Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Tiwonjezereni Chikhulupiriro”

“Tiwonjezereni Chikhulupiriro”

“Limbitsani chikhulupiriro changa.”—MALIKO 9:24.

NYIMBO: 81, 135

1. Kodi kukhala ndi chikhulupiriro n’kofunika bwanji? (Onani chithunzi pamwambapa.)

MWINA munayamba mwadzifunsapo kuti, ‘Kodi Yehova amaona kuti ineyo ndi woyenera kupulumuka chisautso chachikulu n’kulowa m’dziko latsopano?’ Pali zinthu zambiri zimene tiyenera kuchita kuti tidzapulumuke. Chinthu china chofunika kwambiri n’chimene Paulo ananena pa Aheberi 11:6. Iye anati: “Popanda chikhulupiriro n’zosatheka kukondweretsa Mulungu.” Ena angaganize kuti kukhala ndi chikhulupiriro n’kosavuta, koma pa 2 Atesalonika 3:2 timawerenga kuti: “Chikhulupiriro sichikhala ndi anthu onse.” Malemba awiriwa akusonyeza kuti tiyenera kuyesetsa kukhala ndi chikhulupiriro cholimba.

2, 3. (a) Kodi Petulo anasonyeza bwanji kuti chikhulupiriro n’chofunika kwambiri? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

2 Mtumwi Petulo ananena kuti anthu amene chikhulupiriro chawo chayesedwa adzadalitsidwa pa nthawi imene ‘zochita za Yesu Khristu zidzaululika.’ (Werengani 1 Petulo 1:7.) Popeza chisautso chachikulu chikuyandikira, tiyenera kuyesetsa kuti tikhale m’gulu la “anthu okhala ndi chikhulupiriro chosunga moyo.” (Aheb. 10:39) Mfundo zimenezi zingatichititse kupemphera ngati munthu wina amene anati: “Limbitsani chikhulupiriro changa.” (Maliko 9:24) Apo ayi, tikhoza kunena mawu a atumwi a Yesu akuti: “Tiwonjezereni chikhulupiriro.”—Luka 17:5.

3 Koma pali mafunso angapo amene tiyenera kukambirana pa nkhaniyi. Kodi tingalimbitse bwanji chikhulupiriro chathu? Nanga kodi tingasonyeze bwanji kuti tili ndi chikhulupiriro? N’chiyani chingatitsimikizire kuti Yehova adzayankha pemphero lathu loti alimbitse chikhulupiriro chathu?

KODI CHIKHULUPIRIRO CHANU CHIMASANGALATSA MULUNGU?

4. Kodi ndi zitsanzo za anthu ati zimene zingatithandize kulimbitsa chikhulupiriro chathu?

4 M’Baibulo muli zitsanzo za anthu okhala ndi chikhulupiriro amene tiyenera kuwatsanzira. Tikutero chifukwa chakuti “zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize.” (Aroma 15:4) Kuphunzira za anthu monga Abulahamu, Sara, Isaki, Yakobo, Mose, Rahabi, Gidiyoni ndiponso Baraki kumatithandiza kuona ngati tili ndi chikhulupiriro cholimba kapena ayi. (Aheb. 11:32-35) Kuwerenganso nkhani za abale ndi alongo amasiku ano amene asonyeza chikhulupiriro cholimba kungalimbitsenso chikhulupiriro chathu. *

5. (a) Kodi Eliya anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira kwambiri Yehova? (b) Kodi chitsanzo cha Eliya chikutilimbikitsa kuchita chiyani?

5 Munthu wina wotchulidwa m’Baibulo amene anali ndi chikhulupiriro ndi Eliya. Iye anachita zinthu zosonyeza kuti ankadalira kwambiri Yehova. Mwachitsanzo, anauza Mfumu Ahabu kuti Yehova achititsa kuti kukhale chilala ndipo ananena molimba mtima kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo, . . . sikugwa mame kapena mvula zaka zikubwerazi, pokhapokha ine nditalamula.” (1 Maf. 17:1) Eliya ankakhulupirira kuti Yehova aonetsetsa kuti iye ndi anthu ena ali ndi zofunika pa moyo wawo pa nthawi yachilalayo. (1 Maf. 17:4, 5, 13, 14) Pa nthawi ina, anakhulupiriranso kuti Yehova aukitsa mwana amene anamwalira. (1 Maf. 17:21) Anasonyezanso chikhulupiriro chifukwa sanakayikire kuti Yehova atumiza moto wopserezera nsembe yake imene anapereka paphiri la Karimeli. (1 Maf. 18:24, 37) Nthawi itafika kuti Yehova athetse chilalacho, Eliya anauza Ahabu kuti: “Pitani mukadye ndi kumwa, chifukwa kukumveka mkokomo wa chimvula.” (1 Maf. 18:41) Iye ananena mawuwa ngakhale kuti kunalibe chizindikiro chilichonse choti kugwa mvula. Nkhani ngati zimenezi zingatilimbikitse kudzifufuza kuti tione ngati chikhulupiriro chathu ndi cholimba.

