Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muziphunzitsa Ana Anu Achinyamata Kuti Azitumikira Yehova

Muziphunzitsa Ana Anu Achinyamata Kuti Azitumikira Yehova

Yesu anali kukulabe m’nzeru ndi mu msinkhu. Ndipo Mulungu ndi anthu anapitiriza kukondwera naye.”—LUKA 2:52.

NYIMBO: 41, 89

1, 2. (a) N’chifukwa chiyani makolo amada nkhawa pa nthawi imene ana awo ali achinyamata? (b) Kodi ana angachite zinthu zabwino ziti pa nthawi imene ali achinyamata?

MAKOLO amasangalala kwambiri mwana wawo akabatizidwa. Mwachitsanzo, mlongo wina dzina lake Berenice ali ndi ana 4 ndipo onsewo anabatizidwa asanakwanitse zaka 14. Iye anati: “Tinasangalala kwambiri kuona kuti ana athu akufuna kutumikira Yehova. Koma tinkadziwanso kuti anawo akamakula azikumana ndi mavuto ambiri.” Ngati muli ndi mwana wachinyamata, mukhoza kumvetsa zimene zinkamudetsa nkhawa mlongoyu.

2 Katswiri wina wodziwa za kaganizidwe ka ana anavomereza kuti nthawi imene ana ali achinyamata ingakhale yovuta kwa makolo ndiponso kwa anawo. Koma iye ananena kuti makolo sayenera kuona kuti achinyamatawo ndi ovuta kapena achibwana. Ayenera kudziwa kuti nthawi imeneyi amaganiza kwambiri, amafuna kusonyeza kuti ali ndi luso lochita zinthu zina paokha komanso amafunitsitsa kucheza ndi anzawo. Komabe pa nthawiyi, angayambenso kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ngati mmene Yesu anachitira ali wachinyamata. (Werengani Luka 2:52.) Akhozanso kusankha kudzipereka kwa Yehova ndiponso kumumvera. Angawonjezerenso luso lolalikira n’kumafunitsitsa kuchita zambiri potumikira Mulungu. Koma kodi mungawathandize bwanji kuti azitumikira Yehova? Mungachite bwino kutsatira chitsanzo cha Yesu chifukwa ankaphunzitsa otsatira ake mwachikondi, modzichepetsa ndiponso mozindikira.

MUZIWAKONDA

3. N’chifukwa chiyani atumwi ankaona kuti Yesu ndi mnzawo wapamtima?

3 Atumwi ankaona kuti Yesu anali Ambuye wawo komanso mnzawo wapamtima. (Werengani Yohane 15:15.) Kale, nthawi zambiri munthu sankauza akapolo ake zakukhosi kwake. Koma Yesu ankakonda ophunzira ake ndipo ankacheza nawo. Iye ankawauza maganizo ake ndiponso mmene akumvera mumtima mwake. Ankamvetseranso ophunzirawo akamamufotokozera zimene akuganiza komanso mmene akumvera. (Maliko 6:30-32) Izi zinathandiza kuti Yesu azigwirizana kwambiri ndi atumwiwo komanso kuti iwo akhale okonzeka kudzagwira ntchito yomwe anadzapatsidwa.

4. Kodi makolo angakhale bwanji anzawo apamtima a ana awo? (Onani chithunzi patsamba 8.)

4 Bambo wina dzina lake Michael ali ndi ana awiri ndipo ananena kuti: “Ngakhale kuti sitingafanane zaka ndi ana athu, tikhoza kukhalabe anzawo apamtima.” Anthu akamagwirizana amachitira zinthu limodzi. Choncho mungachite bwino kupemphera n’kuona ngati ndi zotheka kuti muchepetse nthawi imene mumagwira ntchito n’cholinga choti muzipeza mpata wocheza ndi ana anu. Anthu amene amagwirizana amakondanso zinthu zofanana. Ndiyeno mungachite bwino kuyesetsa kukonda nyimbo, mafilimu ndiponso masewera amene ana anu amakonda. Mlongo wina wa ku Italy dzina lake Ilaria anati: “Makolo anga ankachita chidwi ndi nyimbo zimene ndinkakonda. Bambo anga anali mnzanga wapamtima kwambiri ndipo ndinkamasuka nawo moti ndinkawauza nkhani zimene zinkandivuta kuuza anthu ena.” Sikuti ana anu adzasiya kukulemekezani mukamayesetsa kukhala anzawo apamtima ndiponso kuwathandiza kuti akhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. (Sal. 25:14) M’malomwake adzaona kuti mumawakonda ndiponso kuwalemekeza ndipo sadzavutika kumasuka nanu n’kumakuuzani zimene zili mumtima mwawo.

