Tiziganizira Kwambiri za Yehova
“Sinkhasinkha zinthu zimenezi mozama. Dzipereke pa zinthu zimenezi kuti anthu onse aone kuti ukupita patsogolo.”—1 TIM. 4:15.
NYIMBO: 57, 52
1, 2. Kodi anthufe timasiyana bwanji ndi nyama?
UBONGO wathu umachita zinthu zodabwitsa kwambiri. Mwachitsanzo, timatha kuphunzira chilankhulo ndipo izi zimatithandiza kuwerenga, kulemba, kulankhula komanso kuzindikira mawu amene munthu wina akulankhula. Timathanso kupemphera ndiponso kuimba nyimbo zotamanda Yehova. Ndife osiyana ndi nyama chifukwa chakuti sizingathe kuchita zinthu zimenezi. Mpaka pano, asayansi samvetsa mmene ubongo wathu umachitira zonsezi.
2 Mulungu ndi amene anatipatsa luso lochita zinthu zimene tatchulazi. (Sal. 139:14; Chiv. 4:11) Koma anthufe timasiyananso ndi nyama m’njira ina yapadera. Tinalengedwa “m’chifaniziro cha Mulungu” ndipo anatipatsa ufulu wosankha zochita. Choncho tingasankhe kugwiritsa ntchito mphatso ya kulankhula potamanda Yehova.—Gen. 1:27.
3. Kodi Yehova watipatsa mphatso iti yotithandiza kuti tikhale anzeru?
3 Baibulo ndi mphatso ina imene Yehova wapereka kwa anthu amene amafuna kumutamanda. Panopa, Baibulo lathunthu kapena mbali yake likupezeka m’zilankhulo zoposa 2,800. Sal. 40:5; 92:5; 139:17) Munthu wotere amapeza ‘nzeru zothandiza kuti adzapulumuke.’—Werengani 2 Timoteyo 3:14-17.
Munthu akamaphunzira Mawu a Mulungu amayamba kuganiza mofanana ndi mmene Yehova amaganizira. (4. (a) Kodi kusinkhasinkha n’kutani? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?
4 Nthawi zina, Baibulo limagwiritsa ntchito mawu oti kusinkhasinkha ponena za kuganizira kwambiri zinthu zinazake. Munthu amatha kusinkhasinkha kapena kuganizira zinthu zabwino kapena zoipa. (Sal. 77:12; Miy. 24:1, 2) Koma zinthu zabwino kwambiri zimene tingaziganizire ndi zokhudza Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu. (Yoh. 17:3) M’nkhaniyi tikambirana mafunso awa: Kodi tingatani kuti tiziganizira kwambiri zimene tikuwerenga? Kodi ndi zinthu ziti zimene tiyenera kuziganizira? Nanga n’chiyani chingatithandize kuti tizikonda kusinkhasinkha?
MUZIGANIZIRA ZIMENE MUKUWERENGA
5, 6. Kodi tingatani kuti tizimvetsa ndiponso kukumbukira zimene timawerenga?
5 Pali zinthu zina zimene timatha kuchita popanda kuganiza monga kupuma, kuyenda kapena kukwera njinga. Nthawi zina zimathekanso kuwerenga popanda kuganizira kwambiri. Choncho tikamawerenga tiyenera kuyesetsa kuti timvetse tanthauzo la zimene tikuwerengazo. Mwachitsanzo, tikamaliza kuwerenga ndime ina kapena tisanayambe kamutu kena, tingaime kaye n’kuganizira zimene tawerengazo kuti tione ngati tazimvetsa bwinobwino.
6 Asayansi amanenanso kuti kuwerenga mokweza kumathandiza kuti tizikumbukira bwino zinthu. M’pake kuti Mulungu anauza Yoswa kuti azisinkhasinkha buku la malamulo. Ndiyeno mawu achiheberi amene anawamasulira kuti “kusinkhasinkha” pa Yoswa 1:8 (Werengani.) amatanthauza kuwerenga “mochita kutchula mawu chapansipansi.” Kuwerenga Baibulo mokweza kumathandiza munthu kuganizira zimene akuwerengazo komanso kuzikumbukira.