KODI TINGALIMBITSE BWANJI CHIKHULUPIRIRO CHATHU?

6. Kodi Yehova angatithandize bwanji kuti tikhale ndi chikhulupiriro?

6 Chikhulupiriro ndi limodzi mwa makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa. (Agal. 5:22) Choncho munthu sangayambe kukhala ndi chikhulupiriro payekha. N’chifukwa chake Yesu anatiuza kuti tizipempha Yehova kuti atipatse mzimu wake woyera. Anatitsimikiziranso kuti Yehova “adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akum’pempha.”—Luka 11:13.

7. Perekani chitsanzo chosonyeza zimene tingachite kuti chikhulupiriro chathu chikhalebe cholimba.

7 Munthu akakhala ndi chikhulupiriro amafunika kuchilimbitsa nthawi zonse. Chikhulupiriro tingachiyerekezere ndi moto. Munthu akayatsa moto amafunika kuusonkhezera kuti usazime. Kupanda kutero umayamba kuzirala mpaka kungotsala phulusa. N’chimodzimodzi ndi chikhulupiriro chathu. Kuphunzira Mawu a Mulungu nthawi zonse kumathandiza kuti chikhulupirirocho chisazirale. Choncho tiyenera kupitiriza kuphunzira Baibulo n’cholinga choti tizilikonda kwambiri komanso tizikonda Mulungu. Tikatero chikhulupiriro chathu chidzalimba kwambiri.

8. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tilimbitse chikhulupiriro chathu?

8 Pali zinthu zinanso zimene tiyenera kuchita kuti tilimbitse chikhulupiriro chathu. Tikaphunzira n’kufika pobatizidwa tiyenera kupitiriza kuphunzira Baibulo mozama. (Aheb. 6:1, 2) Mwachitsanzo, tingaphunzire maulosi amene anakwaniritsidwa kale. Pophunzira Baibulo tiyeneranso kudziyesa n’kuona ngati zochita zathu zikugwirizana ndi zimene Mulungu amayembekezera kwa anthu amene ali ndi chikhulupiriro champhamvu.—Werengani Yakobo 1:25; 2:24, 26.

9, 10. Kodi zinthu zotsatirazi zingatithandize bwanji kukhala ndi chikhulupiriro cholimba? (a) kugwirizana ndi anthu abwino, (b) kusonkhana ndiponso (c) kulalikira.

9 Mtumwi Paulo ananena kuti Akhristu akhoza kulimbikitsana ndiponso kuthandizana kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba. (Aroma 1:12) Kucheza ndi Akhristu anzathu, makamaka amene ‘chikhulupiriro chawo chayesedwa,’ kungathandize kuti chikhulupiriro chathunso chilimbe kwambiri. (Yak. 1:3) Munthu akamagwirizana ndi anthu oipa chikhulupiriro chake chimafooka, koma akamagwirizana ndi anthu abwino chimalimba kwambiri. (1 Akor. 15:33) N’chifukwa chake Baibulo limatiuza kuti “tisaleke kusonkhana pamodzi” komanso kulimbikitsana. (Werengani Aheberi 10:24, 25.) Ubwino wina wa misonkhano ndi wakuti mfundo zimene timaphunzira zimalimbitsa chikhulupiriro chathu. Izi zikugwirizana ndi mawu a Paulo akuti: “Munthu amakhala ndi chikhulupiriro chifukwa cha zimene wamva.” (Aroma 10:17) Kodi ifeyo timaona kuti misonkhano yathu ndi yofunika kwambiri?

