chakuti Mulungu akutithandiza. (Mat. 24:14; Mac. 1:8) M’gulu la Yehova, anthu a mitundu yosiyanasiyana amakhala ogwirizana. Zimenezi n’zosowa m’dzikoli ndipo n’chifukwa chake anthu akaona gulu la Yehova amanena kuti: “Zoonadi Mulungu ali pakati panu.” (1 Akor. 14:25) Zonsezi zikusonyeza kuti Mulungu akuthandizadi anthu ake. (Werengani Yesaya 66:14.) Koma kodi mumaona dzanja la Yehova likukuthandizani inuyo?

KODI INUYO MUMAONA DZANJA LA YEHOVA LIKUKUTHANDIZANI?

15. Kodi n’chiyani chingatilepheretse kuona dzanja la Yehova likutithandiza?

15 Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatilepheretse kuona dzanja la Mulungu likutithandiza? Nthawi zina, mavuto amene timakumana nawo angatisokoneze ndipo tingaiwale zabwino zimene Yehova watichitira kale. Mwachitsanzo, Eliya ataopsezedwa ndi Yezebeli, anachita mantha n’kuiwala zinthu zabwino zimene Mulungu anali atamuchitira. Baibulo limanena kuti iye “anayamba kupempha kuti afe.” (1 Maf. 19:1-4) Apa Eliya anafunika kudalira Yehova kuti amuthandize.—1 Maf. 19:14-18.

16. Kodi tingatani kuti tiziona zimene Mulungu akuchita potithandiza?

16 Nayenso Yobu atakumana ndi mavuto anasiya kuona zinthu mmene Mulungu amazionera. Koma kenako anayesetsa kuti ayambenso kuona Yehova akumuthandiza. (Yobu 42:3-6) Nanga ifeyo tingatani kuti tiziona Yehova akutithandiza tikakumana ndi mavuto? Tiyenera kuganizira mfundo za m’Baibulo n’kumaona kugwirizana kwake ndi zimene zikuchitika pa moyo wathu. Tikamachita zimenezi ifenso tidzatha kunena mawu amene Yobu anauza Yehova akuti: “Ndinkangomva za inu, koma tsopano diso langa lakuonani.”

Yehova akhoza kukugwiritsani ntchito kuti athandize ena kuti azimuona (Onani ndime 17 ndi 18)

17, 18. (a) Kodi dzanja la Yehova limatithandiza m’njira ziti? (b) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti Mulungu amatithandiza masiku ano.

17 Kodi dzanja la Yehova limatithandiza m’njira ziti? Mwina mukaganizira mmene munayambira kuphunzira Baibulo, mumaoneratu kuti Mulungu ndi amene anakuthandizani. Kapena nthawi ina muli pa misonkhano munamva nkhani inayake n’kunena kuti: “Zikungokhala ngati akukambira ineyotu.” N’kuthekanso kuti munaona mmene Mulungu anayankhira pemphero lanu. Mwinanso munaona mmene Yehova anakuthandizirani kuti muwonjezere utumiki wanu. Apo ayi, mwina munasiya ntchito kuti muzitumikira Yehova bwinobwino ndipo mwaona iye akukwaniritsa lonjezo lake lakuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” (Aheb. 13:5) Tonsefe tiyenera kuyesetsa kuti tizizindikira mmene Yehova akutithandizira.

18 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina wa ku Kenya dzina lake Sara. Iye anati: “Ndinkaona kuti munthu wina amene ndinkaphunzira naye analibe chidwi, choncho ndinapemphera kwa Yehova. Ndinamufunsa ngati ndingachite bwino kupitiriza kuphunzira naye. Nditangonena kuti, ‘Ame,’ ndinamva foni yanga ikuitana. Munthu uja anaimba n’kunena kuti akufuna kupita nawo ku misonkhano. Ndinadabwa kwambiri.” Nanunso mukamakhala tcheru mukhoza kuona zimene Mulungu akuchita pokuthandizani. Mlongo wina wa ku Asia dzina lake Rhonna ananena kuti: “Poyamba tingavutike kuti tizindikire zimene Yehova akuchita potitsogolera. Koma tikazindikira tingadabwe kuona kuti Mulungu akuchita zinthu zambiri potithandiza.”

19. Kodi tingatani kuti tikhale m’gulu la anthu amene akuona Mulungu?

19 Yesu ananena kuti: “Odala ndi anthu oyera mtima, chifukwa adzaona Mulungu.” (Mat. 5:8) Kodi tingatani kuti tikhale “oyera mtima”? Tiyenera kukhala ndi maganizo oyera komanso kusiya makhalidwe oipa. (Werengani 2 Akorinto 4:2.) Tikamayesetsa kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu komanso kukhala ndi makhalidwe abwino, timakhala m’gulu la anthu amene akuona Mulungu. M’nkhani yotsatira, tidzaona kuti chikhulupiriro chathu chingatithandizenso kuzindikira zimene Yehova akuchita potitsogolera pa moyo wathu.