7. Kodi tingatani kuti tiziganizira Mawu a Mulungu popanda kusokonezedwa? (Onani chithunzi patsamba 23.)
7 Tiyenera kuchita khama kuti tiziganizira kwambiri zimene tikuwerenga. Tikutero chifukwa chakuti ubongo wathu suchedwa kusokonezedwa ndi zinthu zina. Choncho tingachite bwino kuwerenga ndi kuganizira zimene tikuwerengazo pa nthawi imene sitinatope komanso pamalo opanda zinthu zosokoneza. Davide ananena kuti ankakonda kuganizira za Yehova usiku. (Sal. 63:6) Ngakhale kuti Yesu anali wangwiro, iye ankakonda kupita kumalo aphee kuti azikaganizira zinthu zofunika ndiponso kupemphera.—Luka 6:12.
ZINTHU ZINA ZABWINO ZIMENE TINGAZIGANIZIRE
8. (a) Kodi ndi zinthu zinanso ziti zimene tingaziganizire? (b) Kodi Yehova amamva bwanji tikamauza ena zokhudza iyeyo?
8 Palinso zinthu zina zimene tingaziganizire. Mwachitsanzo, mukaona zinthu zochititsa chidwi zimene Yehova analenga muzidzifunsa kuti: ‘Kodi zimenezi zikundiphunzitsa chiyani za Yehova?’ Mukatero mukhoza kuona ubwino wa Yehova n’kumamutamanda. Mukhozanso kumauza ena za Yehovayo. (Sal. 104:24; Mac. 14:17) Yehova amasangalala tikamapemphera, tikamaganizira zimene taphunzira komanso tikamauza ena zimene taphunzirazo. Paja Baibulo limanena kuti: “Anthu oopa Yehova analankhulana, aliyense ndi mnzake, ndipo Yehova anatchera khutu ndi kumvetsera. Buku la chikumbutso linayamba kulembedwa pamaso pake. Buku limeneli linali lonena za anthu oopa Yehova ndi anthu amene anali kuganizira za dzina lake.”—Mal. 3:16.
9. (a) Kodi Paulo anauza Timoteyo kuti ayenera kuganizira zinthu ziti? (b) Kodi tingaganizire zinthu ziti tisanapite kukalalikira?
9 Mtumwi Paulo anauza Timoteyo kuti ayenera kusinkhasinkha kapena kuti kuganizira zimene amalankhula, kuchita komanso kuphunzitsa. (Werengani 1 Timoteyo 4:12-16.) Ifenso tili ndi zinthu zambiri zimene tingaziganizire. Mwachitsanzo, tikamakonzekera kukaphunzitsa ena, ndi bwino kuganizira mafunso komanso zitsanzo zimene zingathandize wophunzirayo. Zimenezi zingatithandize kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba komanso kuti tiziphunzitsa Mawu a Mulungu mwaluso. Kuganizira zinthu zolimbikitsa tisanapite mu utumiki n’kothandizanso. (Werengani Ezara 7:10.) Ngati tiwerenga nkhani inayake ya m’buku la Machitidwe tikhoza kulalikira mwakhama. Tingachitenso bwino kuganizira mavesi komanso mabuku amene tikufuna kukawagwiritsa ntchito mu utumiki. (2 Tim. 1:6) Tiziganiziranso nkhani zimene zingachititse chidwi anthu a m’gawo lathu. Tikamachita zimenezi tidzatha kuphunzitsa Mawu a Mulungu mogwira mtima.—1 Akor. 2:4.
