Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi ‘Mumakonda Anzanu Ngati Mmene Mumadzikondera Nokha’?

Kodi ‘Mumakonda Anzanu Ngati Mmene Mumadzikondera Nokha’?

“Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.”—MAT. 22:39.

NYIMBO: 73, 36

1, 2. Kodi Malemba amasonyeza kuti chikondi n’chofunika bwanji?

CHIKONDI ndi khalidwe lalikulu kwambiri la Yehova Mulungu. (1 Yoh. 4:16) Poyamba, iye analenga Yesu ndipo anakhala naye kumwamba kwa zaka zosawerengeka. Kumwambako, Yesu anaphunzira makhalidwe a Mulungu monga chikondi. (Akol. 1:15) Ndiyeno pa moyo wake wonse kumwamba ndiponso padzikoli, iye wakhala akutsanzira Yehova posonyeza chikondi. Choncho sitikukayikira kuti ulamuliro wa Yehova ndi Yesu udzakhalabe wachikondi mpaka kalekale.

2 Munthu wina atafunsa Yesu za lamulo lalikulu kwambiri, iye anayankha kuti: “‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.’ Limeneli ndilo lamulo lalikulu kwambiri komanso loyamba. Lachiwiri lofanana nalo ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’”—Mat. 22:37-39.

3. Kodi anzathu amene tiyenera kuwakonda ndi ati?

3 Yesu ananena kuti tiyenera kukonda kwambiri Yehova ndi anzathu. Izi zikusonyeza kuti chikondi n’chofunika kwambiri. Koma kodi anzathu amene tiyenera kuwakondawo ndi ati? Ngati tili pa banja, mnzathu wapamtima kwambiri ndi mwamuna kapena mkazi wathu. Anzathu ena ndi abale ndi alongo mumpingo. Nawonso anthu amene timakumana nawo mu utumiki ndi anzathu. Ndiyeno m’nkhaniyi tikambirana mmene tingasonyezere kuti timakonda anzathu onsewa.

TIZIKONDA MWAMUNA KAPENA MKAZI WATHU

4. N’chiyani chingatithandize kuti tikhale ndi banja losangalala?

4 Yehova ndi amene anayambitsa banja. Iye analenga Adamu ndi Hava n’cholinga choti akhale banja losangalala ndiponso kuti abereke ana n’kudzaza dziko lapansi. (Gen. 1:27, 28) Koma iwo sanamvere Yehova ndipo zinachititsa kuti banja lawo lisokonekere. Zinachititsanso kuti anthu onse akhale ochimwa ndiponso kuti azifa. (Aroma 5:12) Ngakhale zili choncho, malangizo a m’Baibulo angatithandize kuti tikhale ndi banja losangalala. Tikutero chifukwa chakuti malangizowa ndi ochokera kwa amene anayambitsa banja.—Werengani 2 Timoteyo 3:16, 17.

5. Kodi chikondi n’chofunika bwanji m’banja?

5 Baibulo limasonyeza kuti chikondi n’chofunika kwambiri kuti anthu azigwirizana. Zimenezi n’zofunika makamaka m’banja. Pofotokoza za chikondi chenicheni, Paulo anati: “Chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima. Chikondi sichichita nsanje, sichidzitama, sichidzikuza, sichichita zosayenera, sichisamala zofuna zake zokha, sichikwiya. Sichisunga zifukwa. Sichikondwera ndi zosalungama, koma chimakondwera ndi choonadi. Chimakwirira zinthu zonse, chimakhulupirira zinthu zonse, chimayembekezera zinthu zonse, chimapirira zinthu zonse. Chikondi sichitha.” (1 Akor. 13:4-8) Kuganizira ndiponso kugwiritsa ntchito malangizowa kungatithandize kuti tikhale ndi banja losangalala.

Mawu a Mulungu angatithandize kukhala ndi banja losangalala (Onani ndime 6 ndi 7)

6, 7. (a) Kodi Baibulo limati mutu wa mkazi ndi ndani? (b) Kodi mwamuna angatani kuti akhale mutu wabwino?