5. Kodi ophunzira a Yesu anayenera kuchita chiyani kuti azisangalala potumikira Yehova?

5 Yesu ankakonda kwambiri ophunzira ake ndipo ankafuna kuti iwo azisangalala potumikira Yehova mwakhama. Choncho ankawalimbikitsa kuti azikonda kwambiri ntchito yolalikira ndipo anawauza kuti adzawathandiza.—Mat. 28:19, 20.

6, 7. N’chifukwa chiyani makolo achikondi amaphunzitsa ana awo kuti azikonda kuchita zinthu zokhudza kulambira?

6 N’zosachita kufunsa kuti mumafunitsitsa kuti ana anu akhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Nayenso Mulungu amafuna kuti muzilera ana anu “m’malangizo [ake] ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4) Choncho nthawi zonse muyenera kuchita zinthu zothandiza ana anu kulimbitsa ubwenzi wawo ndi Yehova. Paja makolo amaonetsetsa kuti ana awo azipita kusukulu chifukwa chodziwa ubwino wake. N’chimodzimodzinso ndi kuwaphunzitsa za Yehova. Makolo achikondi amaonetsetsa kuti ana awo azikhala nawo pa kulambira kwa pabanja komanso kuti azipita kumisonkhano yampingo ndiponso ikuluikulu. Zimenezi n’zofunika kwambiri chifukwa zingawathandize kudzapulumuka. Choncho muziyesetsa kuthandiza ana anu kuti azisangalala pophunzira za Yehova ndiponso azizindikira kuti iye angawaphunzitse kukhala anzeru. (Miy. 24:14) Yesu anathandiza ophunzira ake kuti azilalikira mwakhama. Inunso muzithandiza ana anu achinyamata kuti azikonda kulalikira ndiponso kuphunzitsa Mawu a Mulungu.

7 Kodi nthawi zonse kuchita zinthu monga kuphunzira Baibulo, kupita kumisonkhano ndiponso kulalikira kungathandize bwanji ana anu achinyamata? Mlongo wina wa ku South Africa dzina lake Erin anati: “Tili ana tinkanyinyirika kuphunzira Baibulo, kupita kumisonkhano ndiponso kulalikira. Nthawi zina tinkachita dala zinthu zosokoneza n’cholinga choti tisachite phunziro la banja. Koma makolo athu sankalola kuti phunzirolo lilephereke.” Zimene makolowo ankachita zinathandiza mlongoyu kuona kuti zinthu zokhudza kulambira ndi zofunika kwambiri. Iye ananenanso kuti: “Ndikalephera kwa kanthawi kuchita zinthu zina potumikira Yehova ndimalakalaka kuti ndiyambirenso kuchita zinthuzo. Ngati makolo athu akanakhala olekerera pa zinthu zokhudza kulambira, bwenzi ndikuona kuti palibe vuto kujomba kumisonkhano, kolalikira kapena kuphunzira Baibulo.”

MUZIKHALA ODZICHEPETSA

8. (a) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ndi wodzichepetsa? (b) Kodi kudzichepetsa kwa Yesu kunathandiza bwanji ophunzira ake?

8 Ngakhale kuti Yesu anali wangwiro, ankadziwa malire a zimene angachite ndipo ankadalira kwambiri Yehova. (Werengani Yohane 5:19.) Kodi zimenezi zinachititsa kuti ophunzira ake asamamulemekeze? Ayi. Koma zinawathandiza kuti azimulemekeza kwambiri ndipo anatengera chitsanzo chake.—Mac. 3:12, 13, 16.

9. Kodi makolo akamavomereza zimene alakwitsa n’kupepesa amathandiza bwanji ana awo?

9 Mosiyana ndi Yesu, ifeyo ndife ochimwa ndipo timalakwitsa zinthu zambiri. Choncho makolo ayenera kukhala odzichepetsa n’kumavomereza akalakwitsa zinazake. (1 Yoh. 1:8) Kuchita zimenezi kungathandize kuti achinyamatawo aziwalemekeza ndiponso kuti nawonso azivomereza mosavuta akalakwitsa zinthu. Paja ambirife timalemekeza bwana amene amavomereza zimene walakwitsa, n’kupepesa. Mlongo wina dzina lake Rosemary ali ndi ana atatu ndipo anati: “Ine ndi mwamuna wanga tinkavomereza tikalakwitsa zinazake ndipo izi zinkachititsa kuti ana athu azimasuka nafe n’kumatiuza mavuto awo. Tinkazindikiranso kuti sitikudziwa zambiri. Choncho tinkapemphera limodzi ndi ana athu n’kuwathandiza kuti azifufuza malangizo m’Baibulo ndiponso m’mabuku athu.”