10. Kodi ndi zinthu zinanso ziti zimene tingaziganizire?
10 Kodi ndi zinthu zinanso ziti zimene tingaziganizire? Ngati mumalemba Buku Lapachaka, mungachite bwino kuganizira kaye nkhani imene mwawerengayo musanapite pa nkhani ina. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti muimvetse bwino nkhaniyo ndiponso kuti ikufikeni pamtima. Mukamawerenga nkhani inayake, mungachite bwino kudula mizere kunsi kwa mfundo zazikulu kapena kulemba notsi zimene mungagwiritse ntchito pa ulendo wobwereza, ulendo waubusa kapena pokamba nkhani. Choncho, tikamaganizira zimene tawerenga, nkhaniyo ingatifike pamtima ndipo tingathokoze Yehova chifukwa cha zimene taphunzirazo.
mfundo zikuluzikulu zimene mumamva pa misonkhano, mungamaziwerenge n’kumaganizira zimene mukuphunzira. Mukhozanso kumaganizira nkhani zopezeka m’magazini atsopano komanso m’mabuku amene timalandira pa msonkhano wachigawo. MukamawerengaTIZIGANIZIRA MAWU A MULUNGU TSIKU LILILONSE
11. Kodi chinthu chofunika kuchiganizira kwambiri n’chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani tikutero? (Onani mawu am’munsi.)
11 Chinthu chofunika kuchiganizira kwambiri ndi Mawu a Mulungu. Tikutero chifukwa chakuti kuchita zimenezi kungatithandize kukumbukira malemba. Ndiyeno ngati nthawi ina taletsedwa kukhala ndi Baibulo, tikhoza kuganizira malemba amene tikuwakumbukirawo kapena nyimbo za Ufumu zimene tinaloweza. * (Mac. 16:25) Mzimu woyera ungatithandize kuti tizikumbukira zinthu zabwino zimene tinaphunzira.—Yoh. 14:26.
12. Kodi tingatsatire njira iti powerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse?
12 Kodi tingatsatire njira iti powerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse? Tingasankhe masiku ena pa mlungu kuti tiziwerenga Baibulo motsatira ndandanda ya Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Koma masiku ena tingamawerenge mabuku monga Mateyu, Maliko, Luka ndi Yohane n’kumaganizira zimene Yesu ankaphunzitsa ndi kuchita. (Aroma 10:17; Aheb. 12:2; 1 Pet. 2:21) Tilinso ndi buku limene limafotokoza mwatsatanetsatane zimene Yesu anachita ali padziko lapansi. Bukuli lingatithandize kuti tizimvetsa bwino nkhani zimene zinalembedwa m’mabuku a m’Baibulo onena za Yesu.—Yoh. 14:6.
N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUGANIZIRA ZA YEHOVA NDI YESU?
13, 14. N’chifukwa chiyani tiyenera kupitiriza kuganizira za Yehova ndi Yesu?
13 Kuganizira kwambiri za Yehova ndi Yesu kumathandiza kuti tikhale Akhristu odalirika komanso tikhale ndi chikhulupiriro cholimba. (Aheb. 5:14; 6:1) Ngati sitipeza mpata wochita zimenezi, ubwenzi wathu ndi Yehova ukhoza kuyamba kusokonekera mpaka kufika potheratu. (Aheb. 2:1; 3:12) Yesu anasonyeza kuti munthu sangasunge Mawu a Mulungu ngati Mawuwo sanamufike pamtima. Zingakhale zosavuta kuti munthu wotereyu atengeke ndi ‘nkhawa, chuma ndi zosangalatsa za moyo uno ndipo zipatso zake sizikhwima.’—Luka 8:14, 15.
14 Choncho tiyeni tisasiye kuganizira kwambiri Mawu a Mulungu. Izi zidzatithandiza kutsatira kwambiri makhalidwe a Yehova. (2 Akor. 3:18) Tili ndi mwayi waukulu wophunzira za Mulungu komanso kutsanzira makhalidwe ake mpaka muyaya.—Mlal. 3:11.
15, 16. (a) Kodi kuganizira kwambiri za Yehova ndi Yesu kwakuthandizani bwanji? (b) Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatilepheretse kuganizira Mawu a Mulungu? (c) N’chifukwa chiyani sitiyenera kusiya kusinkhasinkha?