6 Yehova anasankha mwamuna kuti akhale mutu wa banja. Paja Paulo anati: “Ndikufuna mudziwe kuti mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu. Mutu wa mkazi ndi mwamuna, ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu.” (1 Akor. 11:3) Koma Mulungu amafuna kuti mwamuna azitsogolera banja lake mwachikondi osati mwankhanza. Yehova amatsogolera mwachikondi ndiponso mokoma mtima. N’chifukwa chake Yesu amamulemekeza ndiponso kumukonda. (Yoh. 14:31) Yehova akanakhala wankhanza, si bwenzi Yesu akuchita zimenezi.

7 Ngakhale kuti mwamuna ndi mutu wa mkazi wake, Baibulo limati ayenera ‘kumupatsa ulemu.’ (1 Pet. 3:7) Mwamuna angachite zimenezi poganizira zofuna za mkaziyo ndiponso kumulola kuti azisankha zochita pa zinthu zina. Baibulo limanena kuti: “Amuna inu, pitirizani kukonda akazi anu monga mmene Khristu anakondera mpingo n’kudzipereka yekha chifukwa cha mpingowo.” (Aef. 5:25) Lembali likusonyeza kuti Yesu ankakonda ophunzira ake moti analolera kuwafera. Mwamuna akamatsanzira Yesu potsogolera mkazi wake mwachikondi, zimakhala zosavuta kuti mkaziyo azimukonda, kumulemekeza ndiponso kumumvera.—Werengani Tito 2:3-5.

TIZIKONDA AKHRISTU ANZATHU

8. Kodi Baibulo limanena kuti Akhristu ayenera kuchita chiyani?

8 Padziko lapansi pali Akhristu anzathu ambiri amene amalambiranso Yehova. Ndiyeno Baibulo limanena kuti: “Tiyeni tichitire onse zabwino, koma makamaka abale ndi alongo athu m’chikhulupiriro.” (Agal. 6:10; werengani Aroma 12:10.) Nayenso mtumwi Petulo analemba kuti: “Tsopano, popeza mwayeretsa miyoyo yanu mwa kukhala omvera choonadi ndipo zotsatira zake n’zakuti mumakonda abale mopanda chinyengo, kondanani kwambiri kuchokera mumtima.” Iye anauzanso Akhristu anzake kuti: “Koposa zonse, khalani okondana kwambiri.”—1 Pet. 1:22; 4:8.

9, 10. N’chiyani chimathandiza kuti anthu a Mulungu azigwirizana?

9 Gulu lathu lapadziko lonse ndi lapadera kwambiri chifukwa chakuti timakondana. Yehova amatipatsanso mzimu wake woyera chifukwa choti timamukonda ndiponso kumvera malamulo ake. Mzimuwo ndi wamphamvu kwambiri ndipo umatithandiza kukhala ogwirizana ndi abale ndi alongo athu padziko lonse.—Werengani 1 Yohane 4:20, 21.

10 Paulo anasonyeza kuti Akhristu ayenera kukondana ndipo analemba kuti: “Valani chifundo chachikulu, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa, ndi kuleza mtima. Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake. Monga Yehova anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso teroni. Koma kuwonjezera pa zonsezi, valani chikondi, pakuti chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.” (Akol. 3:12-14) N’zosangalatsa kwambiri kuti timagwirizana chifukwa chokondana ngakhale kuti ndife osiyana mitundu ndiponso zikhalidwe.