10. Kodi Yesu ankasonyeza bwanji kudzichepetsa popereka malamulo?

10 Yesu akanatha kungopereka malamulo kwa ophunzira ake oti azitsatira. Koma popeza kuti anali wodzichepetsa, ankawafotokozera chifukwa chimene akuperekera malamulowo. Mwachitsanzo, pamene ankawauza kuti azifunafuna Ufumu choyamba ndi chilungamo cha Mulungu, ananena kuti: “Ndipo zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu.” Komanso atawauza kuti: “Lekani kuweruza ena,” anawauzanso chifukwa chake. Iye anati: “Kuti inunso musaweruzidwe, pakuti chiweruzo chimene mukuweruza nacho ena inunso mudzaweruzidwa nacho.”—Mat. 6:31–7:2.

11. N’chifukwa chiyani makolo angachite bwino kuuza ana awo chifukwa chimene asankhira zinazake?

11 Ngati n’zotheka, nanunso muziwauza ana anu achinyamata chifukwa chimene chakuchititsani kusankha zinazake kapena kupereka lamulo linalake. Ana anu akamvetsa chifukwacho, sizingawavute kumvera. M’bale wina dzina lake Barry ali ndi ana 4 ndipo anati: “Kufotokoza zifukwa kumathandiza kuti ana anu azikudalirani chifukwa amaona kuti mumapereka malamulo muli ndi zifukwa zomveka.” Tizikumbukira kuti mosiyana ndi ana aang’ono, achinyamata amayamba kuganiza kwambiri ndiponso kusankha okha zochita. (Aroma 12:1) Ndiyeno Barry ananenanso kuti: “Achinyamata ayenera kuphunzira kusankha zinthu ataganizira kaye osati mopupuluma.” (Sal. 119:34) Choncho muzidzichepetsa n’kumauza ana anu achinyamata chifukwa chimene mwasankhira zinazake. Zimenezi zingawathandize kuti azisankha zochita mwanzeru ndiponso kuona kuti simuwaderera.

MUZIKHALA OZINDIKIRA NDIPONSO MUZIWAMVETSA

12. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ndi wozindikira pothandiza Petulo?

12 Yesu anali wozindikira ndipo ankadziwa mmene angathandizire ophunzira ake. Mwachitsanzo, pa nthawi ina Petulo anauza Yesu kuti adzikomere mtima n’cholinga choti asaphedwe. Koma Yesu anadziwa kuti maganizowa ndi olakwika. Choncho anathandiza Petulo komanso ophunzira ena onse kudziwa ubwino wa kudzipereka ndiponso kuipa kwa mtima woopa kuchita zimene Mulungu akufuna. (Mat. 16:21-27) Petulo anamvetsa mfundoyi ndipo anaphunzirapo kanthu.—1 Pet. 2:20, 21.

13, 14. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene zingasonyeze kuti chikhulupiriro cha mwana wanu chayamba kuchepa? (b) Kodi mungasonyeze bwanji kuzindikira pothandiza mwana wanu?

13 Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala wozindikira n’cholinga choti muzidziwa mmene mungathandizire ana anu. (Sal. 32:8) Mwachitsanzo, n’chiyani chingasonyeze kuti chikhulupiriro cha mwana wanu chayamba kuchepa? Kodi wayamba kumangodandaula za abale ndi alongo? Kapena kodi akuoneka kuti akukubisirani zinazake? N’zoona kuti si bwino kufulumira kuganiza kuti akuchita machimo ena akuluakulu ndipo wayamba moyo wachiphamaso. * Koma zimenezi sizikutanthauza kuti muzinyalanyaza ngati akuonetsa zizindikiro zoti ali ndi vuto linalake.