10 Tikamagwira ntchito yolalikira timathandiza anthu ena kukhala ndi chikhulupiriro komanso timalimbitsa chikhulupiriro chathu. Mofanana ndi Akhristu oyambirira, tikamalalikira timayamba kukhulupirira kwambiri Yehova ndiponso kulankhula molimba mtima nthawi zonse.—Mac. 4:17-20; 13:46.

11. (a) N’chiyani chinathandiza Yoswa ndi Kalebe kukhala ndi chikhulupiriro cholimba? (b) Kodi ife tingatani kuti tikhale ngati Kalebe ndi Yoswa?

11 Chikhulupiriro chathu chimalimba tikaona kuti Yehova akutithandiza ndiponso kuyankha mapemphero athu. Izi n’zimene zinachitikira Kalebe ndi Yoswa. Iwo anakhulupirira kwambiri Yehova pamene anapita kukazonda Dziko Lolonjezedwa. Chikhulupiriro chawo chinapitiriza kulimba ataona kuti Yehova ankawatsogolera pa moyo wawo wonse. M’pake kuti Yoswa anauza Aisiraeli ndi mtima wonse kuti: “Pamawu onse abwino amene Yehova Mulungu wanu ananena kwa inu, palibe ngakhale amodzi omwe sanakwaniritsidwe.” Kenako anadzanena kuti: “Tsopano opani Yehova ndi kum’tumikira mosalakwitsa ndiponso mokhulupirika. . . . Ine ndi a m’nyumba yanga, tizitumikira Yehova.” (Yos. 23:14; 24:14, 15) Ifenso tikaona mmene Yehova akutithandizira tingayambe kumukhulupirira kwambiri.—Sal. 34:8.

KODI TINGASONYEZE BWANJI KUTI TILI NDI CHIKHULUPIRIRO?

12. Kodi Yakobo ananena kuti tingasonyeze bwanji kuti tili ndi chikhulupiriro cholimba?

12 Kodi tingasonyeze bwanji kuti tili ndi chikhulupiriro cholimba? Yakobo anayankha funsoli ponena kuti: “Ndikuonetsa chikhulupiriro changa mwa ntchito.” (Yak. 2:18) Zochita zathu zimasonyeza ngati tili ndi chikhulupiriro chenicheni kapena ayi. Tiyeni tikambirane zinthu zina zimene zingasonyeze kuti tili ndi chikhulupiriro cholimba.

Tikamalalikira mwakhama timasonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro cholimba (Onani ndime 13)

13. Kodi kulalikira kumasonyeza bwanji kuti tili ndi chikhulupiriro cholimba?

13 Kulalikira ndi njira imodzi imene tingasonyezere kuti tili ndi chikhulupiriro cholimba. Munthu amene amagwira ntchito imeneyi amakhulupirira kuti Mulungu adzawononga dziko loipali pa nthawi yake ndipo “sadzachedwa.” (Hab. 2:3) Choncho kuti tidziwe ngati chikhulupiriro chathu n’cholimba kapena ayi tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndimaona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri? Kodi ndikuchita zonse zimene ndingathe pa ntchitoyi? Kodi ndimayesetsa kupeza njira zowonjezera zimene ndimachita mu utumiki?’ (2 Akor. 13:5) ‘Tikamalengeza poyera chikhulupiriro chathu kuti tipulumuke’ timasonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro cholimba.—Werengani Aroma 10:10.

14, 15. (a) Kodi tingasonyeze bwanji kuti tili ndi chikhulupiriro? (b) Fotokozani zimene anthu ena anachita posonyeza kuti amakhulupirira Yehova.

14 Timasonyezanso kuti tili ndi chikhulupiriro tikamapirira mavuto a m’dzikoli. Kaya tili ndi mavuto monga matenda, nkhawa kapena umphawi, tiyenera kukhulupirira kuti Yehova ndi Yesu adzatithandiza pa nthawi yoyenera. (Aheb. 4:16) Tingasonyeze kuti timakhulupirira Yehova tikamapemphera kuti azitithandiza. Yesu ananena kuti tikhoza kupempherera zinthu monga ‘chakudya chofunika pa tsiku lililonse.’ (Luka 11:3) Nkhani za m’Baibulo zimatitsimikizira kuti Yehova adzatithandiza. Paja pa nthawi yachilala ku Isiraeli, iye anapatsa Eliya chakudya ndi madzi. Anachititsa kuti ‘akhwangwala azimubweretsera mkate ndi nyama m’mawa ndi madzulo, ndipo iye ankamwa madzi mumtsinje.’ (1 Maf. 17:3-6) Ifenso tizikhulupirira kuti Yehova angatithandize kuti tizipeza zofunika pa moyo.