15 Kuganizira za Yehova ndi Yesu kumathandizanso kuti tisafooke. Tikatero timalimbikitsa kwambiri abale ndi alongo komanso anthu amene timawapeza tikamalalikira. Kuganizira kwambiri zimene Yehova anachita popereka dipo kungatithandizenso kuti tiziona kuti ubwenzi wathu ndi iye ndi wofunika kwambiri. (Aroma 3:24; Yak. 4:8) M’bale wina wa ku South Africa dzina lake Mark anakhala m’ndende kwa zaka zitatu chifukwa chokana usilikali ndipo anati: “Munthu akamasinkhasinkha zimakhala ngati akuyenda ulendo n’kumaona zinthu zatsopano. Zili choncho chifukwa chakuti akamaganizira amazindikira zinthu zatsopano zokhudza Yehova. Nthawi zina ndimada nkhawa ndikaganizira za m’tsogolo. Koma ndikangotenga Baibulo n’kuwerenga nkhani inayake, mtima wanga umakhala m’malo.”
16 Kunena zoona, masiku ano pali zinthu zambiri zimene zingatilepheretse kuganizira Mawu a Mulungu. M’bale wina wa ku Africa dzina lake Patrick ananena kuti m’mutu mwake mumayenda zinthu zambirimbiri. Zina zimakhala zabwino koma zina zimakhala zoipa. Tsiku lililonse amafunika kudzifufuza ndipo nthawi zambiri amapeza kuti akudera nkhawa zinazake. Ndiyeno amapempha Yehova kuti asiye kuganizira zimenezo n’cholinga choti asinkhesinkhe zinthu zofunika. Ngakhale kuti zimenezi zimatenga nthawi, zimamuthandiza kuti asinkhesinkhe bwino komanso kuti ubwenzi wake ndi Yehova ulimbe kwambiri. Zimamuthandizanso kuti amvetse bwino mfundo za m’Malemba. (Sal. 94:19) Anthu amene ‘amafufuza Malemba mosamala’ tsiku lililonse n’kumawaganizira amadalitsidwa kwambiri.—Mac. 17:11.
KODI TINGAPEZE BWANJI NTHAWI YOGANIZIRA MAWU A MULUNGU?
17. Kodi inuyo mumatani kuti mupeze mpata woganizira Mawu a Mulungu?
17 Anthu ena amadzuka m’mawa kwambiri kuti awerenge Baibulo, kuganizira zimene awerengazo ndiponso kupemphera. Ena amachita zimenezi masana pa nthawi yopuma, apo ayi madzulo kapena usiku asanakagone. Palinso anthu ena amene amawerenga Baibulo m’mawa ndi madzulo omwe. Choncho tinganene kuti iwo ‘amaliwerenga usana ndi usiku.’ (Yos. 1:8) Koma mfundo yofunika ndi yakuti tiziyesetsa kupeza mpata wowerenga Mawu a Mulungu n’kumawaganizira tsiku lililonse.—Aef. 5:15, 16.
18. Kodi Baibulo limalonjeza chiyani kwa anthu amene amaganizira Mawu a Mulungu tsiku lililonse ndiponso kuyesetsa kuwatsatira?
18 Baibulo limalonjeza kuti Yehova adzadalitsa anthu amene amaganizira Mawu ake ndiponso kuwatsatira. (Werengani Salimo 1:1-3.) Paja Yesu ananena kuti: “Odala ndi amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga.” (Luka 11:28) Koma chofunika kwambiri n’chakuti tikamaganizira Mawu a Mulungu tsiku lililonse tidzatha kulemekeza Yehova. Ndiyeno iye adzatithandiza kukhala osangalala panopa komanso adzatipatsa moyo wosatha m’dziko latsopano.—Yak. 1:25; Chiv. 1:3.
^ ndime 11 Onani nkhani yakuti, “Tinayesetsa Kuti Tikhale Olimba Mwauzimu” mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 2006.