Muzichita zinthu zothandiza kuti ana anu apeze anzawo mumpingo (Onani ndime 14)

14 Kuti mudziwe mmene mungathandizire mwana wanu, muzimufunsa mafunso mokoma mtima ndiponso mwaulemu ngati mmene Yesu ankachitira. Mukamatunga madzi pachitsime mofulumira kwambiri, amatayika. Mofanana ndi zimenezi, kufunsa mwana wanu mafunso momupanikiza kungachititse kuti asakuuzeni maganizo ndiponso zolinga zake. (Werengani Miyambo 20:5.) llaria amene tamutchula kale uja ananena kuti: “Ndili wachinyamata ndinkafunitsitsa kucheza kwambiri ndi anzanga akusukulu ngakhale kuti ndinkadziwa kuti zimenezi sizingandithandize kutumikira Yehova. Ndiyeno makolo anga anazindikira kuti sindikusangalala, choncho tsiku lina anandifunsa ngati pali vuto linalake limene likundidetsa nkhawa. Ndinayamba kulira ndipo ndinawapempha kuti andithandize. Iwo anandikumbatira n’kundiuza kuti akumvetsa vuto langa ndipo andithandiza.” Nthawi yomweyo, makolo akewo anayamba kumuthandiza kuti apeze anzake abwino mumpingo.

15. Pochita zinthu ndi ena, kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anali wozindikira?

15 Yesu anasonyezanso kuti ndi wozindikira m’njira ina. Iye ankadziwa zimene ophunzira ake ankachita bwino ndiponso zimene ankalephera. Mwachitsanzo, Natanayeli atamva zoti Yesu wachokera ku Nazareti ananena kuti: “Kodi mu Nazareti mungatuluke kanthu kabwino?” (Yoh. 1:46) Kodi mukanakhala inuyo mukanaganiza kuti Natanayeli ndi munthu wotani? Mwina mukanaganiza kuti ndi watsankho, wopanda chikhulupiriro komanso wosaona zabwino zimene ena angachite. Koma Yesu anali wozindikira ndipo anaona kuti Natanayeli anali munthu woona mtima. Iye anati: “Onani Mwisiraeli ndithu, amene mwa iye mulibe chinyengo.” (Yoh. 1:47) Yesu ankatha kudziwa zimene zili mumtima mwa munthu ndipo ankagwiritsa ntchito luso limeneli kuti aone makhalidwe abwino a anthu ena.

16. Kodi mungathandize bwanji mwana wanu wachinyamata kuti akhale ndi makhalidwe abwino?

16 N’zoona kuti ife sitingadziwe zimene zili mumtima mwa munthu koma Yehova akhoza kutithandiza kukhala ozindikira. Iye angatithandize kuona makhalidwe abwino amene ana athu achinyamata ali nawo. Palibe amene amafuna kunenedwa kuti ndi wovuta. Choncho si bwino kulankhula kapena kuchita zinthu zosonyeza kuti mumaona kuti mwana wanuyo ndi wovuta kapena wosamvera. Ngakhale mwanayo atakukhumudwitsani, ndi bwino kumuuza kuti mumaona makhalidwe ake abwino ndipo mukudziwa kuti akufunitsitsa kuchita zabwino. Muziona akamayesetsa kusintha ndipo muzimuyamikira. Ngati n’kotheka, muzimusiya kuti apange yekha zinthu zina n’cholinga choti aziona kuti mumamudalira. Izi n’zimene Yesu ankachita ndi ophunzira ake. Patangopita chaka chimodzi ndi hafu kuchokera pamene anakumana ndi Natanayeli (dzina lake lina linali Batolomeyo), Yesu anamusankha kuti akhale mtumwi wake ndipo anadzakhala Mkhristu wolimba kwambiri. (Luka 6:13, 14; Mac. 1:13, 14) Mukamayamikira mwana wanu mumamuthandiza kuti asamadzikayikire ndipo amadziona kuti ndi Mkhristu wabwino amene Yehova akhoza kumugwiritsa ntchito m’gulu lake.

MUKAWAPHUNZITSA BWINO MUDZAKHALA OSANGALALA

17, 18. Kodi chingachitike n’chiyani mukamayesetsa kuthandiza ana anu achinyamata kuti azitumikira Yehova?

17 Mwina nthawi zina mukhoza kumva ngati mmene Paulo ankamvera akaganizira za anthu amene anawaphunzitsa za Yehova. Iye ankawakonda kwambiri ndipo ‘ankasautsika ndi kuzunzika kwambiri mumtima’ chifukwa chowadera nkhawa. (2 Akor. 2:4; 1 Akor. 4:15) M’bale wina dzina lake Victor ali ndi ana atatu ndipo anati: “Kulera ana athu pa nthawi imene anali achinyamata kunali kovuta. Koma zosangalatsa zinali zambiri kuposa zokhumudwitsa. Yehova anatithandiza kuti tizikondana kwambiri ndi ana athuwo.”

18 Musatope kuphunzitsa ana anu achinyamata kuti azitumikira Yehova. Mukatero mudzasangalala kwambiri kuona kuti akukonda Yehova ndiponso kumutumikira mokhulupirika.—3 Yoh. 4.