Tikamapirira mavuto, timasonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro cholimba (Onani ndime 14)

15 Timakhulupirira kuti kutsatira mfundo za m’Baibulo kungatithandize kupeza zofunika pa moyo. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina wa ku Asia dzina lake Rebecca. Iye ndi mwamuna wake akhala akutsatira mfundo za pa Mateyu 6:33 ndi Miyambo 10:4. Iwo amayesetsa kuika za Ufumu patsogolo komanso kugwira ntchito mwakhama. Rebecca ananena kuti pa nthawi ina mwamuna wake anaona kuti ntchito yake ikhoza kuwalepheretsa kulambira Yehova bwinobwino. Choncho anaisiya ngakhale kuti anali ndi ana 4 oti aziwasamalira. Ndiyeno Rebecca anafotokoza kuti: “Tinayamba kupanga maswiti n’kumagulitsa. Pa zaka zimene tinkachita zimenezi kuti tizipeza kangachepe, tinaona kuti Yehova sanatisiye. Palibe ngakhale tsiku limodzi limene tinagona ndi njala.” Kodi inunso mwakumanapo ndi zinthu zimene zalimbitsa chikhulupiriro chanu?

16. N’chifukwa chiyani tiyenera kudalira Mulungu?

16 Tisamakayikire kuti zinthu zizitiyendera bwino tikamatsatira malangizo a Mulungu. Paulo anagwira mawu a Habakuku polemba kuti: “Wolungama adzakhala ndi moyo mwa chikhulupiriro chake.” (Agal. 3:11; Hab. 2:4) Choncho timafunika kukhulupirira Yehova chifukwa ndi amene angatithandize kwambiri. Paulo ananena kuti Mulungu ndi “amene angathe kuchita zazikulu kwambiri kuposa zonse zimene timapempha kapena kuganiza, malinga ndi mphamvu yake imene ikugwira ntchito mwa ife.” (Aef. 3:20) Atumiki a Yehovafe timachita zonse zimene tingathe potumikira Mulungu. Koma timadziwanso kuti pali zinthu zina zimene sitingakwanitse patokha. Choncho timayamikira kwambiri kuti Mulungu akutithandiza ndiponso kutidalitsa.

TIZIPEMPHA YEHOVA KUTI ALIMBITSE CHIKHULUPIRIRO CHATHU

17. (a) Kodi Yesu anayankha bwanji zimene atumwi ake anapempha? (b) N’chiyani chikusonyeza kuti Mulungu akhoza kuwonjezera chikhulupiriro chathu?

17 Mfundo zimene takambiranazi zingatichititse kulankhula mofanana ndi atumwi amene ananena kuti: “Tiwonjezereni chikhulupiriro.” (Luka 17:5) Yesu anayankha atumwiwo pa mwambo wa Pentekosite mu 33 C.E. Iye anawapatsa mzimu woyera ndipo iwo anayamba kumvetsa bwino cholinga cha Mulungu. Zimenezi zinalimbitsa chikhulupiriro chawo ndipo anayamba kugwira mwakhama ntchito yolalikira. (Akol. 1:23) Koma kodi Mulungu angawonjezere chikhulupiriro chathu masiku ano? Baibulo limanena kuti akhoza kuchita zimenezi ngati “tingamupemphe mogwirizana ndi chifuniro chake.”—1 Yoh. 5:14.

18. Kodi Yehova adzatidalitsa bwanji tikakhala ndi chikhulupiriro cholimba?

18 M’nkhaniyi, taona kuti Yehova amasangalala ndi anthu amene amamukhulupirira ndi mtima wonse. Iye adzayankha tikamapempha kuti atiwonjezere chikhulupiriro. Ndiyeno chikhulupiriro chathu chikalimba, tidzakhala “oyenerera ufumu wa Mulungu.”—2 Ates. 1:3, 5.

^ ndime 4 Kuti muone zitsanzo za anthu ena, werengani mbiri ya moyo wa Josephine Elias (Galamukani! ya September 2009), Edmund Schmidt (Nsanja ya Olonda ya September 1, 2010) ndi Trophim R. Nsomba (Nsanja ya Olonda ya April 15, 2015).