11. N’chiyani chimasonyeza kuti a Mboni za Yehova ndi Akhristu enieni?

11 Kukondana ndiponso kugwirizana kwa anthu a Yehova kumasonyeza kuti chipembedzo chawo ndi choona. Paja Yesu anati: “Onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.” (Yoh. 13:34, 35) Mtumwi Yohane analembanso kuti: “Ana a Mulungu ndiponso ana a Mdyerekezi amaonekera bwino ndi mfundo iyi: Aliyense amene sachita zolungama sanachokere kwa Mulungu, chimodzimodzinso amene sakonda m’bale wake. Pakuti uwu ndi uthenga umene munamva kuyambira pa chiyambi, kuti tizikondana.” (1 Yoh. 3:10, 11) A Mboni za Yehova amakondana komanso kugwirizana ndipo izi zimasonyeza kuti iwo ndi Akhristu enieni. Zimasonyezanso kuti Mulungu akuwagwiritsa ntchito kuti azilalikira uthenga wabwino wa Ufumu padziko lonse lapansi.—Mat. 24:14.

NTCHITO YOSONKHANITSA A “KHAMU LALIKULU”

12, 13. Kodi panopa a khamu lalikulu akuchita chiyani, nanga posachedwapa adzadalitsidwa bwanji?

12 Akhristu ambiri masiku ano ndi a “khamu lalikulu . . . lochokera m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse.” Iwo akuimirira “pamaso pa mpando wachifumu [wa Mulungu] ndi pamaso pa Mwanawankhosa [Yesu Khristu].” A khamu lalikuluwo ndi “amene atuluka m’chisautso chachikulu, ndipo achapa mikanjo yawo ndi kuiyeretsa m’magazi a Mwanawankhosa.” Iwo amachita zimenezi pokhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu. Amakondanso Yehova ndi Yesu ndipo amachita “utumiki wopatulika usana ndi usiku.”—Chiv. 7:9, 14, 15.

13 Posachedwapa, Mulungu awononga dziko loipali pa “chisautso chachikulu.” (Mat. 24:21; werengani Yeremiya 25:32, 33.) Koma popeza Yehova amakonda atumiki ake, adzawapulumutsa n’kuwatsogolera kuti alowe m’dziko latsopano. Paja zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, Mulungu analonjeza kuti: “Adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.” Kodi inuyo mumalakalaka kudzakhalapo pa nthawi imene mavuto onse adzakhala atatha?—Chiv. 21:4.

14. Kodi panopa chiwerengero cha khamu lalikulu chafika pati?

14 Pamene masiku otsiriza ankayamba mu 1914, padziko lonse panali atumiki a Yehova masauzande ochepa chabe. Koma odzozedwa ochepawa anachita khama kwambiri pa ntchito yolalikira ngakhale kuti panali mavuto ambiri. Izi zinatheka chifukwa choti ankakonda kwambiri anzawo komanso ankathandizidwa ndi mzimu wa Mulungu. Zotsatira zake n’zakuti khamu lalikulu la anthu amene adzakhale padzikoli linayamba kusonkhanitsidwa. Panopa atumiki a Yehova afika pafupifupi 8 miliyoni ndipo amasonkhana m’mipingo yoposa 115,400. Koma chiwerengerochi chikuwonjezerekabe. Mwachitsanzo, m’chaka chautumiki cha 2014, anthu oposa 275,500 anabatizidwa. Choncho zinali ngati kuti mlungu uliwonse pankabatizidwa anthu pafupifupi 5,300.

15. Fotokozani zinthu zina zimene zikuchitika pa ntchito yolalikira.

15 Timachita chidwi kwambiri tikaganizira zonse zimene zikuchitika pa ntchito yolalikira. Panopa mabuku athu akumasuliridwa m’zilankhulo zoposa 700. Magazini ya Nsanja ya Olonda ndi imene imasindikizidwa kwambiri padziko lonse ndipo magazini oposa 52,000,000 amasindikizidwa mwezi uliwonse m’zilankhulo 247. Mabuku akuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? oposa 200,000,000 asindikizidwa m’zilankhulo zoposa 250.

16. N’chiyani chikuthandiza kuti gulu lathu lizikula kwambiri?

16 Gulu lathu likukula kwambiri chifukwa chakuti timakhulupirira Mulungu ndiponso timavomereza kuti Baibulo ndi Mawu ake. (1 Ates. 2:13) Yehova akupitiriza kutidalitsa ngakhale kuti “mulungu wa nthawi ino” amadana nafe kwambiri.—2 Akor. 4:4.

TIZIKONDA ANZATHU NTHAWI ZONSE

17, 18. Kodi atumiki a Yehova ayenera kuwaona bwanji anthu amene satumikira Mulungu?

17 Kodi atumiki a Yehova ayenera kuwaona bwanji anthu amene satumikira Mulungu? Tikamalalikira, anthu ena amamvetsera koma ena amadana ndi uthenga wathu. Ngakhale zili choncho, timatsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Nthawi zonse mawu anu azikhala achisomo, okoma ngati kuti mwawathira mchere, kuti mudziwe mmene mungayankhire wina aliyense.” (Akol. 4:6) Tikamakambirana ndi anthu zimene timakhulupirira, timalankhula “ndi mtima wofatsa ndiponso mwaulemu kwambiri” chifukwa chakuti timawakonda.—1 Pet. 3:15.

18 Ngakhale anthu akatilankhula mwachipongwe mu utumiki, timawasonyeza chikondi potsanzira zimene Yesu ankachita. Pamene “anali kunenedwa zachipongwe, sanabwezere zachipongwe. Pamene anali kuvutika, sanawopseze, koma anali kudzipereka kwa iye amene amaweruza molungama.” (1 Pet. 2:23) Nthawi zonse tiyenera kukhala odzichepetsa n’kumatsatira malangizo akuti: “Osabwezera choipa pa choipa kapena chipongwe pa chipongwe, koma m’malomwake muzidalitsa.”—1 Pet. 3:8, 9.

19. Kodi Yesu anatipatsa lamulo lotani lokhudza adani athu?

19 Kudzichepetsa kumatithandiza kumvera lamulo lofunika kwambiri limene Yesu anatipatsa. Iye ananena kuti: “Inu munamva kuti anati, ‘Uzikonda mnzako ndi kudana ndi mdani wako.’ Koma ine ndikukuuzani kuti: Pitirizani kukonda adani anu ndi kupempherera amene akukuzunzani, kuti musonyeze kuti ndinudi ana a Atate wanu wakumwamba. Chifukwa iye amawalitsira dzuwa lake pa anthu oipa ndi abwino, ndi kuvumbitsira mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.” (Mat. 5:43-45) Ngakhale adani athu atatichitira zinthu zoipa, tiyenera kuwakondabe.

20. Kodi tikudziwa bwanji kuti anthu onse padzikoli azidzakonda Mulungu ndiponso anzawo? (Onani chithunzi patsamba 21.)

20 Nthawi zonse tiyenera kuchita zinthu zosonyeza kuti timakonda Yehova komanso anzathu. Mwachitsanzo, anthu ena amene amatitsutsa akakumana ndi mavuto, tiyenera kuwathandiza. Kumbukirani kuti Paulo anati: “Anthu inu musamakhale ndi ngongole iliyonse kwa munthu aliyense, kusiyapo kukondana, popeza amene amakonda munthu mnzake wakwaniritsa chilamulo. Chifukwa malamulo onena kuti, ‘Usachite chigololo, Usaphe munthu, Usabe, Usasirire mwansanje,’ ndiponso lamulo lina lililonse limene lilipo, chidule chake chili m’mawu awa akuti, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’ Chikondi sichilimbikitsa munthu kuchitira zoipa mnzake, chotero chilamulo chimakwaniritsidwa m’chikondi.” (Aroma 13:8-10) Popeza kuti dzikoli likulamulidwa ndi Satana, anthu ambiri amasankhana mitundu komanso amakonda zachiwawa. (1 Yoh. 5:19) Koma Akhristu amayesetsa kukonda anzawo. Yehova akadzawononga Satana, ziwanda ndiponso anthu oipa, padzikoli padzakhala anthu achikondi okhaokha. Pa nthawiyo tidzasangalala kwambiri chifukwa anthu onse azidzakonda Mulungu ndiponso anzawo.